Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhalango ya Biriya ya ku Galileya (pansipa)

KODI MUDZIŴA?

KODI MUDZIŴA?

Kodi ku Isiraeli wakale kunali nkhalango monga mmene Baibulo limanenela?

BAIBULO limafotokoza kuti madela ena a Dziko Lolonjezedwa anali ndi nkhalango zoŵilila. (1 Maf. 10:27; Yos. 17:15, 18) Anthu ena akamaona malo aakulu amene alibe mitengo masiku ano, amakaikila ngati kunalidi nkhalango.

Zipatso za mtengo wamkuyu

Buku lina limati: “Kale ku Isiraeli kunali nkhalango zikuluzikulu kusiyana ndi masiku ano.” (Life in Biblical Israel) Nkhalango zimenezi zinali ndi mitengo ikuluikulu ya paini, oki ndi telebeti. Mitengo ya mkuyu inali kupezekanso m’cigawo ca Sefela, malo amene anali pakati pa mapili ndi nyanja ya Mediterranean.

Buku linanso limakamba kuti madela ena ku Isiraeli kulibiletu mitengo masiku ano. N’cifukwa ciani? Bukuli limafotoza kuti zimenezi zakhala zikucitika mwapang’onopang’ono. Limati: “Anthu akhala akudula mitengo makamaka kuti alambule malo olimapo ndi odyetsela ziŵeto, komanso kuti apezeko zomangila ndi nkhuni.”—Plants of the Bible.