Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi ‘Mumamvetsa Tanthauzo la Malemba’?

Kodi ‘Mumamvetsa Tanthauzo la Malemba’?

“Anatsegulilatu maganizo ao kuti amvetse tanthauzo la Malemba.”—LUKA 24:45.

1, 2. Kodi Yesu analimbikitsa bwanji ophunzila ake tsiku limene anaukitsidwa?

TSIKU limene Yesu anaukitsidwa, ophunzila ake aŵili anali kupita ku mudzi wina umene unali pamtunda wa makilomitala 11.2 kucokela ku Yerusalemu. Iwo anali okhumudwa ndi zimene zinacitika, ndipo sanadziŵe kuti Yesu waukitsidwa. Mwadzidzidzi, Yesu anaonekela ndi kuyamba kuyendela nao limodzi. Iye anatonthoza ophunzilawo. Motani? “Anayamba kuwatanthauzila zinthu zokhudza iyeyo m’Malemba onse, kuyambila ndi Zolemba za Mose ndi za aneneli zonse.” (Luka 24:13-15, 27) Pamenepo mitima yao inayamba kunthunthumila cifukwa anali ‘kuwafotokozela Malemba momveka bwino.’—Luka 24:32.

2 Usiku wa tsiku lomwelo, ophunzila aŵili aja anabwelelanso ku Yerusalemu. Atafika kumeneko, anayamba kuuza atumwi zimene zinawacitikila. Akali kukamba, Yesu anaonekela kwa onsewo. Komabe, atumwi ake anacita mantha ndipo anayamba kukayikakayika m’mitima yao. Kodi Yesu anawalimbikitsa bwanji? Baibulo limati: “Anatsegulilatu maganizo ao kuti amvetse tanthauzo la Malemba.”—Luka 24:45.

3. Ndi zinthu ziti zimene zingatikhumudwitse? Nanga n’ciani cingatithandize kuti tiziona utumiki wathu moyenelela?

3 Mofanana ndi atumwi aja, nthawi zina tingakhumudwe. Mwina tili ndi zocita zambili m’nchito ya Ambuye, koma ndife  olefulidwa cifukwa tikuona kuti utumiki wathu sukubala zipatso. (1 Akor. 15:58) Kapena tingayambe kuona kuti anthu amene tikuphunzila nao Baibulo sakupita patsogolo. Anthu ena amene tikuyesa kuthandiza angasiye Yehova. N’ciani cingatithandize kuti tiziona utumiki wathu moyenelela? Cinthu cimodzi cimene cingatithandize ndi kumvetsetsa bwinobwino tanthauzo la mafanizo a Yesu olembedwa m’Malemba Oyela. Tiyeni tsopano tikambilane mafanizo atatu mwa mafanizo amenewo ndi kuona zimene tikuphunzilapo.

FANIZO LA WOFESA MBEU AMENE AMAGONA

4. Kodi fanizo la Yesu la wofesa mbewu amene amagona limatanthauza ciani?

4 Ŵelengani Maliko 4:26-29. Kodi fanizo la Yesu la wofesa mbewu amene amagona limatanthauza ciani? Munthu wa m’fanizo limeneli amaimila mlaliki wa Ufumu aliyense. Mbeu zimaimila uthenga wa Ufumu umene umalalikidwa kwa a mtima wofuna coonadi. Monga mwa masiku onse, wofesa mbewu ‘amagona usiku n’kudzuka kukacha.’ Kukula kumatenga nthawi yaitali cifukwa kumayamba pamene mbeuzo zabyalidwa mpaka nthawi yokolola. M’nthawi imeneyo “mbewuzo zimamela ndi kukula.” Kukula kumacitika ‘pakokha,’ mwapang’onopang’ono. Mofananamo, kukula kwakuuzimu kumacitika mwapang’onopang’ono. Munthu akapita patsogolo n’kuyamba kutumikila Mulungu, amabala zipatso m’njila yakuti amadzipeleka kwa Yehova n’kubatizidwa.

5. N’cifukwa ciani Yesu anafotokoza fanizo la wofesa mbewu amene amagona?

5 N’cifukwa ciani Yesu anagwilitsila nchito fanizo limeneli? Yesu anafuna kutithandiza kudziŵa kuti Yehova ndi amene amapangitsa coonadi kukula m’mitima ya anthu a “maganizo abwino.” (Mac. 13:48; 1 Akor. 3:7) Timabyala ndi kuthilila, koma sindife amene timakulitsa. Sitingathe kukakamiza kuti mbeuzo zikule kapena kuzifulumizitsa. Mofanana ndi munthu wa m’fanizo limeneli, sitidziŵa mmene mbeu za coonadi zimakulila. Popeza kuti timakhala otangwanika ndi nchito za masiku onse, sitidziŵa kuti mbeu za coonadi zikukula. Koma m’kupita kwa nthawi timangozindikila kuti mbeu za Ufumu zimene tinabyala zabala zipatso. Wophunzila watsopanoyo amayamba kugwilizana nafe m’nchito yokolola ndipo timasangalala kugwilila naye nchito limodzi.—Yoh. 4:36-38.

6. N’ciani cimene sitiyenela kuiwala ponena za kupita patsogolo kwa wophunzila Baibulo?

6 Kodi fanizo limeneli likutiphunzitsa ciani? Coyamba, tiyenela kuzindikila kuti sindife amene tingapangitse kuti wophunzila Baibulo apite patsogolo kuuzimu. Ngati ndife odzicepetsa, tidzapewa kukakamiza wophunzila Baibulo kubatizidwa. Timacita zonse zimene tingathe kuti tithandize wophunzila Baibulo, koma sitiyenela kuiwala kuti munthuyo ayenela kusankha yekha kuti adzipeleke. Munthuyo ayenela kudzipeleka yekha ndi mtima wonse cifukwa cokonda Mulungu. Yehova amakondwela ndi munthu amene amam’tumikila ndi mtima wonse.—Sal. 51:12; 54:6; 110:3.

7, 8. (a) Ndi mfundo zina ziti zimene tikuphunzila m’fanizo la Yesu la wofesa mbeu amene amagona? Pelekani citsanzo. (b) Kodi fanizo limeneli likutiphunzitsa ciani ponena za Yehova ndi Yesu?

7 Caciŵili, kumvetsetsa tanthauzo la fanizo limeneli kudzatithandiza kuti tisalefuke cifukwa coona ngati nchito yathu siikuphula kanthu. Tiyenela kukhala oleza mtima. (Yak. 5:7, 8) Ngakhale kuti mbeu zimene tinabyala sizikubala zipatso, ndipo tacita zonse zotheka kuthandiza wophunzila wathu, koma sakupita patsogolo, sizitanthauza kuti tilibe cikhulupililo. Yehova amalola mbeu za coonadi kukula mwa munthu yekhayo amene ali ndi mtima wodzicepetsa ndi wofunitsitsa kusintha. (Mat. 13:23) Conco, sitiyenela kuganiza kuti utumiki wathu suyenda bwino cifukwa cakuti nchito yathu siikubala zipatso. Yehova amaona kuti zinthu zikutiyendela  bwino mu utumiki osati cifukwa coona mmene anthu amakhudzidwila ndi zimene timawaphunzitsa, koma amayamikila khama lathu kaya anthuwo alabadile uthenga wathu kapena ai.—Ŵelengani Luka 10:17-20; 1 Akorinto 3:8.

8 Cacitatu, nthawi zina sitimaona masinthidwe onse amene munthu akupanga. Mwacitsanzo, banja lina linafikila mmishonale amene anali kuwaphunzitsa Baibulo ndi kumuuza kuti akufuna kukhala ofalitsa osabatizidwa. Mmishonale uja anawakumbutsa kuti ayenela kuleka kukoka fodya coyamba kuti ayenelele kukhala ofalitsa. Mmishonaleyo anadabwa kwambili pamene banja lija linamuuza kuti anasiya kukoka fodya miyezi yambili m’buyomo. N’cifukwa ciani anaganiza zosiya kukoka fodya? Iwo anazindikila kuti Yehova amadana ndi anthu acinyengo, ndipo anali kuwaona akamakoka fodya. Conco anaganiza zopanga cosankha cakuti azikoka fodya pamaso pa mmishonale uja kapena kusiilatu kukoka. Cikondi cao pa Yehova cinawathandiza kupanga cosankha ca nzelu. Mwacionekele, io anali atakula kale kuuzimu ngakhale kuti mmishonale uja sanali kudziŵa za masinthidwe amene io anapanga.

FANIZO LA KHOKA

9. Kodi fanizo la Yesu la khoka limatanthauza ciani?

9 Ŵelengani Mateyu 13:47-50. Kodi fanizo la Yesu la khoka limatanthauza ciani? Yesu anayelekezela nchito yolalikila uthenga wa Ufumu kwa anthu onse ndi kuponya khoka lalikulu m’nyanja. Mofanana ndi khoka limene silisankha, ndipo limasonkhanitsa nsomba zambili ndiponso “zamitundumitundu,” nchito yolalikila imakoka anthu ambilimbili a mitundu yonse. (Yes. 60:5) Timaona umboni wa zimenezi tikaona kuculuka kwa anthu amene amapezeka pa misonkhano yathu ya cigawo ndi pa Cikumbutso caka ciliconse. Ena mwa anthu amenewa ali ngati nsomba “zabwino,” ndipo amasonkhanitsidwila mumpingo wacikristu. Koma ena amene amasonkhanitsidwa amakhala monga nsomba “zosafunika” cifukwa sakhala ovomelezeka kwa Yehova.

Pambuyo poŵelenga Mateyu 13:47-50  . . .

10. N’cifukwa ciani Yesu anafotokoza fanizo la khoka?

10 N’cifukwa ciani Yesu anagwilitsila nchito fanizo limeneli? Nchito yophiphilitsa yolekanitsa nsomba siikuimila ciweluzo comaliza cimene cidzacitika pa cisautso cacikulu. Koma ikuimila zimene zidzacitika m’masiku otsiliza a dongosolo loipa lino. Yesu anasonyeza mfundo yakuti si onse amene amacita cidwi ndi coonadi amene adzakhala kumbali ya Yehova. Ambili a io takhala tikusonkhana nao, ndipo ena amakonda kuphunzila nafe Baibulo, koma safuna kutumikila Mulungu. (1 Maf. 18:21) Palinso anthu ena amene anasiilatu kugwilizana ndi mpingo wacikristu. Acinyamata ena makolo ao ndi a Mboni za Yehova, koma io safuna kutsatila mfundo za Yehova. Mulimonse mmene zingakhalile, Yesu anaonetsa kuti aliyense ayenela kusankha yekha. Ndipo Mulungu amaona anthu amene amasankha kukhala ku mbali yake kuti ndi “zinthu zamtengo wapatali zocokela ku mitundu yonse ya anthu.”—Hag. 2:7.

. . . onani tanthauzo lake masiku ano

11, 12. (a) Tingapindule bwanji ndi fanizo la khoka? (b) Kodi fanizo limeneli likutiphunzitsa ciani ponena za Yehova ndi Yesu.

11 Tingapindule bwanji ndi fanizo la khoka? Kumvetsa tanthauzo la fanizo limeneli kungatithandize kuti tisakhumudwe kapena kulefuka ngati munthu amene tikuphunzila naye Baibulo kapena mwana wathu walephela kupanga coonadi kukhala cakecake. Zimenezi zingacitike ngakhale titacita zilizonse zimene tingathe. Kuvomela kuphunzila Baibulo kapena kuleledwa m’coonadi pakokha sikupangitsa munthu kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova. Posacedwapa, anthu amene amakana ulamulilo wa Yehova adzacotsedwa pakati pa anthu a Mulungu.

Anthu ena amene amacita cidwi ndi coonadi amakhala kumbali ya Yehova (Onani ndime 9-12)

12 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti anthu  amene anasiya coonadi sadzaloledwa kubwelela mumpingo? Nanga bwanji ngati wina akulephela kudzipeleka kwa Yehova, kodi zikutanthauza kuti iye adzakhala monga nsomba ‘yosafunika’ kwamuyaya? Iyai. Anthu amenewo akali ndi mwai wopanga cosankha cisautso cacikulu cisanayambe. Zili monga kuti Yehova akuwaitana kuti: “Bwelelani kwa ine ndipo ine ndibwelela kwa inu.” (Mal. 3:7) Mfundo imeneyi ikugogomezeledwa m’fanizo lina limene Yesu anafotokoza la mwana woloŵelela.—Ŵelengani Luka 15:11-32.

FANIZO LA MWANA WOLOŴELELA

13. Kodi fanizo la mwana woloŵelela limatanthauza ciani?

13 Kodi fanizo la Yesu la mwana woloŵelela limatanthauza ciani? Atate wacifundo m’fanizo ili akuimila Atate wathu wakumwamba Yehova, yemwe ndi wacikondi. Mwana amene anapempha atate wake kuti amupatse colowa cake kenako n’kuononga cumaco akuimila anthu amene anasocela ndi kucoka mumpingo. Mwa kucoka mumpingo, zili monga anapita “kudziko lina lakutali,” limene ndi dziko la Satana lotalikilana ndi Yehova. (Aef. 4:18; Akol. 1:21) M’kupita kwa nthawi, ena amazindikila kuti analakwitsa,’ ndipo amasankha kubwelela ku gulu la Yehova ngakhale kuti sicikhala capafupi. Anthu amene anasiyana ndi mpingo akalapa n’kusintha, Mulungu, Atate wathu amene amakhululukila amamulandila ndi mtima wonse.—Yes. 44:22; 1 Pet. 2:25.

14. N’cifukwa ciani Yesu anakamba fanizo la mwana wolowelela?

14 N’cifukwa ciani Yesu anagwilitsila nchito fanizo limeneli? Mwakugwilitsila nchito fanizo locititsa cidwi limeneli, Yesu anasonyeza kuti Yehova amafuna kuti anthu amene anasocela abwelele kwa Iye. M’fanizoli, atate a mwana uja anali ndi ciyembekezo cakuti mwana wao adzabwelela. Ndiye cifukwa cake pamene anaona mwana waoyo akubwela “capatali ndithu,” io anamuthamangila ndi kumulandila. Imeneyi ndi mfundo yolimbikitsa kwambili kwa anthu onse amene anasiya coonadi kuti abwelele kwa Yehova mwamsanga. N’zoona kuti ocimwawo amakhala kuti anaononga ubwenzi wao ndi Yehova, ndipo angaone kuti n’zovuta ndiponso zocititsa manyazi kubwelela. Koma kubwelela n’kofunika cifukwa ngakhale kumwamba kudzakhala cisangalalo ngati ocimwawo angabwelele.—Luka 15:7.

15, 16. (a) Kodi tikuphunzilapo ciani pa fanizo la Yesu la mwana wolowelela? Pelekani zitsanzo. (b) Kodi fanizo limeneli likutiphunzitsa ciani ponena za Yehova ndi Yesu?

15 Tingapindule bwanji ndi fanizo la mwana wolowelela? Tiyenela kutengela citsanzo ca Yehova mwa kupewa kukhala  “wolungama mopitilila muyezo” mpaka kukana kulandila ocimwa amene abwelela mumpingo. Kucita zimenezo ‘kungationonge’ mwakuuzimu. (Mlal. 7:16) Fanizo limeneli limatiphunzitsanso phunzilo lina. Tiyenela kuona munthu amene wasiya mpingo monga “nkhosa yosocela” osati ngati munthu woipa woti sangabwelelenso m’gulu la Yehova. (Sal. 119:176) Tikapeza munthu wina amene anafoka ndipo anasiya kusonkhana, tizimupatsa malangizo acikondi ndi othandiza kuti abwelelenso m’gulu la Mulungu. Tiyenelanso kudziŵitsa akulu mwamsanga kuti amupatse thandizo loyenelela. Tikamacita zimenezi ndiye kuti tikugwilitsila nchito mfundo zimene taphunzila m’fanizo la Yesu la mwana wolowelela.

16 Anthu ena amene anali monga ana olowelela amayamikila Yehova cifukwa ca cifundo cake ndiponso mmene mpingo unawathandizila ndi kuwasonyeza cikondi. Mwacitsanzo, mbale wina amene anali atacotsedwa kwa zaka 25 anati: “Kucokela pamene ndinabwezeletsedwa mumpingo, cimwemwe canga cikungoonjezeleka cifukwa ndakhala ndikulandila ‘nyengo zotsitsimutsa kucokela kwa Yehova.’ (Mac. 3:19) Aliyense mumpingo amandithandiza ndipo amandikonda. Ndili ndi banja lakuuzimu labwino kwambili.” Mtsikana wina amene anali atasiya Yehova kwa zaka 5 anati: “Sindiziŵa kuti ndingafotokoze bwanji mmene ndinamvelela kuona abale ndi alongo akundisonyeza cikondi cimene Yesu anakamba. Kukhala m’gulu la Yehova ndi cinthu ca mtengo wapatali.”

17, 18. (a) Ndi mfundo zothandiza ziti zimene taphunzila m’mafanizo atatu amene takambilana? (b) Kodi tiyenela kutsimikiza mtima kucita ciani?

17 N’ciani cimene taphunzila m’mafanizo atatu awa? Coyamba, tiyenela kuzindikila kuti sindife amene tingapangitse kuti wophunzila Baibulo apite patsogolo kuuzimu. Imeneyo ndi nchito ya Yehova. Caciŵili, sitiyenela kuganiza kuti anthu onse amene amabwela kudzasonkhana nafe kapena kuphunzila nafe Baibulo adzakhala a Mboni za Yehova. Comaliza, ngakhale anthu ena asiye coonadi ndi kusiya Yehova, tiyenela kukhala ndi ciyembekezo cakuti adzabwelelanso m’gulu la Mulungu. Ndipo anthu amenewo akadzabwelela mumpingo, tiyenela kuwalandila mofanana ndi Yehova.

18 Tiyeni tonse tipitilize kufunafuna cidziŵitso, kumvetsa zinthu, ndi nzelu. Tikamaŵelenga mafanizo a Yesu tiyenela kudziŵa tanthauzo la mafanizo amenewo, cifukwa cake analembedwa m’Baibulo, cifukwa cake tiyenela kugwilitsila nchito mfundo zake, ndi zimene mafanizowo akutiphunzitsa ponena za Yehova ndi Yesu. Tikamatelo, tidzasonyeza kuti tikumvetsetsa tanthauzo la mau a Yesu.