NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA April 2015

Mu Nsanja ya Mlonda ino muli nkhani zophunzila za mlungu woyambila June 1 mpaka June 28, 2015.

Akulu, Kodi Mumakonda Kuphunzitsa Ena?

Onani mfundo 7 zimene akulu amene amaphunzitsa bwino ena anakamba.

Mmene Akulu Angathandizile Ena Kukhala Oyenelela Maudindo

Akulu angapindule akamatsatila mmene Yesu anali kuphunzitsila ena, ndipo ophunzila angapindule mwa kutengela citsanzo ca Elisa.

MBILI YANGA

Madalitso “m’Nthawi Yabwino ndi m’Nthawi Yovuta”

Nkhani ya M’bale Trophim Nsomba, amene anapilila cizunzo coopsa ku Malawi cifukwa ca cikhulupililo cake, ingakulimbikitseni kukhalabe okhulupilika.

Kodi Muli pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova?

Ubwenzi umalimba ngati anthu amakambilana. Kodi mungatsatile bwanji mfundo imeneyi kuti mulimbitse ubwenzi wanu ndi Mulungu?

Muzikhulupilila Yehova Nthawi Zonse

Mungathe kupilila mavuto aakulu amene angalepheletse munthu kulimbitsa ubwenzi wake ndi Mulungu.

Cifukwa Cake Kucotsa Munthu Mumpingo Ndi Makonzedwe Acikondi

Ngakhale kuti kucotsa munthu mumpingo kumapweteka kwambili, kodi kungakhale bwanji kopindulitsa?

Kodi Mtengo Ukadulidwa Ungaphukenso?

Yankho lake lingakuthandizeni kukhala ndi ciyembekezo colimba.