Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kuthandiza Abale a Kristu Mokhulupilika

Kuthandiza Abale a Kristu Mokhulupilika

“Pa mlingo umene munacitila zimenezo mmodzi wa abale anga aang’ono awa, munacitila ine amene.”—MAT. 25:40.

1, 2. (a) Ndi mafanizo ati amene Yesu anauza anzake apamtima? (Onani cithunzi cili pamwamba.) (b) N’ciani cimene tifunika kudziŵa ponena za fanizo la nkhosa ndi mbuzi?

YESU anali kulankhula ndi Petulo, Andireya, Yakobo, ndi Yohane, omwe anali anzake apamtima za nkhani ina yocititsa cidwi. Pambuyo powauza fanizo la kapolo wokhulupilika ndi wanzelu, la anamwali 10, ndi la matalente, Yesu anakambanso za nthawi imene “Mwana wa munthu” adzaweluza “mitundu yonse ya anthu.” Ndiyeno, Yesu anauza anzake fanizo lina. Iye anakamba kuti “Mwana wa munthu” adzalekanitsa anthu m’magulu aŵili. Gulu lina analicha kuti ndi nkhosa, ndipo gulu lina analicha kuti ndi mbuzi. Kuonjezela apo, gulu lina lacitatu lofunika analicha kuti “abale” a Mfumu.—Ŵelengani Mateyu 25:31-46.

2 Mofanana ndi atumwi, atumiki a Yehova a masiku ano amacitanso cidwi ndi fanizo limeneli cifukwa limakhudza tsogolo la anthu. Yesu anafotokoza cifukwa cake anthu ena adzalandila moyo wosatha pamene ena adzaonongedwa. N’cifukwa cake n’kofunika kwambili kuti tidziŵe zimene fanizoli limatanthauza, ndiponso zimene tifunika kucita kuti tikalandile moyo wosatha. Conco, m’nkhani ino tikambilana mafunso awa: Kodi Yehova watithandiza bwanji kumvetsa fanizo limeneli? Timadziŵa bwanji kuti fanizoli limagogomezela nchito yolalikila? Nanga ndani ayenela kulalikila? N’cifukwa ciani n’kofunika kuti anthu tsopano akhale okhulupilika kwa “Mfumu” ndi “abale” ake?

KODI YEHOVA WATITHANDIZA BWANJI KUMVETSA FANIZOLI?

3, 4. (a) N’ciani cimene tifunika kudziŵa kuti timvetse fanizo la nkhosa ndi mbuzi? (b) Kodi Zion’s Watch Tower inafotokoza bwanji fanizo limeneli mu 1881?

3 Kuti timvetse bwino fanizo la nkhosa ndi mbuzi, coyamba tifunika kudziŵa zinthu zitatu zochulidwa m’nkhaniyi. Tifunika kudziŵa anthu amene akuchulidwa, nthawi imene kuweluza kudzacitika, ndiponso cifukwa cimene cidzacititsa kuti ena akhale nkhosa kapena mbuzi.

4 Mu 1881, magazini ya Zion’s Watch Tower inakamba kuti “Mwana wa munthu” kapena kuti “Mfumu” ndi Yesu. Inafotokozanso kuti “abale” a Mfumu ndi anthu amene adzalamulila ndi Yesu kumwamba, ndiponso onse amene adzakhala ndi moyo padziko lapansi akadzakhala angwilo. Magazini imeneyo inakamba kuti anthu adzalekanitsidwa panthawi ya Ulamulilo wa Kristu wa Zaka 1000, ndi kuti anthu amene anatengela khalidwe la Mulungu la cikondi pa zocita zao zonse adzachedwa nkhosa.

5. Mu 1923, kodi anthu a Mulungu analimvetsa bwanji fanizoli?

5 Kuciyambi kwa zaka za m’ma 1920, Yehova anathandiza anthu ake kumvetsa fanizo limeneli. Magazini ya The Watch Tower ya October 15, 1923, inakamba kuti “Mwana wa munthu” ndi Yesu. Koma magaziniyo inagwilitsila nchito mavesi ena a m’Baibulo pofotokoza kuti “abale” a m’fanizoli amaimila anthu okhawo amene adzalamulila ndi Yesu, ndipo onse adzakhala kumwamba panthawi ya Ulamulilo wa Zaka 1000. Inafotokozanso kuti nkhosa zimaimila anthu amene adzakhala padziko lapansi mu ulamulilo wa Yesu ndi abale ake. Nanga bwanji ponena za nthawi imene adzalekanitsa nkhosa ndi mbuzi? Magaziniyo inakamba kuti abale a Kristu adzakhala akulamulila ndi iye kumwamba panthawi ya Ulamulilo wa Zaka 1000, ndipo sadzalandila thandizo kucokela kwa anthu amene adzakhala padziko lapansi. Conco, kulekanitsa nkhosa ndi mbuzi kuyenela kucitika Ulamulilo wa Zaka 1000 usanayambe. Ponena za cifukwa cimene cidzacititsa munthu kuweluzidwa kuti ndi nkhosa, magaziniyo inakamba kuti anthu adzaweluzidwa kuti ndi nkhosa cifukwa cokhulupilila Yesu ndi kukhulupilila kuti Ufumu udzabweletsa zinthu zabwino.

6. Kodi kamvedwe kathu ka fanizoli kanasintha bwanji mu 1995?

6 Kwa zaka zambili, tinali kukhulupilila kuti anthu anali kuweluzidwa kupyolela m’nchito yolalikila imene ikucitika m’nthawi ino ya mapeto. Ngati munthu walandila uthenga wathu, anali kuweluzidwa kuti ndi nkhosa, ndipo ngati wakana, anali kuweluzidwa kuti ndi mbuzi. Komabe, mu 1995, kamvedwe kathu pa fanizo limeneli kanasintha. Nsanja ya Olonda ya October 15, 1995, inaonetsa kufanana kwa mau a Yesu opezeka pa Mateyu 24:29-31 (ŵelengani) ndi opezeka pa Mateyu 25:31, 32. (ŵelengani.) Inafotokozanso kuti Yesu adzaweluza anthu panthawi ya cisautso cacikulu pamene iye “adzafika mu ulemelelo wake.” *

7. Ndi kamvedwe kotani kamene tili nako masiku ano?

7 Masiku ano, tamalimvetsa bwino fanizo la nkhosa ndi mbuzi. Ponena za anthu amene akuchulidwa m’fanizoli, Yesu ndiye “Mwana wa munthu,” kapena kuti Mfumu. Amene akuchulidwa kuti “abale anga,” ndi amuna ndi akazi odzozedwa amene adzalamulila ndi Kristu kumwamba. (Aroma 8:16, 17) “Nkhosa” ndi “mbuzi” zikuimila anthu a mitundu yonse, amene sanadzozedwe ndi mzimu woyela. Nanga bwanji za nthawi pamene ciweluzo cidzacitika? Ciweluzo cimeneco cidzacitika cisautso cacikulu cikadzatsala pang’ono kutha. Bwanji ponena za cifukwa cimene anthu adzaweluzidwila kuti ndi nkhosa kapena mbuzi? Zimenezo zidzadalila mmene io amacitila zinthu ndi abale otsalila odzozedwa a Kristu amene akali padziko lapansi. Pamene mapeto a dongosolo lino ali pafupi kwambili, ndife oyamikila kuti Yehova pang’onopang’ono watithandiza kumvetsa fanizoli, ndi mafanizo ena opezeka pa Mateyu caputala 24 ndi 25.

KODI FANIZOLI LIMAGOGOMEZELA BWANJI NCHITO YOLALIKILA?

8, 9. N’cifukwa ciani Yesu anacha nkhosa kuti ‘olungama’?

8 M’fanizo la nkhosa ndi mbuzi, Yesu sanachule mwacindunji za nchito yolalikila. Nanga n’cifukwa ciani tikukamba kuti fanizoli limagogomezela kufunika kolalikila?

9 Kuti tipeze yankho, coyamba tiyenela kukumbukila kuti Yesu anali kugwilitsila nchito mafanizo pophunzitsa. Conco, iye sanali kukamba za nkhosa ndi mbuzi zenizeni. Mofananamo, Yesu sanatanthauze kuti munthu aliyense amene adzaweluzidwa kuti ndi nkhosa ayenela kupatsa odzozedwa cakudya ndi zovala, kuwasamalila pamene adwala, kapena kupita kukawaona akakhala m’ndende. Yesu anacha anthu omwe ali ngati nkhosa kuti ‘olungama’ cifukwa io amazindikila kuti Kristu ali ndi gulu la odzozedwa amene akali padziko lapansi, ndipo amathandiza odzozedwawo mokhulupilika m’masiku ano otsiliza.—Mat. 10:40-42; 25:40, 46; 2 Tim. 3:1-5.

10. Kodi nkhosa zingathandize bwanji abale a Kristu?

10 Pamene Yesu anapeleka fanizo la nkhosa ndi mbuzi, anali kukamba zinthu zimene zidzacitika panthawi ya mapeto. (Mat. 24:3) Mwacitsanzo, iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mat. 24:14) Ndiyeno, asanakambe za nkhosa ndi mbuzi, Yesu anapeleka fanizo la matalente pofuna kuphunzitsa odzozedwa kuti afunika kugwila nchito yolalikila mwakhama. Koma pali odzozedwa ocepa cabe amene akali padziko lapansi, ndipo pali nchito yaikulu yofunika kucitidwa. Odzozedwa apatsidwa nchito yolalikila “ku mitundu yonse” mapeto asanafike. Monga mmene taphunzilila m’fanizo la nkhosa ndi mbuzi, “nkhosa” zidzathandiza abale a Yesu. Njila yabwino koposa imene io angathandizile abale a Yesu ndi mwa kugwila nao nchito yolalikila. Kodi kungopeleka ndalama zothandiza panchitoyi kapena kuwalimbikitsa kugwila nchitoyi ndi kokwanila?

NDANI AYENELA KULALIKILA?

11. Ndi funso liti limene ena angafunse? Nanga n’cifukwa ciani?

11 Masiku ano, ambili mwa ophunzila a Yesu oposa 8 miliyoni si odzozedwa. Anthu amenewa sanapatsidwe matalente amene Yesu anapatsa akapolo ake odzozedwa. (Mat. 25:14-18) Pa cifukwa cimeneci, ena angafunse kuti, ‘Ngati Yesu sanawapatse matalente, kodi afunikiladi kulalikila?’ Tiyeni tione cifukwa cake yankho lake ndi lakuti inde.

12. Tiphunzilapo ciani pa mau a Yesu opezeka pa Mateyu 28:19, 20?

12 Yesu analamula ophunzila ake onse kulalikila. Pambuyo poukitsidwa, Yesu anauza otsatila ake kuti ayenela kupanga ophunzila, ndi kuwaphunzitsa kusunga “zinthu zonse” zimene analamula. Malamulo amenewo anaphatikizapo lamulo lokhudza kulalikila. (Ŵelengani Mateyu 28:19, 20.) Motelo, ophunzila onse a Kristu ayenela kulalikila, kaya akuyembekezela kukalamulila kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansi.—Mac. 10:42.

13. Kodi masomphenya amene Yohane anaona akuonetsa ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

13 Buku la Chivumbulutso limaonetsa kuti odzozedwa ndiponso anthu ena adzagwila nchito yolalikila. Yesu anaonetsa mtumwi Yohane masomphenya a “mkwatibwi,” amene ndi odzozedwa okwana 144,000 omwe adzalamulila ndi Kristu kumwamba. Iwo anali kuitana anthu kuti “amwe madzi a moyo kwaulele.” (Chiv. 14:1, 3; 22:17) Madzi ophiphilitsila amenewo akuimila zinthu zimene Yehova wapeleka kuti anthu amasuke ku uchimo ndi imfa pa maziko a nsembe ya dipo ya Kristu. (Mat. 20:28; Yoh. 3:16; 1 Yoh. 4:9, 10) Dipo ndi mbali yofunika ya uthenga umene timalalikila, ndipo odzozedwa amatsogolela pa nchito yophunzitsa anthu ponena za dipo limeneli ndi mmene lingawapindulitsile. (1 Akor. 1:23) Koma m’masomphenyawo, Yohane anaona anthu ena amene sali m’gulu la mkwatibwi. Anthu amenewo akuuzidwa kuti “Bwela!” Iwo amamvela ciitano cimeneci, ndipo naonso amaitana ena kuti amwe madzi amoyo. Gulu laciŵili limeneli ndi anthu amene akuyembekezela kudzakhala padziko lapansi. Conco, masomphenya amenewa akuonetselatu kuti onse amene akulandila ciitano cakuti “bwela” ali ndi udindo wolalikila kwa ena.

14. Kodi timaonetsa bwanji kuti tikumvela “cilamulo ca Kristu”

14 Onse amene amamvela “cilamulo ca Kristu” afunika kulalikila. (Agal. 6:2) Yehova amafuna kuti onse amene amam’lambila azimvela malamulo ofanana. Mwacitsanzo, iye anauza Aisiraeli kuti: “Lamulo lililonse ligwile nchito mofanana kwa mbadwa ndi kwa mlendo wokhala pakati panu.” (Eks. 12:49; Lev. 24:22) Akristu samatsatila Cilamulo ca Mose, koma tonse timamvela “cilamulo ca Kristu” kaya ndife odzozedwa kapena ai. Cilamulo cimeneco ciphatikizapo zonse zimene Yesu anaphunzitsa. Cinthu cacikulu cimene Yesu anaphunzitsa n’cakuti ophunzila ake ayenela kuonetsa cikondi. (Yoh. 13:35; Yak. 2:8) Ndipo njila yaikulu imene timaonetsela kuti timakonda Mulungu, Kristu, ndi anzathu, ndi mwa kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu.—Yoh. 15:10; Mac. 1:8.

15. N’cifukwa ciani tingakambe kuti lamulo la Yesu limakhudza otsatila ake onse?

15 Zimene Yesu anauza ophunzila ake ocepa zingakhudzenso ophunzila ambili. Mwacitsanzo, Yesu anacita pangano la Ufumu ndi ophunzila ake 11 okha, koma pangano limenelo limakhudza a 144,000 onse. (Luka 22:29, 30; Chiv. 5:10; 7:4-8) Mofananamo, Yesu analamula otsatila ake ocepa, omwe anamuona ataukitsidwa, kuti ayenela kulalikila. (Mac. 10:40-42; 1 Akor. 15:6) Koma ophunzila ake onse a m’nthawi ya atumwi anazindikila kuti lamulo limenelo linali kuwakhudza ngakhale kuti Yesu sanalankhule kwa io mwacindunji. (Mac. 8:4; 1 Pet. 1:8) Masiku anonso, Yesu salankhula mwacindunji ndi aliyense wa alaliki acangu a Ufumu oposa 8 miliyoni. Ngakhale zili conco, onse amazindikila kuti ali ndi udindo wokhulupilila Kristu ndi kuonetsa cikhulupililo cimeneco mwa kugwila nchito yolalikila.—Yak. 2:18.

INO NDI NTHAWI YOKHALA WOKHULUPILIKA

16-18. Kodi tingathandize bwanji abale a Kristu mokhulupilika? Nanga n’cifukwa ciani ino ndiyo nthawi yocita zimenezi?

16 Satana akumenya nkhondo ndi abale otsalila odzozedwa a Kristu amene akali padziko lapansi. Iye akuonjezela kuukila kwake pamene watsala ndi “kanthawi kocepa.” (Chiv. 12:9, 12, 17) Ngakhale kuti akupilila mayeselo aakulu, odzozedwa akupitilizabe kutsogolela nchito yolalikila. Mosakaikila, Yesu ali nao ndipo akudalitsa khama lao.—Mat. 28:20.

17 Timaona kuti ndi mwai waukulu kuthandiza abale a Kristu kulalikila. Timawathandizanso mwa kupeleka ndalama ndi kucita khama pomanga Nyumba za Ufumu, Nyumba za Misonkhano, komanso maofesi a nthambi. Timaonetsanso kuti timathandiza abale a Kristu mwa kumvela mokhulupilika akulu ndi abale ena oikidwa ndi “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.”—Mat. 24:45-47; Aheb. 13:17.

Anthu amene ali ngati nkhosa amathandiza abale a Kristu m’njila zosiyanasiyana (Onani ndime 17)

18 Posacedwapa, angelo adzasiya kugwila mphepo zoononga za cisautso cacikulu. Izi zidzacitika pambuyo poti abale onse otsalila a Kristu amene adzakhala akali padziko lapansi adindidwa cidindo comaliza. (Chiv. 7:1-3) Aramagedo isanayambe, odzozedwa adzatengedwa kupita kumwamba. (Mat. 13:41-43) Conco, ino ndiyo nthawi yakuti anthu amene akuyembekezela kudzaweluzidwa monga nkhosa athandize abale a Kristu mokhulupilika.

^ par. 6 Kuti mudziŵe zambili ponena za fanizoli, onani nkhani yakuti “Kodi Mudzaima Motani ku Mpando wa Chiweruzo?” ndi yakuti “Kodi Nkhosazo ndi Mbuzizo Zili ndi Mtsogolo Motani?” mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1995.