Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Muzikhulupilila Yehova Nthawi Zonse

Muzikhulupilila Yehova Nthawi Zonse

“Mukhulupilileni nthawi zonse, anthu inu.”—SAL. 62:8.

1-3. Kodi cikhulupililo ca Paulo mwa Yehova cinalimba bwanji? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

M’CAKA ca 64 C.E., Akristu anali kuvutika kwambili ku Roma. Panthawiyo, otsatila a Kristu anali kucitilidwa nkhanza kwambili cifukwa cakuti anali kuwanamizila kuti anayambitsa msokonezo mumzindawo ndiponso kuti anali kudana ndi anthu ena. Inu mukanakhala Mkristu panthawiyo, tsiku lililonse mukanakhala ndi mantha akuti mwina mungamangidwe ndi kumenyedwa. Ena mwa abale ndi alongo anu akuuzimu akanakhadzulidwa ndi nyama zolusa kapena kukhomeledwa pamtengo ndi kutenthedwa ndi moto kuti akhale ngati zounikila usiku.

2 Zioneka kuti panthawi yovutayi ndi pamene Paulo anaikidwa m’ndende kaciŵili ku Roma. Kodi Akristu ena anapita kukamuthandiza? Paulo anada nkhawa kuti kulibe anamuthandiza, ndiye cifukwa cake analembela Timoteyo kuti: “Pamene ndinali kudziteteza koyamba pa mlandu wanga, palibe amene anakhala kumbali yanga. Onse anandisiya ndekha. Ngakhale zinali conco, usakhale mlandu kwa io.” Komabe, Paulo anadziŵa kuti sanali yekha. Iye analemba kuti: “Koma Ambuye anaima pafupi ndi ine ndi kundipatsa mphamvu.” Zoonadi, Ambuye Yesu anapatsa Paulo thandizo lofunikila. Kodi thandizolo linagwila nchito? Inde, cifukwa iye anati: “Ndinapulumutsidwa m’kamwa mwa mkango.”—2 Tim. 4:16, 17. *

3 Kukumbukila zimenezi kuyenela kuti kunalimbikitsa Paulo kukhulupilila kuti Yehova adzamuthandiza kupilila mavuto amene anali kukumana nao, ndiponso amene akanakumana nao mtsogolo. Ndiye cifukwa cake iye anapitiliza kunena kuti: “Ambuye adzandipulumutsa ku coipa ciliconse.” (2 Tim. 4:18) Paulo anadziŵa kuti ngakhale kuti thandizo limene anthu angapeleke lingakhale losakwanila, thandizo limene Yehova ndi Mwana wake amapeleka limakhala lokwanila.

MWAI WOSONYEZA KUTI ‘TIMAKHULUPILILA YEHOVA’

4, 5. (a) Ndani angakupatseni thandizo lofunikila nthawi zonse? (b) Kodi mungalimbitse bwanji ubwenzi wanu ndi Yehova?

4 Kodi nthawi zina mukamakumana ndi mavuto mumadzimva kuti muli nokha? Mwina mukusowa nchito, mumavutitsidwa ku sukulu, mukudwala, kapena muli ndi mavuto ena. N’kutheka kuti munapempha thandizo koma ena anakukhumudwitsani cifukwa sanakuthandizeni m’njila imene munali kuyembekezela. Kunena zoona pali mavuto ena amene anthu sangakwanitse kuwathetsa. Kodi pazocitika zimenezo    malangizo a m’Baibulo akuti tiyenela ‘kukhulupilila Yehova’ ndi osathandiza? (Miy. 3:5, 6) Kodi n’zoona kuti Mulungu amathandiza? Inde, ndipo m’Baibulo muli nkhani zambili zoonetsa kuti Mulungu amathandizadi.

5 Conco mmalo mokhumudwa poona kuti thandizo la anthu ndi losakwanila, muyenela kuona mavuto ngati mmene Paulo anawaonela. Muyenela kuwaona kuti ndi mwai wanu wosonyeza kuti mumakhupilila kwambili Yehova ndi kuyembekezela kuti iye adzakusamalilani mwacikondi. Zimenezi zidzalimbitsa cikhulupililo canu mwa Mulungu, ndipo ubwenzi wanu ndi iye udzalimba kwambili.

KUKHULUPILILA MULUNGU KUMALIMBITSA UBWENZI WATHU NDI IYE

6. N’cifukwa ciani nthawi zina kukhulupilila Yehova tikakhala ndi mavuto kumakhala kovuta?

6 Kodi n’zotheka kuuza Yehova m’pemphelo mavuto athu ndi kukhala ndi mtendele wa m’maganizo, tili ndi cidalilo cakuti tacita mbali yathu ndipo iye adzasamalila zotsala? Inde, n’zotheka. (Ŵelengani Salimo 62:8; 1 Petulo 5:7.) Kucita izi n’kofunika kwambili kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Koma nthawi zina kukhulupilila kuti Yehova adzatithandiza kumakhala kovuta. N’cifukwa ciani? Cifukwa cimodzi n’cakuti nthawi zina Yehova sayankha mapemphelo pa nthawi yomweyo.—Sal. 13:1, 2; 74:10; 89:46; 90:13; Hab. 1:2.

7. N’cifukwa ciani nthawi zina Yehova sayankha mapemphelo athu nthawi yomweyo?

7 N’cifukwa ciani nthawi zina Yehova sayankha nthawi yomweyo mapemphelo ndi kutipatsa ciliconse cimene tikufuna? Kumbukilani kuti ubwenzi wathu ndi iye uli monga wa tate ndi ana. (Sal. 103:13) Mwana sangayembekezele kuti kholo lake lizimucitila mwamsanga ciliconse cimene wapempha. Zinthu zina zimene mwana angapemphe zingakhale zosafunikila kwenikweni. Nthawi zina mwanayo angafunike kuyembekezela mpaka nthawi yoyenela itakwana. Ndiponso zina zimene angapemphe sizikhala zabwino kwa iye ndiponso kwa anthu ena. Kuonjezela apo, ngati kholo limapatsa mwana mwamsanga ciliconse cimene wapempha, khololo limakhala ngati kapolo wa mwanayo. Mofananamo, Yehova, Atate wathu wakumwamba amatikonda. Monga Mlengi wathu wanzelu, amadziŵa zimene timafunikila ndiponso nthawi yabwino yotipatsa zimene tamupempha. Conco, tiyenela kuyembekezela Yehova ndi kuona mmene adzayankhila mapemphelo athu.—Yelekezelani ndi Yesaya 29:16; 45:9.

8. Popeza Yehova amatidziŵa bwino, n’ciani cimene analonjeza?

8 Cifukwa cina n’cakuti Yehova amadziŵa bwino zimene tingakwanitse kucita. (Sal. 103:14) Conco, iye sayembekezela kuti tipilila mwa mphamvu zathu zokha, koma pokhala tate wathu, amatithandiza mwacikondi. N’zoona kuti nthawi zina timaona kuti sitingakwanitse kupilila. Komabe, Yehova analonjeza kuti sadzalola atumiki ake kuyesedwa kufika pamene sangapilile, koma “adzapeleka njila yopulumukila.” (Ŵelengani 1 Akorinto 10:13.) Motelo, tili ndi zifukwa zomveka zokhulupilila kuti Yehova amadziŵa bwino zimene tingakwanitse kupilila.

9. Tiyenela kucita ciani ngati taona kuti mapemphelo athu sakuyankhidwa mwamsanga?

9 Ngati taona kuti mapemphelo athu opempha thandizo sakuyankhidwa mwamsanga, tiziyembelekezela Mulungu amene amadziŵa nthawi yabwino yocitapo kanthu. Tizikumbukila kuti iye amangoleza mtima koma amafunitsitsa kutithandiza. Baibulo limati: “Yehova azidzayembekezela kuti akukomeleni mtima ndipo adzanyamuka kuti akucitileni cifundo, pakuti Yehova ndi Mulungu amene amaweluza mwacilungamo. Odala ndi anthu onse amene amamuyembekezela.”—Yes. 30:18.

“M’KAMWA MWA MKANGO”

10-12. (a) Kodi Mkristu amene akusamalila wacibale amene ali ndi matenda aakulu angakumane ndi mavuto otani? (b) Kodi kukhulupilila Yehova panthawi ya mavuto kumalimbitsa bwanji ubwenzi wathu ndi iye? Pelekani citsanzo.

10 Mukakumana ndi mavuto aakulu mungaone ngati muli pafupi kugwidwa ndi mkango kapena muli kale “m’kamwa mwa mkango” monga mmene Paulo anamvelela. Panthawiyi kukhulupilila Yehova n’kofunika kwambili ngakhale kuti kucita zimenezi kumakhala kovuta. Mwacitsanzo, yelekezelani kuti mukusamalila wacibale wanu amene akudwala matenda aakulu. Mwina mumapemphela kwa Mulungu kuti akupatseni mphamvu ndi nzelu. * Popeza kuti mukucita zonse zimene mungathe, simuyenela kukaikila kuti Yehova akukuyang’anilani ndipo adzakuthandizani kuti mupilile.—Sal. 32:8.

11 Nthawi zina zinthu zingakhale zovuta ndipo madokotala angakuuzeni malingalilo osiyanasiyana. Mwina acibale anu amene munali kuyembekezela kuti akutonthozani, ndi amene akucititsa zinthu kukhala zovutilatu. Zotelo zikacitika, pitilizani kuyembekezela Yehova kuti akulimbitseni. Pitilizani kuyandikila kwa iye. (Ŵelengani 1 Samueli 30:3, 6.) Yehova akapeleka thandizo, ubwenzi wanu ndi iye umalimba kwambili.

12 Mlongo wina dzina lake Linda, * atasamalila makolo ake amene anali kudwala mpaka pamene anamwalila, anaona kuti n’zoona Yehova amalimbitsa. Iye anati: “Panthawiyo, ine, mwamuna wanga, ndi mlongosi wanga tinali kuthedwa nzelu. Nthawi zina tinali kuona ngati palibe amene angatithandize. Koma tikaganizila mmene zinthu zinalili, timaona kuti Yehova anali nafe. Ngakhale pamene tinasoŵelatu cocita, iye anatilimbitsa ndi kutipatsa thandizo limene tinali kufunikila.”

13. Kodi kukhulupilila Yehova kunathandiza bwanji mlongo wina kupilila atakumana ndi mavuto ambili?

13 Kudalila kwambili Yehova kungatithandizenso tikakumana ndi mavuto aakulu. Mlongo winanso dzina lake Rhonda anakumana ndi mavuto aakulu. Pamene mwamuna wake wosakhulupilila anali kukonza zothetsa banja lao, mlongosi wake anadwala matenda oopsa amene amayamba cifukwa ca kusokonezeka kwa citetezo ca m’thupi. Patapita miyezi yocepa, mkazi wa mlongosi wakeyo anamwalila. Izi zinamufooketsa kwambili Rhonda koma pamene anayamba kupezako bwino anayamba kucita upainiya wa nthawi zonse. Koma patapita nthawi yocepa amai ake anamwalila. N’ciani cinathandiza Rhonda kupilila? Iye anafotokoza kuti: “Ndinali kukamba ndi Yehova tsiku lililonse ngakhale ndikafuna kupanga zosankha zing’onozing’ono. Kucita zimenezi kunalimbitsa ubwenzi wanga ndi Yehova. Ndinaphunzilanso kumudalila osati kudzidalila kapena kudalila anthu ena. Ndipo iye anandipatsa zosowa zanga zonse. Cifukwa ca ici, ndimaona kuti ndikuyenda ndi Yehova.”

Ngakhale m’banja, tikhoza kukumana ndi mavuto amene angayese cikhulupililo cathu mwa Yehova (Onani ndime 14 mpaka 16)

14. Kodi Mkristu wokhulupilika amene wacibale wake ndi wocotsedwa, ayenela kukhulupilila ciani?

14 Taganizilani cocitika cina ici: Yelekezelani kuti wacibale wanu wacotsedwa mumpingo. Malinga ndi zimene munaphunzila m’Baibulo, mumadziŵa mmene tiyenela kuonela munthu wocotsedwa. (1 Akor. 5:11; 2 Yoh. 10) Komabe, nthawi zina kupewa kugwilizana ndi wocotsedwa kumakhala kovuta cakuti kumaoneka ngati n’kosatheka. * Zikakhala conco, muyenela kukhulupilila kuti Atate wanu wakumwamba adzakuthandizani kumvela malangizo a m’Baibulo pankhani yokhudza wocotsedwa. Ndiponso muyenela kuona umenewu ngati mwai wolimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova.

15. N’cifukwa ciani Adamu sanamvele lamulo la Yehova mu Edeni?

15 Pankhaniyi, ganizilani za munthu woyamba, Adamu. Kodi iye sanali kudziŵa kuti ngati sadzamvela Yehova adzafa? Iyai, anali kudziŵa, n’cifukwa cake Malemba amati “Adamu sananyengedwe.” (1 Tim. 2:14) Nanga n’cifukwa ciani sanamvele Mulungu? Adamu ayenela kuti anadya cipatso cimene mkazi wake, Hava, anamupatsa cifukwa cofuna kumukondweletsa. Conco, iye anasankha kumvela mau a mkazi wake kuposa mau a Yehova, Mulungu wake.—Gen. 3:6, 17.

16. Ndani amene tiyenela kumukonda koposa? Nanga n’cifukwa ciani?

16 Koma kodi izi zitanthauza kuti sitiyenela kukonda kwambili acibale athu? Iyai. Koma zikutanthauza kuti tiyenela kukonda kwambili Yehova kuposa wina aliyense. (Ŵelengani Mateyu 22:37, 38.) Ndipo zimenezi zimakhala zopindulitsa kwa acibale athu kaya amatumikila Yehova kapena ai. Conco, pitilizani kukulitsa cikondi canu pa Yehova ndi kumukhulupilila kwambili. Ndipo ngati mumavutika maganizo cifukwa cakuti wacibale wanu ndi wocotsedwa, muuzeni Yehova nkhawa yanu m’pemphelo. * (Aroma 12:12; Afil. 4:6, 7) Onani mavuto amenewo ngati mwai wolimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Kucita zimenezi kudzakuthandizani kuyembekeza Yehova kuti akupatseni thandizo lofunika.

PAMENE TIKUYEMBEKEZELA THANDIZO

Sonyezani kuti mumakhulupilila Yehova mwa kuika nchito yolalikila patsogolo (Onani ndime 17)

17 N’cifukwa ciani Paulo anapulumutsidwa “mkamwa mwa mkango”? Iye anati: “Kuti kudzela mwa ine, nchito yolalikila icitidwe mokwanila, ndi kuti mitundu yonse ya anthu imve uthengawo.” (2 Tim. 4:17) Monga Paulo, nafenso pamene tiika nchito yolalikila patsogolo mu umoyo wathu, tiyenela kukhulupilila kuti Yehova adzaonetsetsa kuti zonse zimene timafuna ‘zawonjezedwa kwa ife.’ (Mat. 6:33) Pokhala alengezi a Ufumu ‘tapatsidwa nchito yolalikila uthenga wabwino’ ndipo Yehova amationa kuti “ndife anchito anzake.” (1 Ates. 2:4; 1 Akor. 3:9.) Tikamagwila mwacangu nchito imene Mulungu anatipatsa, sicidzakhala covuta kuyembekezela thandizo lake.

18. Tingacite ciani kuti tizikhulupilila kwambili Yehova ndi kulimbitsa ubwenzi wathu ndi iye?

18 Conco, tiyeni tigwilitsile nchito nthawi ino kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu. Ngati tikukumana ndi vuto linalake, tizigwilitsila nchito nthawi imeneyo kuyandikila kwambili Yehova. Tingacite zimenezo mwa kusinkhasinkha Mau a Mulungu, kupemphela nthawi zonse, ndi kutangwanika ndi zinthu zakuuzimu. Ndipo pamene tikucita zimenezi tiyenela kukhulupilila kuti Yehova adzatithandiza kulimbana ndi mavuto amene tikukumana nao tsopano, ndiponso amene tingakumane nao mtsogolo.

^ par. 2 Mau akuti “m’kamwa mwa mkango” amene Paulo anagwilitsila nchito angatanthauze mkango weniweni kapena wophiphilitsila.

^ par. 10 Nkhani zothandiza Akristu amene akudwala ndi amene akusamalila odwala zinafalitsidwa mu Galamukani! ya February 8, 1994; February 8, 1997; June 8, 2000; ndi ya February 8, 2001.

^ par. 12 Maina asinthidwa

^ par. 14 Onani nkhani yakuti “Cifukwa Cake Kucotsa Munthu Mumpingo Ndi Makonzedwe Acikondi,” m’magazini ino.

^ par. 16 Nkhani zimene zingathandize Akristu okhulupilika kupilila pamene wacibale wao wacotsedwa zinafalitsidwa mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 2006 (tsamba 17 mpaka 21), ndi ya January 15, 2007 (tsamba 17 mpaka 20).