Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tumikilani Mulungu Mokhulupilika Panthawi ya “Masautso Ambili”

Tumikilani Mulungu Mokhulupilika Panthawi ya “Masautso Ambili”

“Tiyenela kukumana ndi masautso ambili kuti tikaloŵe mu ufumu wa Mulungu.”—MAC. 14:22.

1. N’cifukwa ciani masautso sawadabwitsa atumiki a Mulungu?

KODI timadabwa kuti tiyenela kukumana ndi “masautso ambili” tisanalandile mphoto ya moyo wosatha? Mwina iyai. Kaya takhala nthawi yaitali motani m’coonadi, timadziŵa kuti mavuto ndi osapeweka m’dziko la Satanali.—Chiv. 12:12.

2. (a) Kuonjezela pa mavuto amene amagwela anthu onse opanda ungwilo, ndi masautso ati amene Akristu amakumana nao? (Onani cithunzi pamwamba.) (b) Ndani amawacititsa? Tidziŵa bwanji?

2 Kuonjezela pa mavuto amene “amagwela anthu” onse opanda ungwilo, Akristu amakumananso ndi masautso a mtundu wina. (1 Akor. 10:13) Ndi masautso otani amenewo? Iwo amazunzidwa kwambili cifukwa comvela malamulo a Mulungu mokhulupilika. Yesu anauza otsatila ake kuti: “Kapolo sali wamkulu kuposa mbuye wake. Ngati anazunza ine, inunso adzakuzunzani.” (Yoh. 15:20) Ndani amacititsa citsutso cimeneci? Mosakaikila ndi Satana. Baibulo limamucha kuti “mkango wobangula” amene ‘afunitsitsa kuti ameze’ anthu a Mulungu. (1 Pet. 5:8) Satana angagwilitsile nchito njila iliyonse kuti aticititse kukhala osakhulupilika kwa Mulungu. Tiyeni tione zimene zinacitikila mtumwi Paulo.

 MASAUTSO KU LUSITARA

3-5. (a) Ndi masautso otani amene Paulo anakumana nao ku Lusitara? (b) Kodi mau ake onena za masautso a mtsogolo ndi olimbikitsa motani?

3 Nthawi zambili Paulo anali kuzunzidwa cifukwa ca kukhulupilika kwake. (2 Akor. 11:23-27) Panthawi ina iye anazunzidwa ku Lusitara. Pamene Paulo ndi mnzake Baranaba anacilitsa munthu amene anabadwa wolemala, anthu anawatamanda kuti ndi milungu. Iwo anapempha anthu amene anakondwelawo kuti asawalambile. Komabe, posakhalitsa Ayuda otsutsa anafika ndi kuyamba kulankhula zoipa ponena za Paulo ndi Baranaba. Mwamsanga anthuwo anasintha ndi kuyamba kuponya miyala Paulo cakuti anam’siya atakomoka.—Mac. 14:8-19.

4 Paulo ndi Baranaba atacoka ku Derbe, “anabwelela ku Lusitara, ku Ikoniyo ndi ku Antiokeya. M’malo onsewa anali kulimbitsa mitima ya ophunzila ndi kuwalimbikitsa kuti akhalebe m’cikhulupililo. Anali kuwauza kuti: ‘Tiyenela kukumana ndi masautso ambili kuti tikaloŵe mu ufumu wa Mulungu.’” (Mac. 14:21, 22) Mau amenewa ukangowamva samveka olimbikitsa. Mfundo yakuti anayenela kukumana ndi “masautso ambili” inaoneka kukhala yokhumudwitsa, osati yolimbikitsa. Nanga n’cifukwa ciani Paulo ndi Baranaba ‘analimbikitsa ophunzila’ mwa kuwauza kuti adzakumana ndi masautso ambili?

5 Tingapeze yankho mwa kupendanso bwinobwino mau a Paulo. Iye sanangokamba kuti: “Tiyenela kupilila masautso ambili.” M’malo mwake, anati: “Tiyenela kukumana ndi masautso ambili kuti tikaloŵe mu ufumu wa Mulungu.” Conco, Paulo analimbikitsa ophunzila pogogomezela kuti kukhulupilika kumabweletsa mphoto. Mphoto imeneyo si loto cabe. Ndiye cifukwa cake Yesu anati: “Yekhayo amene adzapilile mpaka pa mapeto ndi amene adzapulumuke.”Mat. 10:22.

6. Kodi anthu amene adzapilila adzalandila mphoto yotani?

6 Ngati tipilila tidzalandila mphoto. Akristu odzozedwa mphoto yao ndi moyo wosafa kumwamba, ndipo adzalamulila pamodzi ndi Yesu monga mafumu. Koma a “nkhosa zina” adzalandila moyo wosatha padziko lapansi mmene “mudzakhala cilungamo.” (Yoh. 10:16; 2 Pet. 3:13) Malinga ndi mau a Paulo, panthawi ino tidzakumanabe ndi masautso. Tsopano tiyeni tikambilane mitundu iŵili ya masautso amene tingakumane nao.

KUUKILA MWACINDUNJI

7. Ndi masautso otani amene tinganene kuti ndi acindunji?

7 Yesu anakambilatu kuti: “Anthu adzakupelekani kumakhoti aang’ono, ndipo adzakukwapulani m’masunagoge ndi kukuimikani pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu.” (Maliko 13:9) Mau amenewa aonetsa kuti Akristu adzakumana ndi masautso acindunji monga cizunzo. Nthawi zina atsogoleli acipembedzo kapena andale angacititse kuti tizunzidwe. (Mac. 5:27, 28) Koma ganizilaninso citsanzo ca Paulo. Kodi iye anacita mantha ataganizila za cizunzo? Kutalitali!—Ŵelengani Machitidwe 20:22, 23.

8, 9. Kodi Paulo anaonetsa bwanji kuti anali wofunitsitsa kupilila? Nanga abale ena masiku ano apilila bwanji cizunzo cacindunji?

8 Molimba mtima Paulo anapilila masautso acindunji, ndipo anati: “Moyo wanga sindikuuona ngati wofunika kapena wamtengo wapatali kwa ine ai. Cimene ndikungofuna n’cakuti ndimalize kuthamanga mpikisano umenewu, komanso kuti ndimalize utumiki umene ndinalandila kwa Ambuye Yesu basi. Ndikungofuna kucitila umboni mokwanila za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.” (Mac. 20:24) N’zoonekelatu kuti Paulo sanacite mantha cifukwa cakuti  adzakumana ndi mazunzo. M’malo mwake, iye anatsimikiza mtima kupilila zivute zitani. Colinga cake cinali “kucitila umboni mokwanila” mosasamala kanthu ndi mazunzo.

9 Masiku ano, abale ndi alongo athu ambili apitilizabe kukhala okhulupilika. Mwacitsanzo, ku dziko lina Mboni zinaikidwa m’ndende popanda kuimbidwa mlandu kukhoti. Zinakhala m’ndendemo zaka pafupifupi 20. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti zinakana kuloŵelela m’ndale. Kundendeko sanali kulola ngakhale acibale ao kudzawaona. Ndipo ena anali kumenyedwa koopsa ndi kuzunzidwa.

10. N’cifukwa ciani sitiyenela kuopa masautso a mwadzidzidzi?

10 Abale ndi alongo athu ena amapilila masautso amene amabwela mwadzidzidzi. Zimenezi zikadzacitika kwa inu musakagonje. Muzikumbukila Yosefe amene anagulitsidwa ku ukapolo, koma Yehova “anamulanditsa m’masautso ake onse.” (Mac. 7:9, 10) Yehova adzacitanso cimodzimodzi kwa inu. Musaiŵale kuti “Yehova amadziŵa kupulumutsa anthu odzipeleka kwa iye akakhala pa mayeselo.” (2 Pet. 2:9) Tili ndi zifukwa zabwino zodalila Yehova, ndi kupitiliza kupilila mayeselo molimba mtima. Dziŵani kuti Yehova adzatipulumutsa ku dongosolo la zinthu loipali ndi kutipatsa moyo wosatha.—1 Pet. 5:8, 9.

KUUKILA MWAKABISILA

11. Kuukila mwakabisila kwa Satana kusiyana bwanji ndi kuukila mwacindunji?

11 Mtundu wina wa masautso amene tingakumane nao ndi kuukila mwakabisila. Kodi kuukila kumeneku kusiyana bwanji ndi kuukila mwacindunji? Kuukila mwacindunji kuli monga cimphepo camphamvu cimene cacitika mwadzidzidzi ndi kuononga nyumba yanu nthawi imeneyo. Koma kuukila mwakabisila kuli monga ciswe cimene cimadya pang’onopang’ono mitengo ya nyumba yanu. Panthawi imene mudzazindikila kuti ciswe cadya nyumba ndi m’mbuyo mwa alendo n’kuti nyumbayo ili pafupi kugwa.

12. (a) Ndi macenjela akabisila ena ati a Satana? Nanga n’cifukwa ciani ndi amphamvu? (b) Kodi kulefuka kunam’khudza bwanji Paulo?

12 Colinga ca Satana ndi kuononga ubale wathu ndi Yehova. Iye angagwilitsile nchito cizunzo ca mwacindunji kapena ca mwakabisila kuti atifooketse. Zimenezi ndizo zida zake zamphamvu zimene amagwilitsila nchito. N’cifukwa ciani? Cifukwa pang’onopang’ono zimenezi zingaononge ubwenzi wathu ndi Yehova. Panthawi ina mtumwi Paulo analefuka ndipo anadzicha kuti “munthu wovutika.” (Ŵelengani Aroma 7:21-24.) N’cifukwa ciani Paulo, munthu “wokhwima” kuuzimu amene mwina anali m’bungwe lolamulila m’nthawi ya atumwi, anadzicha kuti “munthu wovutika”? Iye anakamba kuti anali kudzimva conco cifukwa ca kupanda ungwilo. Anali kufunitsitsa kucita cabwino, koma cinthu cina cinali kumulepheletsa. Ngati inu nthawi zina mumadzimva conco, mudzalimbikitsidwa kudziŵa kuti mtumwi Paulo anakumana ndi mavuto ofanana ndi anu.

13, 14. (a) N’ciani cimacititsa kuti anthu a Mulungu afooke? (b) Ndani amafuna kuononga cikhulupililo cathu? Nanga n’cifukwa ciani?

13 Nthawi zina abale ndi alongo ambili amalefuka, amada nkhawa, kapena amadziona kuti ndi acabecabe. Mwacitsanzo, mlongo wina amene ndi mpainiya wacangu anati: “Nthawi zambili ndikaganizila mobwelezabweleza zophophonya zanga, ndimadzimva wacabecabe. Ndikaganizila zolakwa zimene ndinacita, ndimaona monga kuti palibe amene angandikonde ngakhale Yehova amene.”

14 N’ciani cimacititsa atumiki ena acangu a Yehova, monga mlongo amene tachula, kulefuka? Pangakhale zifukwa zambili. Ena angakhale ndi cizoloŵezi codziimba  mlandu, ndipo ena cingakhale cifukwa ca mavuto amene amakumana nao. (Miy. 15:15) Ena amakhumudwa cifukwa ca matenda amene amawavutitsa maganizo. Kaya cifukwa cake cikhale cotani, tizikumbukila amene amafuna kutifooketsa. Nanga ndani amene amafuna kuti tifooke ndi kuleka kutumikila Yehova? Ndi Satana! Iye alibe ciyembekezo ndipo amafuna kuti nafenso tizidziona kuti tilibe ciyembekezo. (Chiv. 20:10) Colinga ca Satana pogwilitsila nchito cizunzo ca mwacindunji kapena ca mwakabisila, ndi kufuna kuti atifooketse mwa kuuzimu kuti tileke kutumikila Mulungu. Conco, tisagonje cifukwa tili pankhondo ya kuuzimu yomenyela cikhulupililo cathu.

15. Malinga ndi 2 Akorinto 4:16, 17, tatsimikiza mtima kucitanji?

15 Tiyeni tiyesetse kuti tisagonje pa nkhondo imeneyi, ndipo tidziyang’anitsitsa pa mphoto. Paulo analembela Akristu a ku Korinto kuti “Sitikubwelela m’mbuyo. Koma ngakhale munthu wathu wakunja akutha, ndithudi munthu wathu wamkati akukhalitsidwanso watsopano tsiku ndi tsiku. Pakuti ngakhale kuti masautso amene tikukumana nao ndi akanthawi ndipo ndi opepuka, masautsowo akuticititsa kuti tilandile ulemelelo umene ukukulilakulila komanso wamuyaya.”—2 Akor. 4:16, 17.

KONZEKELANI MASAUTSO TSOPANO

Akristu acicepele ndi acikulile akuphunzila mmene angatetezele cikhulupililo cao (Onani ndime 16)

16. N’cifukwa ciani ndi bwino tsopano kukonzekelelatu masautso?

16 Satana ali ndi “zocita zacinyengo” zambili zimene amagwilitsila nchito. (Aef. 6:11) Ndiye cifukwa cake tiyenela kutsatila cenjezo la pa 1 Petulo 5:9 limene limati: “Khalani olimba m’cikhulupililo ndipo mulimbane naye.” Kuti ticite zimenezo tiyenela kukonzekeletsa maganizo ndi mtima wathu tsopano, kuti tikhale okonzeka kucita cabwino. Mwacitsanzo, asilikali asanapite kunkhondo, amaphunzitsidwa mwapadela  kuti akhale okonzeka kumenya nkhondo. N’cimodzimodzi ndi ife asilikali a kuuzimu a Yehova. Conco, ndi kwanzelu kukonzekela masautso pasadakhale. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu kuti: “Pitilizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali olimba m’cikhulupililo. Pitilizani kudziyesa kuti mudziŵe kuti ndinu munthu wotani.”—2 Akor. 13:5.

17-19. (a) Tingadziŵe bwanji kuti cikhulupililo cathu n’colimba? (b) Acicepele angakonzekele bwanji kuteteza cikhulupililo cao ku sukulu?

17 Njila imodzi imene tingadziyesele ndi mwa kudzifunsa mafunso monga akuti: ‘Kodi ndimapemphela nthawi zonse? Ena akandisonkhezela kucita zoipa, kodi ndimamvela Mulungu monga wolamulila kuposa anthu? Kodi ndimasonkhana mokhazikika? Nanga ndimalankhula molimba mtima za cikhulupililo canga? Kodi ndimakhululukila mwamsanga zolakwa za abale anga monga mmene ndimafunila kuti io andikhululukile? Nanga ndimagonjela akulu a mpingo wathu ndi aja amene amayang’anila mipingo padziko lonse?’

18 Onani kuti aŵili pa mafunso amenewa, akamba za kuteteza cikhulupililo cathu molimba mtima ndi kusatengela zocita za anzathu. Acicepele athu ambili amacita zimenezi ku sukulu, ndipo sacita manyazi kapena kuopa. N’ciani cawathandiza kulankhula molimba mtima? Iwo amagwilitsila nchito mfundo zopezeka m’magazini athu. Mwacitsanzo, mu Galamukani! ya July 2009, muli mfundo yakuti ngati mnzanu wotsutsa ku sukulu wakufunsani kuti: “N’cifukwa ciani sukhulupilila cisanduliko?” mungangoyankha kuti: “N’cifukwa ciani ndifunikila kukhulupilila cisanduliko? Ngakhale asayansi amene ndi akatswili, sagwilizana pankhani ya cisanduliko.” Makolo muyenela kumakambilana ndi ana anu njila zimene angatetezele cikhulupililo cao ku sukulu.

19 N’zoona kuti si nthawi zonse pamene tingalankhule kapena kucita zinthu zimene Yehova afuna kuti ticite. Nthawi zina pambuyo pogwila nchito maola ambili tingadzikakamize kupita ku misonkhano. Kuuka m’maŵa kuti tipite mu ulaliki nthawi zina kungafune kuti tidukize tulo. Komabe, kumbukilani kuti: Kucita zinthu za kuuzimu nthawi zonse kungakuthandizeni kulimbana ndi mayeselo aakulu mtsogolo.

20, 21. (a) Kuganizila mozama za dipo kudzatithandiza motani kugonjetsa maganizo olefula? (b) Mosasamala kanthu za masautso, kodi tiyenela kucitanji?

20 Nanga bwanji za kuukila mwakabisila? Mwacitsanzo, tingagonjetse bwanji maganizo olefula? Njila imodzi yaikulu imene tingacitile zimenezo ndiyo kuganizila mozama za dipo. N’zimene mtumwi Paulo anacita. Iye nthawi zina anali kudzimva monga munthu wovutika. Koma anadziŵa kuti Kristu sanafele anthu angwilo, koma ocimwa monga iye. Ndiye cifukwa cake analemba kuti: “Moyo umene ndikukhala tsopano, ndikukhala mokhulupilila Mwana wa Mulungu, amene anandikonda ndi kudzipeleka yekha cifukwa ca ine.” (Agal. 2:20) Paulo anakhulupililadi dipo, ndipo anazindikila kuti limagwilanso nchito kwa iye.

21 Nafenso tingapindule kwambili ngati tikhulupilila kuti dipo ndi mphatso yathu yocokela kwa Yehova. Koma zimenezi sizitanthauza kuti sitidzakumana ndi zinthu zokhumudwitsa. Ena adzapitilizabe kupilila masautso a mwakabisila mpaka m’dziko latsopano. Ndipo tizikumbukila kuti: Amene adzalandila mphoto ndi aja amene amapilila. Tsiku lililonse timayandikila nthawi imene Ufumu wa Mulungu udzabwela. Ufumuwo ukadzabwela, padziko padzakhala mtendele, ndipo anthu onse adzakhala angwilo. Conco, kaya tikumane ndi masautso ambili motani, tiyeni ticite zimene tingathe kuti tikaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.