Kodi Muyenela Kusintha Maganizo Anu?
PA NTHAWI ina, Akristu ena acinyamata anaganiza zopita kukapenyelela vidiyo ku malo oonetsela mavidiyo. Iwo anamva kuti anzao ambili a kusukulu anasangalala kwambili atapenyelela vidiyo imeneyo. Atafika ku malowo, anaona zithunzithunzi za zida zoopsa za nkhondo ndi za akazi ovala zovala zoonetsa thupi. Kodi io akanacita ciani? Kodi anafunika kulowabe mkati kukapenyelela vidiyoyo?
Citsanzoci, cikutionetsa mfundo yakuti zosankha zambili zimene timapanga zingalimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova kapena kuuononga. Nthawi zina, mungafune kucita cinacake, koma pambuyo poganizilapo bwino, mungasinthe maganizo anu. Kodi zimenezo zingasonyeze kuti ndinu munthu wokayikakayika? Nanga kusinthako n’koyenela?
Pamene Simuyenela Kusintha Maganizo Anu
Cikondi ndi cimene cinatilimbikitsa kudzipeleka kwa Yehova ndi kubatizidwa. Colinga cathu ndi kukhalabe wokhulupilika kwa Mulungu. Komabe, mdani wathu Satana Mdyelekezi amafuna kuononga cikhulupililo cathu. (Chiv. 12:17) Tinapanga cosankha cotumikila Yehova ndi kusunga malamulo ake. Zingakhale zomvetsa cisoni ngati tingasinthe maganizo athu pankhani yokhudza kudzipeleka kwa Yehova, cifukwa zimenezi zingapangitse kuti tidzaonongedwe.
Zaka zoposa 2,600 zapitazo, Mfumu Nebukadinezara wa ku Babulo anaimika fano lina lalikulu la golide, ndipo anapeleka lamulo lakuti aliyense ayenela kuwelamila fanolo ndi kulilambila. Aliyense amene akanalephela kucita zimenezo anayenela kuponyedwa m’ng’anjo yoyaka moto. Sadirake, Mesake ndi Abedinego, anyamata atatu amene anali oopa Yehova, anakana kutsatila lamulo limenelo. Popeza kuti anyamata amenewa anakana kugwadila fanolo, io anaponyedwa m’ng’anjo yoyaka moto. Yehova anawapulumutsa modabwitsa, ngakhale kuti io anali okonzeka kuphedwa m’malo mosokoneza ubwenzi wao ndi Mulungu.—Dan. 3:1-27.
Patapita nthawi, mneneli Danieli analimbikila kupemphela ngakhale kuti anali atamuopyeza kuti adzaponyedwa m’dzenje la mikango. Iye sanaleke cizoloŵezi cake copemphela kwa Yehova katatu pa tsiku. Danieli sanafune kusintha maganizo ake pankhani yolambila Mulungu woona. Pa cifukwa cimeneci, mneneli ameneyu anapulumutsidwa “kwa mikango.”—Dan. 6:1-27.
Atumiki a Mulungu amakono amakhala ndi moyo wosonyeza kuti anadzipeleka kwa iye. Pa sukulu inayake mu Africa muno, gulu la ana a sukulu amene ndi a Mboni za Yehova linakana kucita nao mwambo wolambila mbendela. Iwo anauzidwa kuti adzacotsedwa sukulu akakana kucita mwambowo. Patapita nthawi yocepa, nduna ya zamaphunzilo ya m’dzikolo inapita ku tauni kumene kuli sukuluyi, ndipo inakambilana ndi ana a sukulu ena a Mboni. Acinyamatawa anafotokoza cikhulupililo cao mwaulemu koma mopanda mantha. Kuyambila nthawi imeneyo, io sanavutitsidwenso pa nkhani imeneyi. Acinyamata a Mboni amenewo sacita mantha kuti adzakakamizidwa kucita zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wao ndi Yehova.
Ganizilaninso za a Joseph, amene akazi ao anamwalila mwadzidzidzi atadwala matenda a kansa. Acibale ao analemekeza cikhulupililo cao pankhani ya mwambo wa malilo. Komabe acibale a akazi ao si Mboni, ndipo anafuna kucita miyambo ina yosakondweletsa Mulungu poika malilo. A Joseph anakamba kuti: “Poona kuti analephela kundigonjetsa, anayamba kunyengelela ana anga koma ionso anakana kucita miyamboyo. Acibalewo anagwilizana zakuti acite mwambo wogona pamalilo koma ndinawaletsa, ndipo ndinawauza kuti ngati aumilila, sayenela kucitila pa nyumba panga mwambowo. Iwo anali kudziŵa kuti kucita mwambowo kunali kosagwilizana ndi zikhulupililo zanga ndi za mkazi wanga. Conco pambuyo pokambilana kwa nthawi yaitali io anakacitila kwina mwambo umenewo.
“Panthawi yovutayi, ndinacondelela Yehova kuti athandize banja langa kukhalabe lokhulupilika. Mulungu anamva mapemphelo anga, ndipo anatithandizadi kukhala olimba mosasamala kanthu za ziyeso zimene tinakumana nazo.” A Joseph ndi ana ao anakanilatu kusintha maganizo ao pankhani yokhudza kulambila.
Pamene Mungasankhe Kusintha Maganizo Anu Kapena Ai
Mayi wina wacisurofoinike anafikila Yesu Kristu ku dela la Sidoni mwamsanga pambuyo pa Pasika wa mu 32 C.E. Iye anali kupempha Yesu mobwelezabweleza kuti akatulutse ciŵanda mwa mwana wake wamkazi. Poyamba Yesu sanamuyankhe ciliconse. Anauza ophunzila ake kuti: “Ine sananditumize kwa wina aliyense koma kwa nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.” Pamene mayiyo analimbikila, Yesu anakamba kuti: “Si bwino kutenga cakudya ca ana n’kuponyela tiagalu.” Pofuna kuonetsa kuti anali ndi cikhulupililo cacikulu mwa Yesu, maiyo anayankha kuti: “Inde Ambuye, komatu tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa patebulo la ambuye ao” Yesu anacita mogwilizana ndi pempho la mayiyo, ndipo anacilitsa mwana wake.—Mat. 15:21-28.
Mwakucita zimenezo, Yesu anali kutengela citsanzo ca Yehova cokhala wofunitsitsa kusintha ngati pakufunika kutelo. Mwacitsanzo, Mulungu anafuna kuononga Aisiraeli pamene anapanga fano la mwana wa ng’ombe wa golide, koma Mose atamucondelela, iye anasintha maganizo Ake.—Eks. 32:7-14.
Mtumwi Paulo anatengela citsanzo ca Yehova ndi Yesu. Kwa kanthawi ndithu, Paulo sanali kufuna kuyenda ndi Yohane Maliko pa maulendo ao aumishonale cifukwa panthawi ina Maliko anasiya Paulo ndi anthu ena paulendo wao woyamba waumishonale. Koma patapita nthawi, Paulo anazindikila kuti Maliko anakhala wakhama ndi kuti akanatha kumuthandiza pa utumiki wake. Motelo Paulo anauza Timoteyo kuti: “Pobwela utengenso Maliko, pakuti iye ndi wofunika kwa ine cifukwa amandithandiza pa utumiki wanga.”—2 Tim. 4:11.
Nanga bwanji ife? Potengela citsanzo ca Atate wathu wakumwamba amene ndi wacifundo, woleza mtima ndi wacikondi, nthawi zina tingaone kuti tifunika kusintha maganizo athu. Mwacitsanzo, tingafunike kusintha mmene timaonela anthu ena. Mosiyana ndi Yehova ndi Yesu, ife ndife opanda ungwilo. Popeza kuti Mulungu ndi Yesu ndi okonzeka kusintha maganizo ao, ifenso tiyenela kuganizila zifukwa zimene zapangitsa munthu kucita zinthu mwa njila ina yake ndi kusintha maganizo athu.
Kusintha maganizo kungakhale kofunika pankhani yokhudza zolinga zakuuzimu. Anthu ena amene timaphunzila nao Baibulo ndiponso amene akhala akusonkhana nafe kwa nthawi yaitali, amazengeleza kubatizidwa. Naonso ofalitsa ena amene angathe kucita upainiya, amazengeleza kuyamba utumiki umenewo. Komanso abale ena safuna kukalamila maudindo mumpingo. (1 Tim. 3:1) Pa zinthu zimene tachulazi, kodi pali cimene muona kuti mufunika kuongolela? Mwacikondi, Yehova amafuna kuti mukhale ndi mwai womutumikila ndi kuonjezela utumiki wanu. Conco, mungacite bwino kusintha maganizo anu, ndipo mukatelo mudzasangalala kutumikila Mulungu ndi anthu ena.
Ella, amene akutumikila pa ofesi ina ya nthambi ya Mboni za Yehova mu Africa muno anati: “Pamene ndinangofika pa Beteli, ndinaona monga sindidzakhalitsapo. Ndinali kufuna kutumikila Yehova ndi moyo wanga wonse, koma ndinali kukondanso kwambili acibale anga. Poyamba ndinali kuwasoŵa kwambili acibale anga. Koma mnzanga amene ndinali kukhala naye m’cipinda cimodzi anali kundilimbikitsa. Conco ndinaganiza zopitiliza kutumikila. Tsopano ndakhala ndikutumikila pa Beteli kwa zaka 10, ndipo ndifuna kupitilizabe kuthandiza abale ndi alongo mwa kutumikila pa Beteli.”
Pamene Mufunikadi Kusintha Maganizo Anu
Kodi mukumbukila zimene zinacitikila Kaini pamene anakwiila kwambili m’bale wake cifukwa ca nsanje? Mulungu anauza mwamuna wokwiya ameneyu kuti ngati angasinthe ndi kucita cabwino, iye adzamuyanja. Mulungu anauza Kaini kuti agonjetse ucimo umene unali ‘utamyata pakhomo kumudikilila.’ Kaini akanafuna, akanasintha maganizo ake, koma anasankha kunyalanyaza uphungu wa Mulungu. N’zacisoni kuti Kaini anapha m’bale wake, ndipo anakhala woyamba kupha munthu.—Gen. 4:2-8.
Taganizilaninso citsanzo ca Mfumu Uziya. Poyamba, iye anali kucita zoyenela pamaso pa Yehova ndipo anali kufunafuna Mulungu. Koma n’zomvetsa cisoni kuti Uziya anaononga mbili yake pamene anakhala wodzikuza. Iye analoŵa m’kacisi kukapeleka nsembe ngakhale kuti sanali wansembe. Kodi iye anasintha maganizo ake pamene ansembe anamucenjeza za khalidwe lake lodzikuza? Iyai. M’malomwake, Uziya “anakwiya kwambili,” ndipo ananyalanyaza cenjezo lao. Ndiyeno Yehova anamukantha ndi khate.—2 Mbiri 26:3-5, 16-20.
Zoona, nthawi zina timafunikadi kusintha maganizo athu. Taganizilani citsanzo camakono ici: Joachim anabatizidwa mu 1955, koma mu 1978 anacotsedwa mumpingo. Patapita zaka 20, iye analapa ndipo anabwezeletsedwa mumpingo monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Posacedwapa, mkulu wina anamufunsa cifukwa cake anatenga nthawi yaitali asanapemphe kubwezeletsedwa mumpingo. Joachim anayankha kuti: “Ndinali wokhumudwa ndi wonyada. Koma ndimadzimvela cisoni poona kuti ndinatenga nthawi yaitali ndisanapemphe kubwezeletsedwa. Ngakhale pamene ndinali wocotsedwa, ndinali kudziŵa kuti Mboni za Yehova zimaphunzitsa coonadi.” Ndithudi, Joachim anafunika kusintha maganizo ndi kulapa.
Malinga ndi zocitika paumoyo, nthawi zina tingafunike kusintha maganizo athu ndi zocita zathu. Tiyeni tizikhala ofunitsitsa kusintha n’colinga cofuna kukondweletsa Yehova.—Sal. 34:8.