Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mtengo Ukadulidwa Ungaphukenso?

Kodi Mtengo Ukadulidwa Ungaphukenso?

MTENGO wakale wa maolivi sukhala wokongola kwenikweni tikauyelekezela ndi mtengo waukulu wa mkungudza wa ku Lebanon. Koma mitengo ya maolivi imapilila kwambili ngakhale pamene kuli cilala. Pali mitengo ina ya maolivi imene anthu amanena kuti yakwanitsa zaka pafupifupi 1,000. Mtengo wa maolivi akaudula umaphukanso cifukwa cakuti mizu yake imapita pansi kwambili ndiponso imayala malo aakulu. Ngati mizu yake ikali bwino, mtengowu sulephela kuphuka.

Yobu anali kukhulupilila kuti ngakhale atafa, adzakhalanso ndi moyo. (Yobu 14:13-15) Iye anagwilitsila nchito citsanzo ca mtengo pofuna kuonetsa kuti anali ndi cikhulupililo cakuti Mulungu adzamuukitsa. Pankhaniyi, mwina iye anagwilitsila nchito citsanzo ca mtengo wa maolivi. Yobu anati: “Ngakhale mtengo umakhala ndi ciyembekezo. Ukadulidwa umaphukanso.” Mvula ikagwa pambuyo pa cilala coopsa, mizu ya citsa couma ca mtengo wa maolivi imaphuka n’kumela “nthambi ngati mtengo watsopano.”—Yobu 14:7-9.

Mlimi wa mitengo ya maolivi amafunitsitsa kuti mizu ya mtengo umene anadula iphukenso. Nayenso Yehova Mulungu amalakalaka kuukitsa atumiki ake ndi anthu ena ambili amene anafa. (Mat. 22:31, 32; Yoh. 5:28, 29; Mac. 24:15) Ndithudi, tidzasangalala kwambili kulandila akufa amene adzaukitsidwa ndi kuwaona akusangalalanso ndi moyo.