Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Muzicita Zinthu Mogwilizana ndi Pemphelo Lacitsanzo—Mbali 1

Muzicita Zinthu Mogwilizana ndi Pemphelo Lacitsanzo—Mbali 1

Dzina lanu liyeletsedwe.”—MAT. 6:9.

1. Tingagwilitsile nchito bwanji pemphelo lopezeka pa Mateyu 6:9-13 mu ulaliki?

ANTHU ambili amaloweza pamtima Pemphelo la Ambuye. Pocita ulaliki wa kunyumba ndi nyumba, timagwilitsila nchito pempheloli pofuna kuthandiza eninyumba kumvetsa kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni limene lidzasintha zinthu pa dziko lapansi. Tingagwilitsilenso nchito pempho loyamba mpempheloli, kuonetsa anthu kuti Mulungu ali ndi dzina limene liyenela kuyeletsedwa.—Mat. 6:9.

2. Timadziŵa bwanji kuti Yesu sanatanthauze kuti tizibweleza mau a m’pemphelo lacitsanzo popemphela?

2 Kodi Yesu anatanthauza kuti tizibweleza mau a m’pemphelo lacitsanzo nthawi iliyonse imene tikupemphela monga mmene amacitila Machechi Acikristu? Iyai. Yesu asanapeleke pemphelo lacitsanzo limeneli anati: “Popemphela, usanene zinthu mobwelezabweleza.” (Mat. 6:7) Patapita nthawi, Yesu anafotokozanso pemphelo limeneli koma sanagwilitsile nchito mau amodzimodzi. (Luka 11:1-4) Pamenepa Yesu anatithandiza kudziŵa zinthu zimene tifunika kupempha. Conco, m’pomveka kulichula kuti pemphelo lacitsanzo.

3. Ndi mafunso ati amene tifunika kuwaganizila mozama pokambilana pemphelo lacitsanzo?

3 M’nkhani ino ndi yotsatila, tikambilana pemphelo lacitsanzo. Conco, pokambilana zimenezi mungadzifunse kuti, ‘kodi pemphelo lacitsanzoli lingandithandize bwanji kupeleka mapemphelo okonzedwa bwino?’ Ndipo cofunika kwambili ndi kudzifunsa kuti, ‘kodi ndikucita zinthu mogwilizana ndi pemphelo limeneli?’

“ATATE WATHU WAKUMWAMBA”

4. Kodi mau akuti “Atate wathu” amatikumbutsa ciani? Nanga n’cifukwa ciani Yehova amachedwa “Atate” kwa Akristu amene ali ndi ciyembekezo cokhala pa dziko lapansi?

4 Mau akuti “Atate wathu” osati “Atate wanga,” amatikumbutsa kuti tili ‘m’gulu la abale’ amene amakondanadi. (1 Pet. 2:17) Umenewu ndi mwai waukulu kwambili. Akristu odzozedwa, amene asankhidwa ndi Mulungu kukhala ana ake amene adzakhala ndi moyo kumwamba, moyenelela amachula Yehova kuti “Atate.” (Aroma 8:15-17) Akristu amene ali ndi ciyembekezo cokhala padziko lapansi kosatha amachula Yehova kuti “Atate.” Yehova ndiye Mpatsi wa Moyo ndipo mwacikondi amapeleka zosowa kwa olambila onse oona. Awo amene ali ndi ciyembekezo codzakhala padziko lapansi adzachedwa ana a Mulungu enieni, akadzakhala angwilo ndi kupyola ciyeso comaliza.—Aroma 8:21; Chiv. 20:7, 8.

5, 6. Ndi mphatso yabwino iti imene makolo angapatse ana ao? Nanga mwana ayenela kucita ciani ndi mphatsoyi? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

5 Makolo amapatsa ana ao mphatso zabwino mwa kuwaphunzitsa kupemphela ndi kuwathandiza kuona Yehova monga Atate wakumwamba amene amatisamalila. M’bale amene akutumikila monga woyang’anila dela ku South Africa anati: “Kucokela pamene ana athu aakazi anabadwa, ndinali kupemphela nao usiku uliwonse kupatulapo ndikapita kwina. Tsopano ana athu amenewa amakamba kuti sakumbukila bwinobwino mau a mapemphelo amenewo. Komabe amakumbukila mmene anali kumvela pamene tinali kulankhula ndi Atate wathu Yehova. Iwo anali kudzimva kuti ali pa mtendele ndiponso otetezeka. Pamene anaphunzila kupemphela, ndinali kuwalimbikitsa kuti azipemphela mokweza n’colinga cakuti ndimve mmene amafotokezela maganizo ao kwa Yehova. Kucita zimenezi kunandipatsa mwai wodziŵa bwino zimene zili mu mtima mwao. Ndiyeno pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kuwathandiza kuti popemphela azichulanso mfundo zofunika zopezeka mpemphelo lacitsanzo kuti mapemphelo ao azikhala atanthauzo.”

6 N’zosadabwitsa kuti ana a m’bale ameneyu anapita patsogolo mwa kuuzimu. Iwo tsopano anakwatiwa ndipo pamodzi ndi amuna ao akucita cifunilo ca Mulungu mu utumiki wanthawi zonse. Palibe mphatso yabwino imene makolo angapatse ana ao kuposa kuwathandiza kukhala pa ubwenzi wabwino komanso wolimba ndi Yehova. Ngakhale n’telo, aliyense ali ndi udindo wosunga ubwenzi wapadela umenewu. Ndipo kuusunga kumaphatikizapo kuphunzila kukonda dzina la Mulungu ndi kulilemekeza kwambili.—Sal. 5:11, 12; 91:14.

“DZINA LANU LIYELETSEDWE”

7. Ndi mwai wotani umene anthu a Mulungu ali nao? Nanga tifunika kucita ciani ndi mwai umenewo?

7 Tili ndi mwai waukulu kwambili osati wodziŵa dzina la Mulungu cabe komanso woliimila monga “anthu ochedwa ndi dzina lake.” (Mac. 15:14; Yes. 43:10) Timapempha Atate wathu wa kumwamba kuti: “Dzina lanu liyeletsedwe.” Pempho limeneli lingakusonkhezeleni kupempha Yehova kuti akuthandizeni kupewa kucita kapena kukamba zinthu zilizonse zosalemekeza dzina lake lopatulika. Tisakhale monga anthu a m’nthawi ya atumwi amene sanali kucita zimene anali kuphunzitsa. Mtumwi Paulo anawalembela kuti: “Dzina la Mulungu likunyozedwa pakati pa anthu amitundu cifukwa ca inu.”—Aroma 2:21-24.

8, 9. Pelekani citsanzo coonetsa kuti Yehova amadalitsa anthu amene amafuna kuyeletsa dzina lake.

8 Timafuna kuyeletsa dzina la Mulungu. Mwacitsanzo, mlongo wina ku Norway mwamuna wake atafa mwadzidzidzi, anatsala yekha ndi mwana wake wa zaka ziŵili. Mlongoyu anati: “Inali nthawi yovuta kwambili pa umoyo wanga.” Anaonjezela kuti: “Ndinali kupemphela tsiku lililonse pafupifupi nthawi iliyonse kuti ndikhale wolimba pa cisoni cimene ndinali naco. Komanso sindinafune kupatsa Satana mwai wotonza Yehova mwa kusankha zinthu mopanda nzelu kapena kucita zinthu mosakhulupilika. Ndinali kufunitsitsa kuyeletsa dzina la Yehova ndipo ndinali kufuna kuti mwana wanga adzaonanenso ndi atate wake m’paladaiso.”—Miy. 27:11.

9 Kodi Yehova anayankha pemphelo limeneli? Inde. Mlongo ameneyu anathandizidwa ndi okhulupilila anzake. Patapita zaka 5, iye anakwatiwa ndi mkulu. Mwana wake amene ali ndi zaka 20, tsopano ndi m’bale wobatizidwa. Mlongoyo anati: “Ndine wokondwa kwambili kuti mwamuna wangayu anandithandiza kulela mwana wanga.”

10. Kodi cofunika n’ciani kuti dzina la Mulungu liyeletsedwe kothelatu?

10 Kodi cofunika n’ciani kuti dzina la Mulungu liyeletsedwe kothelatu ndi kucotsedwa citonzo ciliconse? Kuti zimenezi zitheke, Yehova afunika kucitapo kanthu kuti acotse onse amene amakana ulamulilo wake mwadala. (Ŵelengani Ezekieli 38:22, 23.) Anthu adzakhala angwilo pang’ono ndi pang’ono. Tikulakalaka nthawi imene anthu onse adzalemekeza dzina la Yehova. Ndiyeno potsilizila pake, Atate wathu wa kumwamba amene ndi wacikondi adzakhala “zinthu zonse kwa aliyense.”—1 Akor. 15:28.

“UFUMU WANU UBWELE”

11, 12. Cakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, kodi Akristu oona anapatsidwa cizindikilo cotani?

11 Yesu asanakwele kumwamba atumwi ake anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi mubwezeletsa ufumu kwa Isiraeli pa nthawi ino?” Yankho la Yesu linaonetsa kuti nthawi yakuti io adziŵe pamene Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulila inali isanakwane. Iye anauza ophunzila ake kuika maganizo ao pa nchito yolalikila imene anali kugwila. (Ŵelengani Machitidwe 1:6-8.) Ngakhale n’telo, Yesu anaphunzitsa otsatila ake kuyembekezela Ufumu wa Mulungu. Kuyambila m’nthawi ya atumwi, Akristu ambili akhala akupemphela kuti Ufumuwo ubwele.

12 Pamene nthawi inafika yakuti Yesu ayambe kulamulila monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu kumwamba, Yehova anathandiza anthu kudziŵa nthawi ya zocitika zimenezo. Mu 1876, nkhani ina imene Charles Taze Russell analemba inasindikizidwa m’magazini yochedwa Bible Examiner. Nkhaniyo inali ya mutu wakuti: “Kodi Nthawi za Akunja Zidzatha Liti?” ndipo inakamba kuti caka ca 1914 cidzakhala caka capadela. Nkhaniyo inagwilizanitsa “nthawi zokwanila 7” zimene mneneli Danieli analosela ndi “nthawi zoikidwilatu za anthu a mitundu” zimene Yesu anakamba. *Dan. 4:16; Luka 21:24.

13. N’ciani cinacitika m’caka ca 1914? Nanga zimene zakhala zikucitika padzikoli zikutsimikizila ciani?

13 M’caka ca 1914, nkhondo inabuka pakati pa maiko a ku Ulaya ndipo inafalikila pa dziko lonse lapansi. Pamene nkhondoyi inali kutha m’caka ca 1918, padziko lonse panagwa njala yadzaoneni ndi mlili wa fuluwenza umene unapulula anthu ambili kuposa amene anafa pa nkhondo. Conco, “cizindikilo” cimene Yesu anapeleka ca kukhalapo kwake kosaoneka monga Mfumu yatsopano ya dziko lapansi cinayamba kukwanilitsidwa. (Mat. 24:3-8; Luka 21:10, 11) Pali maumboni ambili amene aonetsa kuti Ambuye Yesu Kristu “anapatsidwa cisoti cacifumu” m’caka ca 1914. Iye ‘anapita kukagonjetsa adani ake ndipo anapambana pa nkhondo yolimbana nao.’ (Chiv. 6:2) Anayeletsa kumwamba pankhondo yake yolimbana ndi Satana ndi ziwanda zake, amene anaponyedwa padziko lapansi. Kucokela nthawiyo, anthu aona kukwanilitsidwa kwa mau ouzilidwa awa: “Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, cifukwa Mdyelekezi watsikila kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziŵa kuti wangotsala ndi kanthawi kocepa.”—Chiv. 12:7-12.

14. (a) N’cifukwa ciani kupemphela kuti Ufumu wa Mulungu ubwele n’kofunikabe? (b) Ndi mwai wotani umene tapatsidwa?

14 Ulosi wolembedwa pa Chivumbulutso 12:7-12 umafotokoza kugwilizana kwa zocitika zoipa zimene zakhala zikuononga mtundu wa anthu ndi kubadwa kwa Ufumu wa Mulungu. Yesu amene ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu anayamba kulamulila pakati pa adani ake. Tidzapitilizabe kupemphela kuti Ufumu wa Mulungu ubwele mpaka iye atapambana pa nkhondo yake ndi kucotsa zoipa zonse zimene zikucitika padziko lapansi. Panthawi imodzimodziyo, tiyenela kukhala mogwilizana ndi mapemphelo amenewa mwa kucita nao nchito yofunika kwambili imene ndi “cizindikilo” cimene cikukwanilitsidwa. Yesu ananena kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mat. 24:14.

“CIFUNILO CANU CICITIKE . . . PANSI PANO”

15, 16. Kodi tingakhale bwanji mogwilizana ndi pempho lakuti cifunilo ca Mulungu cicitike padziko lapansi?

15 Pafupifupi zaka 6,000 zapitazo, cifunilo ca Mulungu cinali kucitika bwinobwino padziko lapansi. Ndiye cifukwa cake Yehova ataona anthu akucita cifunilo cake anakamba kuti zonse zimene anapanga “zinali zabwino kwambili.” (Gen. 1:31) Komabe Satana anamupandukila ndipo kucokela nthawi imeneyo, ndi anthu ocepa cabe amene akucita cifunilo ca Mulungu padziko lapansi. Ngakhale n’telo masiku ano pali Mboni za Yehova zokwanila 8 miliyoni zimene zikutumikila Yehova. Iwo amapemphela kuti cifunilo ca Mulungu cicitike pa dziko lapansi, ndiponso amacita cifunilo ca Mulungu. Amakhalanso ndi moyo wokondweletsa Mulungu ndi kugwila nchito mwakhama yopanga ophunzila.

Kodi mukuthandiza ana anu kucita zinthu mogwilizana ndi pempho lakuti cifunilo ca Mulungu cicitike pa dziko lapansi? (Onani ndime 16)

16 Mwacitsanzo, mlongo wina amene anali mmishonale mu Africa muno yemwe anabatizidwa mu 1948 anakamba kuti: “Mogwilizana ndi pemphelo lacitsanzo limeneli, ndimapemphela kuti anthu onse amene ali ngati nkhosa athandizidwe kudziŵa Yehova nthawi isanathe. Komanso ndisanayambe kulalikila munthu, ndimapempha nzelu kwa Yehova kuti munthuyo ndimufike pa mtima. Ndipo ndimapemphela kwa Yehova kuti adalitse khama lathu posamalila anthu oona mtima amene tawapeza kale.” N’zosadabwitsa kuti mlongo wa za 80 ameneyu akucita bwino kwambili mu ulaliki ndipo mothandizidwa ndi ena, iye wathandiza ambili kukhala Mboni za Yehova.Sitikukayikila kuti inunso mukudziŵa ena amene ndi citsanzo cabwino ca kudzipeleka pocita cifunilo ca Mulungu ngakhale kuti ndi acikulile.—Ŵelengani Afilipi 2:17.

17. Kodi mumamva bwanji mukaona mmene Yehova adzayankhila pempho lathu lakuti cifunilo cake cicitike pa dziko lapansi?

17 Tidzapitilizabe kupempha kuti cifunilo ca Mulungu cicitike mpaka Ufumu wa Mulungu utacotsa adani ake padziko lapansi. Ndipo tidzaona cifunilo ca Mulungu cikucitika mokwanila pamene anthu mabiliyoni adzaukitsidwa ndi kukhala m’paladaiso pa dziko lapansi. Yesu anati: “Musadabwe nazo zimenezi, cifukwa idzafika nthawi pamene onse ali m’manda acikumbutso adzamva mau [anga] ndipo adzatuluka.” (Yoh. 5:28, 29) Idzakhala nthawi yosangalatsa zedi kulandila okondedwa athu amene adzaukitsidwa. Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso [mwathu].” (Chiv. 21:4) Ambili mwa anthu amene adzaukitsidwa adzakhala “osalungama” amene anakhalako kalekale ndipo anafa asanaphunzile coonadi conena za Yehova Mulungu ndi Mwana wake. Tidzakhala ndi mwai wophunzitsa anthu oukitsidwawo cifunilo ca Mulungu ndi colinga cake. Mwa kucita zimenezi tidzawathandiza kuti ayenelele kukhala ndi “moyo wosatha.”—Mac. 24:15; Yoh. 17:3.

18. N’ciani cimene anthu akufunikila kwambili?

18 Ufumu wa Mulungu ukadzabwela udzayeletsa dzina lake, ndipo anthu onse adzayamba kulambila Yehova mogwilizana. Motelo, Mulungu adzapatsa anthu zinthu zofunika kwambili pamene adzayankha mapempho atatu oyambilila a m’pemphelo lacitsanzo. Koma pali mapempho ena anai amene atsala opezeka m’pemphelo lacitsanzo la Yesu. M’nkhani yotsatila tidzakambilana mapempho amenewa.

^ par. 12 Kuti mumvetse bwino mmene ulosiwu unakwanilitsidwila mu 1914, onani buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni masamba 215 mpaka 218.