“Cipulumutso Canu Cikuyandikila”
“Mudzaimilile cilili ndi kutukula mitu yanu, cifukwa cipulumutso canu cikuyandikila.”—LUKA 21:28.
1. Ndi zinthu zotani zimene zinacitika ku Yerusalemu mu 66 C.E.? (Onani cithunzi pamwambapa.)
YELEKEZELANI kuti ndinu Mkristu, ndipo mukukhala ku Yerusalemu mu 66 C.E. Zinthu zambili zikucitika mumzindawo. Coyamba, bwanamkubwa waciroma Florus akulanda ndalama zokwana matalente 17 zocokela m’thumba la kacisi wopatulika. Pasanapite nthawi yaitali, Ayuda akuukila Aroma ndi kupha asilikali aciroma mu Yerusalemu ndipo ayamba kudzilamulila. Koma Aroma akucitapo kanthu mwamsanga. Patangopita miyezi itatu, asilikali 30,000 aciroma akubwela mumzindawo motsogoleledwa ndi bwanamkubwa waciroma wa ku Siriya, dzina lake Seshasi Galasi. Mwamsanga io akuloŵa mu Yerusalemu ndipo Ayuda opandukawo akuthaŵila m’kacisi. Kenako asilikali a Aroma akuyamba kugwetsa linga la kacisiyo. Anthu ambili mumzindawo akucita mantha kwambili. Kodi mukanamva bwanji poona zonsezi?
2. Kodi Akristu anafunika kucita ciani mu 66 C.E? Nanga anakwanitsa bwanji kucita zimenezo?
2 Mosakaikila Akristu anakumbukila mau a Yesu amene analembedwa ndi Luka. Yesu anati: “Mukadzaona magulu ankhondo atazungulila Luka 21:20) Koma mwina io anali kudzifunsa kuti, ‘Tidzatsatila bwanji cenjezo la Yesu limeneli?’ Yesu anakambanso kuti: “Pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthaŵila kumapili, ndipo amene ali mkati mwa mzindawo adzatulukemo. Amene ali m’madela akumidzi asadzaloŵe mumzindawo.” (Luka 21:21) Kodi io akanatuluka bwanji mu Yerusalemu popeza asilikali ambilimbili anali atazungulila mzindawo? Kenako panacitika zinthu zosayembekezeka. Akristuwo anaona asilikali aciroma akucoka ku Yerusalemu. Monga mmene Yesu anakambila, kuukila kwao ‘kunafupikitsidwa.’ (Mat. 24:22) Tsopano io anali ndi mwai womvela malangizo a Yesu. Mwamsanga Akristu onse okhulupilika a mumzindawo ndi a m’madela ozungulila anathaŵila ku mapili a ku mtsinje wa Yorodano. * Ndiyeno mu 70 C.E., gulu lina la asilikali aciroma linapita ku Yerusalemu ndi kuononga mzindawo. Koma Akristu okhulupilika anapulumuka cifukwa cakuti anamvela malangizo a Yesu.
Yerusalemu, mudzadziŵe kuti cionongeko cake cayandikila.” (3. Ndi zocitika ziti zimene Akristu adzakumana nazo posacedwapa? Nanga tikambilana ciani m’nkhani ino?
3 Posacedwapa aliyense wa ife adzakumana ndi zinthu zofanana ndi zimenezi. Yesu anacenjeza Akristu za kuonongedwa kwa Yerusalemu ndipo anasonyeza kuti zocitika za m’nthawi ya atumwi zidzafanana ndi za pa “cisautso cacikulu.” (Mat. 24:3, 21, 29) Ndipo cosangalatsa n’cakuti “khamu lalikulu” la anthu lidzapulumuka cisautso ca padziko lonse cimeneco. (Ŵelengani Chivumbulutso 7:9, 13, 14.) Kodi Baibulo limafotokoza kuti cidzacitika n’ciani panthawiyo? Tifunika kudziŵa zimene zidzacitika cifukwa zidzatithandiza kuti tidzapulumuke. Tiyeni tsopano tikambilane mmene zocitika zamtsogolo zimenezo zidzakhudzila aliyense wa ife.
KUYAMBA KWA CISAUTSO CACIKULU
4. Kodi cisautso cacikulu cidzayamba bwanji? Nanga zimenezi zidzacitika bwanji?
4 Kodi cisautso cacikulu cidzayamba bwanji? Buku la Chivumbulutso limayankha funso limeneli mwa kufotokoza za kuonongedwa kwa “Babulo Wamkulu.” (Chiv. 17:5-7) Baibulo limayelekezela zipembedzo zonse zonyenga ndi hule, ndipo izi n’zoyenela cifukwa atsogoleli a machalichi amacita cigololo cauzimu ndi atsogoleli a maiko a m’dziko loipali. M’malo mocilikiza mokhulupilika Yesu ndi Ufumu wake, io amacilikiza maulamulilo a anthu ndiponso amaphwanya mfundo za m’Baibulo kuti akhale ndi mphamvu pandale. Zocita zao n’zosiyana kwambili ndi za odzozedwa a Mulungu amene ndi oyela ngati namwali. (2 Akor. 11:2; Yak. 1:27; Chiv. 14:4) Nanga ndani amene adzaononga zipembedzo zimenezi zomwe zili ngati hule? Yehova Mulungu adzaika “maganizo ake” m’mitima ya “nyanga 10” za ‘cilombo cofiila kwambili.’ Nyanga zimenezi zikuimila maulamulilo onse andale amene amathandiza bungwe la United Nations limene likuimilidwa ndi “cilombo cofiila kwambili.”—Ŵelengani Chivumbulutso 17:3, 16-18.
5, 6. Cifukwa n’ciani timanena kuti si anthu onse a m’zipembedzo amene adzaphedwa pamene Babulo Wamkulu adzaonongedwa?
5 Koma kodi anthu onse amene ali m’zipembedzo za Babulo Wamkulu adzaphedwa pamene zipembedzo zimenezi zidzaonongedwa? Iyai. Mouzilidwa, mneneli Zekariya analemba zimene zidzacitika panthawiyo. Pofotokoza za munthu amene poyamba anali m’cipembedzo conyenga, Zekariya analemba kuti: “Mneneli aliyense azidzanena kuti, ‘Ine si mneneli. Ndine mlimi, cifukwa munthu wina anandigula kuti ndikhale kapolo wake kuyambila ndili mnyamata.’ Akadzafunsidwa kuti, ‘Kodi zilonda zimene zili pathupi pakozi watani?’ Iye azidzayankha kuti, ‘Zilonda zimenezi zinabwela cifukwa comenyedwa Zek. 13:4-6) Conco, zikuoneka kuti ngakhale atsogoleli ena a zipembedzo adzacoka m’zipembedzo zao ndi kuyamba kukana kuti anali m’zipembedzo zimenezo.
m’nyumba ya anthu amene anali kundikonda kwambili.’” (6 Nanga n’ciani cidzacitikila anthu a Mulungu panthawiyo? Yesu anati: “Kunena zoona, masikuwo akanapanda kufupikitsidwa, palibe amene akanapulumuka. Koma cifukwa ca osankhidwawo, masikuwo adzafupikitsidwa.” (Mat. 24:22) Monga mmene taonela, mu 66 C.E. cisautso ca ku Yerusalemu ‘cinafupikitsidwa.’ Zimenezi zinathandiza kuti “osankhidwawo,” kapena kuti Akristu odzozedwa, athaŵe mumzindawo ndi m’madela ozungulila mzindawo. Mofananamo, mbali yoyamba ya cisautso cacikulu idzafupikitsidwa cifukwa ca “osankhidwawo.” Maulamulilo andale amene akuimilidwa ndi “nyanga 10” sadzaloledwa kuononga anthu a Mulungu. M’malo mwake kuukila kwao kudzaimitsidwa kwakanthawi.
NTHAWI YA CIYESO NDI CIWELUZO
7, 8. Ndi mwai wotani umene tidzakhala nao pambuyo pa kuonongedwa kwa zipembedzo zonyenga? Nanga anthu okhulupilika a Mulungu adzaonetsa bwanji kuti ndi osiyana ndi anthu ena?
7 N’ciani cidzacitika pambuyo pakuonongedwa kwa zipembedzo zonyenga? Imeneyo idzakhala nthawi yoonetsa zimene zili mumtima mwathu. Anthu ambili adzafunafuna citetezo ku mabungwe a anthu amene ali ngati ‘matanthwe a m’mapili.’ (Chiv. 6:15-17) Komabe, anthu a Mulungu adzathaŵila ku malo acitetezo ophiphilitsa amene Yehova adzapeleka. M’nthawi ya atumwi, pamene Aroma anacoka ku Yerusalemu, sikuti inali nthawi yakuti Ayuda ambili atembenukile ku Cikristu. Koma inali nthawi yakuti anthu amene anali kale Akristu amvele cenjezo la Yesu ndi kuthaŵa mu Yerusalemu. Mofananamo, sitingayembekezele kuti anthu ambili adzabwela m’gulu la Yehova panthawi yocepa yabata imeneyo mkati mwa cisautso cacikulu. Koma panthawiyo Akristu onse oona adzakhala ndi mwai woonetsa kuti amakondadi Yehova ndi kucilikiza abale a Kristu.—Mat. 25:34-40.
8 Ngakhale kuti sitidziŵa zonse zimene zidzacitika pa nthawi yaciyeso imeneyo, n’zoonekelatu kuti tidzafunika kukhala ndi mtima wodzimana kwambili. M’nthawi ya atumwi, Akristu anafunika kusiya katundu wao ndi kupilila mavuto ambili kuti apulumuke. (Maliko 13:15-18) Kodi ifeyo tidzalolela kusiya kapena kulandidwa zinthu zina kuti tidzakhalebe okhulupilika kwa Mulungu? Kodi tidzakhala okonzeka kucita ciliconse cotheka kuti tidzasonyeze kukhulupilika kwathu kwa Yehova? Ndipo dziŵani kuti panthawiyo ndife cabe amene tidzakhala tikutsatila citsanzo ca mneneli Danieli mwa kupitilizabe kulambila Mulungu zivute zitani.—Dan. 6:10, 11.
9, 10. (a) Panthawi yocepa ya bata, kodi anthu a Mulungu adzalengeza uthenga wotani? (b) Kodi adani athu adzamva bwanji?
9 Imeneyo siidzakhala nthawi yolengeza ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ Nthawi yolengeza uthenga umenewu idzakhala itatha, ndipo nthawi ya “mapeto” idzakhala itafika. (Mat. 24:14) Mosakaikila, panthawiyo anthu a Mulungu azidzalengeza uthenga woŵaŵa waciweluzo. Uthenga umenewo uyenela kuti udzaphatikizapo uthenga wakuti dziko la Satana lili pafupi kuonongedwa. Baibulo limayelekezela uthengawo ndi matalala pamene limati: “Matalala aakulu, lililonse lolemela pafupifupi makilogalamu 20, anagwela anthu kucokela kumwamba. Anthuwo ananyoza Mulungu cifukwa ca mlili wa matalalawo, pakuti mliliwo unali waukulu modabwitsa.”—Chiv. 16:21.
10 Koma adani athu adzakhumudwa kwambili ndi uthengawo. Mneneli Ezekieli anauzilidwa kufotokoza zimene Gogi wa Magogi adzacita, amene akuimila mgwilizano wa mitundu. Iye analemba kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa tsikulo maganizo adzakubwelela mumtima mwako ndipo udzaganiza zocita ciwembu coipa kwambili. Ezek. 38:10-12) Kunena mophiphilitsa, anthu a Mulungu adzakhala “pakatikati pa dziko lapansi,” kutanthauza kuti adzadziŵika kuti ndi apadela. Anthu a mitundu adzakhumudwa kwambili ndi zimenezi, ndipo adzalakalaka kuononga odzozedwa a Yehova ndi a nkhosa zina.
Udzanena kuti: “Ndipita kukaukila dziko lokhala ndi midzi yopanda mipanda. Ndipita kukaukila anthu amene akukhala mwabata, popanda cowasokoneza. Ndikaukila anthu onsewo amene akukhala m’midzi yopanda mipanda ndipo alibe zotsekela ndiponso zitseko.” Udzapita kumeneko kuti ukalande ndi kutengako zinthu zambili, ndiponso kuti ukaukile dziko loonongedwa limene tsopano mukukhala anthu. Udzapita kukaukila anthu amene anasonkhanitsidwa pamodzi kucokela ku mitundu ina, amene akusonkhanitsa cuma ndi katundu, komanso amene akukhala pakatikati pa dziko lapansi.’” (11. (a) Kodi tiyenela kukumbukila ciani cokhudza mmene zinthu zidzacitikila pa cisautso cacikulu? (b) Kodi anthu adzacita ciani cifukwa ca zizindikilo zimene zidzakhala kumwamba?
11 Pamene tikukambilana zimene zidzacitika pambuyo pake, tiyenela kukumbukila kuti Mau a Mulungu safotokoza ndondomeko ya mmene zinthu zidzacitikila. Mwacionekele, zocitika zina zidzayamba pamene zina zikali kucitika. Pofotokoza ulosi wokhudza mapeto a nthawi ino ya zinthu, Yesu anati: “Padzakhala zizindikilo padzuŵa, mwezi ndi nyenyezi. Padziko lapansi anthu a mitundu ina adzazunzika, ndipo adzathedwa nzelu cifukwa ca mkokomo wa nyanja ndi kuwinduka kwake. Mwakuti anthu adzakomoka cifukwa ca mantha ndi kuyembekezela zimene zicitikile dziko lapansi kumene kuli anthu, pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. Kenako adzaona Mwana wa munthu akubwela mumtambo ndi mphamvu ndi ulemelelo waukulu.” (Luka 21:25-27; ŵelengani Maliko 13:24-26.) Kodi zizindikilo zodabwitsa zimenezi tidzaziona ndi maso pamene ulosi umenewu udzakwanilitsidwa? Tiyeni tiyembekezele ndipo tidzaona mmene zidzakhalila. Komabe, mulimonse mmene zidzakhalile, adani a Mulungu adzacita mantha kwambili cifukwa ca zizindikilozo.
12, 13. (a) N’ciani cidzacitika pamene Yesu adzabwela “ndi mphamvu ndi ulemelelo waukulu”? (b) Kodi atumiki a Mulungu adzacita ciani panthawiyo?
12 N’ciani cidzacitika pamene Yesu adzabwela “ndi mphamvu ndi ulemelelo waukulu”? Imeneyo idzakhala nthawi yopeleka mphoto kwa anthu okhulupilika ndi yopeleka cilango kwa osakhulupilika. (Mat. 24:46, 47, 50, 51; 25:19, 28-30) M’buku la Mateyu, Yesu anatsiliza kukamba cizindikilo ca mapeto a nthawi ino mwa kufotokoza fanizo la nkhosa ndi mbuzi. Iye anati: “Mwana wa munthu akadzafika mu ulemelelo wake, limodzi ndi angelo ake, adzakhala pampando wake wacifumu waulemelelo. Mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kwa iye ndipo adzalekanitsa anthu, mmene m’busa amalekanitsila nkhosa ndi mbuzi. Adzaika nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi adzaziika kumanzele kwake.” (Mat. 25:31-33) Kodi nkhosa ndi mbuzi zidzapatsidwa ciweluzo cotani? Fanizolo limatha ndi mau akuti: “Iwowa [amene ali ngati mbuzi] adzacoka kupita ku cionongeko cothelatu, koma olungama ku moyo wosatha.”—Mat. 25:46.
13 Kodi anthu okhala ngati mbuzi adzamva bwanji pamene adzadziŵa kuti atsala pang’ono ‘kuonongedwa kothelatu’? “Adzadziguguda pacifuwa cifukwa ca cisoni.” (Mat. 24:30) Nanga abale a Kristu ndi a nkhosa zina adzacita ciani? Cifukwa cokhulupilila kwambili Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, io adzamvela lamulo la Yesu lakuti: “Zinthu izi zikadzayamba kucitika, mudzaimilile cilili ndi kutukula mitu yanu, cifukwa cipulumutso canu cikuyandikila.” (Luka 21:28) Ndithudi, panthawiyo sitidzacita mantha, koma tidzakhala ndi cikhulupililo cakuti tipulumuka.
ADZAWALA KWAMBILI MU UFUMU
14, 15. Ndi nchito yosonkhanitsa iti imene idzayamba Gogi wa Magogi akadzayamba kuukila anthu a Mulungu? Nanga n’ciani cidzacitika pa nthawi yosonkhanitsa imeneyi?
14 Kodi cidzacitika n’ciani Gogi wa Magogi akadzayamba kuukila anthu a Mulungu? Mabuku a Mateyo ndi Maliko amanena kuti: “[Mwana wa munthu] adzatumiza angelo ndipo adzasonkhanitsa pamodzi osankhidwa ake kucokela kumphepo zinai, kucokela kumalekezelo ake a dziko lapansi kukafika kumalekezelo a m’mlengalenga.” (Maliko 13:27; Mat. 24:31) Kusonkhanitsa kumeneku sikukutanthauza kusonkhanitsa koyamba kwa Akristu odzozedwa kapena kuwadinda cidindo comaliza. (Mat. 13:37, 38) Iwo adzadindidwa cidindo comaliza cisautso cacikulu cisanayambe. (Chiv. 7:1-4) Nanga Yesu anali kukamba za kusonkhanitsa kuti? Kusonkhanitsa kumeneku kudzacitika panthawi imene otsalila a 144,000 adzalandila mphoto yao yakumwamba. (1 Ates. 4:15-17; Chiv. 14:1) Zimenezi zidzacitika panthawi inayake Gogi wa Magogi atayamba kale kuukila anthu a Mulungu. (Ezek. 38:11) Apa m’pamene mau a Yesu adzakwanilitsidwa, akuti: “Pa nthawi imeneyo olungama adzawala kwambili ngati dzuŵa mu ufumu wa Atate wao.”—Mat. 13:43. *
15 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti odzozedwa ‘adzakwatulidwa’ kupita kumwamba ndi thupi la nyama? Anthu ambili a m’Machalichi Acikristu amakhulupilila kuti, Akristu adzatengedwa ndi matupi ao. Ndiponso amaganiza kuti Yesu adzabwela ndipo adzamuona ndi maso ao akulamulila. Koma Baibulo limanena momveka bwino kuti “cizindikilo ca Mwana wa munthu” cidzaonekela kumwamba ndipo Yesu adzabwela “pamitambo ya kumwamba.” (Mat. 24:30) Mau amenewa akusonyeza kuti kubwela kwake kudzakhala kosaonekela ndi maso. Kuonjezela apo, “mnofu ndi magazi sizingaloŵe ufumu wa Mulungu.” Motelo odzozedwa akalibe kutengedwa kupita kumwamba, coyamba ‘adzasandulika, m’kamphindi, m’kuphethila kwa diso, pa kulila kwa lipenga lomaliza.’ * (Ŵelengani 1 Akorinto 15:50-53.) Conco, sitimanena kuti Akristu odzozedwa ‘adzakwatulidwa’ cifukwa cakuti anthu amalimva molakwika liuli. Koma adzatengedwa m’kanthawi kocepa.
16, 17. N’ciani cidzacitika ukwati wa Mwanawankhosa ukalibe kucitika kumwamba?
16 Odzozedwa onse akadzapita kumwamba, adzakonzekela komaliza ukwati wa Mwanawankhosa. (Chiv. 19:9) Koma nthawi ya ukwati isanakwane, pali cinacake cimene cidzacitika. Kumbukilani kuti odzozedwa atatsala pang’ono kupita kumwamba, Gogi adzaukila anthu a Mulungu. (Ezek. 38:16) Kodi n’ciani cidzacitika Gogi akadzaukila anthu a Mulungu? Padziko lapansi, anthu a Mulungu adzaoneka ngati alibe citetezo ciliconse. Iwo adzamvela malangizo amene anapelekedwa m’nthawi ya Mfumu Yehosafati, akuti: “Ulendo uno simufunikila kumenya nkhondo. Khalani m’malo anu, imani cilili ndi kuona Yehova akukupulumutsani. Inu Ayuda ndi anthu a ku Yerusalemu, musaope kapena kucita mantha.” (2 Mbiri 20:17) Koma kumwamba kudzacitika zinthu zosiyanako. Ponena za nthawi imene odzozedwa onse adzakhala kumwamba, lemba la Chivumbulutso 17:14 limanena zimene zidzacitikila adani a anthu a Mulungu. Lembali limati: “Iwowa adzamenyana ndi Mwanawankhosa, koma pakuti iye ndiye Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, Mwanawankhosayo adzawagonjetsa. Komanso oitanidwa aja, amene ali osankhidwa mwapadela ndi okhulupilika, naonso adzagonjetsa naye limodzi.” Yesu pamodzi ndi olamulila anzake okwana 144,000 adzabwela kudzalanditsa anthu a Mulungu pano padziko lapansi.
17 Zimenezo zidzacititsa kuti pakhale nkhondo ya Aramagedo imene idzapangitsa kuti dzina loyela la Yehova lilemekezeke. (Chiv. 16:16) Panthawiyo, anthu onse amene ali ngati mbuzi “adzacoka kupita ku ciwonongeko cothelatu.” Zoipa zonse zidzatha padziko lapansi, ndipo a khamu lalikulu adzapulumuka mbali yomaliza ya cisautso cacikulu. Kukonzekela kukadzatha, ukwati wa Mwanawankhosa udzayamba. Ukwati umenewu ndi cocitika cosangalatsa kwambili cochulidwa m’buku la Chivumbulutso. (Chiv. 21:1-4) * Anthu onse amene adzapulumuka padziko lapansi adzasangalala ndi zinthu zambili zabwino zimene Mulungu adzapeleka cifukwa ca cikondi cake. Lidzakhaladi phwando losaiŵalika la ukwati. Kodi sitikuyembekezela mwacidwi nthawi yosangalatsa imeneyo?—Ŵelengani 2 Petulo 3:13.
18. Popeza tikuyembekezela zinthu zosangalatsa, n’ciani cimene aliyense wa ife ayenela kucita?
18 Popeza kuti tikuyembekezela zinthu zosangalatsa zimenezi, kodi aliyense wa ife ayenela kucita ciani? Mtumwi Petulo anauzilidwa kulemba kuti: “Conco popeza zinthu zonsezi zidzasungunuka, ganizilani za mtundu wa munthu amene muyenela kukhala. Muyenela kukhala anthu akhalidwe loyela ndipo muzicita nchito zosonyeza kuti ndinu odzipeleka kwa Mulungu. Muzicita zimenezi poyembekezela ndi kukumbukila nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova. . . Cotelo okondedwa, pakuti mukuyembekezela zinthu zimenezi, citani ciliconse cotheka kuti iye adzakupezeni opanda banga, opanda cilema ndiponso muli mu mtendele.” (2 Pet. 3:11, 12, 14) Inde, tiyeni tiyesetse kukhala oyela ndi kupitilizabe kucilikiza Mfumu Yamtendele.
^ par. 2 Onani Nsanja ya Olonda ya April 15, 2012, tsamba 25 mpaka 26.
^ par. 14 Onani Nsanja ya Mlonda July 1, 2013, tsamba 13 ndi 14.
^ par. 15 Matupi a nyama a odzozedwa amene adzakhala ndi moyo panthawiyo sadzatengedwa kupita kumwamba. (1 Akor. 15:48, 49) Yesu sanapite kumwamba ndi thupi la nyama, naonso odzozedwa sadzapita kumwamba ndi matupi ao a nyama.
^ par. 17 Lemba la Salimo 45 limasonyezanso mmene zinthu zidzacitikila. Coyamba Mfumu idzamenya nkhondo, kenako ukwati udzacitika.