Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pitilizani Kukhala Wacangu mu Utumiki

Pitilizani Kukhala Wacangu mu Utumiki

NCHITO yofunika kwambili imene ikugwilidwa padziko lapansi masiku ano ndi yolalikila uthenga wabwino. Inunso monga mmodzi wa atumiki a Yehova, mosakaikila mumaona kuti kugwila nchito yopanga ophunzila ndi mwai wamtengo wapatali. Ndipo mumadziŵa bwino kuti nthawi zina, apainiya ndi ofalitsa amakumana ndi mavuto amene angacepetse cangu cao mu utumiki.

N’ciani cingakuthandizeni kupitiliza kukhala wacangu mu utumiki?

Ofalitsa ena, zimawavuta kupeza munthu woti amulalikile akakhala mu ulaliki wa khomo ndi khomo. Nthawi zina anthu ambili a kumaloko samapezeka pa nyumba. Akapezeka pa nyumba, samafuna kumva uthenga wa Ufumu, m’malo mwake amakhala amphwayi, mwinanso ankhanza. Ofalitsa ena amakhala ndi magawo aakulu osavuta kulalikilamo. Pa cifukwa cimeneci, io amacita mantha kuti mwina angalephele kumaliza kulalikila gawo lonse. Anthu ena mumpingo agwa ulesi poona kuti akhala akulalikila kwa zaka zambili kuposa mmene anali kuganizila.

Kodi tiyenela kudabwa kuti anthu onse a Mulungu amakumana ndi mavuto amene angacepetse cangu cao m’nchito yolalikila? Iyai. Kunena zoona, tonse tiyenela kuyembekezela kukumana ndi mavuto polalikila uthenga wa Mulungu wopatsa moyo wa coonadi m’dziko limene likulamulidwa ndi “woipayo,” amene ndi Satana Mdyelekezi.—1Yoh. 5:19.

Kaya mukukumana ndi mavuto otani polalikila uthenga wabwino, dziŵani kuti Yehova angakuthandizeni kuwagonjetsa. Nanga n’ciani cingakuthandizeni kuonjezela cangu canu mu utumiki wacikristu umenewu? Tiyeni tikambilane zinthu zina zimene mungacite.

THANDIZANI ATSOPANO

Caka ciliconse, anthu masauzande ambili amabatizidwa kukhala Mboni za Yehova. Ngati munasonyeza kudzipeleka kwanu kwa Mulungu mwa ubatizo wa m’madzi posacedwapa, mosakaikila mudzapindula ndi thandizo locokela kwa ena amene akhala akulalikila kwa nthawi yaitali kuposa inu. Ndipo ngati mwakhala wofalitsa wa Ufumu kwa zaka zambili, ndi kwanzelu ndiponso kopindulitsa kuti muthandize kuphunzitsa atsopano

Yesu anadziŵa kuti ophunzila ake anali kufunikila malangizo owathandiza kukhala alaliki ogwila  mtima, ndipo anawasonyeza mmene ayenela kugwilila nchito imeneyo. (Luka 8:1) Ngakhale masiku ano, n’kofunika kuphunzitsa ena kuti akhale alaliki ogwila mtima.

Sitiyenela kuganiza kuti wofalitsa watsopano angaphunzile luso lophunzitsa mwa kungopita mu utumiki. Wofalitsayo afunika kupatsidwa malangizo acindunji kucokela kwa mphunzitsi wokoma mtima ndi wacikondi. Maphunzilowo angaphatikizepo kuthandiza wofalitsa watsopano (1) kukonzekela ndi kuyeseza ulaliki, (2) kuloŵetsa mwininyumba kapena munthu amene akumana naye pamseu mumakambilano, (3) kugaŵila zofalitsa, (4) kupanga ulendo wobwelelamo kwa munthu wacidwi, ndi (5) kuyambitsa phunzilo la Baibulo. Mosakaikila, watsopanoyo adzapindula mwa kuona ndi kutengela njila zimene womuphunzitsayo akugwilitsila nchito mu utumiki. (Luka 6:40) Wofalitsa watsopanoyo, mosakaikila adzasangalala kukhala ndi munthu amene angamuthandize pakafunikila thandizo lililonse. Wofalitsa amene ali ndi cidziŵitso cocepa, adzapindulanso mwa kumuyamikila pa zimene akucita bwino ndi kum’patsa malangizo othandiza.—Mlal. 4:9, 10.

MUZIKAMBILANA NDI MNZANU AMENE MULI NAYE MU ULALIKI

Masiku ena, makambilano amene mungakhale nao ndi mnzanu amene muli naye mu ulaliki angakhale olimbikitsa kwambili kuposa makambilano amene mungakhale ndi eninyumba. Musaiŵale kuti Yesu anatumiza ophunzila ake “aŵiliaŵili” kokalalikila. (Luka 10:1) Iwo anali kulimbikitsana pogwilila nchito limodzi. Motelo, nthawi imene timakhala ndi Akristu anzathu mu ulaliki, imatipatsa mwai ‘wolimbikitsana.’—Aroma 1:12.

Ndi zinthu zina ziti zimene mungakambilane? Kodi pali zinthu zolimbikitsa zimene zinacitikila aliyense wa inu mu utumiki ca posacedwapa? Kodi munaphunzila mfundo yocititsa cidwi pa phunzilo lanu laumwini kapena la banja? Kodi pali mfundo imene inakulimbikitsani pamisonkhano? Mwina ndi koyamba kuyenda ndi munthu amene muli naye mu ulaliki. Kodi mukudziŵa mmene anaphunzilila coonadi? N’ciani cinamuthandiza kutsimikiza mtima kuti ili ndi gulu la Yehova? Ndi mautumiki ena ati amene akhala nao m’gulu la Mulungu? Nanga akumanapo ndi zotani? Mwina mungamuuzenso zimene mwakumana nazo mu utumiki. Kugwila nchito yolalikila ndi wina kumakupatsani mwai ‘wopitiliza . . . kulimbikitsana’ mosasamala kanthu za mmene ulaliki wanu ulili pa tsikulo.—1 Ates. 5:11.

TSATILANI NDANDANDA YANU YOPHUNZILA BAIBULO

Cinthu cofunika kwambili cimene cingatithandize kukhalabe acangu mu utumiki ndi kukhala ndi  ndandanda yokhazikika yophunzila Baibulo. “Kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” wakhala akufalitsa nkhani zosiyanasiyana. (Mat. 24:45) Conco, pali nkhani zambili zimene mungagwilitsile nchito kuti mudye cakudya cakuuzimu. Tiyeni tikambilane citsanzo ca nkhani imene mungagwilitsile nchito pa phunzilo lanu laumwini. Nkhani yake ndi yakuti: N’cifukwa ciani nchito yolalikila za Ufumu ndi yofunika kwambili? Kabokosi kali pa tsamba 16 kasonyeza zifukwa zina.

Kusinkhasinkha pa mfundo zimene zili m’kabokosi kameneka kungakuthandizeni kupitiliza kulalikila mwacangu. Pamene mukucita phunzilo laumwini, mungacite bwino kupeza zifukwa zina zimene mungaonjezele pa ndandanda imeneyi. Ndiyeno, sinkhasinkhani pa zifukwazo ndi Malemba amene akucilikiza mfundozo. Kucita zimenezi kudzakuthandizani kukhalabe wacangu mu utumiki.

KHALANI WOKONZEKA KUTSATILA MALANGIZO ENA

Nthawi zonse, gulu la Yehova limatipatsa malangizo othandiza kuongolela ulaliki wathu. Mwacitsanzo, kuonjezela pa ulaliki wa khomo ndi khomo, tingacite ulaliki wa m’makalata, wa pafoni, wa mu mseu ndi kumalo ena kumene kumapezeka anthu ambili, ndiponso kulalikila anthu mwamwai ndi ku malo a malonda. Tingasinthenso zinthu zina paumoyo wathu kotelo kuti tizilalikila ku magawo amene samalalikilidwa kaŵilikaŵili.

Kodi ndinu wokonzeka kutsatila malingalilo awa? Kodi mwayesapo kale ena a io? Ofalitsa ena amene ayesa kutsatila malingalilo awa akhala osangalala ndi zotsatilapo zake. Taganizilani zitsanzo zitatu izi.

Citsanzo coyamba ndi cokhudza mfundo ina ya mu Utumiki wa Ufumu pa mbali zoyambitsa maphunzilo a Baibulo. Nkhani zimenezi zinathandiza  mlongo wina dzina lake April kuyamba kuphunzila Baibulo ndi anthu atatu amene amagwila nao nchito. Mlongoyu anadabwa ndipo anakondwela kuti onse atatu anavomela kuphunzila Baibulo, ndi kuyamba kupezeka pa misonkhano ya mpingo.

Citsanzo caciŵili ndi cokhudza mmene timagaŵila magazini athu. Timalimbikitsidwa kufunafuna anthu amene angakhuzidwe ndi nkhani inayake yopezeka m’magazini athu. Woyang’anila dela wina ku United States anafotokoza kuti anagaŵila Galamukani! imene munali nkhani yokhudza matayala, kwa a manijala onse a masitolo ogulitsa matayala kudela limenelo. Iye ndi mkazi wake anagaŵilanso magazini a Galamukani! yacingelezi mmene munali nkhani zakuti “Understanding Your Doctor” [Kudziŵa Bwino Dokotala Wanu] mu maofesi oposa 100 a madokotala m’dela lake. Iye anati: “Kukambilana nkhani za conco kwathandiza kuti anthu atidziŵe ndi kulandila zofalitsa zathu. Pambuyo popanga ubwenzi ndi anthu amenewa, takhala ndi mwai wokambilana nao kaŵilikaŵili.”

Citsanzo cacitatu ndi cokhudza ulaliki wa pafoni. Mlongo wina dzina lake Judy analemba kalata ku likulu lathu kuyamikila kaamba kolimbikitsidwa kucita ulaliki wa pafoni. Iye anakamba kuti amai ake a zaka 86 omwe anali ndi mavuto athanzi, nthawi zonse anali kucita ulaliki wa pafoni umenewu moti anali kusangalala kwambili kutsogoza phunzilo mai wina wa zaka 92.

Malangizo amene amapezeka m’zofalitsa zathu okhudza mmene tingacitile umboni ndi othandizadi. Conco, muziwagwilitsila nchito cifukwa angakuthandizeni kukhalabe acangu ndi acimwemwe mu utumiki.

KHALANI NDI ZOLINGA ZOYENELA

Kukhala mlaliki wopambana sikumadalila pa kuculuka kwa zofalitsa zimene timagaŵila, maphunzilo amene timacititsa, kapena anthu amene tathandiza kukhala atumiki a Yehova. Ndi acibale angati amene Nowa anathandiza kukhala alambili a Yehova? Komabe, iye anali mlaliki wopambana. Cofunika kwambili ndi kutumikila Yehova mokhulupilika.—1 Akor. 4:2.

Ofalitsa Ufumu ambili azindikila kuti ayenela kukhala ndi zolinga zoyenela kuti aonjezele cangu cao mu ulaliki. Kodi zina mwa zolinga zimenezo ndi ziti? Malangizo ena afotokozedwa m’kabokosi patsamba lino.

Ndi thandizo la Yehova, pezani njila za mmene mungapangile utumiki wanu kukhala wokhutilitsa ndiponso waphindu. Mukakwanilitsa zolinga zanu, mudzakhala wacimwemwe ndi wokhutila podziŵa kuti mwacita zonse zimene mungathe kuti mulalikile uthenga wabwino.

N’zoona kuti kulalikila uthenga wabwino kungakhale kovuta. Koma pali zina zimene mungacite kuti mukhale wolengeza Ufumu wacangu. Muyenela kulimbikitsana ndi mnzanu amene muli naye mu ulaliki, kukhala ndi ndandanda yophunzila Baibulo, kugwilitsila nchito malangizo ocokela kwa kapolo wokhulupilika, ndi kukhala ndi zolinga zoyenela. Koposa zonse, kumbukilani kuti Mulungu wakupatsani udindo waukulu wolengeza uthenga wabwino monga Mboni yake. (Yes. 43:10) Ndithudi, muzapeza cimwemwe cacikulu mukapitilizabe kukhala wacangu mu utumiki.