Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Cikumbumtima Canu N’codalilika?

Kodi Cikumbumtima Canu N’codalilika?

“Colinga cokulamulila zimenezi n’cakuti tikhale ndi cikondi cocokela mumtima woyela, m’cikumbumtima cabwino.”—1 TIMOTEYO 1:5

NYIMBO: 57, 48

1, 2. Ndani anatipatsa cikumbumtima? N’cifukwa ciani tifunika kuyamikila kuti tili ndi cikumbumtima?

YEHOVA MULUNGU analenga anthu ndi ufulu wodzisankhila zocita. Pofuna kutithandiza kuti tizisankha mwanzelu, Yehova anatipatsa cikumbumtima. Cikumbumtima ndi umunthu wamkati umene umatithandiza kuzindikila cabwino ndi coipa. Ngati tigwilitsila nchito bwino cikumbumtima cathu, cidzatithandiza kucita zabwino ndi kupewa zoipa. Cikumbumtima cathu ndi umboni wakuti Yehova amatikonda ndipo amatifunila zabwino.

2 Anthu ena masiku ano amacita zabwino ndi kudana ndi zinthu zoipa ngakhale kuti sadziŵa miyezo ya m’Baibulo. (Ŵelengani Aroma 2:14, 15.) N’cifukwa ciani amacita zimenezo? Cifukwa cakuti ali ndi cikumbumtima. Cikumbumtima cimathandiza anthu ambili kupewa kucita zoipa. Ganizilani cabe mmene dziko likanaipila ngati aliyense analibe cikumbumtima. Mwacionekele, tikanamva zinthu zambili zoipa kuposa zimene tamvapo kale. Tiyamikila kwambili kuti Yehova anatipatsa cikumbumtima.

Kodi cikumbumtima cophunzitsidwa bwino cingatithandize bwanji popanga zosankha?

3. Kodi cikumbumtima cathu cingatithandize bwanji mumpingo?

3 Anthu ambili safuna kuphunzitsa cikumbumtima cao. Koma anthu a Yehova amafuna kuti cikumbumtima cao cizigwila bwino nchito cifukwa cingawathandize kukhala pamtendele ndi ena mumpingo. Tifuna kuti cikumbumtima cathu cizitikumbutsa miyezo ya m’Baibulo ya cabwino ndi coipa. Kuti tiphunzitse cikumbumtima cathu ndi kucigwilitsila nchito, tifunika kucita zambili kuposa kungophunzila Baibulo. Tifunika kukonda miyezo ya Mulungu ndi kukhulupilila kuti ingatithandize paumoyo wathu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Colinga cokulamulila zimenezi n’cakuti tikhale ndi cikondi cocokela mumtima woyela, m’cikumbumtima cabwino, ndiponso m’cikhulupililo copanda cinyengo.” (1 Timoteyo 1:5) Ngati timaphunzitsa bwino cikumbumtima cathu ndi kucitsatila, timakonda kwambili Yehova ndipo cikhulupililo cathu cimalimba. Mmene timagwilitsila nchito cikumbumtima cathu zimaonetsa kaya ubwenzi wathu ndi Yehova ndi wolimba kapena ai, ndiponso ngati tifuna kum’kondweletsa kapena ai. Cikumbumtima cathu cimaonetsanso mtundu wa munthu amene tili.

4. Kodi tingaphunzitse bwanji cikumbumtima cathu?

4 Koma kodi tingaphunzitse bwanji cikumbumtima cathu? Tifunika kuphunzila Baibulo nthawi zonse, kusinkhasinkha pa zimene taŵelenga, ndi kupempha Yehova kuti atithandize kugwilitsila nchito zimene taphunzila. Zimenezi zikutanthauza kuti tifunika kucitanso zina kuonjezela pa kuphunzila mfundo ndi malamulo a Mulungu. Tikamaphunzila Baibulo, colinga cathu n’cakuti tim’dziŵe bwino Yehova. Timadziŵa kuti iye ndi Munthu wotani, zimene amakonda, ndi zimene sakonda. Pamene tiphunzila zambili za Yehova, cikumbumtima cathu cidzatithandiza kuzindikila mwamsanga zimene iye amaona kuti n’zabwino kapena zoipa. Tikapitiliza kuphunzitsa cikumbumtima cathu, timayamba kuona zinthu monga mmene Yehova amazionela.

5. Tikambilana ciani m’nkhani ino?

5 Komabe, tingafunse kuti: Kodi cikumbumtima cabwino cingatithandize bwanji popanga zosankha? Kodi tingalemekeze bwanji cikumbumtima ca Akristu anzathu? Nanga cikumbumtima cathu cingatilimbikitse bwanji kucita cabwino? Tiyeni tikambilane mbali zitatu pamene tifunika kugwilitsila nchito cikumbumtima cabwino. Mbali zimenezi ndi (1) cithandizo ca mankhwala, (2) zosangulutsa, ndi (3) nchito yathu yolalikila.

KHALANI OGANIZA BWINO

6. Ndi zosankha zotani zimene timapanga zokhudza cithandizo ca mankhwala?

6 Baibulo limatiuza kuti tiyenela kupewa zinthu zimene zingationonge. Limatiuzanso kuti tiyenela kukhala oganiza bwino pa zinthu zimene timacita monga kudya ndi kumwa. (Miyambo 23:20; 2 Akorinto 7:1) Kutsatila malangizo a m’Baibulo kungatithandize kuteteza thanzi lathu. Koma timadwalabe ndi kukalamba. Kodi tingasankhe kucita ciani pankhaniyi? M’maiko ena, amagwilitsila nchito njila zambili zocilitsila matenda. Nthawi zambili, maofesi a nthambi amalandila makalata kucokela kwa abale ndi alongo opempha malangizo a cithandizo ca mankhwala cimene io angatsatile. Ambili amafunsa kuti: “Kodi mtumiki wa Yehova angalandile cithandizo ca mankhwala cimeneci?”

7. Kodi tingapange cosankha cotani pankhani ya magazi?

7 Ofesi ya nthambi kapena akulu mumpingo alibe mphamvu yosankhila Mkristu cithandizo ca mankhwala, ngakhale kuti iye wafunsila kwa io. (Agalatiya 6:5) Komabe, akulu angakambilane naye malangizo a Yehova kuti am’thandize kusankha mwanzelu. Mwacitsanzo, Mulungu watipatsa lamulo lakuti tizipewa magazi. (Machitidwe 15:29) Lamulo limeneli, limathandiza Mkristu kuzindikila kuti sayenela kulandila cithandizo ca mankhwala cimene ciphatikizapo kuikidwa magazi athunthu, kapena zigawo zinai zikuluzikulu za magazi. Mfundo imeneyi ingakhudze cikumbumtima ca Mkristu ngati iye angasankhe kulandila tuzigawo tung’onotung’ono twa magazi, tumene tumacokela ku zigawo zinai zikuluzikulu za magazi. * (Onani mau a munsi.) Ndi malangizo ena ati a m’Baibulo amene angatithandize kusankha mwanzelu pankhani ya cithandizo ca mankhwala?

8. Kodi kuganiza bwino kugatithandize bwanji kusankha mwanzelu pankhani ya cithandizo ca mankhwala?

8 Lemba la Miyambo 14:15 limati: “Munthu amene sadziŵa zinthu amakhulupilila mau alionse, koma wocenjela amaganizila za mmene akuyendela.” Masiku ano, pali matenda ena amene alibe mankhwala. Conco, tifunika kukhala osamala pankhani ya mankhwala amene angaoneke monga angaticilitse, koma palibe umboni wakuti anacilitsapo munthu. Paulo analemba kuti: “Anthu onse adziŵe kuti ndinu ololela [kapena kuti oganiza bwino].” (Afilipi 4:5) Kukhala woganiza bwino kungatithandize kuika maganizo athu pa kulambila Yehova m’malo moganizila kwambili za thanzi lathu. Ngati tiona kuti cithandizo ca mankhwala n’cofunika kwambili kwa ife, ndiye kuti tikuganizila zofuna zathu zokha. (Afilipi 2:4) Tikudziŵa kuti n’zosatheka kukhalilatu ndi thanzi labwino m’dongosolo lino. Motelo, onetsetsani kuti kutumikila Yehova ndiye cinthu cofunika kwambili kwa inu.—Ŵelengani Afilipi 1:10.

Kodi mumakakamiza ena kucita zimene inu muona kuti n’zabwino? (Onani ndime 9)

9. Kodi lemba la Aroma 14:13, 19 limakhudza bwanji cosankha cathu pankhani ya thanzi? Nanga mgwilizano wathu mumpingo ungasokonezeke bwanji?

9 Mkristu woganiza bwino sakakamiza ena kucita zimene iye akuona kuti n’zabwino. M’dziko lina, apabanja ena anali kuuza abale ndi alongo kuti azidya cakudya cinacake copatsa thanzi. Banjalo linali kulimbikitsa abalewo kutsatila malangizo amene linawapatsa, koma ena sanatsatile. Ataona kuti zakudyazo sizinagwile nchito, abale ndi alongo ambili anakhumudwa. Banja limeneli linali ndi ufulu wosankha lokha kudya zakudyazo kapena ai m’malo mokakamiza ena. Koma kodi n’canzelu kusokoneza mgwilizano mumpingo cabe cifukwa ca cithandizo ca mankhwala? Ku Roma wakale, Akristu anali ndi maganizo osiyanasiyana pankhani ya zakudya zina ndi mapwando. Ndi malangizo otani amene Paulo anawapatsa? Iye anati: “Wina amaona tsiku lina ngati loposa linzake, koma wina amaona tsiku lina mofanana ndi masiku ena onse. Conco munthu aliyense akhale wotsimikiza ndi mtima wonse m’maganizo mwake.” Tiyeni tikhale osamala kwambili kuti tisakhumudwitse ena.—Ŵelengani Aroma 14:5, 13, 15, 19, 20.

Onetsetsani kuti kutumikila Yehova n’kofunika kwambili pa umoyo wanu

10. N’cifukwa ciani tiyenela kulemekeza zosankha za ena? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

10 Nthawi zina, sitingamvetse cifukwa cake munthu wina mumpingo angasankhe mosiyanako pankhani inayake yaumwini. Kodi tiyenela kucita ciani? Sitiyenela kufulumila kumuweluza kapena kumukakamiza kusintha maganizo ake. Mwina iye akungofunika kuphunzitsa bwino cikumbumtima cake, kapena cikumbumtima cake cili bwino. (1 Akorinto 8:11, 12) Kapenanso cikumbumtima cathu ndiye cosaphunzitsidwa bwino. Pankhani yokhudza cithandizo ca mankhwala, aliyense afunika kusankha yekha, ndipo ayenela kuvomeleza zotsatilapo za zosankhazo.

MUZISANGALALA NDI ZOSANGULUTSA

11, 12. Kodi Baibulo limatithandiza bwanji posankha zosangulutsa?

11 Yehova anatilenganso m’njila yakuti tizisangalala ndi zosangulutsa ndiponso kupindula nazo. Solomo analemba kuti pali “nthawi yoseka” ndi “nthawi yodumphadumpha mosangalala.” (Mlaliki 3:4) Komabe, si zosangulutsa zonse zopindulitsa kapena zotsitsimula. Tifunikanso kupewa kutaila nthawi yaitali pa zosangulutsa. Kodi cikumbumtima cathu cingatithandize bwanji kusangalala ndiponso kupindula ndi zosangulutsa zimene Yehova amavomeleza?

‘Kodi cikumbumtima canga cimandicenjeza ndikamayesedwa?’

12 Baibulo limatiuza kuti tizipewa “nchito za thupi.” Nchito zimenezi ndi “dama, zinthu zodetsa, khalidwe lotayilila, kupembedza mafano, kucita zamizimu, udani, ndeu, nsanje, kupsa mtima, mikangano, kugaŵikana, magulu ampatuko, kaduka, kumwa mwaucidakwa, mapwando aphokoso, ndi zina zotelo.” Paulo analemba kuti “anthu amene amacita zimenezi sadzaloŵa mu ufumu wa Mulungu.” (Agalatiya 5:19-21) Conco, tingadzifunse kuti: ‘Kodi cikumbumtima canga cimandithandiza kupewa maseŵela amene amalimbikitsa ciwawa, mpikisano, kapena kukonda kwambili dziko langa? Kodi cikumbumtima canga cimandicenjeza ndikayesedwa kuti ndionelele filimu imene muli zamalisece, kumwa mwaucidakwa, kucita zamizimu kapena imene imalimbikitsa ciwelewele?’

13. Kodi malangizo apa 1 Timoteyo 4:8 ndi Miyambo 13:20 angatithandize bwanji posankha zosangulutsa?

13 Mfundo za m’Baibulo zingatithandize kuphunzitsa bwino cikumbumtima cathu pankhani ya zosangulutsa. Mwacitsanzo, Baibulo limati “kucita maseŵela olimbitsa thupi n’kopindulitsa pang’ono.” (1 Timoteyo 4:8) Ambili amaona kuti kucita maseŵela olimbitsa thupi nthawi zonse ndi kothandiza. Nanga bwanji ngati tifuna kucita maseŵela olimbitsa thupi ndi anthu ena? Kodi ndi anthu otani amene tifunika kucita nao zimenezo? Lemba la Miyambo 13:20 limatiuza kuti: “Munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu, koma wocita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” N’zoonekelatu kuti tifunika kugwilitsila nchito cikumbumtima cathu cophunzitsidwa bwino posankha zosangulutsa.

14. Kodi banja lina linagwilitsila nchito bwanji lemba la Aroma 14:2-4?

14 Christian ndi Daniela ali ndi ana aŵili acitsikana. Christian anati: “Tsiku lina pa Kulambila kwathu kwa Pabanja, tinakambilana nkhani ya zosangulutsa. Tinakambilana kuti pali zosangulutsa zina zabwino, zina zoipa. Tinakambilanso za anthu abwino amene tingaziceza nao. Ndiyeno, mmodzi wa ana athu aakazi anatiuza kuti panthawi yopumula ku sukulu, acinyamata ena a Mboni amacita zosangulutsa zina zimene iye amaona kuti ndi zosayenela. Ndipo anali kukakamizidwa kucitako zimenezo. Tinagwilizana kuti aliyense ali ndi cikumbumtima, ndipo tifunika kucigwilitsila nchito posankha zosangulutsa ndi anthu amene tifunika kucita nao.”—Ŵelengani Aroma 14:2-4.

Cikumbumtima canu cophunzitsidwa bwino cingakuthandizeni kupewa mavuto (Onani ndime 14)

15. Kodi lemba la Mateyu 6:33 limatithandiza bwanji pamene ticita zosangulutsa?

15 Kodi mumathela nthawi yaitali bwanji pocita zosangulutsa? Kodi mumaika misonkhano, ulaliki, ndi phunzilo laumwini pamalo oyamba pa umoyo wanu? Kapena mumakonda kwambili zosangulutsa? Kodi zofunika kwambili kwa inu ndi ziti? Yesu anati: “Pitilizani kufunafuna ufumu coyamba ndi cilungamo cake, ndipo zina zonsezi zidzaonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Mukamataila nthawi yanu pa zosangulutsa, kodi cikumbumtima canu cimakukumbutsani mau a Yesu?

TIMALIMBIKITSIDWA KULALIKILA

16. Kodi cikumbumtima cathu cimatilimbikitsa bwanji kulalikila?

16 Cikumbumtima cophunzitsidwa bwino sikuti cimangoticenjeza tikafuna kucita zoipa, koma cimatilimbikitsanso kucita zinthu zabwino. Cimodzi mwa zinthu zimenezi ndi kulalikila kunyumba ndi nyumba ndiponso mwamwai. Izi ndi zimene Paulo anacita. Iye analemba kuti: “Pakuti ndinalamulidwa kutelo. Ndithudi, tsoka kwa ine ngati sindilengeza uthenga wabwino!” (1 Akorinto 9:16) Ngati titengela Paulo, tidzakhala ndi cikumbumtima cabwino, podziŵa kuti ticita zabwino. Ndiponso pamene tikulalikila ena, timawafika pa mtima. Paulo anati: “Pamaso pa Mulungu, takhala citsanzo cabwino kwa cikumbumtima ca munthu aliyense.”—2 Akorinto 4:2.

17. Kodi mlongo wina wacitsikana anatsatila bwanji zimene cikumbumtima cake cophunzitsidwa bwino cinamuuza?

17 Pamene Jacqueline anali ndi zaka 16, anaphunzila za sayansi yokhudza zinthu zamoyo ku sukulu. Ponena zanthawi imene ana sukulu anali kuphunzila za cisanduliko, iye anati: “Cikumbumtima canga sicinali kundilola kutengamo mbali panthawi yokambilana. Zinali kundivuta kucilikiza cisanduliko. Mpaka tsiku lina ndinafikila aphunzitsi kuti ndiwafotozele za cikhulupililo canga. Zondidabwitsa n’zakuti, mphunzitsiyo anali womasuka ndipo anandilola kuti ndikafotokoze cikhulupililo canga pa nkhani ya cilengedwe m’kalasi.” Jacqueline anasangalala cifukwa cotsatila zimene cikumbumtima cake cophunzitsidwa bwino cinamuuza. Kodi cikumbumtima canu cimakulimbikitsani kucita zabwino?

18. N’cifukwa ciani tifunika kukhala ndi cikumbumtima cabwino ndi codalilika?

18 Colinga cathu ndi kucita zinthu mogwilizana ndi mfundo za makhalidwe abwino a Yehova nthawi zonse. Ndipo cikumbumtima cathu cingatithandize kukwanitsa zimenezo. Ngati timaphunzila Mau a Mulungu, kuwasinkhasinkha, ndi kugwilitsila nchito zimene timaphunzila, tidzaphunzitsa bwino cikumbumtima cathu. Tikatelo, mphatso yocokela kwa Mulungu imeneyi idzakhala yodalilika pa umoyo wathu wacikristu.

^ par. 7 Onani nkhani yakuti “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2004, masamba 29-31.