Kodi mukukumbukila?
Kodi mwaŵelenga mosamala magazini aposacedwapa a Nsanja ya Mlonda? Yesani kuyankha mafunso otsatilawa:
Tingatsimikize bwanji kuti Mulungu sindiye amacititsa zinthu zoipa?
Mulungu ndi wolungama m’njila zake zonse.Iye ndi wolungama, wokhulupilika, ndi woongoka. Yehova ndi wacikondi cacikulu ndi wacifundo.(Deut. 32:4; Sal. 145:17; Yak. 5:11)—July-August, tsamba 4.
Ndi mavuto atatu ati amene ofalitsa osamukila ku maiko ena kumene kulibe ofalitsa Ufumu okwanila angakumane nao?
Mavuto amenewo ndi (1) kuzoloŵela umoyo watsopano, (2) kuyewa kunyumba [acibale] (3) kuzoloŵelana ndi abale a kumeneko. Ofalitsa ambili amene apitilizabe kutumikila m’maiko ena mosasamala kanthu za mavutowa apeza madalitso oculuka.—7/15, tsamba 4-5.
N’cifukwa ciani abale a Yosefe anali kudana naye?
Cifukwa cimodzi cinali cakuti Yakobo anali kukonda kwambili Yosefe, ndipo anamupatsa mkanjo wapadela. Zimenezo zinapangitsa kuti abale ake am’citile nsanje kwambili moti anamugulitsa ku ukapolo.—September-October, tsamba 11-13.
N’cifukwa ciani tumapepala twauthenga twatsopano n’tothandiza kwambili ndiponso tosavuta kugaŵila?
Tumapepala tonse twatsopano twauthenga tunalembedwa mofanana. Kapepala kalikonse kali ndi lemba limene timaŵelenga ndi funso limene timafunsa mwininyumba. Kaya yankho lake ndi lotani, timamuonetsa mkati mwa kapepalako ndi kumusonyeza zimene Baibulo limanena. Timamuonetsanso funso lofunika kudzakambilana ulendo wotsatila.—8/15, tsamba 13-14.
Kodi makolo acikristu angacite ciani kuti aŵete ana ao?
Makolo afunika kumvetsela ana ao akamalankhula kuti awadziŵe bwino. Ayenela kuyesetsa kuwadyetsa bwino mwakuuzimu. Ayenelanso kuwatsogo lela mwacikondi makamaka akayamba kukaikila zinthu zina zimene timaphunzila m’Baibulo.—9/15, tsamba 18-21.
Ndi pangano liti lopezeka m’Baibulo limene limapangitsa kuti zikhale zotheka kuti anthu ena akalamulile ndi Kristu?
Yesu atamaliza kudya Pasika womaliza pamodzi ndi atumwi ake, iye anacita pangano ndi ophunzila ake okhulupilika. Pangano limeneli limachedwa pangano la Ufumu. (Luka 22:28-30) Pangano limeneli linawatsimikizila kuti adzalamulila naye limodzi kumwamba.—10/15, tsamba 16-17.
Kodi “anthu odziŵika ndi dzina lake” amene Yakobo anakamba pa Machitidwe 15:14, ndani?
Amenewa ndi Ayuda ndiponso anthu a mitundu ina okhulupilila amene Mulungu anawasankha kukhala mtundu wapadela ‘kuti alengeze makhalidwe abwino kwambili’ a amene anawaitana. (1 Pet. 2:9, 10)—11/15, tsamba 24-25.