Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Yehova Amadalitsa Kwambili Anthu Ofunitsitsa Kupeleka

Yehova Amadalitsa Kwambili Anthu Ofunitsitsa Kupeleka

MLENGI wathu anatilemekeza kwambili mwa kutipatsa mphatso yamtengo wapatali ya ufulu wodzisankhila zocita. Kuonjezela apo, iye amadalitsa kwambili anthu amene amadzipeleka ndi mtima wonse kuti apititse patsogolo kulambila koona ndiponso amene amathandiza kuti dzina lake liyeletsedwe ndi kuti colinga cake cabwino cikwanilitsidwe. Yehova safuna kuti tizimumvela mwamwambo cabe, mokakamizika kapena cifukwa coopa cilango. Koma amayamikila kwambili anthu amene amadzipeleka mofunitsitsa cifukwa comukonda ndi mtima wonse ndiponso cifukwa coyamikila kwambili zimene amawacitila.

Mwacitsanzo, pamene Aisiraeli anali m’cipululu ca Sinai, Yehova anawalamula kuti amange malo olambilila. Iye anati: “Nonse mupeleke zopeleka kwa Yehova. Aliyense amene ali ndi mtima wofunitsitsa apeleke kwa Yehova.” (Eks. 35:5) Mwiisiraeli aliyense anali ndi ufulu wopeleka copeleka ciliconse caufulu cimene akanakwanitsa mosasamala kanthu za kuculuka kwake malinga ngati copelekaco cinali cakuti angathe kucigwilitsila nchito pomanga malo olambilila. Kodi Aisiraeli anacita ciani atapemphedwa kupeleka zopeleka?

“Aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa” ndi “aliyense amene anali ndi mzimu wofunitsitsa,” anapeleka copeleka caufulu “ndi mtima wofunitsitsa.” Amuna ndi akazi mofunitsitsa anapeleka zopeleka zothandiza pa nchito ya Yehova. Iwo anapeleka zinthu monga zokometsela zomanga pazovala, ndolo, mphete, golide, siliva, mkuwa, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiilila, ulusi wofiila kwambili, nsalu zabwino kwambili, ubweya wa mbuzi, zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiila, zikopa za akatumbu, matabwa a mthethe, miyala yamtengo wapatali, mafuta a basamu, ndi mafuta ena. Conco “zinthuzo zinali zokwanila pa nchito yonse yoyenela kucitika, ndipo zinaposanso zinthu zofunikila pa nchitoyo.”—Eks 35:21-24, 27-29; 36:7.

Cimene cinakondweletsa kwambili Yehova ndi mzimu wopeleka mofunitsitsa wa anthu amene anacilikiza kulambila koona osati zinthu zimene anapelekazo. Anthuwo anagwilitsilanso nchito nthawi yao ndi mphamvu zao pa nchitoyo. Nkhaniyi imanena kuti, “akazi onse aluso anawomba nsalu ndi manja ao.” Ndipo imanenanso kuti, “akazi onse aluso amene anali ndi mtima wofunitsitsa anawomba nsalu za ubweya wa mbuzi.” Komanso, Yehova anapatsa Bezaleli mtima ‘wanzelu, wozindikila, wodziŵa zinthu, kuti akhale mmisili waluso pa nchito ina iliyonse.’ Zoonadi, Mulungu anacititsa Bezaleli ndi Oholiabu kukhala ndi luso lofunika kuti akwanitse kugwila nchito yonse imene anawapatsa.—Eks. 35:25, 26, 30-35.

Pamene Yehova anapempha Aisiraeli kupeleka zopeleka, iye sanakaikile kuti “aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa” adzacilikiza kulambila koona. Iye anadalitsa kwambili Aisiraeli amene anali ndi mtima wofunitsitsa kupeleka mwa kuwatsogolela, ndipo anthuwo anali kukhala acimwemwe. Motelo Yehova anaonetsa kuti amadalitsa anthu ake amene ali ndi mtima wofunitsitsa kupanga copeleka, ndipo amaonetsetsa kuti anthu akewo sakusowa ciliconse cimene cingawathandize kukwanilitsa colinga cake. (Sal. 34:9) Mukamatumikila Yehova ndi mtima wonse, iye sadzalephela kukudalitsani.