Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mumakhulupilila Kuti Muli ndi Coonadi? N’cifukwa Ciani?

Kodi Mumakhulupilila Kuti Muli ndi Coonadi? N’cifukwa Ciani?

‘Zindikilani cimene cili cifunilo ca Mulungu, cabwino, covomelezeka ndi cangwilo.’—AROMA 12:2.

1. N’ciani cimene atsogoleli a cipembedzo Acikristu anacita panthawi ya nkhondo?

KODI Mulungu amafuna kuti Akristu oona azipita ku nkhondo kukapha anthu amitundu ina? M’zaka 100 zapitazi, anthu odzicha Akristu ndi amene akhala akucita zimenezi. Atsogoleli acipembedzo a nkhondo acikatolika, amadalitsa magulu a nkhondo ndi zida zao pocita nkhondo ndi Akatolika a kumaiko ena. Atsogoleli acipulotesitanti naonso amacita cimodzimodzi. Pankhondo yaciŵili ya padziko lonse, ndi pamene anthu anaphedwa kwambili.

2, 3. Panthawi ya nkhondo yaciŵili ndi pambuyo pake, ndi kaimidwe kotani kamene Mboni za Yehova zinatenga? Nanga n’cifukwa ciani?

2 Nanga Mboni za Yehova zinacita bwanji panthawi ya nkhondo? Mbili imaonetsa kuti izo sizinatengeko mbali m’nkhondo. N’cifukwa ciani? Cifukwa cacikulu n’cakuti zinatsatila citsanzo ndi ziphunzitso za Yesu. Iye anati: “Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) Mboni zinatsatilanso kwambili malangizo amene mtumwi Paulo anapeleka kwa Akristu a ku Korinto.—Ŵelengani 2 Akorinto 10:3, 4.

 3 Motelo, Akristu oona, amene ali ndi cikumbumtima cophunzitsidwa Baibulo, saphunzila nkhondo kapena kutengako mbali m’nkhondo. Cifukwa cosaloŵelela m’nkhondo, masauzande a Mboni, acicepele ndi acikulile, amuna ndi akazi, amazunzidwa. Ambili a io amatengedwa kundende zimene amagwilitsa nchito ya kalavulagaga. Ena anaphedwa mu ulamulilo wa Nazi ku Germany. Mosasamala kanthu ndi cizunzo ca nkhanza cimene Mboni zinakumana naco ku Europe, izo sizinaiŵale nchito yao yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu wa Yehova. Zinalalikila mokhulupilika m’ndende, m’misasa ya cibalo ndi kumadela ena akutali. Pambuyo pake, mu 1994, Mboni ku Rwanda zinakana kuloŵelela m’nkhondo yofuna kuseselatu mtundu. Mboni zinakananso kutengako mbali pa nkhondo zimene zinacitika ku maiko a Balkans pamene ulamulilo wakale wa Yugoslavia unagwa.

4. Kusatengako mbali m’nkhondo kwa Mboni za Yehova kwakhudza bwanji owaona?

4 Kulimba mtima kwa Mboni za Yehova pankhani yosatengako mbali m’nkhondo, kwathandiza anthu masauzande ambili padziko lonse kudziŵa kuti Mboni zili ndi cikondi ceniceni pa Mulungu ndi pa anthu. M’mau ena, tingakambe kuti io ndi Akristu oona. Koma palinso mbali zina za kulambila kwathu zimene zathandiza anthu kudziŵa kuti Mboni za Yehova ndi Akristu oona.

NCHITO YAIKULU YOPHUNZITSA M’MBILI YONSE

5. Ndi kusintha kotani kumene ophunzila oyambilila a Kristu anakhala nako?

5 Kucokela pamene Yesu anayamba kulalikila, iye anagogomezela kufunika kolengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Iye anasankha atumwi ake 12 kuti ayale maziko a nchito ya padziko lonse. Pambuyo pake anaphunzitsa ophunzila ake 70. (Luka 6:13; 10:1) Anali okonzeka kukalalikila uthenga wabwino kwa ena. Coyamba anawalangiza kukalalikila kwa Ayuda, ndiyeno pambuyo pake anawauza kukalalikila kwa anthu amitundu ina. Ndithudi, kumeneku kunali kusintha kwakukulu kwa ophunzila acangu aciyuda!—Mac 1:8.

6. N’ciani cinacititsa kuti Petulo kuazindikile kuti Yehova alibe tsankho?

6 Mtumwi Petulo anatumidwa kupita kunyumba ya Koneliyo, munthu wakunja wosadulidwa. Ndiyeno, Petulo anazindikila kuti Mulungu alibe tsankho. Koneliyo ndi banja lake anabatizika. Ndipo cikristu cinayamba kufalikila ku magawo atsopano, ndipo anthu amitundu yonse analandila coonadi. (Mac. 10:9-48) Panthawiyo gawo lolalikila linakhala dziko lonse lapansi.

7, 8. Kodi gulu la Yehova lacita zinthu zotani? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

7 M’mbili ya makono ya Mboni za Yehova, aja amene akutsogolela nchito yolalikila amacita khama kulalikila ndi kuphunzitsa uthenga wabwino padziko lonse. Tsopano, pali Mboni zacangu pafupifupi 8 miliyoni. Ndipo izo zimafalitsa mwakhama uthenga wa Kristu m’zinenelo zoposa 600, ndipo zinenelo zina zikuonjezeka. Mboni za Yehova zimadziŵika cifukwa ca nchito yolalikila kunyumba ndi nyumba ndi m’miseu, ndipo nthawi zina zimagwilitsila nchito matebulo ndi mashelufu amawilo oikapo mabuku ndi magazini.

8 Anthu omasulila mabuku opitilila pa 2,900 alandila maphunzilo apadela owathandiza kumasulila Baibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo. Nchito yao si kumasulila zinenelo zikuluzikulu zokha. Iwo amamasulilanso mabuku m’zinenelo zina zambili zosachuka, koma zimene zimalankhulidwa ndi mamiliyoni a anthu. Mwacitsanzo,  ku Spain, mamiliyoni a anthu acikatalani, amakamba cinenelo cao ca Cikatalani nthawi zonse. Masiku ano, anthu amagwilitsila nchito cinenelo ca Cikatalani, ndi zinenelo zina zofanana naco m’zigawo za ku Andorra, Alicante, zilumba za Balearic, ndi ku Valencia. Tsopano, Mboni za Yehova zimafalitsa mabuku ofotokoza Baibulo m’Cikatalani. Ndipo anthu acikatalani apindula ndi misonkhano ya mpingo m’cinenelo cao.

9, 10. N’ciani cionetsa kuti gulu la Mulungu ndi lofunitsitsa kuthandiza anthu onse mwa kuuzimu?

9 Nchito yomasulila ndi kuphunzitsa imeneyi, ikucitika mobwelezabweleza m’zikhalidwe zosiyanasiyana. Ku Mexico, anthu ambili amakamba Cisipanishi, koma kulinso anthu ocepa amene amakamba zinenelo zina. Cimaya ndi cimodzi mwa zinenelo zimenezo. Nthambi ya ku Mexico, inatumiza kagulu ka omasulila cinenelo ca Cimaya kukakhala kudela la cineneloco, kuti azimva ndi kukamba cineneloco nthawi zonse. Citsanzo cina ndi dziko la Nepal kumene kuli anthu oposa 29 miliyoni. M’dzikolo muli zinenelo 120, ndipo anthu oposa 10 miliyoni amakamba Cinepali, koma ena ambili anangociphunzila. Mabuku athu ofotokoza Baibulo amafalitsidwanso m’cinenelo cimeneci.

10 Thandizo limene limapelekedwa kwa magulu omasulila mabuku padziko lonse, limaonetsa kuti gulu la Yehova limaona nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse kukhala yofunika kwambili. Padziko lonse lapansi, mamiliyoni a tumapepala twauthenga, tumabuku, ndi magazini zimagaŵilidwa panchito yapadela kwaulele. Nchito imeneyi imacilikizidwa ndi zopeleka zaufulu za Mboni za Yehova. Iwo amatsatila malangizo a Yesu akuti: “Munalandila kwaulele, patsani kwaulele.”—Mat. 10:8.

Omasulila mabuku akugwila nchito yao yomasulila m’Cijelemani (Onani ndime 8, 9)

Mabuku a Cijelemani amagwilitsidwa nchito ku Paraguay (Onaninso cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino)

11, 12. Nchito yolalikila ya padziko lonse ya Mboni za Yehova yathandiza anthu kuzindikila ciani?

11 Popeza kuti Mboni za Yehova ndi alaliki ndi aphunzitsi odzipeleka, io amakhulupilila kuti anapeza coonadi. Ndipo zimenezi zimawalimbikitsa kudzipeleka kuti azilalikila kwa anthu amitundu yonse ndi a zikhalidwe zosiyanasiyana. Kuti atengeko mbali panchito yofunika yolalikila imeneyi, ena afeŵetsa umoyo wao, aphunzila cinenelo ndi cikhalidwe cina. Nchito yolalikila ndi kuphunzitsa yapadziko lonse imeneyi, yathandizanso anthu ambili kudziŵa kuti  Mboni za Yehova ndi otsatila oona a Kristu Yesu.

12 Mboni zimacita zimenezi cifukwa zimakhulupilila kuti zapeza coonadi. Nanga n’ciani cina cacititsa anthu kukhulupilila kuti Mboni za Yehova zili ndi coonadi?—Ŵelengani Aroma 14:17, 18.

CIFUKWA CAKE AMAKHULUPILILA

13. Kodi Mboni zimacita ciani kuti gulu likhalebe loyela?

13 Tingapindule ndi ndemanga za Akristu acangu amakono, amene amakhulupilila kuti ali ndi coonadi. Mtumiki wina wa Yehova amene ndi ciyamba kale anafotokoza malingalilo ake motele: “Mboni zimayesetsa kusunga gulu la Yehova kukhala loyela ndi losadetsedwa. Ndipo cilango cimapelekedwa kwa aliyense amene walakwa.” Nanga Mboni zakwanitsa bwanji kutsatila miyezo ya pamwamba imeneyi? Izo zimatsatila miyezo ya m’Baibulo ndi citsanzo cimene Yesu ndi ophunzila ake anapeleka. Mbili ya makono ya Mboni za Yehova, ionetsa kuti ocepa acotsedwa mu mpingo cifukwa cosatsatila miyezo ya Mulungu. Koma ambili, kuphatikizapo aja amene kale anali ndi khalidwe losavomelezeka ndi Mulungu koma anasintha, apitilizabe ndi khalidwe lao labwino.—Ŵelengani 1 Akorinto 6:9-11.

14. N’ciani cimacitika munthu wocotsedwa akalapa? Nanga pakhala zotsatilapo zotani?

14 Baibulo limakamba mosapita m’mbali kuti ao amene satsatila malangizo a Mulungu ayenela kucotsedwa mumpingo. Zokondweletsa n’zakuti anthu masauzande alapa ndi kuleka khalidwe lao loipa, ndipo abwezedwa mumpingo. (Ŵelengani 2 Akorinto 2:6-8.) Kutsatila mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino kwathandiza mpingo kukhala woyela. Zimenezi zathandiza anthu kudziŵa kuti Mboni ndi zimene zili ndi coonadi. Ndipo anthu ambili amakhulupilila kuti Mboni za Yehova zilidi ndi coonadi, cifukwa zimasiyana ndi zipembedzo zimene zimalekelela makhalidwe oipa.

15. N’ciani cinathandiza m’bale wina kukhulupilila kuti ali ndi coonadi?

15 N’cifukwa ciani Mboni zimene zatumikila kwa zaka zambili zimakhulupilila kuti zinapeza coonadi? M’bale wina wa zaka 54 anati: “Kuyambila ndili mwana ndimakhulupilila kuti cikhulupililo canga n’cozikidwa pa mfundo zitatu izi: (1) kuti Mulungu aliko; (2) kuti ndi amene anauzila Baibulo; ndi (3) kuti masiku ano akugwilitsila nchito gulu la Mboni za Yehova ndi kulidalitsa. Pa kuphunzila kwanga Baibulo zaka zonsezi, nthawi zonse ndimayesa kuti ndione ngati ndikali kukhulupilila mfundo zimenezi. Caka ciliconse, ndimakhulupilila kwambili mfundo zimenezi, ndipo cidalilo canga cakuti tilidi ndi coonadi calimbilako.”

16. N’ciani cinacititsa cidwi mlongo wina ponena za coonadi?

16 Mlongo wina wokwatiwa amene akutumikila  ku likulu ku New York, anakamba izi ponena za gulu la Yehova: “Ndilo gulu lokha limene limalengeza dzina la Yehova mokhulupilika. Mau amenewa ndi oona cifukwa dzina la Mulungu limapezeka nthawi zokwanila 7,000 m’Baibulo. Lemba la 2 Mbiri 16:9 limandilimbikitsa. Limati: ‘Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wao uli wathunthu kwa iye.’” Anapitiliza kuti: “Coonadi candithandiza kukhala ndi mtima wathunthu kuti Yehova aonetse mphamvu zake kwa ine. Ndimaona kuti ubale wanga ndi Yehova n’cinthu cofunika kwambili. Ndipo ndimayamikila udindo wa Yesu pondithandiza kum’dziŵa bwino Mulungu. Zimenezi zandilimbikitsa kwambili.”

17. N’ciani cinacititsa cidwi munthu wina amene kale sanali kukhulupilila Mulungu? Ndipo n’cifukwa ninji?

17 Munthu wina amene kale sanali kukhulupilila Mulungu anati: “Cilengedwe cinandithandiza kukhulupilila kuti Mulungu amafuna kuti anthu azisangalala ndi moyo, conco sadzalola kuti mavuto apitilize kwamuyaya. Ndipo pamene dziko liipilaipila, anthu a Yehova apitiliza kulimbitsa cikhulupililo cao, kukhala acangu, ndi kukondana. Cozizwitsa ca makono cimeneci, catheka kokha cifukwa ca mzimu wa Yehova.”—Ŵelengani 1 Petulo 4:1-4.

18. Kodi ndemanga za abale aŵili zakukhudzani bwanji?

18 Mboni ina imene yatumikila kwa zaka zambili inachula cifukwa cake imakhulupilila coonadi cimene timalalikila. Inati: “Kuphunzila kwanga Baibulo zaka zonsezi, kwandithandiza kukhulupilila kuti Mboni zimayesetsa kwambili kutsatila citsanzo ca Akristu a m’nthawi ya atumwi. Pamene ndapita kumaiko osiyanasiyana, ndatsimikiza kuti Mboni za Yehova n’zogwilizana padziko lonse lapansi. Coonadi candithandiza kukhala wokhutila ndi wacimwemwe.” Pamene m’bale wina wa zaka za m’ma 60 anafunsidwa cifukwa cake amakhulupilila kuti wapeza coonadi, iye analoza kwa Yesu Kristu mwa kufotokoza kuti: “Tinaphunzila umoyo ndi utumiki wa Yesu mwakhama, ndipo timatsatila citsanzo cake. Tinasintha umoyo wathu kuti tiyandikile kwambili Mulungu kupyolela mwa Kristu Yesu. Tazindikila kuti nsembe ya dipo la Kristu ndiyo maziko a cipulumutso. Ndipo timakhulupilila kuti anaukitsidwa kwa akufa. Tili ndi umboni wodalilika wa anthu amene anaona ndi maso zimenezi.”—Ŵelengani 1 Akorinto 15:3-8.

TIYENELA KUCITANJI NDI COONADI?

19, 20. (a) Kodi Paulo anagogomezela ciani ku mpingo wa ku Roma? (b) Pokhala Akristu, tili ndi udindo wotani?

19 Pokhala Akristu timakonda anthu, ndipo timauzako anthu ena coonadi ca mtengo wapatali. Paulo anauza abale a ku mpingo wa ku Roma kuti: “Ngati ukulengeza kwa anthu ‘mau amene ali m’kamwa mwakowo,’ akuti Yesu ndiye Ambuye, ndipo mumtima mwako ukukhulupilila kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. Munthu amakhala ndi cikhulupililo mumtima mwake kuti akhale wolungama, koma ndi pakamwa pake amalengeza poyela cikhulupililo cake kuti apulumuke.”—Aroma 10:9, 10.

20 Pokhala Mboni za Yehova zodzipeleka, timakhulupilila kuti tili ndi coonadi, ndipo timazindikila udindo wathu wophunzitsa ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Conco, pamene tigwila nchito yathu yolalikila, anthu afunika kukhudzika mtima ndi zimene timawaphunzitsa kucokela m’Baibulo. Ndipo afunikanso kuona kuti cikhulupililo cathu n’colimba.