Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Muzicita Zinthu Mogwilizana ndi Pemphelo Lacitsanzo—Mbali 2

Muzicita Zinthu Mogwilizana ndi Pemphelo Lacitsanzo—Mbali 2

“Tate wanu amadziŵa zimene mukufuna.”—MAT. 6:8.

1-3. N’cifukwa ciani mlongo wina ndi wotsimikiza kuti Yehova amadziŵa zimene tikufuna?

LANA sadzaiŵala zimene zinacitika tsiku lina mu 2012 ku Germany. Iye amaona kuti mapemphelo ake aŵili acindunji anayankhidwa. Pemphelo loyamba analipeleka pamene anali paulendo wautali wa pa sitima wopita ku bwalo la ndeke. Iye anapempha Yehova kuti atsegule njila yakuti alalikile. Atafika ku bwalo la ndeke, anauzidwa kuti ndeke siipita tsikulo koma idzapita maŵa lake. Apa m’pamene iye anapeleka pemphelo laciŵili. Iye anapemphela kwa Yehova kuti amuthandize cifukwa analibe ndalama zokwanila ndi malo ogona.

2 Lana atangomaliza pemphelo laciŵili munthu wina anamupatsa moni, amvekele “Bwanji Lana! Ukucita ciani kuno?” Munthu amene anam’patsa moni anali mnzake amene anali kuphunzila naye kusukulu. Mnzakeyo anali ndi amai ake ndi ambuye ake aakazi amene anali kumuyembekeza kuti akwele ndeke yopita ku South Africa. Lana atawafotokozela mmene zinthu zinalili, a Elke, amai a mnzakeyo anamutenga n’kupita naye kunyumba kwao. Amai ndi ambuye ake a mnzakeyo anamulandila bwino ndipo anamufunsa mafunso ambili okhudza zikhululupililo zake ndi nchito yake monga mlaliki wa nthawi zonse.

3 Kutaca, io anakonza cakudya ca m’maŵa cogwila pamimba. Pambuyo polandila cakudyaco, Lana anayankha mafunso ambili a m’Baibulo ndipo anatenga adilesi, nambala ya foni, ndi imelo yao ndi colinga cakuti azikambilana nao popeza anali ataonetsa cidwi. Lana anafika kwao bwinobwino ndipo anapitiliza kutumikila monga mpainiya wa nthawi zonse. Iye amatsimikiza kuti “Wakumva pemphelo” ndi amene anamuthandiza kuti zinthu zimuyendele bwino.—Sal. 65:2.

4. Kodi tikambilana zinthu zofunika ziti?

4 Tikakumana ndi vuto ladzidzidzi, tingapemphe thandizo kwa Yehova ndipo iye amasangalala kumva mapemphelo otelo a anthu olungama. (Sal. 34:15; Miy. 15:8) Conco, ngati timaganizila mozama pemphelo lacitsanzo, tingazindikile zinthu zofunika kwambili zimene nthawi zina timazinyalanyaza. Mwacitsanzo, ganizilani mmene zosoŵa zathu za kuuzimu zimaonekela m’mapempho atatu omalizila m’pemphelo la citsanzo. Kodi pali zinthu zina zimene tingacite zogwilizana ndi pempho lacinai lokhudza cakudya cathu calelo?—Ŵelengani Mateyu 6:11-13.

“MUTIPATSE IFE LELO CAKUDYA CATHU CALELO”

5, 6. N’cifukwa ciani pempho la cakudya cathu calelo ndi lofunika ngakhale kuti tili ndi zinthu zokwanila za kuthupi?

5 Onani kuti pempho laumwini limeneli silikukamba kuti cakudya “canga” calelo koma likuti cakudya “cathu” calelo. Victor, woyang’anila dela wa mu Africa muno anati: “Ndimayamikila kwambili Yehova kuti ine ndi mkazi wanga sitikhala ndi nkhawa yadzaoneni yakuti cakudya ticipeza kuti komanso sitidela nkhawa kuti tipeza bwanji ndalama zolipila nyumba ya lendi. Tsiku lililonse abale amatisamalila mwacikondi. Ngakhale n’telo, ndimapemphelanso kuti aja amene amatithandiza athe kulimbana ndi mavuto a zacuma.”

6 Ngakhale tili ndi cakudya cokwanila, tingacite bwino kuganizila abale amene ali pa umphawi kapena amene akukumana ndi zovuta zina. Tiziwapemphelela ndi kucita zinthu mogwilizana ndi mapemphelo athu. Mwacitsanzo, tikaona kuti olambila anzathu alibe zinthu zina zofunika, tingagaŵane nao zinthu zimene ife tili nazo. Nthawi zonse tizicita zopeleka za nchito ya padziko lonse, podziŵa kuti ndalama zimenezi zimagwilitsidwa nchito mwanzelu.—1 Yoh. 3:17.

7. Kodi Yesu anapeleka fanizo lotani pofuna kuticenjeza kuti ‘tisamade nkhawa za tsiku lotsatila’?

7 Pamene Yesu anakamba kuti tizipempha cakudya cathu calelo, anali kutanthauza kuti tiyenela kupempha zofunika za pa umoyo. Ndiyeno anapitiliza kufotokoza mmene Mulungu amasamalila maluwa akuchile. Iye anati: “Kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo, acikhulupililo cocepa inu? Conco musamade nkhawa n’kumanena kuti, . . . ‘Tivala ciani?’” Iye anamaliza mwa kubweleza langizo lofunika kwambili ili: “Musamade nkhaŵa za tsiku lotsatila.” (Mat. 6:30-34) Mau amenewa aonetsa kuti tiyenela kukhala okhutila ndi zinthu zofunika za tsiku ndi tsiku zimene tili nazo m’malo mofunafuna cuma. Zinthu zofunika zimenezi zingaphatikizepo nyumba yabwino, nchito yotithandiza kupeza zosoŵa za banja, ndi nzelu zotithandiza kulimbana ndi matenda. Koma sitiyenela kumangopempha zinthu zakuthupi. Tiyenelanso kupempha zosoŵa zathu za kuuzimu zimene n’zofunika kwambili.

8. Kodi mau amene Yesu anakamba onena za cakudya calelo, ayenela kutikumbutsa ciani cimene ndi cofunika kwambili? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

8 Mau amene Yesu anakamba onena za cakudya cathu calelo ayenela kutikumbutsa zosoŵa zathu za kuuzimu. Ambuye wathu anati: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi cakudya cokha, koma ndi mau onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (Mat. 4:4) Conco tiyenela kupemphelabe kuti Yehova apitilize kutipatsa cakudya ca kuuzimu panthawi yake.

“MUTIKHULULUKILE ZOLAKWA ZATHU” KAPENA KUTI NKHONGOLE

9. N’cifukwa ciani macimo athu ali ngati nkhongole?

9 N’cifukwa ciani Yesu anagwilitsila nchito mau akuti “zolakwa” kapena kuti nkhongole koma pambuyo pake anakamba za “macimo”? (Mat. 6:12; Luka 11:4) Kwa zaka zoposa 60 zapitazo, magazini ina ya Nsanja ya Mlonda inafotokoza bwino kwambili nkhaniyi. Inati: “Kucimwila lamulo la Mulungu kumaticititsa kukhala ndi nkhongole kwa iye. . . . Cifukwa ca macimo athu kwa Mulungu sitinali oyenela kukhala ndi moyo. . . . Sitikanakhala pa mtendele ngakhalenso paubale wabwino ndi iye. . . . Conco tifunika kumukonda ndi kumumvela, cifukwa tikacimwa zimakhala ngati talephela kulipila nkhongole ya kumukonda popeza kucita chimo ndi kusakonda Mulungu.”—1 Yoh. 5:3.

10. N’cifukwa ciani Yehova amatikhululukila? Nanga tifunika kumva bwanji ndi zimenezi?

10 Tsiku ndi tsiku timafunika kukhululukidwa macimo, ndipo ndife okondwa kuti Yehova anatipatsa nsembe ya dipo la Yesu imene imatheketsa kuti macimo athu akhululukidwe. Papita zaka 2,000 kucokela pamene Yesu anatifela, koma tikupindulabe ndi dipo lake lelolino. Tiyenela kuyamikila Yehova cifukwa ca mphatso yamtengo wapatali imeneyi. Palibe ngakhale mmodzi wa ife amene akanatha kulipila dipo limene linali kufunikila kuti timasuke ku ucimo ndi imfa. (Ŵelengani Masalimo 49:7-9; 1 Petulo 1:18, 19.) Mau amene ali m’pemphelo lacitsanzo akuti, “mutikhululukile zolakwa zathu” akutikumbutsa kuti monga mmene ife tifunikila dipo, naonso abale ndi alongo afunika dipo. Yehova amafuna kuti tiziganizila abale ndi alongo athu amenewa ndiponso ubwenzi wao ndi iye. Izi zimaphatikizapo kuwakhululukila akatilakwila. Mwina zimene amatilakwilazo zingakhale zazing’ono, koma tikawakhululukila timaonetsa kuti timawakonda. Timaonetsanso kuyamikila kuti Yehova amatikhululukila.—Akol. 3:13.

Ngati mufuna kuti Mulungu azikukhululukilani, inunso muzikhululukila ena (Onani ndime 11)

11. N’cifukwa ciani tifunika kukhululukila ena?

11 N’zomvetsa cisoni kuti nthawi zina anthu opanda ungwilofe timasungila ena cakukhosi. (Lev. 19:18) Tikamakamba nkhani inayake, ena akhoza kukhala kumbali yathu. Zimenezi zimabweletsa magaŵano mumpingo. Ngati timalola zotele kucitika, ndiye kuti tikuonetsa kuti sitiyamikila cifundo ca Mulungu ndi dipo lake. Ngati tilephela kukhululukila ena, Atate wathu angacititse mphamvu ya nsembe ya Mwana wake kuleka kugwila nchito kwa ife. (Mat. 18:35) Yesu anafotokoza zimenezi atangopeleka pemphelo lacitsanzo. (Ŵelengani Mateyu 6:14, 15.) Conco tiyenela kuyesetsa kupewa kucita macimo aakulu kuti Mulungu azitikhululukila. Komanso cifukwa cakuti sitifuna kucita cimo, timam’pempha kuti asatilowetse m’mayeselo.—1 Yoh. 3:4, 6.

“MUSATILOWETSE M’MAYESELO”

12, 13. (a) N’ciani cinacitikila Yesu atangobatizidwa? (b) N’cifukwa ciani sitiyenela kuimba mlandu ena tikakumana ndi mayeselo? (c) Kodi Yesu anasonyeza ciani mwa kukhala wokhulupilika mpaka imfa?

12 Kuganizila zimene zinacitikila Yesu atangobatizidwa kungatithandize kumvetsa kufunika kwa pempho lakuti: “Musatilowetse m’mayeselo.” Mzimu wa Mulungu unatsogolela Yesu kucipululu. Cifukwa ciani? “Kuti akayesedwe ndi Mdyelekezi.” (Mat. 4:1; 6:13) N’cifukwa ciani Yehova analola zimenezi kucitika? Adamu ndi Hava anakana ulamulilo wa Yehova. Satana anayambitsa mafunso amene anafunika nthawi yaitali kuti ayankhidwe. Mwacitsanzo, kodi panali colakwika ciliconse ndi mmene Mulungu anapangila anthu? Kodi zinali zotheka kuti munthu wangwilo akhale wokhulupilika kwa Yehova akayesedwa ndi “woipayo”? Kodi cikanakhala bwino kuti anthu azidzilamulila okha? (Gen. 3:4, 5) Kukhulupilika kwa Yesu kunaonetsa kuti Mdyelekezi ndi wabodza. Kuyankha mafunso amenewa kunafunika nthawi kuti zolengedwa zonse za nzelu zizindikile kuti ulamulilo wa Yehova ndi wabwino kwambili.

13 Yehova ndi woyela, conco sayesa munthu aliyense kuti acite zinthu zoipa. Koma “Woyesayo” ndi Mdyelekezi. (Mat. 4:3) Mdyelekezi amatiyesa m’njila zambili koma tili ndi ufulu wosankha. Conco zimadalila munthu aliyense payekha kudziika mwadala pa mayeselo kapena ai. (Ŵelengani Yakobo 1: 13-15.) Yesu anagwilitsila nchito Mau a Mulungu pokana mayeselo onse a Satana. Mwakucita zimenezo, Yesu anaonetsa kuti Mulungu ndi woyenela kulamulila. Koma Satana sanalekele pamenepo. Iye anayembekeza “kufikila nthawi ina yabwino.” (Luka 4:13) Yesu sanagonje pa mayeselo onse a Satana ofuna kuononga kukhulupilika kwake. Kristu anacilikiza ulamulilo wa Yehova wacilungamo ndipo anaonetsa kuti anthu angwilo angakhale okhulupilika ngakhale akumane ndi mayeselo otani. Satana amafuna kusoceletsa otsatila a Yesu kuphatikizapo inuyo.

14. Kodi tifunika kucita ciani kuti tisagwele m’mayeselo?

14 Mafunso amene anabuka okhudza ulamulilo wa Mulungu, anafunikabe kuyankhidwa. Conco palipano, Yehova walola kuti Satana atiyese. Komabe zimenezi sizitanthauza kuti Mulungu amatiyesa. M’malo mwake, iye amatidalila kuti tidzakhalabe wokhulupilika ndipo amafuna kutithandiza. Iye satikakamiza kucita coyenela koma amalemekeza ufulu wathu wosankha. Conco amatilola kudzisankhila tokha kaya tifuna kukhala okhulupilika kapena ai. Motelo, kuti tipewe mayeselo tifunika kucita zinthu ziŵili izi: Kuyandikila kwa Yehova ndi kupitilizabe kupempha thandizo lake. Koma kodi Yehova amayankha bwanji mapemphelo athu?

Pitilizani kukhala olimba mwa kuuzimu ndipo khalani acangu pogwila nchito yolalikila (Onani ndime 15)

15, 16. (a) Ndi ziyeso zina ziti zimene tifunika kupewa? (b) Ndani amene afunika kuimbidwa mlandu ngati munthu wagonja pa ciyeso?

15 Yehova amatipatsa mphamvu ya mzimu woyela kuti itilimbitse ndi kutithandiza kulimbana ndi mayeselo. Mulungu amaticenjeza kudzela m’Mau ake ndi mumpingo kuti tiyenela kupewa zinthu zimene zingatigwetsele m’mayeselo. Zina mwa zinthu zimenezi ndi kuonongela nthawi yathu, ndalama zathu ndi mphamvu zathu pa zinthu zosathandiza kwenikweni. Espen ndi Janne amakhala m’dziko lolemela la ku Ulaya. Kwa zaka zambili, io anali kucita upainiya ndipo anali kutumikila kumalo amene kukufunika ofalitsa ambili m’dziko lao. Koma mwana wao woyamba atabadwa, io analeka kucita upainiya ndipo tsopano ali ndi mwana waciŵili. Espen ananena kuti: “Nthawi zambili timapemphela kwa Yehova kuti tisagwele m’mayeselo popeza kuti masiku ano timathela nthawi yocepa pa zinthu za kuuzimu kusiyana ndi kale. Timapempha Yehova kuti atithandize kukhala olimba mwa kuuzimu ndi kuti tikhale acangu pa nchito yolalikila.”

16 Ciyeso cina cimene tifunika kupewa ndi kuonelela zamalisece. Ngati tagwela m’ciyeso cimeneci, sitingaimbe mlandu Satana. Cifukwa ciani? Cifukwa Satana ndi dziko lake satikakamiza kucita zinthu zimene ife sitifuna kucita. Ena agwela m’ciyeso cimeneci mwa kulola maganizo ao kuganizila kwambili zinthu zoipa. Abale masauzande ambili apewa ciyeso cimeneci, conco nafenso tingakwanitse.—1 Akor. 10:12, 13.

“MUTILANDITSE KWA WOIPAYO”

17. (a) Tingacite bwanji zinthu mogwilizana ndi pempho lathu lakuti Yehova atilanditse kwa woipayo? (b) Kodi tikuyembekezela ciani posacedwapa?

17 Kuti ticite zinthu mogwilizana ndi pempho lakuti “mutilanditse kwa woipayo,” tiyenela kuyesetsa “kusakhala mbali ya dziko [la Satana].” Sitifunikanso ‘kukonda dziko [la Satana] kapena zinthu za m’dziko.’ (Yoh. 15:19; 1 Yoh. 2:15-17) Timafunika kuyesetsa kupewa zimenezi nthawi zonse. Tidzasangalala kwambili Yehova akadzayankha pempho limeneli mwa kucotsapo Satana ndi kuononga dziko lake. Tifunika kukumbukila kuti pamene Satana anaponyedwa pansi kucokela kumwamba, iye anadziŵa kuti watsala ndi kanthawi kocepa. Popeza kuti ndi wokwiya kwambili, iye akucita zilizonse zimene angathe kuti aticititse kukhala wosakhulupilika. Conco, tifunika kupempha Yehova kuti atilanditse kwa woipayo.—Chiv. 12:12, 17.

18. N’ciani cimene tifunika kucita kuti tikapulumuke pamene dziko la Satanali lidzaonongedwa?

18 Kodi mukufuna kudzakhala osangalala? Pitilizani kupempha Ufumu wa Mulungu kuti udzayeletse dzina lake ndi kupangitsa cifunilo cake kucitika pa dziko lapansi. Nthawi zonse muzidalila Yehova kuti akuthandizeni kupeza zosoŵa zanu za kuuzimu ndi zakuthupi. Inde, citani zinthu mogwilizana ndi pemphelo lacitsanzo.