Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mumayamikila Zimene Munalandila?

Kodi Mumayamikila Zimene Munalandila?

‘Tinalandila mzimu wocokela kwa Mulungu, kuti tidziŵe zinthu zimene Mulungu watipatsa mokoma mtima.’—1 AKOR. 2:12.

1. Ndi mwambi wotani umene anthu ena amakonda kukamba?

ANTHU ena anamvapo mwambi wakuti: ‘Munthu amaona kufunika kwa citsime madzi akauma.’ Kodi inunso mumaona conco? Anthu ambili amene anakulila m’mabanja ocita bwino, okhala ndi zinthu zambili zabwino, samaona kufunika kwa zinthuzo. Ndipo zimenezi n’zofala pakati pa acinyamata amene sasamala katundu cifukwa sanakumanepo ndi mavuto.

2, 3. (a) Kodi acinyamata acikristu ayenela kupewa ciani? (b) N’ciani cingatithandize kukhala oyamikila?

2 Ngati ndinu wacinyamata wazaka zosakwana 20 kapena kuposelapo pang’ono, kodi cinthu cofunika kwambili kwa inu n’ciani? Anthu ambili m’dzikoli amakonda kukhala ndi zinthu zambili za kuthupi, kulandila malipilo oculuka, kukhala ndi nyumba yabwino kapena zipangizo zina za makono. Ngati timaona kuti zinthu zimenezi ndizo zofunika, ndiye kuti tikusoŵa cinthu cina cofunika kwambili cimene ndi cuma cakuuzimu. Koma n’zomvetsa cisoni kuti ambili sanayambe kufunafuna cuma cakuuzimu cimeneci. Inu acinyamata amene munaleledwa ndi makolo amene ndi a Mboni za Yehova, muyenela kukhala osamala kwambili kuti musataye colowa cakuuzimu cimene munalandila. (Mat. 5:3) Kukhala osayamikila kungacititse kuti mukumane ndi zinthu zoipa zimene zingakhudze umoyo wanu wonse.

3 Koma inu mukhoza kupewa zimenezi. N’ciani cingakuthandizeni kuyamikila colowa canu cakuuzimu? Tiyeni tikambilane  zitsanzo zina za m’Baibulo zimene zidzatithandiza kuona ubwino woyamikila colowa cathu cakuuzimu. Zitsanzo zimene tidzakambilana zidzatithandiza tonse kaya ndife acinyamata kapena acikulile kuyamikila zinthu zakuuzimu zimene tinalandila.

ANALI OSAYAMIKILA

4. N’ciani cimene lemba la 1 Samueli 8:1-5 limavumbula ponena za ana a Samueli?

4 M’Baibulo muli zitsanzo za anthu ambili amene analandila colowa cakuuzimu koma analephela kukhala oyamikila. Zimenezi n’zimene zinacitika m’banja la mneneli wina dzina lake Samueli amene anali ndi mbili yabwino, ndipo anayamba kutumikila Yehova ali mwana kwambili. (1 Sam. 12:1-5) Samueli anapeleka citsanzo cabwino cimene ana ake Yoweli ndi Abiya, anali kufunika kutsatila. Koma io sanatsatile citsanzo ca atate ao ndipo anakhala anthu oipa. Baibulo limatiuza kuti mosiyana ndi atate ao anawa anali “kupotoza ciweluzo.”—Ŵelengani 1 Samueli 8:1-5.

5, 6. Kodi ana a Yosiya ndiponso mdzukulu wake anadzakhala anthu otani?

5 Ndi mmenenso zinalili ndi ana a Mfumu Yosiya. Yosiya anali citsanzo cabwino pankhani yolambila Yehova. Buku la cilamulo ca Mulungu litapezeka ndi kuŵelengedwa pamaso pa Yosiya, iye anayesetsa kugwilitsila nchito malangizo a Yehova. Anathetsa kulambila mafano ndi kukhulupilila mizimu m’dzikolo, ndipo analimbikitsa anthu kuti azimvela Yehova. (2 Maf. 22:8; 23: 2, 3, 12-15, 24, 25) Ana ake anali ndi colowa cakuuzimu cabwino kwambili cakuti m’kupita kwa nthawi, ana ake aamuna atatu ndi mdzukulu wake mmodzi anadzakhala mafumu. Koma n’zomvetsa cisoni kuti onsewa sanayamikile colowa ca Yosiya.

6 Yosiya atamwalila, mwana wake Yehoahazi anayamba kulamulila monga mfumu, koma anali “kucita zoipa pamaso pa Yehova.” Yehoahazi anangolamulila kwa miyezi itatu, kenako anamangidwa ndi Farao wa ku Iguputo, ndipo anafela kumeneko. (2 Maf. 23: 31-34) Ndiyeno m’bale wake, Yehoyakimu analamulila kwa zaka 11. Iyenso analephela kuyamikila colowa ca atate wake. Cifukwa ca khalidwe loipa la Yehoyakimu, Yeremiya analosela kuti: “Adzaikidwa m’manda ngati mmene amaikila bulu wamphongo.” (Yer. 22: 17-19) Zedekiya mwana wa Yosiya ndiponso mdzukulu wake Yehoyakini naonso analephela kutengela citsanzo cabwino ca Yosiya.—2 Maf. 24: 8, 9, 18, 19.

7, 8. (a) Kodi Solomo anaononga bwanji colowa cake cakuuzimu? (b) N’ciani cimene tikuphunzila pa zitsanzo za anthu a m’Baibulo amene anaononga colowa cao cakuuzimu?

7 Solomo anali mfumu imene inalandila zambili kucokela kwa atate ake, Davide. Ngakhale kuti Solomo anacokela ku banja lokonda kwambili zinthu zauzimu, ndipo poyamba anali mfumu yabwino, m’kupita kwa nthawi anaononga colowa cake cakuuzimu. “Pamene iye anali kukalamba, akazi ake anali atapotoza mtima wake moti iye anali kutsatila milungu ina. Sanatumikile Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu monga mmene anacitila Davide bambo ake.” (1 Maf. 11:4) Conco, Yehova anasiya kukonda Solomo.

8 N’zomvetsa cisoni kuti anthu amene analeledwa m’mabanja abwino, ndipo anali ndi mwai woti akanacita zinthu zabwino, analephela kuyamikila zimene anapatsidwa. Koma si acinyamata onse a m’nthawi za m’Baibulo amene anali osayamikila. Ngakhale masiku ano, alipo acinyamata amene amayamikila zinthu zauzimu. Tiyeni tikambilane zitsanzo za acinyamata ena zimene Akristu acinyamata angatengele.

ANAYAMIKILA ZIMENE ANALANDILA

9. N’ciani cimene cinapangitsa ana a Nowa kukhala citsanzo cabwino kwambili? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

9 Tili ndi citsanzo cabwino kwambili ca ana a Nowa. Atate ao analamulidwa kumanga  cingalawa ndi kulowetsamo banja lao lonse. Ana a Nowa anazindikila kufunika kocita cifunilo ca Yehova, ndipo anagwilizana ndi zocita za atate ao. Anawo anathandiza atate ao kumanga cingalawa, kenako onse analowamo. (Gen. 7: 1, 7) Kodi io anali ndi colinga cotani? Lemba la Genesis 7:3 limakamba kuti analowetsa nyama m’cingalawa “kuti zisungike padziko lonse lapansi.” Naonso anthu anapulumutsidwa. Popeza kuti ana a Nowa anayamikila colowa cao cakuuzimu, io anali ndi mwai wopititsa patsogolo mtundu wa anthu ndiponso kubwezeletsa kulambila koyela padziko lapansi loyeletsedwa.—Gen. 8: 20; 9: 18, 19.

10. Kodi anyamata anai aciheberi amene anali ku Babulo anaonetsa bwanji kuyamikila coonadi cimene anaphunzila?

10 Pambuyo pa zaka zambili, anyamata anai aciheberi anasonyeza kuti anali kudziŵa cimene cinali cofunika kwambili. Hananiya, Misayeli, Azariya ndi Danieli, anatengedwa ku ukapolo mu 617 B.C.E. Anyamata amenewo anali okongola kwambili, anzelu, ndipo sizikanawavuta kutengela umoyo wa ku Babulo. Koma io anakana kutengela umoyo wa kumeneko. Zimene io anali kucita zinasonyeza kuti sanaiwale colowa cao, kapena kuti zimene io anaphunzitsidwa. Anyamata amenewa anadalitsidwa kwambili cifukwa cotsatila mfundo zakuuzimu zimene anaphunzitsidwa ali ana.—Danieli 1:8, 11-15, 20.

11. Kodi anthu ena anapindula bwanji ndi maphunzilo a Yesu akuuzimu?

11 Pakati pa zitsanzo zabwino za anthu amene anayamikila colowa cao ca kuuzimu, sitingalephele kuchula Mwana wa Mulungu, Yesu. Iye anaphunzitsidwa zinthu zambili ndi Atate wake, ndipo anali kuyamikila kwambili zinthu zimene Mulungu anamuphunzitsa. Timadziŵa zimenezo cifukwa ca zimene iye anakamba kuti: “Ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsila.” (Yoh. 8:28) Iye anali kufuna kuti anthu ena adzipindulanso ndi zimene anaphunzila. Iye anauza khamu la anthu kuti: “Ndiyenela kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, cifukwa ndi zimene anandituma kudzacita.” (Luka 4:18, 43) Anathandizanso anthu kuona kufunika kosakhala “mbali ya dzikoli,” limene silimayamikila zinthu zakuuzimu.—Yoh. 15:19.

MUZIYAMIKILA ZIMENE MUNAPATSIDWA

12. (a) Kodi lemba la 2 Timoteyo 3:14-17 limakhudza bwanji acinyamata ambili masiku ano? (b) Ndi mafunso ati amene acinyamata ayenela kudzifunsa?

12 Mofanana ndi acinyamata amene takambilanawa, mwina inunso munaleledwa ndi makolo amene amatumikila Yehova Mulungu. Ngati zili conco, ndiye kuti zimene Malemba amakamba ponena za Timoteyo zimakhudzanso inu. (Ŵelengani 2 Timoteyo 3:14-17) ‘Munaphunzila’ kwa makolo anu za Mulungu woona ndi zimene muyenela kucita kuti mumukondweletse. Makolo anu ayenela kuti anayamba kukuphunzitsani muli wakhanda. Zimene anakuphunzitsani zakuthandizani kukhala ndi nzelu ‘kuti mudzapulumuke kudzela m’cikhulupililo cokhudza Kristu Yesu.’ Ndiponso zakuthandizani kuti mukhale “woyenelela bwino” kugwila nchito ya Mulungu. Koma tifunse motele: Kodi mudzaonetsa kuti mumayamikila zimene munalandila? Kuti muyankhe funso limeneli, coyamba muyenela kudzifunsa mafunso monga awa: ‘Ndimamva bwanji kukhala mbali ya mzela wautali wa mboni zokhulupilika? Ndimamva bwanji kukhala pakati pa anthu ocepa amene amadziŵika ndi Yehova padziko lapansi? Kodi kudziŵa coonadi ndimakuona kukhala mwai wapadela ndiponso waukulu?’

Mumamva bwanji kukhala mbali ya mzela wautali wa mboni zokhulupilika? (Onani ndime 9, 10, 12)

13, 14. Ndi ziyeso zotani zimene acinyamata acikristu amakumana nazo? N’cifukwa ciani n’kupanda nzelu kugonja ku ziyeso zimenezo? Pelekani citsanzo.

13 Acinyamata ambili amene analeledwa  ndi makolo acikristu angalephele kuona kusiyana pakati pa paladaiso wa kuuzimu ndi dziko lamdima la Satana. Acinyamata ena agwa m’ciyeso cofuna kulaŵa umoyo wa m’dzikoli. Koma kodi cingakhale canzelu kuthamangila kutsogolo kwa galimoto imene ikuyenda kuti ikugundeni pofuna kudziŵa mmene imaphwetekela kapena kuti muone ngati ingakupheni? Iyai. Mofananamo, si canzelu kuloŵa “m’cithaphwi ca makhalidwe oipa” a m’dzikoli n’colinga cakuti mudziŵe kupweteka kwake.—1 Petulo 4:4.

14 Gener, amene amakhala ku Asia, anakulila m’banja lacikristu, ndipo anabatizidwa ali ndi zaka 12. Koma ali wacinyamata, anakopeka ndi makhalidwe a m’dzikoli. Iye anati: “Ndinali kufuna kulaŵa ‘ufulu’ umene dziko limapeleka.” Gener anayamba kukhala ndi moyo waciphamaso. Panthawi imene anali kukwanitsa zaka 15, iye anali atatengela kale makhalidwe oipa a anzake. Iye anayamba kumwa ndi kutukwana monga anzake. Gener anali kufika panyumba usiku pambuyo poseŵela maseŵela ena ocedwa billiard ndiponso maseŵela aciwawa a pa kompyuta ndi anzake. Koma m’kupita kwa nthawi anayamba kuona kuti zisangalalo za m’dzikoli sizinali zokhutilitsa ndipo ndi zopanda phindu. Atabwelela mumpingo, iye anati: “Ndikali kukumana ndi mavuto ena pa umoyo, koma madalitso a Yehova ndi ambili kuposa mavutowo.”

15. N’ciani cimene acinyamata amene analeledwa ndi makolo amene si Mboni ayenela kukumbukila?

15 N’zoona kuti pali acinyamata ena amene akugwilizana ndi mpingo omwe analeledwa ndi makolo amene si Mboni. Ngati ndinu mmodzi wa acinyamatawo, kodi simuona kuti ndi mwai wamtengo wapatali kudziŵa Mlengi ndi kumtumikila? Padziko lapansi pali anthu mabiliyoni ambili. Conco ndi mwai wamtengo wapatali kukhala pakati pa anthu amene Yehova wawakokela kwa iye mokoma mtima, ndi kuwavumbulila coonadi ca m’Baibulo. (Yoh. 6:44, 45) Pa anthu 1,000 alionse padziko lapansi, ndi munthu umodzi yekha amene ali ndi cidziŵitso colondola ca Baibulo, ndipo inu muli pakati pa anthu ocepawo. Mfundo imeneyi iyenela kutipangitsa kukhala osangalala mosasamala kanthu kuti tinaphunzila coonadi m’njila yotani. (Ŵelengani 1 Akorinto 2:12) Gener anapitiliza ndi mau akuti: “Ndine ndani kuti ndikhale pakati pa anthu amene amadziŵika ndi Yehova, Mwini cilengedwe? Kuganizila mfundo imeneyi kumandicitisa nthumanzi kwambili.” (Sal. 8:4) Mlongo wina wa  kudela lomwelo anati: “Ana a sukulu amanyadila kwambili akangodziŵika ndi aphunzitsi ao. Kodi ifenso sitiyenela kunyadila koposa pokhala ndi mwai wodziŵidwa ndi Yehova, Mphunzitsi Wamkulu?”

NANGA INU MUDZACITA CIANI?

16. Ndi cosankha canzelu citi cimene acinyamata acikristu ayenela kupanga?

16 Poganizila mwai wapadela umene muli nao, kodi si canzelu kutsimikiza mtima kuposa kale kukhala pakati pa anthu amene asankha kucita zinthu zoyenela paumoyo wao? Mwakutelo, mudzakhala pa mzela wa atumiki a Mulungu okhulupilika ambili. Ndipo ndi nzelu kusankha kucita zimenezi m’malo mongotsatila acinyamata ena mopanda nzelu ndi kuonongedwa limodzi ndi dzikoli.—2 Akor. 4:3, 4.

17-19. N’ciani cimene cingakuthandizeni kukhala ndi maganizo oyenela pankhani yokhala osiyana ndi dziko?

17 Zimenezi sizitanthauza kuti kukhala osiyana ndi dziko kumakhala kopepuka nthawi zonse. Kukhala anzelu ndi kumene kungatithandize kuti tikhale osiyana ndi dziko. Mwacitsanzo, taganizilani za munthu amene amacita maseŵela a Olympic. Mosakaikila iye amakhala katswili cifukwa cocita zinthu mosiyana ndi anzake. Ayenelanso kuti amadzimana zinthu zambili zotaitsa nthawi ndi zosokoneza maganizo ake n’colinga coti asadzipanikize pocita pulakatisi. Kukhala osiyana ndi anzake kungamuthandizenso kukhala ndi nthawi yambili yocita pulakatisi kuti akwanilitse colinga cake.

18 Anthu m’dzikoli saganizila za moyo wao wa m’tsogolo. Koma kukhala osiyana ndi dziko ndiponso kupewa makhalidwe oipa ndi zinthu zina zimene zingaononge ubwenzi wanu ndi Mulungu, kudzakuthandizani ‘kugwila mwamphamvu moyo weniweniwo.’ (1 Tim. 6:19) Mlongo amene tachula poyamba paja anati: “Tikamatsatila zimene timakhulupilila, timasangalala kwambili. Tikamacita zimenezo timaonetsa kuti ndife ofunitsitsa kupewa mzimu woipa wa dziko la Satanali. Ndipo koposa zonse, Yehova Mulungu amakondwela nafe ndi kutinyadila. Tikamacita zimene timakhulupilila m’pamene timaona ubwino wokhala wosiyana ndi anzathu.”

19 Moyo umakhala wopanda phindu ngati munthu amangoika maganizo ake pa zinthu zimene angakhale nazo panopa. (Mlal. 9:2, 10) Ngati ndinu wacinyamata ndipo mumaganizila kwambili za colinga ca moyo wanu ndi utali wake, kodi si canzelu kupewa ‘kuyenda monga mmene anthu a mitundu’ amayendela? Mukamayesetsa kucita zimenezo, mudzakhala ndi moyo watanthauzo.—Aef. 4:17; Mal. 3:18.

20, 21. Ndi madalitso otani amene tidzapeza ngati tipanga zosankha zanzelu? Nanga tifunika kucita ciani?

20 Ngati tipanga zosankha zabwino, timakhala ndi moyo wokhutilitsa panopa ndi kukhala pakati pa anthu amene “adzalandila dziko lapansi” ndi kukhala ndi moyo wosatha. Ndipo pali madalitso oculuka kwambili amene tikuyembekezela, ndipo sitingathe kuwaona onse m’maganizo mwathu. (Mat. 5:5; 19:29; 25:34) Koma sikuti Yehova amangotipatsa zinthu popanda kuyembekezela ciliconse kwa ife. (Ŵelengani 1 Yohane 5:3, 4) Ndi cinthu ca nzelu kumutumikila mokhulupilika panopa.

21 Ndi mwai wamtengo wapatali kulandila zinthu zambili kucokela kwa Mulungu. Tili ndi cidziŵitso colongosoka ca Mau ake ndipo timadziwa bwino coonadi conena za iye ndi zolinga zake. Timasangalala ndi mwai wokhala anthu ocedwa ndi dzina lake ndiponso cifukwa cokhala Mboni zake. Yehova walonjeza kuti adzakhala ku mbali yathu. (Sal. 118:7) Tiyeni tonse, tizisonyeza kuti timayamikila zimene talandila mwa kukhala ndi moyo wosonyeza kuti tikufunitsitsa kupatsa Yehova ‘ulemelelo kwamuyaya,’ kaya ndife acinyamata kapena acikulile.—Aroma 11:33-36; Sal. 33:12.