Awa Ndi Malo Athu Olambilila
“Kudzipeleka kwambili panyumba yanu kudzandidya.”—YOH. 2:17.
1, 2. (a) Ndi malo olambilila ati amene atumiki a Yehova anali kugwilitsila nchito kale? (b) Kodi Yesu anali kumuona bwanji kacisi wa Mulungu ku Yerusalemu? (c) Kodi colinga ca nkhani ino n’ciani?
KUYAMBILA kale, atumiki a Mulungu akhala akugwilitsila nchito malo apadela polambila Yehova. Abele ayenela kuti anagwilitsila nchito guwa la nsembe popeleka nsembe kwa Mulungu. (Gen. 4:3, 4) Nowa, Abulahamu, Isaki, Yakobo ndi Mose, onse anamanga maguwa a nsembe. (Gen. 8:20; 12:7; 26:25; 35:1; Eks. 17:15) Molamulidwa ndi Yehova, Aisiraeli anamanga cihema. (Eks. 25:8) Pambuyo pake, io anamanga kacisi wolambililamo Yehova. (1 Maf. 8:27, 29) Ayuda atabwelela kwao kucokela kuukapolo ku Babulo, anali kusonkhana nthawi zonse m’masunagoge. (Maliko 6:2; Yoh. 18:20; Mac. 15:21) Komanso Akristu oyambilila anali kusonkhana m’nyumba za abale ndi alongo. (Mac. 12:12; 1 Akor. 16:19) Masiku ano, anthu a Mulungu padziko lonse lapansi amasonkhana m’Nyumba za Ufumu masauzande ambilimbili kuti aphunzile Baibulo ndi kulambila Yehova.
2 Yesu anali kukonda kwambili kacisi wa Yehova ku Yerusalemu. Ndiye cifukwa cake ponena za Yesu, wolemba uthenga wabwino wina anagwilitsila nchito mau aulosi akuti: “Kudzipeleka kwambili panyumba yanu kudzandidya.” (Sal. 69:9; Yoh. 2:17) Lelolino, palibe Nyumba ya Ufumu imene ingachedwe “nyumba ya Yehova” monga mmene analili kacisi wa ku Yerusalemu. (2 Mbiri 5:13; 33:4) Ngakhale n’conco, m’Baibulo muli mfundo zimene zingatithandize kudziŵa mmene tiyenela kuonela malo athu olambilila ndi mmene tiyenela kuwagwilitsila nchito. Colinga ca nkhani ino ndi kukambilana mfundo zimenezi kuti tidziŵe mmene tiyenela kuonela Nyumba za Ufumu, mmene tingacilikizile nchito yomanga nyumba zimenezi mwa kupeleka ndalama, ndi mmene tingazisamalile. *
MUZIONETSA KUTI MUMALEMEKEZA KULAMBILA KOONA
3-5. Kodi nchito ya Nyumba ya Ufumu n’ciani? Nanga zimenezi ziyenela kukhudza bwanji mmene timaonela misonkhano yathu?
3 Nyumba ya Ufumu ndi cimake ca kulambila koona m’dela lililonse. Njila imodzi imene Yehova amatipatsila cakudya ca kuuzimu ndi kudzela m’misonkhano ya mpingo imene timakhala nayo mlungu ndi mlungu ku Nyumba ya Ufumu. Ku misonkhano imeneyi timatsitsimulidwa mwauzimu ndi kulandila malangizo kudzela mu gulu lake. Anthu onse amene amapezeka pa misonkhanoyi amakhala kuti aitanidwa ndi Yehova ndi Mwana wake. Ngakhale kuti timaitanidwa nthawi zonse kuti tidzadye “patebulo la Yehova,” sitiyenela kuona mwai umenewu mopepuka.—1 Akor. 10:21.
4 Yehova amaona kuti misonkhano yathu ndi yofunika kwambili moti anauzila mtumwi Paulo kulemba mau otilimbikitsa kuti tisaleke kusonkhana pamodzi. (Ŵelengani Aheberi 10:24, 25.) Kodi tingasonyeze kuti timalemekeza Yehova ngati timaphonya misonkhano popanda zifukwa zomveka? Tingaonetse kuti timayamikila kwambili Yehova ndi zinthu zimene amatipatsa mwa kukonzekela misonkhano ndi kutengamo mbali mokwanila.—Sal. 22:22.
5 Zocita zathu ziyenela kuonetsa kuti timalemekeza Nyumba ya Ufumu ndi misonkhano imene imacitika pa malowa. Zocita zathu pambali imeneyi zimaonetsa mmene timaonela dzina la Mulungu limene limalembedwa pa cikwangwani ca Nyumba ya Ufumu.—Yelekezani ndi 1 Mafumu 8:17.
6. Kodi anthu ena anakamba ciani ataona Nyumba za Ufumu ndi anthu amene anasonkhana pa nyumbazo? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)
6 Ngati timalemekeza malo athu olambilila, anthu ena amene si Mboni amaona zimenezi. Mwacitsanzo, mwamuna wina ku Turkey anati: “Ndinacita cidwi kwambili cifukwa cakuti pa Nyumba ya Ufumu panali posamalidwa bwino ndi padongosolo. Anthu anavala bwino, anali ndi nkhope zacimwemwe, ndipo anandilandila ndi manja aŵili. Zimenezi zinandisangalatsa kwambili.” Mwamunayo anayamba kusonkhana nthawi zonse, ndipo patapita nthawi yocepa anabatizidwa. Mumzinda wina wa ku Indonesia, abale anaitana akuluakulu a boma ndi anthu ena kuti adzaone Nyumba ya Ufumu yatsopano ikalibe kupelekedwa. Meya wa mumzindawo anabwela. Iye anacita cidwi ataona kukongola kwa nyumbayo ndi maluwa ake ndiponso atamvetsetsa colinga cake. Iye anati: “Mmene nyumbayi ikuonekela zionetsa kuti cipembedzo canu n’coona.”
7, 8. Ndi mfundo zofunika kwambili ziti zimene tiyenela kukumbukila tikakhala pa misonkhano?
7 Khalidwe lathu, kavalidwe kathu, ndi mmene timadzikonzela ziyenela kuonetsa kuti timalemekeza Mulungu amene amatiitana ku misonkhano yacikristu. Tingaonetsenso ulemu mwa kupewa kucita zinthu mopitilila malile. Zioneka kuti ena pamisonkhano yathu amakhwimitsa malamulo pankhani ya kavalidwe, pamene ena amavala motailila kwambili. N’zoona kuti Yehova amafuna kuti atumiki ake ndi alendo azisangalala pamisonkhano. Komabe, anthu amene amapezeka Mlal. 3:1.
pamisonkhano ayenela kupewa kudodometsa ena mwa kuvala motailila, kutuma mameseji, kulankhula, kudya kapena kumwa, ndi kucita zinthu zina pamisonkhano. Makolo ayenela kuphunzitsa ana ao kuti asamaseŵele kapena kuthamangathamanga m’Nyumba ya Ufumu.—8 Yesu anakhumudwa kwambili ndi anthu amene anali kucita malonda m’kacisi wa Mulungu ndipo anawapitikitsa. (Yoh. 2:13-17) Nyumba za Ufumu nazonso ndi malo olambilila Yehova ndi kuphunzilila mau ake. Conco, sipayenela kucitika cina ciliconse cokhudza malonda.—Yelekezani ndi Nehemiya 13:7, 8.
KUMANGA NYUMBA ZA UFUMU NDI KUPELEKA NDALAMA ZOCILIKIZILA NCHITOYI
9, 10. (a) Kodi Nyumba za Ufumu zatsopano zimamangidwa bwanji? Nanga zotsatila zake zakhala zotani? (b) Ndi makonzedwe ati acikondi amene athandiza kuti Nyumba za Ufumu zimangidwe m’madela amene mipingo ilibe ndalama zokwanila zomangila Nyumba za Ufumu?
9 Gulu la Yehova limayesetsa kumanga Nyumba za Ufumu ndi kupeleka ndalama zothandiza pa nchito yomanga nyumbazi. Anthu odzipeleka ndi amene amagwila nchito yopanga mapulani a nyumbazi, kumanga, ndi kukonzanso zimene zaonongeka. Kodi zotsatila zake zakhala zotani? Kuyambila pa November 1, 1999, Nyumba za Ufumu zokongola zoposa pa 28,000 zamangidwa pa dziko lonse. Zimenezi zikuonetsa kuti mu zaka 15 zapitazi Nyumba za Ufumu zatsopano 5 pa avaleji zimamangidwa tsiku lililonse.
10 Gulu la Yehova likuyesetsa kuthandiza pa nchito yomanga Nyumba za Ufumu kulikonse kumene zikufunika. Makonzedwe amenewa ndi ogwilizana ndi mfundo ya m’Malemba yonena kuti zoculuka zimene ena ali nazo zithandizile pa zimene ena akusowa, n’colinga cakuti “pakhale kufanana.” (Ŵelengani 2 Akorinto 8:13-15.) Zimenezi zapangitsa kuti Nyumba za Ufumu zimangidwe ngakhale m’madela amene mipingo ilibe ndalama zokwanila zomangila Nyumba za Ufumu.
11. Kodi abale ndi alongo ena ananena ciani poyamikila Nyumba ya Ufumu yatsopano? Ndipo zimenezi zikukucititsani kumva bwanji?
11 Abale ndi alongo a mumpingo wina m’dziko la Costa Rica anapindula kwambili ndi makonzedwe amenewa. Iwo analemba kuti: “Tikayang’ana Nyumba yathu ya Ufumu, timaona ngati tikulota. N’zovuta kukhulupilila. Nyumba yathu yokongola imeneyi inamangidwa m’masiku 8 cabe. Zimenezi zinatheka cifukwa ca dalitso la Yehova, thandizo la abale, ndiponso cifukwa ca makonzedwe amene gululi linapanga. Malo athu olambilila amenewa ndi mphatso yamtengo wapatali ndiponso cuma capadela cimene Yehova watipatsa. Kunena zoona ndife osangalala kwambili.” Kodi sizikusangalatsani kumva mau oyamikila amene abale ndi alongo amanena cifukwa ca Nyumba za Ufumu zimene zamangidwa ku madela ao? Ndipo abale ndi alongo enanso m’madela ambili padziko lonse akusangalala kwambili cifukwa ca Nyumba za Ufumu Sal. 127:1.
zimenezi. Nchitoyi ndi ya Yehova. Ndiye cifukwa cake kaŵilikaŵili Nyumba ya Ufumu yatsopano ikamalizidwa, anthu ambili oona mtima amene amalakalaka kudziŵa zambili za Mlengi wathu wacikondi amabwela kudzasonkhana.—12. Mungacilikize bwanji nchito yomanga Nyumba za Ufumu?
12 Abale ndi alongo ambili apeza cimwemwe coculuka cifukwa cogwila nao nchito yomanga Nyumba za Ufumu. Kaya tingakwanitse kumanga nao Nyumba za Ufumu kapena ai, tonse tili ndi mwai wothandiza panchitoyi mwa kupeleka zopeleka. Cifukwa cakuti anali ndi cangu pa kulambila koona, anthu a Mulungu m’nthawi zakale anali kupeleka ndalama zokonzela malo olambilila. Ndi mmenenso zilili masiku ano. Kucita zimenezi kumapangitsa kuti Yehova alemekezeke.—Eks. 25:2; 2 Akor. 9:7.
KUYELETSA NYUMBA YA UFUMU
13, 14. Ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zimatilimbikitsa kusamalila Nyumba zathu za Ufumu?
13 Nyumba ya Ufumu yatsopano ikangomangidwa, tiyenela kumaiyeletsa nthawi zonse kuti izipeleka cithunzi cabwino ca Mulungu amene timalambila yemwe ndi wadongosolo. (Ŵelengani 1 Akorinto 14:33, 40.) Baibulo limasonyeza kuti ciyelo ndiponso kukhala oyela mwa kuuzimu zimagwilizana ndi kukhala waukhondo. (Chiv. 19:8) Motelo, anthu amene amafuna kukhala ovomelezeka kwa Yehova ayenela kukhala aukhondo.
14 Tikamasamalila Nyumba yathu ya Ufumu, timakhala omasuka kuitanila anthu acidwi kumisonkhano yathu podziŵa kuti Nyumbayo ndi yooneka bwino mogwilizana ndi uthenga umene timalalikila. Iwo adzaona kuti Mulungu amene timalambila ndi woyela ndi kuti posacedwapa adzasintha dzikoli Yes. 6:1-3; Chiv. 11:18.
kukhala paladaiso wokongola.—15, 16. (a) N’cifukwa ciani ena amanyalanyaza kuyeletsa pa Nyumba ya Ufumu? Koma n’cifukwa ciani kuyeletsa n’kofunika kwambili? (b) Kodi pampingo pali makonzedwe otani okhudza kuyeletsa pa Nyumba ya Ufumu? Nanga aliyense wa ife ali ndi udindo wotani?
15 Anthu ena amaona nchito yoyeletsa kukhala yofunika kwambili kuposa mmene ena amaionela. Ena amaona kuti kuyeletsa Nyumba ya Ufumu si kofunika cifukwa ca mmene analeledwela. Ndipo ena amaona kuti m’pofunika kuiyeletsa kokha ngati kumaloko kulibe miseu yabwino ndiponso kumacita matika kapena fumbi. Komanso ena amanyalanyaza nchitoyi cifukwa cakuti kumaloko kulibe madzi okwanila kapena zipangizo zogwilitsila nchito. Mulimonse mmene zinthu zilili, tiyenela kuonetsetsa kuti Nyumba yathu ya Ufumu ndi yosamalidwa bwino cifukwa cakuti imadziŵika ndi dzina la Yehova ndiponso ndi malo a kulambila koona.—Deut. 23:14.
16 Sitiyenela kunyalanyaza nchito yoyeletsa pa Nyumba ya Ufumu. Bungwe la akulu lililonse liyenela kuonetsetsa kuti pampingo pali ndandanda ya kuyeletsa pa Nyumba ya Ufumu ndi zipangizo zokwanila zogwilitsila nchito. Popeza kuti nchito zina zoyeletsa zimafunika kucitika nthawi zonse pambuyo pa misonkhano, koma zina zimacitika pakapita nthawi, nchito yoyeletsa ifunika kuyang’anilidwa bwino n’colinga cakuti nchito zina zisamanyalanyazidwe. Aliyense mumpingo ali ndi udindo wogwila nao nchito zimenezi.
KUKONZA ZOONONGEKA PA MALO ATHU OLAMBILILA
17, 18. (a) Ndi zitsanzo ziti za m’Baibulo za anthu amene anakonza zinthu zoonongeka pa malo olambilila? (b) N’cifukwa ciani tifunika kusamalila Nyumba ya Ufumu nthawi zonse?
17 Atumiki a Yehova amayesetsa kukonza zinthu zoonongeka pa malo olambilila. Mfumu Yehoasi ya Yuda analamula ansembe kuti atenge ndalama zimene anthu anapeleka kunyumba ya Yehova ndi ‘kukonzela ming’alu ya nyumbayo paliponse pamene panali mng’alu.’ (2 Maf. 12:4, 5) Patapita zaka zoposa 200, Mfumu Yosiya nayenso anagwilitsila nchito zopeleka za pa kacisi pokonza zinthu zina zoonongeka.—Ŵelengani 2 Mbiri 34:9-11.
18 Malipoti ocokela ku maofesi ena a nthambi amaonetsa kuti m’maiko ena, anthu sakonza zinthu zoonongeka pa Nyumba za Ufumu. Mwina anthu ambili m’madela amenewo alibe luso logwilila nchitoyo kapena alibe zipangizo zogwilitsila nchito. Koma kunena zoona, ngati Nyumba ya Ufumu siisamalidwa bwino ingaonongeke mwamsanga ndipo zimenezi zingapeleke cithunzi coipa kwa anthu a m’delalo. Koma abale ndi alongo mumpingo akamacita zilizonse zotheka kuti Nyumba ya Ufumu izioneka bwino, Yehova amatamandidwa ndiponso zimathandiza kuti ndalama zimene abale amapeleka zisaonongeke.
19. Kodi inuyo mwatsimikiza mtima kucita ciani cokhudza malo athu olambilila?
19 Nyumba ya Ufumu ndi nyumba yopelekedwa kwa Yehova. Conco, nyumbayi si ya munthu kapena ya mpingo mosasamala kanthu za dzina limene lili pa mapepala a kuboma. Tiyenela kutsatila mfundo za m’Baibulo mwa kugwila nchito yosamalila Nyumba ya Ufumu kuti izioneka bwino monga malo olambilila. Aliyense mumpingo angathandize pa mbali imeneyi mwa kulemekeza malo athu olambilila, kupeleka ndalama zothandizila kumanga Nyumba za Ufumu zatsopano, ndi kugwila nao nchito yosamalila Nyumba ya Ufumu. Mwa kucita zimenezi, timaonetsa kuti ndife odzipeleka pa nyumba ya Yehova monga mmene Yesu anacitila.—Yoh. 2:17.
^ par. 2 Ngakhale kuti nkhani ino ikukamba makamaka za Nyumba za Ufumu, mfundo zake zimagwilanso nchito pa Malo a Misonkhano, ndi malo ena olambilila.