Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Yehova Akutsogolela Nchito Yathu Yophunzitsa Padziko Lonse

Yehova Akutsogolela Nchito Yathu Yophunzitsa Padziko Lonse

“Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino, amene ndimakucititsani kuti muyende m’njila imene muyenela kuyendamo.”—YES. 48:17.

1. Kodi Akristu akumana ndi mavuto otani polalikila masiku ano?

PAMENE Ophunzila Baibulo * anayamba kulalikila uthenga wabwino zaka zoposa 130 zapitazo, io anakumana ndi mavuto ambili. Mofanana ndi Akristu a m’nthawi ya atumwi, io anali kagulu kocepa, ndipo anali kulalikila uthenga umene anthu ambili sanali kusangalala nao. Anthu ena anali kuwaona kuti ndi osaphunzila. Satana atagwetsedwa padziko lapansi, io anazunzidwa. (Chiv. 12:12) Kucokela nthawiyo, io akhala akulalikila ‘m’masiku otsiliza’ ano omwe ndi “nthawi yapadela komanso yovuta.”—2 Tim. 3:1.

2. N’ciani cimene Yehova wakhala akucita kuti nchito yolalikila ipite patsogolo masiku ano?

2 Yehova wakhala akuthandiza anthu ake masiku ano. Iye akufuna kuti io alalikile uthenga wabwino padziko lonse, ndipo sadzalola ciliconse kusokoneza nchitoyi. Iye wathandiza anthu ake kumulambila m’njila imene amaivomeleza mwa kuwalekanitsa ndi cipembedzo cabodza. Mulungu anacita zofanana ndi zimenezi  m’nthawi yakale pamene anamasula Aisiraeli kucoka ku Babulo. (Chiv. 18:1-4) Zimene Yehova amatiphunzitsa zimatipindulitsa. Iye amatithandiza mmene tingakhalile pamtendele ndi ena, ndipo amatiphunzitsa mmene tingaphunzitsile ena za iye. (Ŵelengani Yesaya 48:16-18.) Mfundo yakuti Yehova amatsogolela nchito yathu, sitanthauza kuti iye nthawi zonse amasintha zocitika za m’dziko kuti atithandize kulalikila. N’zoona kuti zinthu zina zimene zakhala zikucitika m’dziko zatithandiza kulalikila mosavuta. Koma timanzuzidwabe ndipo timakumana ndi mavuto ambili cifukwa ca dziko la Satana. Zakhala zotheka kulalikila cifukwa ca thandizo la Yehova.—Yes. 41:13; 1 Yoh. 5:19.

3. Kodi ulosi wa Danieli wakwanilitsidwa bwanji?

3 Yehova anauzila mneneli Danieli kulosela kuti m’nthawi yamapeto, anthu “adzadziŵa zinthu zambili zoona.” (Ŵelengani Danieli 12:4.) Yehova anathandiza Ophunzila Baibulo kumvetsetsa coonadi cofunika ca m’Malemba cimene cinali citabisika cifukwa ca ziphunzitso zabodza za cikristu ca dziko. Iye panopa akugwilitsila nchito anthu ake kudziŵikitsa coonadi padziko lonse lapansi. Masiku ano, tikuona kukwanilitsidwa kwa ulosi wa Danieli umenewu. Anthu pafupifupi 8 miliyoni aphunzila coonadi ca m’Baibulo, ndipo akulalikila coonadi cimeneci padziko lonse lapansi. Ndi zinthu zina ziti zimene zathandiza kuti nchito yolalikila padziko lapansi itheke?

KUMASULILA BAIBULO

4. Kodi Baibulo linali litamasulidwa m’zinenelo zingati podzafika m’caka ca 1900?

4 Masiku ano, anthu ambili ali ndi Baibulo ndipo zimenezi zimatithandiza kuwaphunzitsa uthenga wabwino. Koma sikuti zinthu zinali conco kuyambila kale. Kwa zaka zambili, atsogoleli acipembedzo sanali kufuna kuti anthu aziŵelenga Baibulo. Iwo anali kuzunza aliyense amene anali kupeza akuŵelenga Baibulo, ndipo anapha anthu ena amene anali kulimasulila. Koma ca m’ma 1800, mabungwe ena anamasulila Baibulo kapena kulisindikiza m’zinenelo pafupifupi 400. Podzafika m’caka ca 1900, anthu ambili anali ndi Baibulo laolao, koma sanali kulimvetsetsa.

5. N’ciani cimene Mboni za Yehova zacita kuti zimasulile Baibulo?

5 Ophunzila Baibulo anali kudziŵa kuti ayenela kulalikila, ndipo anali kucita khama kufotokoza zimene Baibulo limaphunzitsa. Kuonjezela pamenepo, anthu a Yehova akhala akugwilitsila nchito Mabaibulo osiyanasiyana ndiponso kuwagaŵila. Kuyambila mu 1950, io afalitsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, lathunthu kapena mbali yake cabe m’zinenelo zoposa 120. Mu 2013, anafalitsa Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso. Baibulo limeneli ndi losavuta kumvetsa ndi kumasulila. Ndipo kugwilitsila nchito Baibulo losavuta kumvetsa kumatithandiza pa nchito yathu yolalikila.

PA NTHAWI ZA MTENDELE

6, 7. (a) Ndi nkhondo zotani zimene zacitika pa zaka 100 zapitazo? (b) Kodi kukhala ndi nthawi za mtendele m’maiko ena kwathandiza bwanji pa nchito yolalikila?

6 Inu mungadabwe kuti, ‘Kodi padziko lapansi pakhalako mtendele woculuka bwanji?’ Pa zaka 100 zapitazi anthu mamiliyoni ambili anafa cifukwa ca nkhondo makamaka pa nkhondo ziŵili za padziko lonse lapansi. Koma mu 1942, pamene Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse inali mkati, M’bale Nathan Knorr yemwe anali kutsogolela Mboni za Yehova, anakamba nkhani pa msonkhano wacigawo ya mutu wakuti “Kodi Padzikoli Padzakhala Mtendele?” Pofotokoza ulosi wa pa Chivumbulutso caputala 17, M’bale Knorr anapeleka umboni wosonyeza kuti padziko lapansi padzakhala mtendele pambuyo pa nkhondoyo.—Chiv. 17:3, 11.

 7 Koma Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse itatha, padziko lapansi panalibe mtendele weniweni. Kucokela nthawiyo, anthu mamiliyoni ambili afa pankhondo zina. Koma m’maiko ena, mwakhalako nthawi za mtendele, ndipo panthawizi anthu a Yehova akhala akulalikila popanda zovuta. Kodi pakhala zotsatilapo zotani? Panthawi ya nkhondo yaciŵili ya padziko lonse, panali Mboni za Yehova zosakwana 110,000. Koma masiku ano pali Mboni za Yehova pafupifupi 8 miliyoni. (Ŵelengani Yesaya 60:22.) Zoonadi, panthawi za mtendele timatha kulalikila uthenga wabwino kwa anthu ambili.

NJILA ZA MAKONO ZA MAYENDEDWE

8, 9. Ndi motani mmene kayendedwe kakhalila kosavuta? Nanga zimenezi zathandiza bwanji pa nchito yathu?

8 Pamene anthu a Yehova anayamba kulalikila ku United States, zinali zovuta kwambili kuyenda mitunda yaitali. Mu 1900, pafupifupi zaka 21 pambuyo poti ayamba kufalitsa magazini a The Watch Tower, m’dzikolo munali cabe magalimoto pafupifupi 8,000, ndipo miseu yabwino inali yoŵelengeka cabe. Koma masiku ano, padziko lonse pali magalimoto oposa 1.5 biliyoni, ndipo m’maiko ambili muli miseu yabwino. Zimenezi zathandiza kuti zikhale zosavuta kupita kukalalikila kwa anthu amene amakhala kumadela a ku midzi omwe ndi ovuta kufikako. Ngakhale kuti tikukhala ku dela kumene mayendedwe ndi ovuta, ndipo timafunika kuyenda mitunda yaitali, timacita zonse zothekela kupita kukalalikila kulikonse kumene tingapeze anthu.—Mat. 28:19, 20.

9 Timagwilitsilanso nchito njila zina za mayendedwe. Timagwilitsila nchito mathilaki, masitima a pamadzi ndi a pa mtunda potumiza Mabaibulo komanso zofalitsa zina. Zimenezi zimapangitsa kuti abale amene amakhala ku madela akutali azilandila zofalitsa zathu pambuyo pa milungu yocepa akamaliza kuzisindikiza. Oyang’anila dela, abale a m’ma Komiti a Nthambi, amishonale, ndi abale ena amayenda pandege kuti akakambe nkhani ku misonkhano yacigawo ndi kulimbikitsa mipingo. Abale a m’Bungwe Lolamulila komanso abale ena a ku likulu lathu, amayendanso pandege kupita ku maiko ena kuti akalimbikitse ndi kuphunzitsa abale nchito zina. Zonsezi zimathandiza anthu a Yehova kukhala ogwilizana.—Sal. 133:1-3.

NCHITO YOMASULILA

10. N’cifukwa ciani tingakambe kuti Cingelezi ndi cinenelo codziŵika padziko lonse?

10 M’nthawi ya atumwi, anthu ambili mu  Ufumu wa Roma anali kulankhula Cigiliki. Kodi palinso cinenelo cofala kwambili masiku ano? Anthu ambili angakambe kuti Cingelezi ndi cofala kwambili. Buku lina linati: “Anthu ambili padziko lapansi amalankhula bwino Cingelezi.” (English as a Global Language) Anthu ambili amaphunzila Cingelezi cimeneci, n’colinga cakuti acigwilitsile nchito pokambilana zamalonda, zandale, ndi zasayansi.

11. Kodi Cingelezi cakhudza bwanji nchito ya anthu a Yehova?

11 Cifukwa cakuti anthu ambili amadziŵa cingelezi, zakhala zosavuta kufalitsa coonadi. M’zaka za m’mbuyomu, zofalitsa zathu zinali kupezeka cabe m’Cingelezi. Anthu ambili anali kukwanitsa kuŵelenga zofalitsazo cifukwa Cingelezi cinali codziŵika. Cingelezi ndi cinenelo cimene amagwilitsilanso nchito ku likulu lathu. Komanso, cingelezi ndi cimene amagwilitsila nchito ku Patterson, New York, pophunzitsa abale ocokela ku maiko osiyanasiyana.

12. Kodi zofalitsa zathu zikumasulidwa m’zinenelo zingati? Nanga mapulogalamu a pakompyuta akhala othandiza bwanji pa nchitoyi?

12 Tili ndi udindo wolalikila uthenga wabwino kwa anthu padziko lonse lapansi. Pa cifukwa cimeneci, timamasulila zofalitsa zathu m’zinenelo zoposa 700. Kodi zimenezi zatheka bwanji? Takhala tikugwilitsila nchito makompyuta ndiponso mapulogalamu ena a pakompyuta monga MEPS panchito yomasulila (Multilanguage Electronic Publishing System). Zimenezi zathandiza kuti Mboni za Yehova padziko lonse lapansi zizimvetsetsa “cilankhulo coyela” ca m’Baibulo ndi kukhala ogwilizana.—Ŵelengani Zefaniya 3:9.

MALAMULO NDIPONSO ZIGAMULO ZA KU MAKHOTI

13, 14. Kodi malamulo ndiponso zigamulo za ku makhoti zatithandiza bwanji pa nchito yolalikila?

13 Monga mmene tinaonela m’nkhani yapita, Akristu oyambilila anapindula ndi lamulo laciroma limene linali kugwila nchito mu ufumu wonsewo. Masiku ano, Akristu naonso amapindula ndi malamulo ena. Mwacitsanzo, ku United States, kumene kuli likulu lathu, malamulo amapeleka ufulu wa cipembedzo, wolankhula ndi wosonkhana pamodzi. Zimenezi zathandiza abale ku United States kuti azisonkhana ndi kukambilana Baibulo poyela, ndiponso kuuzako ena zimene amaphunzila. Koma pakhalanso nthawi zina pamene tinafunika kupita ku makhoti kuti titeteze ufulu wathu wolalikila uthenga wabwino. (Afil. 1:7) Ndipo pamene oweluza a  ku makhotiwo anali kufuna kutilanda ufulu wathu wolalikila, tinacita apilo ku makhoti apamwamba ndipo nthawi zambili tinapambana milanduyo.

14 M’maiko ena, tapitanso ku makhoti pofuna kuteteza ufulu wathu wa kulambila Yehova ndi kulalikila poyela. Ngati mlandu wathu sunayende bwino ku makhoti aang’ono, timapita ku makhoti aakulu padziko lonse. Mwacitsanzo, nthawi zambili timapita ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Podzafika mu June 2014, tinali titapambana kale milandu yoposa 57 mu khoti limeneli, ndipo maiko ambili a ku Ulaya amafunikila kutsatila zigamulo zimene khotili limapeleka. Ngakhale kuti ‘mitundu yonse imadana nafe,’ malamulo a m’maiko ambili amatilola kulambila Yehova mwaufulu.—Mat. 24:9.

ZINTHU ZINANSO ZOTHANDIZA PA NCHITO YATHU YOPHUNZITSA

Tikufalitsa mabuku othandiza kuphunzila Baibulo kwa anthu padziko lonse lapansi

15. Kodi njila yosindikizila mabuku yasintha motani? Nanga zimenezi zatithandiza bwanji pa nchito yathu yolalikila?

15 Njila zatsopano zosindikizila zofalitsa zatithandiza kulalikila kwa anthu ambili. Kwa zaka zambili, anthu anali kusindikiza mabuku pogwilitsila nchito makina amene Johannes Gutenberg anapanga mu 1450. Koma makina osindikizila asintha kwambili pa zaka 200 zapitazi. Kunabwela makina atsopano osindikizila amene athandiza kuti mabuku ambili azipulintidwa panthawi imodzi ndiponso azioneka okongola. M’kupita kwa nthawi, zinakhalanso zosavuta kupanga mapepala ndi kukonza mabuku. Kodi masinthidwe amenewa akhudza bwanji zofalitsa zathu? Mu 1879, magazini yoyamba ya The Watch Tower inasindikizidwa mu Cingelezi. Magaziniyo inalibe zinthuzi zilizonse, ndipo makope 6,000 ndi amene anasindikizidwa. Masiku ano, Nsanja ya Mlonda imasindikizidwa m’zinenelo zoposa 200. Magaziniwa ali ndi zithunzi zokongola kwambili, ndipo makope oposa 50 miliyoni a magazini imeneyi amasindikizidwa mwezi uliwonse ndi kufalitsidwa.

16. Ndi zinthu zina ziti zimene zatithandiza pa nchito yathu yolalikila padziko lonse? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

16 Makina ena atsopano amene apangidwa pa zaka 200 zapitazi athandiza anthu a Yehova pa nchito yao yolalikila uthenga wabwino. Tachulapo kale za ma sitima, magalimoto, ndi ndege. Koma takhala tikugwilitsilanso nchito njinga, mataipilaita, makina olembela zilembo za anthu akhungu, ma telegalafu, matelefoni, makamela, makina ojambulila mau, makina ojambulila mavidiyo, mawailesi, ma T.V., mafilimu, makompyuta, ndiponso Intaneti. Ngakhale kuti zinthu zimenezi sizinapangidwe ndi anthu a Yehova, io amazigwilitsila nchito kupanga Mabaibulo ndi zofalitsa zina m’zinenelo zambili ndi kulalikila padziko lonse lapansi. Mwakutelo, io ‘amayamwa mkaka wa mitundu ya anthu’ monga mmene ulosi wa m’Baibulo umanenela.—Ŵelengani Yesaya 60:16.

17. N’cifukwa ciani Yehova watilola kukhala “anchito anzake”?

17 Apa n’zoonekelatu kuti Yehova akutsogolela nchito yolalikila. N’zoona kuti Yehova samadalila thandizo lathu kuti akwanilitse cifunilo cake. Koma Atate wathu wacikondi watilola kukhala “anchito anzake.” Mwakutelo, timaonetsa kuti timakonda Mulungu komanso anthu ena. (1 Akor. 3:9; Maliko 12:28-31) Tiyeni tizigwilitsila nchito mpata uliwonse umene tingakhale nao kulalikila uthenga wa Ufumu, imene ndi nchito yofunika kwambili padziko lapansi. Ndipo tiyeni tionetse Yehova kuti ndife oyamikila potitsogolela ndi kudalitsa nchito yathu yophunzitsa padziko lapansi.

^ par. 1 Ophunzila Baibulo anayamba kuchedwa Mboni za Yehova mu 1931.—Yes. 43:10.