Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Cifukwa Cake Kucotsa Munthu Mumpingo Ndi Makonzedwe Acikondi

Cifukwa Cake Kucotsa Munthu Mumpingo Ndi Makonzedwe Acikondi

M’BALE wina dzina lake Julian anati: “Pamene ndinamva cilengezo cakuti mwana wanga wamwamuna wacotsedwa mumpingo, ndinaona monga dziko landicepela ndipo zonse zathela pamenepo. Iye ndi mwana wanga woyamba, tinali kukondana kwambili, ndiponso ndinali kucitila naye pamodzi zinthu zambili. Iye anali mwana wacitsanzo cabwino, koma mwadzidzidzi anayamba kucita zinthu zoipa. Nthawi zambili mkazi wanga anali kulila, ndipo ndinali kulephela kumutonthoza. Kaŵilikaŵili tinali kuganiza kuti mwina sitinamulele bwino mwanayo.”

Popeza kuti Mkristu akacotsedwa mumpingo cimapweteka kwambili, n’cifukwa ciani tinganene kuti amenewa ndi makonzedwe acikondi? Ndi zifukwa ziti za m’Malemba zocotsela munthu mumpingo? Nanga n’ciani cimapangitsa kuti munthu acotsedwe?

ZIMENE ZIMACITITSA KUTI MUNTHU ACOTSEDWE

Mkristu wa Mboni za Yehova wobatizidwa amacotsedwa mumpingo ngati anacita chimo lalikulu ndipo sanalape.

Ngakhale kuti Yehova sayembekezela kuti tizicita zinthu mwangwilo, iye amafuna kuti atumiki ake azitsatila miyezo yake yolungama. Mwacitsanzo, Yehova amafuna kuti tizipewa macimo akuluakulu monga ciwelewele, kulambila mafano, kuba, kulanda, kupha, ndi kukhulupilila mizimu.—1 Akor. 6:9, 10; Chiv. 21:8.

Kodi simukuvomeleza kuti miyezo yolungama ya Yehova ndi yabwino ndipo imatiteteza? Ndani amene safuna kukhala ndi anthu amtendele, a khalidwe loyela, ndi odalilika? Timapeza anthu a makhalidwe otelo pakati pa abale ndi alongo athu akuuzimu cifukwa cakuti pa nthawi imene tinali kudzipeleka kwa Mulungu tinalonjeza kuti tidzatsatila malamulo ake.

Nanga n’ciani cimacitika Mkristu wobatizidwa akacita chimo lalikulu cifukwa ca kufooka? Atumiki a Yehova okhulupilika akale anacitapo macimo aakulu, koma Mulungu sanawasiye. Mfumu Davide ndi munthu mmodzi wodziŵika bwino amene anacita chimo lalikulu. Davide anacita cigololo ndiponso anapha munthu, koma mneneli Natani anamuuza kuti: “Yehova wakukhululukila chimo lako.”—2 Sam. 12:13.

Mulungu anakhululukila Davide cifukwa cakuti analapa moona mtima. (Sal. 32:1-5) Mofananamo, masiku ano mtumiki wa Yehova amacotsedwa mumpingo pokhapo ngati ndi wosalapa kapena akupitilizabe kucita chimo. (Mac. 3:19; 26:20) Akulu a m’komiti yaciweluzo ayenela kucotsa mumpingo munthu amene sanaonetse kulapa kwenikweni pa nthawi yoweluza mlandu wake.

Nthawi zina tingaone kuti kucotsa munthu mumpingo ndi nkhanza, makamaka ngati munthuyo ndi m’bale wathu. Komabe, m’Mau a Yehova muli zifukwa zomveka zotithandiza kukhulupilila kuti kucotsa munthu mumpingo ndi makonzedwe acikondi.

KODI KUCOTSA MUNTHU MUMPINGO KULI NDI MAPINDU OTANI?

Yesu anakamba kuti “nzelu imatsimikizilika kuti ndi yolungama cifukwa ca nchito zake.” (Mat. 11:19) Kucotsa munthu wosalapa mumpingo ndi cinthu canzelu, ndipo kumakhala ndi mapindu ake. Ganizilani mapindu atatu awa:

Kucotsa wolakwa mumpingo kumacititsa kuti dzina la Yehova lilemekezedwe. Popeza kuti timadziŵika ndi dzina la Yehova, zocita zathu zimakhudza mmene ena amaonela dzina lake. (Yes. 43:10) Khalidwe la mwana lingapangitse kuti anthu azilemekeza makolo ake kapena kuwanyoza. Mofananamo, khalidwe la anthu odziŵika ndi dzina la Mulungu limakhudza mmene anthu ena amaonela Yehova. Dzina labwino la Yehova limalemekezedwa ngati anthu odziŵika ndi dzina lake amatsatila miyezo yake ya makhalidwe abwino. Zinthu masiku ano n’zofanana ndi mmene zinalili m’nthawi ya Ezekieli. Panthawiyo, zocita za Ayuda zinakhudza mmene anthu a mitundu ina anali kuonela dzina la Yehova.—Ezek. 36:19-23.

Ngati tacita ciwelewele, tinganyozetse dzina loyela la Mulungu. Mtumwi Petulo analangiza Akristu kuti: “Monga ana omvela, lekani kukhala motsatila zilakolako zimene munali nazo kale pamene munali osadziŵa. Koma khalani motsanzila Woyela amene anakuitanani. Inunso khalani oyela m’makhalidwe anu onse, cifukwa Malemba amati: ‘Mukhale oyela, cifukwa ine ndine woyela.’” (1 Pet. 1:14-16) Khalidwe loyela limapangitsa kuti dzina la Mulungu lilemekezedwe.

Ngati mmodzi wa Mboni za Yehova amacita chimo, nthawi zambili mabwenzi ake amadziŵa. Conco, kucotsa munthu mumpingo kumathandiza anthu ena kudziŵa kuti anthu a Yehova ndi oyela ndipo amayesetsa kutsatila malangizo a m’Malemba kuti akhalebe oyela. Tsiku lina, munthu wina anabwela ku Nyumba ya Ufumu ina m’dziko la Switzerland ndi kunena kuti afuna kukhala wa Mboni. Iye anacita izi cifukwa cakuti mlongosi wake anali atacotsedwa mumpingo cifukwa ca khalidwe la ciwelewele. Munthuyo anakamba kuti amafuna kukhala m’gulu limene “sililekelela khalidwe loipa.”

Kucotsa munthu kumateteza mpingo woyela wacikristu. Mtumwi Paulo anacenjeza Akristu a ku Korinto za kuipa kolekelela anthu ocita macimo mwadala mumpingo. Anakamba kuti anthu otelo ali ngati cofufumitsa cimene cimafufumitsa mtanda wonse. Iye anati: “Cofufumitsa cacing’ono cimafufumitsa mtanda wonse.” Kenako analangiza Akristuwo kuti: “M’cotseni pakati panu munthu woipayo.”—1 Akor. 5:6, 11-13.

Mwacionekele, ‘munthu woipa’ amene Paulo anachula anali kucita ciwelewele, ndipo analibe mantha kapena manyazi. Ndipo Akristu ena mumpingowo anayamba kuona kuti zimene munthuyo anali kucita zinalibe vuto. (1 Akor. 5:1, 2) Akristu a ku Korinto akanalekelela chimo lalikulu limenelo, ena mumpingowo akanayamba kutsatila miyambo yonyansa yaciwelewele ya anthu a mumzindawo. Kulekelela anthu ocita macimo mwadala mumpingo kumasonkhezela ena kunyalanyaza miyezo ya Mulungu. (Mlal. 8:11) Kuonjezela apo, anthu amene amacita macimo koma safuna kulapa amakhala ngati “miyala ikuluikulu yobisika m’madzi” ndipo angaononge cikhulupililo ca ena mumpingo.—Yuda 4, 12.

Kucotsa munthu wocimwa mumpingo kungamuthandize kuzindikila chimo lake. Nthawi ina, Yesu anakamba za mnyamata wina amene anacoka pakhomo pa atate wake ndi kuononga colowa cake conse mwa kulowelela m’makhalidwe oipa. (Luka 15:11-24) Atakumana ndi mavuto, Mwana wolowelelayo anazindikila kuti analakwitsa kucoka pakhomo pa makolo ake. Atazindikila kulakwa kwake, analapa, ndi kubwelela kwa makolo ake. (Luka 15:11-24) Zimene Yesu anakamba zokhudza tate wacikondi wa mwanayo, amene anakondwela ataona kuti mwana wake walapa, zimatiphunzitsa mmene Yehova amaonela munthu wolapa. Mulungu amatiuza kuti: “Ine sindisangalala ndi imfa ya munthu woipa, koma ndimafuna kuti munthu woipa abwelele kusiya njila zake n’kukhala ndi moyo.”—Ezek. 33:11.

Nayenso munthu amene wacotsedwa mumpingo wacikristu, umene ndi banja lake lakuuzimu, angazindikile kuti anataya mwai. Mavuto amene angakumane nao cifukwa ca khalidwe lake loipa, ndiponso kukumbukila mmene anali kusangalalila pamene anali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndi anthu ake, zingamuthandize kuzindikila kulakwa kwake.

Pamafunika cikondi ndi kulimba mtima kuti tithandize munthu wocimwa. Wamasalimo Davide anati: “Wolungama akandimenya ndiye kuti wandisonyeza kukoma mtima kosatha, ndipo akandidzudzula ndiye kuti wandidzoza mafuta pamutu panga.” (Sal. 141:5) Tiyelekezele motele: Tinene kuti munthu wina akudya nsima ndipo nyama yamukhala pakhosi. Iye akulephela kupuma bwinobwino, ndipo akusowa cocita. Komanso akulephela kukamba, ndipo aoneka kuti angafe ngati munthu wina sangamuthandize mwamsanga. Kenako mnzake akumumenya kumsana kuti nyamayo icoke. N’zoona kuti iye angamve kuŵaŵa cifukwa comenyedwa, koma kucita zimenezi kungapulumutse moyo wake. Mofanana ndi zimenezi, Davide anadziŵa kuti munthu wolungama nthawi zina amafunika kupatsidwa uphungu wamphamvu kuti asinthe khalidwe lake.

Nthawi zambili munthu wocimwa amafunika kucotsedwa mumpingo kuti asinthe khalidwe lake. Patapita zaka 10, mwana wa M’bale Julian, amene tachula kuciyambi kwa nkhani ino, anasintha khalidwe lake, ndi kubwezeletsedwa mumpingo ndipo tsopano akutumikila monga mkulu. Iye anati: “Pamene ndinacotsedwa ndinazindikila kuipa kwa khalidwe langa. Ndinali kufunika cilango cotelo.”—Aheb. 12:7-11.

NJILA YACIKONDI YOTHANDIZILA ANTHU OCOTSEDWA

N’zoona kuti cimapweteka ngati munthu wacotsedwa mumpingo, koma zotele zikacitika sitiyenela kutaya mtima. Tonsefe tingathandize kuti munthu wocotsedwa apindule ndi cilango cimene wapatsidwa.

Akulu amayesetsa kuthandiza anthu olapa kuti abwelele kwa Yehova

Akulu amene ali ndi udindo wofotokozela munthu cigamulo cakuti wacotsedwa ayenela kucita zinthu mwacikondi monga mmene Yehova amacitila. Pofotokozela munthu cigamulo cao, io ayenela kukamba mokoma mtima ndi kumufotokozela momveka bwino zimene afunika kucita kuti adzabwezeletsedwe mumpingo. Pofuna kukumbutsa ocotsedwa zimene angacite kuti abwelele kwa Yehova, nthawi ndi nthawi akulu amayendela anthu ocotsedwa amene aonetsa mtima wolapa. *

Acibale angasonyeze kuti amakonda mpingo ndi munthu wolakwayo mwa kulemekeza cigamulo ca kucotsa munthuyo. M’bale Julian anati: “Iye anali mwana wanga ndithu, koma khalidwe lake linapangitsa kuti tisamacite naye zinthu pamodzi.”

Tonse mumpingo tingasonyeze kuti tili ndi cikondi ceniceni mwa kupewa kulankhulana ndi munthu wocotsedwa. (1 Akor. 5:11; 2 Yoh. 10, 11) Kucita zimenezi, kumathandiza kuti cilango cimene Yehova wapatsa munthuyo kudzela mwa akulu cigwile nchito bwino. Komanso tonse tiyenela kucilikiza ndi kukonda kwambili abale a munthu wocotsedwayo kuti asamaone ngati akusalidwa ndi abale anzao.—Aroma 12:13, 15.

Pomaliza M’bale Julian anati: “Kucotsa munthu mumpingo ndi makonzedwe abwino amene amatithandiza kutsatila miyezo ya Yehova pa umoyo wathu. Ngakhale kuti cilangoci cimaŵaŵa, pambuyo pake cimakhala ndi zotsatila zabwino. Ndikanalekelela khalidwe loipa la mwana wanga, iye sakanabwelelanso.”

^ par. 24 Onani Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991, tsamba 21 mpaka 23.