Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Akulu, Kodi Mumakonda Kuphunzitsa Ena?

Akulu, Kodi Mumakonda Kuphunzitsa Ena?

“Ciliconse cili ndi nthawi yake.” —MLAL. 3:1.

1, 2. Kodi oyang’anila madela aona kuti m’mipingo yambili muli vuto lotani?

WOYANG’ANILA DELA wina anali pafupi kutsiliza msonkhano wake ndi bungwe la akulu. Iye anasangalala ndi akuluwo cifukwa anali abusa odzipeleka ndipo ena mwa io anali acikulile ngati atate ake. Koma panali cinacake cimene cinamudetsa nkhawa. Conco anawafunsa kuti, “Abale, mwacita zotani kuti muphunzitse ena kukhala oyenelela maudindo mumpingo?” Akuluwo anakumbukila kuti pamene woyang’anila dela anabwela ulendo wapita anawalimbikitsa kuti ayeyesetse kuphunzitsa ena. Kenako mmodzi wa akuluwo anati, “Kunena zoona, palibe zimene tacita kwenikweni.” Ndipo akulu enawo anavomeleza.

2 Ngati ndinu mkulu, kodi zotele zinakucitikilamponi? N’zosakaikitsa. Padziko lonse, oyang’anila madela aona kuti m’mipingo yambili akulu afunika kucita khama kuphunzitsa abale ena, acinyamata ndi acikule, kuti azisamalila gulu la nkhosa. Koma zimenezi zimawavuta. N’cifukwa ciani?

3. (a) Kodi Malemba amaonetsa bwanji kuti kuphunzitsa ena n’kofunika? Nanga nkhaniyi ikutikhudza bwanji tonsefe? (Onani mau a munsi.) (b) N’cifukwa ciani akulu ena amalephela kuphunzitsa ena?

3 Mwacionekele, inuyo monga m’busa, mumadziŵa kuti kuphunzitsa ena n’kofunika. * Mumadziŵanso kuti pafunika abale ambili amene angalimbitse mipingo imene ilipo ndi kukhazikitsa mipingo ina yatsopano. (Ŵelengani Yesaya 60:22.) Komanso mumadziŵa kuti Mau a Mulungu amatilimbikitsa “kuphunzitsa ena.” (Welengani 2 Timoteyo 2:2) Komabe, mofanana ndi akulu amene tawachula m’ndime yoyamba, mungaone kuti kucita zimenezi n’kovuta. Pambuyo posamalila zosowa za banja, kugwila nchito yakuthupi, kusamalila maudindo a mumpingo, ndi kucita zinthu zina zofunika cisamalilo mwamsanga, mumaona kuti mulibe nthawi yokwanila yophunzitsa ena mumpingo. Conco tiyeni tikambilane cifukwa cake tiyenela kuona nchito yophunzitsa ena kukhala yofunika kwambili.

KUPHUNZITSA ENA N’KOFUNIKA KWAMBILI

4. N’cifukwa ciani nthawi zina akulu amanyalanyaza kuphunzitsa ena?

4 N’cifukwa ciani akulu ena sapatula nthawi kuti aphunzitse abale ena mumpingo? Mwina amaganiza kuti: ‘Kuphunzitsa ena n’kofunika, koma mumpingo muli maudindo ena ofunika kusamalidwa mwamsanga. Ndipo ngati sindinaphunzitse ena, mpingo sungalephele kuyenda bwino.’  Ngakhale kuti inu akulu muli ndi maudindo ambili ofunika kusamalidwa mwamsanga, dziŵani kuti kunyalanyaza kuphunzitsa ena kungapangitse kuti mpingo usapite patsogolo.

5, 6. N’ciani cimene tikuphunzila pa citsanzo ca dalaivala amene amanyalanyaza kusamalila injini ya galimoto yake? Nanga zimenezi zikugwilizana bwanji ndi nchito yophunzitsa ena mumpingo?

5 Ganizilani citsanzo ici: Dalaivala amadziŵa kuti nthawi ndi nthawi amafunika kuthila oilo watsopano mu injini kuti galimoto yake iziyenda bwino. Koma iye angaganize kuti kucita zimenezo si kofunika kwambili poyelekezela ndi kuthila petulo m’galimoto. Ndipo n’zoona kuti ngati sathila petulo, galimotoyo ingaleke kuyenda. Mwina iye angaganize kuti, ‘Ndilibe nthawi yosintha oilo, ndipo ngakhale ndisaisinthe, galimotoyi ipitilizabe kuyenda kwa kanthawi.’ Koma kodi kucita zimenezi kuli ndi vuto lotani? Ngati iye anyalanyazabe kusintha oilo mu injini, tsiku lina galimotoyo ingaonongeke kwambili ndi kulekelatu kuyenda. Zikakhala conco, iye angafunike kuononga nthawi ndi ndalama zambili kuti akonze galimotoyo. Kodi tikuphunzilapo ciani pamenepa?

6 Akulu amasamalila maudindo ambili ofunika amene ngati sangawasamalile mwamsanga mpingo ungakhale pangozi. Conco mofanana ndi dalaivala amene tachula m’citsanzo cija, yemwe amaonetsetsa kuti wathila mafuta m’galimoto yake, akulu amafunika ‘kutsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ndi ziti.’ (Afil. 1:10) Komabe, mofanana ndi dalaivala uja amene amalephela kusamalila injini ya galimoto yake, akulu ambili amatangwanika kwambili kusamalila maudindo ena cakuti amanyalanyaza kuphunzitsa ena. Ngati akulu amanyalanyaza kuphunzitsa ena, m’kupita kwa nthawi mumpingo mungasowe abale oyenelela amene angasamalile maudindo.

7. Kodi akulu amene amapatula nthawi kuti aphunzitse ena tiyenela kuwaona bwanji?

7 Motelo sitiyenela kuona kuti kuphunzitsa ena mumpingo n’kosafunika kwenikweni. Akulu amene amaganizila zamtsogolo mwa kuphunzitsa abale ena amaonetsa kuti ndi oyang’anila anzelu ndipo mpingo wonse umapindula. (Ŵelengani 1 Petulo 4:10) Kodi mpingo umapindula bwanji?

KUPHUNZITSA ENA NDI NZELU

8. (a) N’ciani cimene ciyenela kulimbikitsa akulu kuphunzitsa ena? (b) Kodi akulu amene akutumikila m’madela osowa ali ndi udindo wofunika kwambili uti? (Onani bokosi lakuti “ Nchito Yofunika Kwambili.”)

8 Ngakhale akulu odziŵa bwino nchito yao ayenela kukumbukila kuti mtsogolo adzalephela kusamalila maudindo ena mumpingo cifukwa ca ukalamba. (Mika 6:8) Iwo afunikanso kukumbukila kuti “nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezeleka” zingawalepheletse kusamalila maudindo monga mmene anali kucitila poyamba. (Mlal. 9:11, 12; Yak. 4:13, 14) Motelo cifukwa cokonda nkhosa za Yehova, akulu amene amaganizila zamtsogolo amaphunzitsako abale ena acinyamata zinthu zimene aphunzila pa nthawi imene akhala akutumikila Mulungu mokhulupilika.—Ŵelengani Salimo 71:17, 18.

9. Kodi kutsogolo kudzacitika ciani cimene cikuonetsa kuti kuphunzitsa ena n’kofunika kwambili?

9 Akulu amene amaphunzitsa ena amathandizanso mpingo m’njila ina. Iwo amathandiza mpingo kukhala wolimba. Motani? Akulu akamayesetsa kuthandiza ena, pamakhala abale ambili amene angathandize mpingo kukhala wolimba ndi wogwilizana masiku ano ndiponso makamaka panthawi yovuta ya cisautso cacikulu. (Ezek. 38:10-12; Mika 5:5, 6) Cifukwa ca ici tikupempha akulu nonse kuti muyambe lelo kuphunzitsa ena ndi kuona nchitoyi kukhala mbali yofunika ya utumiki wanu.

10. Kodi mkulu angacite ciani kuti akhale ndi nthawi yophunzitsa ena?

10 Timadziŵa kuti akulu mumathela nthawi yoculuka posamalila maudindo ena pampingo, ndipo mumakhala ndi nthawi yocepa yocita zinthu zina. Koma, mungafunike kupatulako nthawi ina mwa nthawi imene mumagwilitsila nchito posamalila maudindo ena kuti muphunzitse abale ena. (Mlal. 3:1) Kucita zimenezo ndi cinthu canzelu.

KONZEKELETSANI MTIMA WA WOPHUNZILA

11. (a) N’cifukwa ciani malangizo amene abale anapeleka okhudza kuphunzitsa ena ndi ocititsa cidwi? (b) Mogwilizana ndi Miyambo 15:22, n’cifukwa ciani tifunika kukambilana malangizo amene abale ena anapeleka?

11 Posacedwapa, akulu ena amene akwanitsa kuthandiza abale kupita patsogolo mwa kuuzimu anafunsidwa kuti afotokoze zimene amacita pophunzitsa ena. * Ngakhale kuti akuluwo ndi ocokela m’maiko osiyanasiyana, malangizo amene anapeleka ndi ofanana kwambili. Kodi zimenezi zikusonyeza ciani? Zikusonyeza kuti mfundo za m’Baibulo zimene akulu amagwilitsila nchito pophunzitsa abale zimagwila nchito kwa wophunzila aliyense “kulikonse mumpingo uliwonse,” monga mmene zinalili m’nthawi ya mtumwi Paulo. (1 Akor. 4:17) Motelo, m’nkhani ino ndiponso yotsatila, tikambilana zimene abalewa anafotokoza. (Miy. 15:22) Kuti timvetsetse mosavuta nkhani zimenezi, tigwilitsila nchito liu lakuti “mphunzitsi” ponena za mkulu amene amaphunzitsa ena, ndi liu lakuti “wophunzila” ponena za m’bale amene akuphunzitsidwa.

12. Kodi mphunzitsi afunika kucita ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

12 Mphunzitsi afunika kukonzekeletsa mtima wa wophunzila asanayambe kumuphunzitsa. Mlimi amagaula nthaka kuti nthakayo ikhale yofewa asanabyale mbeu. Mofananamo, mphunzitsi amafunika kukonzekeletsa mtima wa wophunzila asanayambe kumuphunzitsa zinthu zatsopano. Kodi mphunzitsi angacite bwanji kuti akonzekeletse mtima wa wophunzila? Iye ayenela kutengela citsanzo ca mmodzi wa aneneli akale. N’ciani cimene mneneliyo anacita?

13-15. (a) Kodi mneneli Samueli anapatsidwa nchito yotani? (b) Kodi Samueli anaigwila bwanji nchitoyo? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.) (c) N’cifukwa ciani akulu ayenela kucita cidwi ndi nkhani ya m’Baibulo imeneyi?

13 Tsiku lina, zaka zoposa 3,000 zapitazo, Yehova anauza mneneli Samueli amene anali wokalamba panthawiyo kuti: “Maŵa nthawi ngati ino ndikutumizila munthu kucokela ku dela la Benjamini, ndipo udzam’dzoze kukhala mtsogoleli wa anthu anga Isiraeli.” (1 Sam. 9:15, 16) Samueli anadziŵa kuti udindo wake wokhala mtsogoleli watha ndi kuti Yehova anamupatsa nchito yodzoza munthu wina wom’lowa mmalo. Mwina Samueli anali kudzifunsa kuti, ‘Kodi munthu ameneyo ndingamuthandize bwanji kukonzekela udindo wake?’ Kenako iye anapeza njila yocitila zimenezo.

14 Tsiku lotsatila Samueli ataona Sauli, Yehova anauza mneneliyo kuti: “Ameneyu ndiye munthu ndimakuuza uja.” Kenako Samueli anacita zimene anali kuganiza zija. Iye anapempha Sauli kuti akadye naye cakudya m’cipinda codyela. Kumeneko, iye anapatsa Sauli ndi mtumiki wake malo apamwamba kwambili ndi nyama yabwino. Ndiyeno Samueli anati: “Tenga, udye cifukwa anasungila iweyo kuti udzaidye panthawi ino.” Pambuyo pake, Samueli ndi Sauli ananyamuka kupita ku nyumba ya mneneliyo ndipo m’njila anali kuceza. Samueli anafuna kugwilitsila nchito nthawi ya cakudya ndi maceza kuti athandize Sauli kukhala womasuka. Conco, iye anapempha Sauli kuti apite naye padenga la nyumba yake. Madzulo pamene kunali kuomba kamphepo kayeziyezi, Samueli “anapitiliza kulankhula ndi Sauli ali padenga la nyumba” mpaka usiku pamene anapita kukagona. Tsiku lotsatila, Samueli anadzoza Sauli, anamupsompsona, ndi kumupatsa malangizo oonjezeleka. Kenako anauza Sauli kuti apite atamuthandiza kukonzekela udindo wake wamtsogolo.—1 Sam. 9:17-27; 10:1.

15 Kudzoza munthu kukhala mtsogoleli wa anthu ndi kosiyana kwambili ndi kuphunzitsa m’bale kuti ayenelele kukhala mkulu kapena mtumiki wothandiza mumpingo. Ngakhale n’conco, akulu angaphunzile zambili mwakuona mmene Samueli anacitila zinthu ndi Sauli. Tiyeni tione zinthu ziŵili zimene angaphunzilepo.

KHALANI MPHUNZITSI WODZIPELEKA NDIPONSO BWENZI LENILENI

16. (a) Kodi Samueli anamva bwanji pamene Aisiraeli anamuuza kuti afuna mfumu? (b) Kodi Samueli anaigwila bwanji nchito yodzoza Sauli?

16 Citani zinthu modzipeleka osati mokakamizika. Samueli atamva kuti Aisiraeli akufuna mfumu, anakhumudwa ndipo anaona kuti anthu ake amukana. (1 Sam. 8:4-8) Iye sanafune kucita zimene anthuwo anamuuza cakuti Yehova anacita kumuuza katatu kuti awamvele. (1 Sam. 8:7, 9, 22) Komabe, Samueli sanacite nsanje ndi munthu amene anali kudzamulowa mmalo. Yehova atamuuza kuti adzoze Sauli, mneneliyo anamvela ndi mtima wonse cifukwa ca cikondi osati mokakamizika.

17. Kodi akulu amatsatila bwanji citsanzo ca Samueli? Nanga io amamva bwanji akatelo?

17 Mofanana ndi Samueli, akulu aluso masiku ano amacita zinthu mokoma mtima pophunzitsa ena. (1 Pet. 5:2) Akulu otelo saopa kuphunzitsa ena cifukwa coganiza kuti adzawalanda maudindo mumpingo. Aphunzitsi okoma mtima amaona ophunzila monga “anchito anzao” ndiponso mphatso zamtengo wapatali mumpingo osati monga anthu opikisana nao. (2 Akor. 1:24; Aheb. 13:16) Aphunzitsi odzipeleka amenewo amakhala osangalala kwambili akaona kuti ophunzila akugwilitsila nchito luso lao potumikila mpingo.—Mac. 20:35.

18, 19. Kodi mkulu angakonzekeletse bwanji mtima wa wophunzila? Nanga n’cifukwa ciani kucita zimenezo n’kofunika kwambili?

18 Khalani bwenzi, osati cabe mphunzitsi. Pa tsiku limene Samueli anakumana ndi Sauli, mneneliyu akanangodzoza Sauli popanda kumukonzekeletsa. Iye akanangotenga botolo la mafuta ndi kuthila pa mutu pa Sauli mwamsanga ndi kuuza mfumu yatsopanoyo kuti izipita. Koma Samueli anayesetsa kukonzekeletsa mtima wa Sauli pang’onopang’ono. Pambuyo pakuti Samueli ndi Sauli adyela pamodzi cakudya cokoma, kuyendela pamodzi, kuceza, ndi kupuma, Samueli anaona kuti tsopano inali nthawi yabwino yakuti adzoze Sauli.

Mukafuna kuphunzitsa munthu, ndi bwino kukhala bwenzi lake coyamba (Onani ndime 18 ndi 19)

19 Mofananamo, mphunzitsi masiku ano afunika kupatula nthawi yoceza ndi wophunzila kuti io akhale mabwenzi ndiponso kuti wophunzilayo akhale womasuka. Zimene mkulu angacite kuti akhale bwenzi la wophunzila zimasiyanasiyana malinga ndi cikhalidwe ca kumaloko. Komabe, mosasamala kanthu za kumene mumakhala, ngati mumapatula nthawi yoceza ndi wophunzila ngakhale kuti mumakhala ndi zocita zambili, iye adzadziŵa kuti mumamuona kukhala wofunika. (Ŵelengani Aroma 12:10.) Mukatelo wophunzila aliyense amene akufunitsitsa kuphunzila adzaona kuti mumam’konda ndipo adzakuyamikilani mocokela pansi pa mtima.

20, 21. (a) Kodi mphunzitsi wabwino amacita ciani? (b) Kodi m’nkhani yotsatila tidzakambilana ciani?

20 Akulu, kumbukilani kuti mphunzitsi wabwino sayenela kukonda cabe nchito yophunzitsa koma ayenelanso kukonda wophunzila. (Yelekezelani ndi Yohane 5:20.) Ngati mphunzitsi amakonda wophunzila, sicikhala covuta wophunzilayo kuzindikila zimenezo, ndipo zimakhudza kwambili mmene iye angagwilitsile nchito malangizo amene wapatsidwa. Conco, inu akulu okondedwa, pophunzitsa ena muziyesetsa kukhala bwenzi la wophunzila osati cabe mphunzitsi.—Miy. 17:17; Yoh. 15:15.

21 Pambuyo pakuti mkulu wakonzekeletsa mtima wa wophunzila, ayenela kumupatsa malangizo oyenelela. Kodi mkulu angacite bwanji zimenezi? Tidzakambilana zimenezi m’nkhani yotsatila.

^ par. 3 Nkhani ino ndiponso yotsatila zalembedwela makamaka akulu. Koma nkhanizi zikhudza onse mumpingo. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa zidzathandiza abale onse obatizidwa kudziŵa kuti afunika kuphunzitsidwa kuti azisamalila maudindo mumpingo. Ndipo abale ambili akakhala paudindo, aliyense mumpingo amapindula.

^ par. 11 Akuluwa amakhala ku Australia, Bangladesh, Belgium, Brazil, France, French Guiana, Japan, Korea, Mexico, Namibia, Nigeria, Réunion, Russia, South Africa, ndi ku United States.