Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Anali Kukonda Anthu

Anali Kukonda Anthu

“Zinthu zimene zinali kundisangalatsa, zinali zokhudzana ndi ana a anthu.”—MIY. 8:31.

1, 2. N’ciani cimaonetsa kuti Yesu amakonda kwambili anthu?

MWANA woyamba kubadwa wa Mulungu ndi colengedwa capamwamba koposa cimene cimaonetsa nzelu zakuya za Yehova. Iye anali pa mbali pa Mulungu monga “mmisili waluso.” Yesu ayenela kuti anali wosangalala kwambili pamene Atake ake “anali kukonza kumwamba” ndi ‘kukhazikitsa maziko a dziko lapansi’. Ndipo kuonjezela pamenepo, mwana woyamba kubadwa wa Mulungu anali ‘kusangalala ndi zinthu zokhudzana ndi ana a anthu.’ (Miy. 8:22-31) N’zoonekelatu kuti ngakhale asanabwele padziko lapansi, Yesu anali kukonda anthu.

2 Patapita nthawi, Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu anasonyeza kukhulupilika ndi cikondi kwa Atate ake ndiponso kwa “ana a anthu” mwa ‘kusiya zonse zimene anali nazo,’ ndi kukhala wofanana ndi anthu. Anacita zimenezo kuti apeleke “dipo kuwombola anthu ambili.” (Afil. 2:5-8; Mat. 20:28) Kunena zoona, Yesu amakonda kwambili anthu. Pamene Yesu anali padziko, Yehova anam’patsa mphamvu yocita zozizwitsa zomwe zinatsimikizila kuti amakondadi anthu. Ndipo zozizwitsa zimenezo zimapeleka cithunzi ca zinthu zabwino zimene zidzacitika padziko lonse mtsogolo.

3. Tikambilana ciani tsopano?

3 Cina cimene Yesu anacita atabwela padziko lapansi ndi ‘kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.’ (Luka 4:43) Yesu anadziŵa kuti Ufumuwo udzayeletsa dzina la Atate ake ndi kuthetselatu mavuto onse a anthu. Conco, zimene Yesu anacita mu utumiki wake zimasonyeza kuti amakonda mtundu wa anthu. Kodi zimenezi zimatikhudza bwanji? Zimatikhudza cifukwa cakuti zimatipatsa ciyembekezo ca zinthu zabwino zamtsogolo. Tiyeni tikambilane zozizwitsa zinai za Yesu.

‘MPHAMVU INALI PA IYE KUTI ATHE KUCILITSA’

4. N’ciani cinacitika Yesu atakumana ndi munthu wodwala khate?

4 Tsiku lina Yesu anapita kukalalikila ku Galileya. Ndipo mumzinda wina kumeneko anakumana ndi mwamuna wina amene anali ndi matenda oopsa a khate. (Maliko 1:39, 40) Mwamunayo anali wodwala kwambili moti Luka, amene anali dokotala, ananena kuti munthuyo anali “wakhate thupi lonse.” (Luka 5:12) “Pamene anaona Yesu, munthuyo anagwada n’kuwelama mpaka nkhope yake pansi ndi kum’pempha, kuti: ‘Ambuye, ngati mukufuna, mukhoza kundiyeletsa.’” Munthuyo anali kudziŵa kuti Yesu anali ndi mphamvu zotha kumucilitsa, koma sanali kudziŵa ngati Yesu anali wofunitsitsa kumuthandiza. Kodi Yesu anavomela pempho lake? Nanga anamva bwanji pamene anaona munthuyo amene anali wa maonekedwe oipa? Kodi iye anamuumila mtima monga mmene Afalisi anali kucitila ndi anthu odwala matendawa? Kodi inu mukanacita bwanji?

5. N’ciani cinacititsa Yesu kunena kuti “Ndikufuna” pamene anali kucilitsa wakhate?

5 Malinga ndi Cilamulo ca Mose, munthu wakhateyo anafunika kufuula kuti “Wodetsedwa, wodetsedwa!” koma zikuoneka kuti iye sanacite zimenezo. Yesu sanakalipe ndi zimenezo. M’malomwake, iye anaganizila kwambili za vuto la munthuyo ndi mmene akanamuthandizila. (Lev. 13:43-46) Sitikudziŵa zimene Yesu anali kuganiza kwenikweni, koma timadziŵa mmene anali kumvelela. Cifukwa ca cifundo, Yesu anacita zinthu zimene anthu sanali kuyembekezela. Iye anatambasula dzanja lake n’kukhudza  wakhateyo, ndipo mwacikondi anati: “Ndikufuna. Khala woyela. Nthawi yomweyo khate lakelo linatha.” (Luka 5:13) Yehova anapatsa Kristu mphamvu yocita zozizwitsa n’colinga cakuti Yesu aonetse kuti amakonda kwambili anthu.—Luka 5:17.

6. N’ciani cimakucititsani cidwi ndi mmene Yesu anali kucilitsila anthu? Nanga zimenezi zimasonyeza ciani?

6 Mphamvu za Yehova zinathandiza Yesu Kristu kucita zozizwitsa zambili. Iye sanacilitse khate cabe, koma anacilitsanso matenda amtundu uliwonse ndi zofooka zilizonse za anthu. Baibulo limati: “Khamu la anthulo linadabwa kuona osalankhula akulankhula, olumala akuyenda ndiponso akhungu akuona.” (Mat. 15:31) Pocita zimenezi, Yesu sanali kucotsa ciwalo coonongeka ndi kuikapo cina. Koma anali kucilitsa ziwalo zoonongekazo. Iye anali kucilitsa anthu nthawi yomweyo, ndipo nthawi zina anali kucilitsa ngakhale anthu amene anali kutali. (Yoh. 4:46-54) Kodi zinthu zocititsa cidwi zimenezi zikusonyeza ciani? Zikusonyeza kuti Yesu, amene tsopano ndi Mfumu kumwamba, ali ndi mphamvu ndipo ndi wofunitsitsa kuthetsa matenda. Kuphunzila mmene Yesu anali kucitila ndi anthu kumatipatsa cidalilo cakuti m’dziko latsopano ulosi wa m’Baibulo, wakuti: “Adzamvela cisoni munthu wonyozeka ndi wosauka,” udzakwanilitsidwa. (Sal. 72:13) Ndithudi, Yesu mofunitsitsa adzathandiza anthu ovutika.

‘NYAMUKA, NYAMULA MACILA AKO NDI KUYAMBA KUYENDA’

7, 8. Fotokozani zimene Yesu anacita asanakumane ndi munthu wolemala ku Yerusalemu.

7 Patapita miyezi yocepa kucokela pamene Yesu anakumana ndi munthu wakhate ku Galileya, iye anapita ku Yudeya kukalengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Anthu masauzande anakhudzidwa kwambili ndi uthenga umene Yesu anali kulalikila ndiponso khalidwe lake. Iye anali wofunitsitsa kulengeza uthenga wabwino kwa osauka, kulalikila za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo ndi kumanga zilonda za anthu osweka mtima.—Yes. 61:1, 2; Luka 4:18-21.

8 Mwezi wa Nisani utafika, Yesu anapita ku Yerusalemu kukacita Pasika potsatila malamulo a Atate ake. Anthu anali pilingupilingu mumzindamo pamene anali kubwela kudzacita cikondwelelo capadela cimeneci. Kumpoto kwa kacisi wa ku Yerusalemu kunali dziwe lochedwa Betesida. Ndipo kumeneko Yesu anakumana ndi munthu wina wolemala.

9, 10. (a) N’cifukwa ciani anthu anali kupita kudziwe la Betesida? (b) Kodi Yesu anacita ciani kudziwelo? Nanga zimenezi zikutiphunzitsa ciani? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

9 Anthu ambili odwala ndiponso olemala anali kupita ku dziwe la Betesida. N’cifukwa ciani io anali kupita ku malo amenewa? Pa cifukwa cosadziŵika bwino, io anali kukhulupilila kuti munthu wodwala amacila mozizwitsa akalowa m’dziwelo pamene madzi akuwinduka. Anthu ambili amene anali padziwepo ayenela kuti anali othedwa nzelu ndi ankhawa kwambili. Nanga n’cifukwa ciani Yesu anapita kumeneko popeza anali wangwilo ndiponso sanali kudwala? Cifukwa ca cifundo, Yesu anayamba kulankhula ndi munthu amene anayamba kudwala Yesuyo asanabadwe padziko. —Ŵelengani Yohane 5:5-9.

10 Yelekezelani kuti mukuona mmene wodwalayo akuonekela wacisoni pamene Yesu akumufunsa ngati akufuna kucila. Cifukwa cakuti anali kufunitsitsa kucila, iye anayankha mwamsanga, koma anali ndi nkhawa kuti adzacila bwanji popeza kunalibe womuviika m’dziwe. Ndiyeno Yesu anamuuza zinthu zimene zinali kuoneka ngati zosatheka, anamuuza kuti anyamule macila ake ndi kuyamba kuyenda. Pomvela mau a Yesu, munthuyo ananyamuladi macila ake ndi kuyamba kuyenda. Zimenezi n’zolimbikitsa kwambili cifukwa zionetsa kuti Yesu adzacita zinthu zambili m’dziko latsopano. Cozizwitsaci cikuonetsanso kuti Yesu ndi wacifundo. Iye anali kufunafuna anthu amene anali kufunika thandizo. Citsanzo ca Yesu ciyenela kutilimbikitsa kupitiliza kufunafuna anthu m’magawo athu amene ndi acisoni cifukwa ca zinthu zoipa zimene zikucitika m’dziko lino.

‘NDANI WAGWILA MALAYA ANGA?’

11. Kodi lemba la Maliko 5:25-34 limaonetsa bwanji kuti Yesu anali kucitila cifundo odwala?

11 Ŵelengani Maliko 5:25-34. Kwa zaka 12, mayiyo anali kukhala mwamanyazi. Matenda ake anali kukhudza umoyo wake wonse kuphatikizapo mbali ya kulambila. “Madokotala ambili anam’cititsa kumva zopweteka zambili. Iye anawononga cuma cake conse koma . . . matendawo ankangokulilakulila.” Tsiku lina mayiyo anaganiza zina zimene zinamuthandiza kuti acile. Iye anaimilila pamalo ena ake kuti akhale pafupi ndi Yesu. Iye analoŵa pakati pa khamu pamene panali Yesu ndi kugwila covala cake cakunja. (Lev. 15:19, 25) Yesu anamva kuti m’thupi mwake mwatuluka mphamvu. Conco anafunsa kuti adziŵe amene anamugwila. “Mayiyo anacita mantha ndi kuyamba kunjenjemela, ndipo . . . anafika pafupi n’kugwada pamaso pake ndi kumuuza zoona zonse.” Podziŵa kuti Atate wake, Yehova ndiye wacilitsa mayiyo, Yesu anamukomela mtima n’kumuuza kuti: “Mwanawe, cikhulupililo cako cakucilitsa. Pita mu mtendele, matenda ako aakuluwo atheletu.”

Zozizwitsa za Yesu zimaonetsa kuti iye amatikonda ndiponso amakhudzidwa ndi mavuto athu (Onani ndime 11 ndi 12)

12. (a) Malinga n’zimene takambilana, kodi Yesu anali munthu wotani? (b) Ndi citsanzo cotani cimene Yesu anatisiila?

12 Yesu ndi wokoma mtima kwambili. Iye amadela nkhawa anthu amene akuvutika cifukwa ca matenda. Koma Satana amafuna kuti tiziganiza kuti ndife acabecabe ndipo Mulungu ndi Yesu satikonda. Zozizwitsa za Yesu zimaonetsa kuti iye amatikonda ndiponso amakhudzidwa ndi mavuto athu. Iye ndi Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe wacifundo kwambili. (Aheb. 4:15) Nthawi zina zimakhala zovuta kumvetsa mmene anthu odwala matenda aakulu akumvela, makamaka ngati ife sitinakumanepo ndi mavuto otelo. Koma cimene tiyenela kukumbukila n’cakuti, Yesu anali kumvela cifundo odwala ngakhale kuti iye sanadwalepo. Conco, tiyenela kutengela citsanzo ca Yesu mwa kumvela ena cifundo.—1 Pet. 3:8.

“YESU ANAGWETSA MISOZI”

13. Kodi kuukitsidwa kwa Lazalo kumaonetsa kuti Yesu ndi munthu wotani?

13 Yesu anali kukhudzidwa kwambili ndi mavuto a ena. Iye ataona anthu amene anali kulila cifukwa ca imfa ya bwenzi lake Lazalo, “anadzuma povutika mumtima ndi kumva cisoni.” Iye anamva conco ngakhale kuti anali kudziŵa kuti adzaukitsa Lazalo. (Ŵelengani Yohane 11:33-36.) Yesu sanacite manyazi kuonetsa mmene anali kumvelela. Anthu amene analipo anaona kuti Yesu anali kukonda kwambili Lazalo ndi acibale ake. Yesu pogwilitsila nchito mphamvu za Yehova anaukitsa bwenzi lake, ndipo zimenezi zinaonetsa kuti iye ndi wacifundo kwambili.—Yoh. 11:43, 44.

14, 15. (a) N’ciani cionetsa kuti Yehova amalakalaka kuthetsa mavuto onse a anthu? (b) Kodi liu lakuti “manda acikumbutso” limasonyeza ciani?

14 Baibulo limanena kuti Yesu ndiye “cithunzi ceniceni ca Mulungu weniweniyo.” (Aheb. 1:3) Zozizwitsa zimene Yesu anacita zimatsimikizila kuti iye ndi Atate ake amalakalaka kuthetsa matenda ndi imfa. Ndipo anthu olembedwa m’Baibulo amene anaukitsidwa ndi ocepa poyelekezela ndi anthu amene Mulungu akulakalaka kudzaukitsa. Yesu ananena kuti: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda acikumbutso . . . adzatuluka.”—Yoh. 5:28, 29.

15 M’pomveka kuti Yesu anagwilitsila nchito mau akuti “manda acikumbutso” cifukwa Yehova adzaukitsa ao amene iye akukumbukila. Mulungu Wamphamvuyonse, amene analenga cilengedwe conse angakumbukile zonse zokhudza okondedwa athu amene anamwalila kuphatikizapo makhalidwe ao. (Yes. 40:26) Ndipo sikuti Yehova ndi Yesu amangokumbukila amene anamwalila koma amafunitsitsa kudzawaukitsa. Kuukitsidwa kwa Lazalo ndi ena amene analembedwa m’Baibulo kumasonyeza zimene zidzacitika mtsogolo m’dziko latsopano.

KODI ZOZIZWITSA ZA YESU ZIMATIKHUZA BWANJI?

16. Kodi Akristu okhulupilika masiku ano adzakhala ndi mwai wotani mtsogolo?

16 Tikayesetsa kukhala okhulupilika, tidzakhala ndi mwai woona cocitika capadela kwambili kuposa zonse. Cocitika cimeneco ndi kupulumuka cisautso cacikulu. Nkhondo ya Aramagedo ikadzatha, padzikoli padzacitika zozizwitsa zambili. Mulungu adzathandiza anthu kukhalanso ndi thanzi labwino. (Yes. 33:24; 35:5, 6; Chiv. 21:4) Yelekezelani kuti mukuona zimene zidzacitika. Anthu adzayamba kutaya magalasi a maso, ndodo, njinga za olemala, ndi zipangizo zina za olemala. Cifukwa cimodzi cimene Yehova adzacilitsila anthu opulumuka pa Aramagedo n’cakuti adzawapatsa nchito. Iye afuna kuti adzagwile mwamphamvu nchito yokonza dziko lapansi kukhala paladaiso.—Sal. 115:16.

17, 18. (a) Kodi colinga cacikulu cimene Yesu anali kucitila zozizwitsa cinali ciani? (b) N’cifukwa ciani mufunika kuyesetsa kuti mukapezeke m’dziko latsopano?

17 Zozizwitsa zimene Yesu anacita zimalimbikitsa a “khamu lalikulu.” Iwo amasangalala kukhala ndi ciyembekezo cakuti adzacilitsidwa ku matenda onse. (Chiv. 7:9) Zozizwitsa zimenezo zinasonyezanso kuti Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu amakonda kwambili anthu. (Yoh. 10:11; 15:12, 13) Ndipo cifundo cimene Yesu anasonyeza cimaonetsa kuti Yehova amakonda mtumiki wake aliyense payekha.—Yoh. 5:19.

18 Anthu akubuula, kumva zowawa, ndiponso kufa. (Aroma 8:22) Kunena zoona, tifunika dziko latsopano mmene Mulungu adzathetselatu matenda onse monga mmene analonjezela. Lemba la Malaki 4:2 limatitsimikizila kuti anthu amene adzacilitsidwa ‘adzadumphadumpha ngati ana a ng’ombe amphongo onenepa’ cifukwa codziŵa kuti amasulidwa ku ucimo. Conco kuyamikila zimene Mulungu waticitila ndi kukhulupilila kwambili malonjezo ake kuyenela kutilimbikitsa kucita zimene tingathe kuti tiyenelele kudzaloŵa m’dziko latsopano. N’zosangalala kudziŵa kuti zozizwitsa zimene Yesu anacita pamene anali padziko zinali kusonyeza zinthu zabwino zimene Mulungu adzacitila anthu mu ulamulilo wa Mesiya.