Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Khalani Wolimba Mtima ndi Wozindikila Monga Yesu

Khalani Wolimba Mtima ndi Wozindikila Monga Yesu

“Ngakhale kuti simunamuonepo, mumamukonda. Ngakhale simukumuona panopa, mumakhulupilila mwa iye.”—1 PET. 1:8.

1, 2. (a) Tiyenela kucita ciani kuti tidzapulumuke? (b) N’ciani cingatithandize kupitilizabe kuyenda panjila ya ku cipulumutso?

PAMENE tinakhala ophunzila a Kristu, tinayamba ulendo. Ngati tipitilizabe kukhala okhulupilika, ulendowo ungatitsogolele kumoyo wosatha. Yesu anakamba kuti: “Amene adzapilile mpaka pa mapeto, [mapeto a moyo wake kapena a dongosolo loipa la zinthu] ndiye amene adzapulumuke.” (Mat. 24:13) Zoonadi, ngati tikhalabe okhulupilika tidzapulumuka. Komabe, pamene tili paulendowu, tiyenela kupewa zoceukitsa kapena zimene zingatisoceletse. (1 Yoh. 2:15-17) N’ciani cingatithandize kupitilizabe kuyenda ulendowu?

2 Yesu anapeleka citsanzo ca mmene tingayendele ulendo umenewu. Ulendo wake unalembedwa m’Baibulo. Kuphunzila za ulendowo kungatithandize kudziŵa umunthu wa Yesu, kumukonda ndi kumukhulupilila. (Ŵelengani 1 Petulo 1:8, 9.) Kumbukilani kuti mtumwi Petulo anakamba kuti Yesu anatisiyila citsanzo kuti titsatile mapazi ake mosamala kwambili. (1 Pet. 2:21) Ngati titsatila mapazi ake mosamala kwambili, tidzakhala “otsimikiza  kuti” tidzapulumuka. * M’nkhani yapita, tinakambilana mmene tingatengele citsanzo ca Yesu pankhani yokhala wodzicepetsa ndi wacifundo. Tsopano tiyeni tikambilane mmene tingatengele citsanzo cake pankhani yokhala wolimba mtima ndi wozindikila.

YESU NDI WOLIMBA MTIMA

3. Kodi kukhala wolimba mtima kumatanthauza ciani? N’ciani cingatithandize kukhala wolimba mtima?

3 Kukhala wolimba mtima kumatanthauza kukhala ndi cidalilo ndipo kumatithandiza kupilila mavuto. Kulimba mtima kungatithandize kuima pacilungamo. Kungatithandizenso kukhala wodekha ndi wokhulupilika kwa Mulungu pamayeselo. Kuti munthu akhale wolimba mtima afunika kuopa Mulungu, kukhala ndi ciyembekezo, ndiponso cikondi. N’cifukwa ciani tikutelo? Kuopa Mulungu kumaticititsa kuti tisamaope anthu. (1 Sam. 11:7; Miy. 29:25) Kukhala ndi Ciyembekezo ceniceni kumatithandiza kupilila mayeselo ndi kuyembekeza za mtsogolo molimba mtima. (Sal. 27:14) Cikondi codzimana cimaticititsa kukhala wolimba mtima ngakhale moyo wathu utakhala pangozi. (Yoh. 15:13) Tikamadalila Mulungu ndi kutsatila mapazi a Mwana wake, timakhala olimba mtima.—Sal. 28:7.

4. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kulimba mtima “atakhala pakati pa aphunzitsi” m’kacisi? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

4 Pamene Yesu anali ndi zaka 12, iye anaonetsa kulimba mtima pamene anali “m’kacisi, atakhala pakati pa aphunzitsi.” (Ŵelengani Luka 2:41-47.) Aphunzitsiwo anali kudziŵa bwino Cilamulo ca Mose ndi miyambo ya anthu, imene inapeputsa Cilamuloco. Yesu sanacite nao mantha, koma anali “kuwafunsa mafunso.” Iye sanali kufunsa mafunso amene ana onse amafunsa. Iye anali kufunsa mafunso amene anacititsa aphunzitsiwo kudabwa kwambili. Ndipo ngati aphunzitsiwo anali kufuna kuyesa Yesu mwa kum’funsa mafunso odzutsa mikangano, io analephela. Onse amene anali kumumvetsela, kuphatikizapo aphunzitsi, anadabwa “ndi mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambili.” Ndithudi, Yesu molimba mtima anateteza coonadi copezeka m’Mau a Mulungu.

5. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti ndi wolimba mtima?

5 Yesu ali padziko lapansi anaonetsa kulimba mtima m’njila zambili. Anatsutsa atsogoleli acipembedzo molimba mtima cifukwa cosoceletsa anthu ndi ziphunzitso zabodza. (Mat. 23:13-36) Iye sanagonjele ku zocitika za padziko lapansi. (Yoh. 16:33) Anapitilizabe kulalikila ngakhale kuti anthu anali kumutsutsa. (Yoh. 5:15-18; 7:14) Iye mopanda mantha anayeletsa kacisi kaŵili konse mwa kuthamangitsa anthu amene anali kuipitsa nyumba yolambililamo.—Mat. 21:12, 13; Yoh. 2:14-17.

6. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kulimba mtima patsiku lomaliza la moyo wake padziko lapansi?

6 Cikhulupililo cathu cimalimba tikaganizila mmene Yesu anakhalila wolimba mtima pamavuto. Ganizilani mmene anaonetsela kulimba mtima patsiku lomaliza la moyo wake padziko lapansi. Iye anadziŵa zimene womupelekayo anali kufuna kucita. Pa mwambo wa Pasika, Yesu anauza Yudasi kuti: “Zimene wakonza kucita, zicite mwamsanga.” (Yoh. 13:21-27) M’munda wa Getsemane, Yesu molimba mtima anadzidziŵikitsa kwa asilikali amene anabwela kudzam’gwila. Ngakhale kuti moyo wake unali pangozi, iye analankhula molimba mtima conco kuti ateteze ophunzila ake. (Yoh. 18:1-8) Atafunsidwa mu  Khoti Yapamwamba ya Ayuda, iye molimba mtima anavomela kuti anali Kristu ndiponso Mwana wa Mulungu, ngakhale kuti anadziŵa kuti mkulu wa ansembe anali kufunafuna cifukwa coti amuphele. (Maliko 14:60-65) Yesu anakhalabe wokhulupilika mpaka imfa pamtengo wophelapo anthu. Atatsala pang’ono kufa, iye anafuula mwamphamvu kuti: “Ndakwanilitsa cifunilo canu!”—Yoh. 19:28-30.

KHALANI WOLIMBA MTIMA MONGA YESU

7. Kodi anyamata mukumva bwanji kudziŵika ndi dzina la Yehova? Nanga mungaonetse bwanji kuti ndinu olimba mtima?

7 Tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu pankhani yokhala wolimba mtima? Ku sukulu. Acinyamata, mumaonetsa kuti ndinu wolimba mtima pamene mumauza anzanu a kusukulu ndi ena kuti ndinu wa Mboni za Yehova. Mukatelo, mumaonetsa kuti mumanyadila kudziŵika ndi dzina la Yehova, ngakhale kuti ena angakusekeni. (Ŵelengani Salimo. 86:12.) Ngakhale kuti ena angakusonkhezeleni kukhulupilila ciphunzitso ca cisanduliko, inu muli ndi zifukwa zomveka zokhulupilila zimene Baibulo limanena pankhani ya cilengedwe. Mungagwilitsile nchito kabuku kacingelezi kakuti The Origin of Life—Five Questions Worth Asking, kuti mupeleke mayankho omveka kwa anthu ofuna kudziŵa za “ciyembekezo cimene muli naco.” (1 Pet. 3:15) Ndiyeno, mudzakhala okhutila podziŵa kuti mwateteza coonadi ca m’Baibulo molimba mtima.

8. N’cifukwa ciani timalalikila molimba mtima?

8 Mu ulaliki. Pokhala Akristu oona, tifunika kupitiliza ‘kulankhula molimba mtima cifukwa ca mphamvu ya Yehova.’ (Mac. 14:3) N’cifukwa ciani timalalikila molimba mtima? Coyamba, timadziŵa kuti zimene timaphunzitsa ndi coonadi cifukwa zimacokela m’Baibulo. (Yoh. 17:17) Caciŵili, “ndife anchito anzake a Mulungu,” ndipo watipatsa mzimu woyela kuti utitsogolele. (1 Akor. 3:9; Mac. 4:31) Cacitatu, timakonda Yehova ndi anzathu. Conco, timayesetsa kuuza ena uthenga wabwino mmene tingathele. (Mat. 22:37-39) Tikakhala wolimba mtima, sitidzaleka kulalikila. Ndife ofunitsitsa kuphunzitsa coonadi anthu amene acititsidwa “khungu,” kapena kunamizidwa ndi atsogoleli acipembedzo. (2 Akor. 4:4) Ndipo tidzapitizabe kulalikila uthenga wabwino ngakhale kuti anthu alibe cidwi, amatinyoza, kapena kutitsutsa.—1 Ates. 2:1, 2.

9. Tingaonetse bwanji kulimba mtima pa mavuto?

9 Pa mavuto. Kudalila Mulungu kumatithandiza kukhala ndi cikhulupililo ndiponso wolimba mtima tikakumana ndi mavuto. Munthu amene timakonda akamwalila, timamva cisoni, koma timakhala ndi ciyembekezo. Mwacidalilo, timayang’ana kwa “Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse” kuti atilimbikitse. (2 Akor. 1:3, 4; 1 Ates. 4:13) Tikadwala kwambili kapena tikavulala, timamva ululu, koma timapewa kulandila cithandizo ca mankhwala cimene sicigwilizana ndi mfundo za m’Baibulo. (Mac. 15:28, 29) Tikapsinjika maganizo, “mitima yathu ingatitsutse.” Koma cifukwa codalila Mulungu amene “ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka,” timapilila. *Yoh. 3:19, 20; Sal. 34:18.

YESU NDI WOZINDIKILA

10. Kodi kukhala wozindikila kumatanthauza ciani? Nanga Mkristu wozindikila amalankhula ndi kucita zinthu motani?

10 Kukhala wozindikila kumatanthauza  kukhala ndi luntha losiyanitsa cabwino ndi coipa, ndi kusankha njila yabwino. (Aheb. 5:14) Mkristu wozindikila amapanga zosankha zimene zimalimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova. Mau ndi zocita zake zimakondweletsa Mulungu. Munthu waconco amasankha mau amene angathandize ena osati kuwakhumudwitsa. (Miy. 11:12, 13) Iye ‘safulumila kukwiya.’ (Miy. 14:29) “Amayenda panjila yabwino,” kutanthauza kuti amapanga zosankha zabwino paumoyo wake. (Miy. 15:21) Kodi tingakhale bwanji ozindikila? Tifunika kuphunzila Mau a Mulungu ndi kuwagwilitsila nchito. (Miy. 2:1-5, 10, 11) Tingaphunzilenso za Yesu ndi kutengela citsanzo cake cabwino pankhani yokhala wozindikila.

11. Kodi mau a Yesu amaonetsa bwanji kuti iye anali wozindikila?

11 Yesu anaonetsa kuti anali wozindikila m’mau ndi zocita zake. Mau ake. Pamene anali kulalikila uthenga wabwino, iye anagwilitsila nchito mau abwino amene anadabwitsa omvela. (Luka 4:22; Mat. 7:28) Nthawi zonse iye anali kuŵelenga Mau a Mulungu kapena kuwachula. Anali kudziŵa bwino kugwilitsila nchito malemba pa zocitika zosiyanasiyana. (Mat. 4:4, 7, 10; 12:1-5; Luka 4:16-21) Komanso, anthu amene anamva Yesu akufotokoza Malemba anakhuzidwa mtima kwambili ndi mau ake. Pambuyo poukitsidwa, iye analankhula ndi ophunzila ake aŵili amene anali paulendo wopita ku Emau, ndipo ‘anawatanthauzila zinthu zokhudza iyeyo m’Malemba onse.’ (Luka 24:27, 32) Pambuyo pake ophunzilawo anati: “Kodi si paja mitima yathu inali kunthunthumila pamene anali . . . kutifotokozela Malemba momveka bwino?”—Luka 24:27, 32.

12, 13. Ndi zitsanzo ziti zimene zionetsa kuti Yesu anali wosakwiya msanga ndi woganizila ena?

12 Khalidwe lake ndi mtima wake. Kukhala wozindikila kunathandiza Yesu ‘kusakwiya msanga.’ (Miy. 16:32) Iye anali “wofatsa.” (Mat. 11:29) Nthawi zonse anali kuleza mtima ndi ophunzila ake mosasamala kanthu za zofooka zao. (Maliko 14:34-38; Luka 22:24-27) Iye sanabwezele ngakhale kuti anacitilidwa zinthu mopanda cilungamo.—1 Pet. 2:23.

13 Kuzindikila kunathandizanso Yesu kuganizila ena. Iye anali kudziŵa bwino mfundo za m’Cilamulo ca Mose, ndipo mfundozo zinakhudza mmene anali kucitila zinthu ndi anthu. Mwacitsanzo, ganizilani nkhani ya pa Maliko 5:25-34. (Ŵelengani.) Mkazi wina amene anali ndi nthenda yotaya magazi, analoŵa m’khamu la anthu ndi kugwila malaya a Yesu, ndiyeno mkaziyo anacila. Malinga ndi Cilamulo, mkaziyo anali wodetsedwa, ndipo sanafunikile kukhudza munthu aliyense. (Lev. 15:25-27) Koma Yesu, amene anali kuzindikila kuti “zinthu zofunika za m’Cilamulo,” zinali kuphatikizapo “cifundo ndi kukhulupilika,” sanadzudzule mkaziyo cifukwa cogwila malaya ake. (Mat. 23:23) M’malo mwake, iye mokoma mtima anamuuza kuti: “Mwanawe, cikhulupililo cako cakucilitsa. Pita mu mtendele, matenda ako aakuluwo atheletu.” N’zolimbikitsa kwambili kuti khalidwe la kuzindikila la Yesu linam’cititsa kuonetsa cifundo mwanjila imeneyo.

14. Kodi Yesu anasankha kucita ciani? Nanga anakwanilitsa bwanji zimenezo?

14 Mmene anali kucitila zinthu. Mmene Yesu anali kucitila zinthu paumoyo wake zinaonetsa kuti iye anali wozindikila. Nchito yake yaikulu inali kutumikila Mulungu. (Luka 4:43) Yesu anapanga zosankha zimene zinam’thandiza kuika maganizo ake panchitoyo ndi kukwanilitsa utumiki wake. Mwacitsanzo, iye anakhala umoyo wosalila zambili n’colinga cofuna kugwilitsila nchito nthawi yake ndi mphamvu zake mu utumiki. (Luka 9:58) Anazindikila kufunika  kophunzitsa ena kuti adzapitilize nchitoyo pambuyo pa imfa yake. (Luka 10:1-12; Yoh. 14:12) Analonjeza otsatila ake kuti adzagwila nao nchitoyo “mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.”—Mat. 28:19, 20.

KHALANI WOZINDIKILA MONGA YESU

Zindikilani zimene eninyumba amakonda, ndipo sankhani mau anu moyenelela (Onani ndime 15)

15. Kodi mau athu angaonetse bwanji kuti ndife ozindikila?

15 Tiyeni tione njila ina ya mmene tingatengele citsanzo ca Yesu. Mau athu. Polankhula ndi okhulupilila anzathu, tiyenela kugwilitsila nchito mau olimbikitsa osati ofooketsa. (Aef. 4:29) Tikamauza ena za Ufumu wa Mulungu, mau athu ayenela kukhala okoma ngati kuti ‘tawathila mcele.’ (Akol. 4:6) Kuzindikila zosoŵa za eninyumba ndi zimene amakonda, kudzatithandiza kusankha mau athu moyenelela. Ngati tigwilitsila nchito mau okoma, anthu angamvetsele uthenga wathu ndipo ungawafike pamtima. Kuonjezela pamenepo, tiyenela kugwilitsila nchito Baibulo pofotokoza zimene timakhulupilila, cifukwa Mau a Mulungu ali ndi mphamvu. Timadziŵa kuti uthenga wa m’Baibulo uli ndi mphamvu kuposa mau athu.—Aheb. 4:12.

16, 17. (a) Tingaonetse bwanji kuti sitifulumila kukwiya ndipo ndife ololela? (b) N’ciani cingatithandize kuika maganizo athu pautumiki?

16 Mwa khalidwe lathu ndi mtima wathu. Kukhala wozindikila kumatithandiza kukhala wodziletsa ndi ‘kusafulumila kukwiya.’ (Yak. 1:9) Ena akatikhumudwitsa, timayesa kuganizila zimene zawacititsa kukamba mau oipa kapena kuticitila zoipa. Kuzindikila mwa njila imeneyo kungacepetse mkwiyo ndi kutithandiza “kunyalanyaza colakwa.” (Miy. 19:11) Kuzindikila kumatithandiza kukhala ololela. Mwakutelo,sitidzayembekezela Akristu anzathu kucita zinthu zimene sangakwanitse. Sitiyenela kuiŵala kuti naonso mwina akukumana ndi mavuto amene ife sitikuwadziŵa. Timakhala ofunitsitsa kumva maganizo ao ndi kukhala ololela ngati pakufunika kutelo.—Afil. 4:5.

17 Mwa zocita zathu. Monga otsatila a Kristu, tiyenela kuzindikila kuti palibe nchito ina yapamwamba imene ingapose nchito yolalikila uthenga wabwino. Tingapitilize kugwila nchitoyi ngati tipanga zosankha zimene sizingadodometse utumiki wathu. Timaika zinthu za kuuzimu patsogolo ndi kukhala umoyo wosalila zambili n’colinga cogwilitsila nchito nthawi yathu yaikulu pa nchito yolalikila mapeto asanafike.—Mat. 6:33; 24:14.

18. N’ciani cingatithandize kukhalabe paulendo wathu wopita ku cipulumutso? Nanga mwatsimikiza mtima kucita ciani?

18 Zakhaladi zosangalatsa kuphunzila za makhalidwe a Yesu ocititsa cidwi. Tingaphindule kwambili kuphunzila za makhalidwe ake ena ndiponso kuyesa kutengela citsanzo cake. Conco, tiyeni titsimikize mtima kutengela citsanzo ca Yesu. Mwakutelo, tidzapitilizabe ulendo wathu wa ku moyo wosatha ndi kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova.

^ par. 2 Lemba la 1 Petulo 1:8, 9 linalembedwela Akristu amene ali ndi ciyembekezo cakumwamba. Komabe, mfundo yake imagwilanso nchito kwa amene ali ndi ciyembekezo ca padziko lapansi.

^ par. 9 Onani zitsanzo za anthu amene anakhala olimba mtima pa mavuto mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 2000, masamba 24-28; Galamukani! ya May 8, 2003, masamba 26-29, ndi yacingelezi ya January 22, 1995, masamba 11-15.