Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Muli pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova?

Kodi Muli pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova?

“Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.”—YAK. 4:8.

1. N’cifukwa ciani tiyenela kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova nthawi zonse?

KODI ndinu Mboni ya Yehova yodzipeleka ndi yobatizidwa? Ngati ndi conco, ndiye kuti muli ndi cinthu camtengo wapatali cimene ndi ubwenzi wanu ndi Mulungu. Koma ubwenziwu ungasokonezeke cifukwa cakuti tikukhala m’dziko la Satana loipali ndiponso cifukwa ca thupi lathu lopanda ungwilo. Vutoli limakhudza Akristu onse. Conco nthawi zonse tiyenela kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova.

2. (a) Kodi ubwenzi n’ciani? (Onani mau amunsi.) (b) Kodi tingalimbitse bwanji ubwenzi wathu ndi Yehova?

2 Kodi ubwenzi wanu ndi Yehova ndi wolimba? Kapena mufunika kuulimbitsa? Lemba la Yakobo 4:8 limafotokoza mmene mungacitile zimenezo. Lembali limati: “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.” Lembali likusonyeza kuti ubwenzi wathu ndi Mulungu umadalila pa mbali ziŵili. * Ifeyo tikamayesetsa kuyandikila Mulungu, nayenso amatiyandikila. Zimenezi zikapitiliza kucitika, mkupita kwa nthawi, ubwenzi wathu ndi Yehova umalimba. Zikatelo, timadzimva kuti tili pa ubwenzi weniweni ndi Mulungu, ndipo timakhala ndi cikhulupililo ngati cimene Yesu anali naco pamene anati: “Alipo ndithu amene anandituma . . . Ine ndikumudziŵa.” (Yoh. 7:28, 29) Nanga ndi zinthu ziti zimene mungacite kuti mulimbitse ubwenzi wanu ndi Yehova?

Kodi tingakambilane bwanji ndi Mulungu? (Onani ndime 3)

3. Kodi timakambilana bwanji ndi Yehova?

3 Kukamba ndi Yehova nthawi zonse n’kofunika kwambili kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba. Kodi tingakambe naye bwanji Mulungu? Tisanayankhe funsoli, tifunse kuti, mumacita ciani mukafuna kukambilana ndi bwenzi lanu limene limakhala kutali? Mwacionekele, mumalembelana makalata ndi kutumilana foni kaŵilikaŵili. Ifenso timakamba ndi Yehova mwa kupemphela kwa iye kaŵilikaŵili. (Ŵelengani Salimo 142:2.) Komanso timalola Yehova kukamba nafe mwa kuŵelenga Mau ake ndi kuwasinkhasinkha nthawi zonse. (Ŵelengani Yesaya 30:20, 21.) Tsopano tiyeni tikambilane mmene kucita zinthu ziŵilizi kumalimbitsila ubwenzi wathu ndi Yehova.

KUPHUNZILA BAIBULO NDI NJILA IMENE YEHOVA AMAKAMBILA NAFE

4, 5. Kodi Yehova amakamba nanu bwanji panokha kupyolela m’Mau ake? Pelekani citsanzo.

4 Mosakaikila inuyo mudziŵa kuti m’Baibulo muli uthenga umene Mulungu analembela anthu onse. Koma kodi Baibulo lingakuthandizeni inuyo kuyandikila Yehova? Inde. Kodi lingakuthandizeni bwanji? Mukamaŵelenga ndi kuphunzila Mau a Mulungu nthawi zonse, muziganizila mmene mawuwo akukukhudzilani ndiponso mmene mungawagwilitsile nchito pa umoyo wanu. Mukatelo, ndiye kuti mukulola Yehova kukamba nanu kupyolela m’Mau ake. Kucita zimenezi kumalimbitsa ubwenzi wanu ndi iye.—Aheb. 4:12; Yak. 1:23-25.

5 Mwacitsanzo, ŵelengani ndi kusinkhasinkha mau a Yesu akuti “lekani kudziunjikila cuma padziko lapansi.” Ngati pambuyo poŵelenga mau amenewa mwaona kuti mumaika zinthu za Ufumu patsogolo, mumadziŵa kuti Yehova akukondwela nanu. Koma ngati mwaona kuti mufunika kusintha zinthu zina pa umoyo wanu kuti muziika zinthu za Ufumu patsogolo, ndiye kuti Yehova wakuuzani zimene mufunika kuongolela kuti mulimbitse ubwenzi wanu ndi iye.—Mat. 6:19, 20.

6, 7. (a) Kodi kuphunzila Baibulo kumalimbitsa bwanji ubwenzi wathu ndi Yehova? (b) Kodi tiyenela kukhala ndi colinga cotani pamene tikucita phunzilo laumwini?

6 Kuphunzila Malemba sikutithandiza cabe kudziŵa mbali imene tiyenela kuongolela. Kumatithandizanso kudziŵa bwino njila za Yehova, ndipo tikadziŵa njila zake timayamba kumukonda kwambili. Tikamamukonda kwambili Mulungu, iyenso amayamba kutikonda kwambili, ndipo ubwenzi wathu ndi iye umalimba.—Ŵelengani 1 Akorinto 8:3.

7 Komabe, kuti tiyandikile Yehova, tifunika kuphunzila ndi colinga coyenela. Lemba la Yohane 17:3 limati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziŵa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Kristu, amene inu munamutuma.” Conco, tiyenela kuphunzila n’colinga cakuti ‘tidziŵe’ bwino Yehova osati kuti tidziŵe cabe zinthu zatsopano.—Ŵelengani Ekisodo 33:13; Sal. 25:4.

8. (a) Kodi anthu angaganize ciani pa zimene Yehova anacitila Mfumu Azariya, zimene zinalembedwa pa 2 Mafumu 15:1-5? (b) Kodi kudziŵa Yehova kumatithandiza bwanji kuti tisamakaikile zocita zake?

8 Tikamudziŵa kwambili Yehova, sitidzakhumudwa ndi nkhani za m’Baibulo zimene sizifotokoza cifukwa cake iye anacita zinthu m’njila inayake. Mwacitsanzo, kodi mumamva bwanji mukaganizila mmene Yehova anacitila zinthu ndi Mfumu Azariya ya Yuda? (2 Maf. 15:1-5) Onani kuti ngakhale kuti ‘anthu anali kufukizabe ndi kupeleka nsembe yautsi m’malo okwezeka,’ Azariya “anapitiliza kucita zolungama pamaso pa Yehova.” Komabe, “Yehova anaicititsa khate mfumuyo moti inakhalabe yakhate mpaka tsiku limene inamwalila.” N’cifukwa ciani Mulungu anacita zimenezo? Lembali silifotokoza cifukwa cake. Kodi izi ziyenela kutivutitsa maganizo kapena kutipangitsa kuganiza kuti Yehova analanga Azariya popanda cifukwa? Sitingaganize conco ngati timadziŵa bwino njila za Yehova. Munthu amene amadziŵa njila za Yehova, amadziŵanso kuti iye nthawi zonse amalanga munthu “pa mlingo woyenela.” (Yer. 30:11) Kudziŵa mfundo imeneyi kumatithandiza kukhulupilila kuti Yehova anacita zinthu mwacilungamo ndi Azariya ngakhale kuti sitikudziŵa cifukwa cake anacita zimenezo.

9. Ndi mfundo ziti zimene zimatithandiza kudziŵa cifukwa cake Yehova anakantha Azariya ndi khate?

9 Koma pa nkhani ya Azariya, Malemba ena amafotokoza mfundo zoonjezeleka. M’Baibulo, Mfumu Azariya imachedwanso Mfumu Uziya. (2 Maf. 15:7, 32) Nkhani ya Azariya imapezekanso pa 2 Mbiri 26:3-5, 16-21. Lembali limanena kuti Uziya anacita zinthu zoyenela pamaso pa Yehova kwa kanthawi, koma pambuyo pake “mtima wake unadzikuza mpaka kufika pom’pweteketsa.” Cifukwa codzikuza, Uziya anapita kukacisi kukagwila nchito ya ansembe imene siinali nchito yake. Ansembe 81 anafika ndi kumuletsa. Kodi Uziya anacita ciani? Iye ‘anawakwiila kwambili’ ansembewo, ndipo zimenezi zinaonetsa kuti anali wodzikuza kwambili. Ndiye cifukwa cake Yehova anamukantha ndi khate.

10. N’cifukwa ciani si nthawi zonse pamene tingatifunike kudziŵa cifukwa cake Yehova amacita zinthu mwa njila inayake? Nanga tiyenela kucita ciani kuti tizikhulupilila kuti njila za Yehova n’zolungama?

10 Koma tisaiŵale mfundo imene tikukambilana. Nanga bwanji m’Baibulo mukanakhala kuti mulibe mfundo zina zofotokoza cifukwa cake Mulungu anakantha Azariya ndi khate, monga mmene nkhani zina za m’Baibulo zilili? Kodi   mukanayamba kuganiza kuti mwina Mulungu ndi wopanda cilungamo? Kapena   mukanaganiza kuti m’Baibulo muli mfundo zokwanila zoonetsa kuti nthawi zonse Yehova amacita zinthu zoyenela, ndipo iye ndiye muyezo wa cabwino ndi coipa? (Deut. 32:4) Tikamudziŵa kwambili  Yehova, timayamba kumukonda kwambili ndi kukondanso njila zake, cakuti sitingafune kuti nthawi zonse tizidziŵa cifukwa cake amacita zinthu mwa njila inayake. Zimenezi zingatheke tikamaphunzila mwakhama Mau a Mulungu ndi kuwasinkhasinkha. (Sal. 77:12, 13) Mukamacita zimenezi, ubwenzi wanu ndi Yehova umalimba kwambili.

TIMAKAMBA NDI YEHOVA KUPYOLELA M’PEMPHELO

11-13. Mumadziŵa bwanji kuti Yehova amayankha mapemphelo? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

11 Tikamapemphela timayandikila Yehova. Timamutamanda, kumuyamikila, ndi kumupempha kuti atitsogolele. (Sal. 32:8) Koma kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ukhale wolimba, tiyenela kukhulupilila kuti iye amamva mapemphelo.

12 Anthu ena amaganiza kuti pemphelo limangokhazika mtima pansi. Iwo amanena kuti cimene cimapangitsa munthu kuganiza kuti pemphelo lake layankhidwa n’cakuti popemphela amakamba maganizo ake momasuka, amazindikila vuto lake, ndiponso amaganizila mmene angalithetsele. Nanga n’ciani cimakupangitsani kukhulupilila kuti Yehova amamva mapemphelo anu ocokela pansi pa mtima?

13 Ganizilani izi: Pamene anali kumwamba, Yesu anaona Yehova akuyankha mapemphelo a atumiki Ake pano padziko lapansi. Ndipo mu utumiki wake wa padziko lapansi, Yesu anali kufotokoza maganizo ake kwa Atate ake akumwamba kupyolela m’pemphelo. Nthawi ina Yesu anapemphela usiku wonse. Kodi iye akanacita zimenezo akanadziŵa kuti Yehova samvela mapemphelo? (Luka 6:12; 22:40-46) Kodi  akanaphunzitsa atumwi ake kupemphela akanadziŵa kuti pemphelo limangokhazika mtima pansi? N’zoonekelatu kuti Yesu anali kudziŵa kuti munthu akamapemphela amakambadi ndi Yehova. Nthawi ina, Yesu anati: “Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimva. Inde, ndikudziŵa kuti mumandimva nthawi zonse.” Ifenso tiyenela kukhala ndi cikhulupililo cakuti Yehova ndi “Wakumva pemphelo.”—Yoh. 11:41, 42; Sal. 65:2.

14, 15. (a) Timapindula bwanji tikamafotokoza zinthu mwacindunji m’pemphelo? (b) Kodi mapemphelo amene mlongo wina anapeleka analimbitsa bwanji ubwenzi wake ndi Yehova?

14 Mukamafotokoza zinthu mwacindunji m’pemphelo, zimakhala zosavuta kudziŵa kuti Yehova wayankha pemphelo lanu. Ndipo Yehova akamayankha mapemphelo anu, ubwenzi wanu ndi iye umalimba kwambili. Komanso mukamafotokozela Yehova nkhawa zanu kucokela pansi pa mtima, iye amakuyandikilani kwambili.

15 Ganizilani citsanzo ca Kathy. * Iye sanali kukonda ulaliki ngakhale kuti anali kulalikila kaŵilikaŵili. Iye anati: “Sindinali kuikonda nchito yolalikila. Kunena zoona, sindinali kuikonda nchitoyi. Nditapuma pa nchito, mkulu wina anandiuza kuti ndingakwanitse kucita upainiya wa nthawi zonse, ndipo anandipatsa fomu yofunsila  upainiya. Ndinaganiza zoyamba upainiya, ndipo ndinayamba kupemphela kwa Yehova tsiku lililonse kuti andithandize kukonda ulaliki.” Kodi Yehova anayankha mapemphelo ake? Iye anati: “Tsopano ndacita upainiya kwa zaka zitatu. Cifukwa cakuti ndimatenga nthawi yaitali mu ulaliki ndiponso  kuphunzila zinthu zina kwa alongo ena,  ndaonjezela luso langa pa nchito yolalikila. Masiku ano, nchito yolalikila ndimaikonda kwambili. Kuonjezela apo, ubwenzi wanga ndi Yehova walimba kwambili kuposa kale.”  Conco tingathe kuona kuti mapemphelo amene Kathy anali kupeleka anamuthandiza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.

TIZICITA MBALI YATHU

16 Sitiyenela kuleka kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Timafunika kuyamba ndife kuyandikila Mulungu ngati tifuna kuti iyenso atiyandikile. Motelo, tiyenela   kupitilizabe kukambilana ndi Mulungu mwa kuphunzila Baibulo ndi kupemphela nthawi zonse. Tikamatelo, tidzakhala pa ubwenzi wolimba kwambili ndi Yehova ndipo ubwenzi umenewo udzatithandiza kupilila ziyeso.

Sitiyenela kuleka kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova (Onani ndime 16 ndi 17)

16, 17. (a) Tiyenela kucita ciani kuti tikhalebe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova? (b) Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

17 Koma cimakhala covuta kupilila ngati mavuto akupitilizabe ngakhale kuti  timapemphela mocokela pansi pa mtima. Zinthu zikatelo, cikhulupililo cathu mwa Yehova cingafooke. Ndipo tingayambe kukaikila ngati Yehova amamva mapemphelo athu kapena ngati amationa monga mabwenzi ake. Pamene tikukumana ndi mavuto amenewa, kodi tingapilile bwanji ndi kukhalabe pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu? Nkhani yotsatila idzafotokoza mmene tingacitile zimenezi.

^ par. 2 Ubwenzi umatanthauza mmene anthu aŵili amamvelela akamaganizilana ndiponso mmene amacitila zinthu kwa wina ndi mnzake. Conco, onse aŵili amafunika kucitapo kanthu kuti ubwenzi ukhalepo.

^ par. 15 Dzina lasinthidwa.