Kutumikila Yehova ‘m’Masiku Oipa’
“MATENDA amandilepheletsa kucita zambili mu utumiki,” anatelo modandaula Ernst wa zaka za m’ma 70. * Kodi nanunso mumamva conco? Ngati ndinu wokalamba ndipo mumadwaladwala komanso mphamvu zanu zikucepelacepela, mungakumbukile mau a pa Mlaliki caputala 12. Mu vesi 1, masiku a ukalamba amachedwa “masiku oipa.” Ngakhale n’conco, mungathe kukhala ndi umoyo wacimwemwe ndi kumatumikila Yehova mosangalala.
PITILIZANI KULIMBITSA CIKHULUPILILO CANU
Inu abale ndi alongo athu okalamba, dziŵani kuti enanso akhala akukumana ndi mavuto ngati anu. Kale atumiki a Yehova okalamba naonso anakumana ndi mavuto ofanana ndi amenewa. Mwacitsanzo, lsaki, Yakobo, ndi Ahiya atakalamba, anafa maso. (Gen. 27:1; 48:10; 1 Maf. 14:4) Sara anaganiza kuti anali ‘wothelatu’ cifukwa ca ukalamba. (Gen. 18:11, 12) Mfumu Davide atakalamba “sankamva kutentha.” (1 Maf. 1:1) Barizilai anali munthu wacuma. Koma atakalamba sanali kumva kukoma kwa cakudya ndi mau a nyimbo. (2 Sam. 19:32-35) Abulahamu anataikilidwa mkazi wake ndipo Naomi anafedwa mwamuna wake.—Gen. 23:1, 2; Rute 1:3, 12.
N’ciani cinawathandiza kukhalabe okhulupilika kwa Yehova ndi kupitiliza kukhala acimwemwe? Abulahamu atakalamba, anapitilizabe kukhulupilila lonjezo la Mulungu ndipo “cikhulupililo cakeco cinamulimbitsa.” (Aroma 4:19, 20) Ifenso tifunika cikhulupililo colimba. Cikhulupililo cotelo, sicidalila pa msinkhu wathu, mphamvu zathu, kapena mmene zinthu zilili pa umoyo wathu. Mwacitsanzo, Yakobo anaonetsa cikhulupililo colimba m’malonjezo a Mulungu, ngakhale pamene anali wofooka, wosaona, ndiponso wodwala kwambili. (Gen. 48:1-4, 10; Aheb. 11:21) Mlongo wina wa zaka 93 dzina lake Ines, amene akudwala matenda amene amafooketsa minofu, anati: “Tsiku lililonse ndimaona kuti Yehova akundidalitsa. Tsiku lililonse ndimaganizila za Paladaiso. Zimenezo zimandithandiza kukhala ndi ciyembekezo.” Amenewa ndi maganizo abwino amene tiyenela kukhala nao.
Timalimbitsa cikhulupililo cathu mwa kupemphela, kuphunzila Mau a Mulungu, ndi kupezeka pa misonkhano. Mneneli wokalamba Danieli anali kupemphela katatu tsiku lililonse ndi kuphunzila Mau a Mulungu. (Dan. 6:10; 9:2) Mkazi wacikulile wamasiye Anna “sanali kusoŵa pakacisi.” (Luka 2:36, 37) Mukamapezeka pa misonkhano ndi kutengamo mbali mmene mungathele, mumadzilimbitsa ndiponso mumalimbikitsa ena. Dziŵani kuti Yehova amasangalala ndi mapemphelo anu ngakhale kuti simungacite zambili mu utumiki wake.—Miy. 15:8.
Ambili a inu mungakonde kuyambanso kuona bwino kuti muziŵelenga ndi kukhalanso ndi mphamvu kuti muzipezeka pa misonkhano, koma mukuona kuti n’zovuta kapena n’zosatheka. N’ciani cingakuthandizeni? Gwilitsilani nchito bwino zimene muli nazo. Ambili amene sakwanitsa kufika pamisonkhano amasangalala kumvetsela misonkhano pa foni. Mlongo wina wa zaka 79 dzina lake Inge, amene ali ndi vuto la maso, amakonzekela misonkhano pogwilitsila nchito mapepala a zilembo zazikulu amene m’bale wa mumpingo wao amamusindikizila.
Mwina inu mumakhala ndi nthawi kusiyana ndi ena. Mungagwilitsile nchito nthawi yanu kumvetsela Baibulo pa CD, mabuku ofotokoza Baibulo, nkhani za onse, ndiponso masewelo. Komanso mungatumile foni okhulupilila anzanu kuti mugaŵane nao mphatso yauzimu ndi ‘kulimbikitsana.’—Aroma 1:11, 12.
PITILIZANI KUKHALA ACANGU MU UTUMIKI WA MULUNGU
Mlongo wina wa zaka za m’ma 80, dzina lake Christa anadandaula kuti: “Cimaŵaŵa kwambili ukamalephela kucita zambili mu utumiki monga mmene unali kucitila kale.” Nanga n’ciani cingathandize okalamba kukhalabe acimwemwe? M’bale Peter, amene ali ndi zaka 75 anati: “Muziona zinthu moyenela. Musamangoganizila zinthu zimene
simungakwanitse kucita koma muzisangalala ndi zimene mumakwanitsa.”Ganizilani njila zosiyanasiyana zolalikilila zimene mungakwanitse kucita. Mlongo Heidi wa zaka za m’ma 80, sakwanitsa kulalikila kunyumba ndi nyumba monga mmene anali kucitila kale. Koma anaphunzila kugwilitsila nchito kompyuta kuti azilemba makalata. Ofalitsa ena okalamba amalalikila atakhala m’mbali mwa mseu kapena pa sitesheni ya basi. Ngati mumakhala ku malo osungila okalamba, bwanji osapanga malowo kukhala “gawo” lanu mwa kulalikila kwa ogwila nchito ku malowo ndi anthu ena okhala kumeneko?
Ngakhale pamene Mfumu Davide anali wokalamba, anayesetsa kulimbikitsa kulambila koona. Iye anapeleka ndalama zomangila kacisi ndi kulimbikitsa anthu kuti acilikize nchitoyo. (1 Mbiri 28:11–29:5) Mofananamo, mungacite zilizonse zimene mungakwanitse kuti muthandize pa nchito imene ikucitika m’gulu la Yehova padziko lonse. Mwacitsanzo, mungalimbikitse apainiya ndi ofalitsa ena acangu mumpingo wanu mwa kuwauza mau olimbikitsa, kuwapatsa mphatso ina iliyonse, kapena kuwaitanila ku cakudya. M’mapemphelo anu, mungaphatikizemo acinyamata, mabanja, atumiki a nthawi zonse, odwala, ndi aja amene ali ndi maudindo akuluakulu.
Yehova amakukondani ndiponso amakuonani kuti ndinu amtengo wapatali. Atate wathu wakumwamba sadzakutayani nonsenu abale ndi alongo athu okalamba. (Sal. 71:9) Posacedwapa, tonse tidzayamba kukula koma osakumana ndi mavuto alionse a ukalamba kapena kuti masiku oipa. M’malomwake, tidzapitiliza kutumikila Yehova Mulungu wathu kwamuyaya tili ndi mphamvu ndiponso thanzi langwilo.
^ par. 2 Maina ena asinthidwa.