Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Munafikapo pa Ucikulile Umene Kristu Anafikapo?

Kodi Munafikapo pa Ucikulile Umene Kristu Anafikapo?

‘Fikani . . . pa msinkhu waucikulile umene Kristu anafikapo.’—AEFESO 4:13.

NYIMBO: 69, 70

1, 2. Kodi colinga ca Mkristu aliyense n’ciani? Pelekani citsanzo.

N’CIANI cimene azimai amacita posankha zipatso zoti agule pamsika? Mwacionekele, io sayang’ana kukula kwa cipatso kapena kutsika mtengo kwa cipatsoco. M’malo mwake, amasankha zipatso zonunkhila bwino, zokongola, zimene zangothyoledwa kumene, zakupsa bwino, ndi zokhwima.

Mkristu wofikapo amafufuza mfundo za m’Baibulo zimene zingam’thandize kudziŵa cabwino ndi coipa

2 Munthu akaphunzila za Yehova ndi kubatizidwa, amapitiliza kukulitsa ubwenzi wake ndi Mulungu. Colinga cake n’cakuti akhale Mkristu wokhwima. Kukhwima kumeneku sikutanthauza kukula kwa kuthupi. Koma kumatanthauza kukhwima kuuzimu ndi kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova. Mtumwi Paulo anafuna kuti Akristu a ku Efeso akhale ofikapo kuuzimu. Iye anawalimbikitsa kukhala ogwilizana m’cikhulupililo ndi kupitiliza kuphunzila za Kristu kuti akhale ‘anthu acikulile, ofika pa msinkhu waucikulile umene Kristu anafikapo.’—Aefeso 4:13.

3. Kodi mpingo wa ku Efeso umafanana bwanji ndi atumiki a Yehova masiku ano?

3 Mpingo wa ku Efeso utakhazikitsidwa, mtumwi Paulo analembela kalata Akristu a kumeneko. Ambili mumpingowo anatumikila kwa nthawi yaitali, ndipo anali Akristu ofikapo kuuzimu. Komabe, panali ena amene anali kufunika kulimbitsa ubwenzi wao ndi Yehova. Mofananamo, masiku ano abale ndi alongo ambili atumikila Yehova kwa nthawi yaitali, ndipo ndi Akristu ofikapo kuuzimu. Ngakhale n’conco, pali ena amene akalibe kufikapo kuuzimu. Mwacitsanzo, anthu masauzande amabatizidwa caka ciliconse. Iwo afunikilabe kufikapo kuuzimu. Nanga bwanji za inu?—Akolose 2:6, 7.

KODI MKRISTU ANGAKHALE BWANJI WOFIKAPO KUUZIMU?

4, 5. Kodi Akristu ofikapo ndi osiyanasiyana bwanji? Nanga ndi ofanana pa ciani? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

4 Mukayang’ana zipatso zakupsa, mukhoza kuona kuti sizifanana ndendende. Koma pali maonekedwe ena ake amene amaonetsa kuti zipatso zonse ndi zakupsa. N’cimodzimodzi ndi Akristu ofikapo kuuzimu. Iwo safanana cifukwa amacokela ku maiko osiyanasiyana, anakulila ku malo osiyanasiyana, ndi a msinkhu wosiyana, ndipo amakonda zinthu zosiyana. Komabe, Akhristu onse okhwima ali ndi makhalidwe ena ofanana amene amaonetsa kuti ndi ofikapo kuuzimu. Kodi ena a makhalidwe amenewo ndi ati?

‘Kodi pali zinthu zina zimene ndingasinthe kuti nditsatile Yesu mosamala kwambili?’

5 Mkristu wofikapo amatsatila ‘mapazi a Yesu mosamala kwambili.’ (1 Petulo 2:21) Yesu anakamba kuti munthu ayenela kukonda Yehova ndi mtima wake wonse, moyo wake wonse, ndi maganizo ake onse. Ndipo ayenelanso kukonda mnzake mmene amadzikondela yekha. (Mateyu 22:37-39) Mkristu wofikapo amayesetsa kumvela malangizo amenewo. Mmene amakhalila umoyo wake zimaonetsa kuti ubwenzi wake ndi Yehova, ndiponso kukonda ena, ndi zofunika kwambili kwa iye.

Akristu okalamba amatengela kudzicepetsa kwa Yesu mwa kucilikiza acinyamata amene akutsogolela mumpingo (Onani ndime 6)

6, 7. (a) Ndi makhalidwe ena ati amene amaonetsa kuti Mkristu ndi wofikapo? (b) Ndi mafunso ati amene tiyenela kudzifunsa?

6 Cikondi ndi limodzi mwa makhalidwe ambili amene Mkristu wofikapo amaonetsa. (Agalatiya 5:22, 23) Iye amaonetsanso kufatsa, kudziletsa ndiponso kuleza mtima. Makhalidwe amenewa amamuthandiza kupilila mavuto aakulu popanda kukhumudwa. Mkristu wofikapo akamacita phunzilo laumwini, amafufuza mfundo za m’Baibulo zimene zimam’thandiza kudziŵa cabwino ndi coipa. Ndiyeno, amagwilitsila nchito cikumbumtima cake cophunzitsidwa bwino kupanga zosankha mwanzelu. Mkristu wofikapo amakhala wodzicepetsa, ndipo amatsatila malangizo ndi miyezo ya Yehova osati maganizo ake. * (Onani mau a munsi.) Iye amalalikila uthenga wabwino mwakhama ndipo amacita zonse zimene angathe kuti mpingo ukhale wogwilizana.

7 Ngakhale kuti tatumikila Yehova kwa nthawi yaitali kapena ai, aliyense wa ife ayenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi pali zinthu zina zimene ndingasinthe kuti nditsatile Yesu mosamala kwambili? Kodi pali penapake pamene ndingaongolele?’

“CAKUDYA COTAFUNA NDI CA ANTHU OKHWIMA MWAUZIMU”

8. Kodi Yesu anali kulidziŵa bwanji Baibulo?

8 Yesu Kristu anali kuwadziŵa bwino Malemba ndi kuwamvetsetsa. Ngakhale pamene anali ndi zaka 12, iye anagwilitsila nchito Malemba pokambilana ndi aphunzitsi m’kacisi. “Onse amene anali kumumvetsela anadabwa kwambili ndi mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambili.” (Luka 2:46, 47) Panthawi ina, pamene iye anali kulalikila, anagwilitsila nchito Mau a Mulungu mwaluso poyankha adani ake cakuti io anasoŵa zokamba.—Mateyu 22:41-46.

9. (a) Ndi ndandanda yotani imene Mkristu wofikapo amakhala nayo? (b) N’cifukwa ciani timaphunzila Baibulo?

9 Mkristu amene afuna kukhala wokhwima kuuzimu amatsatila citsanzo ca Yesu, ndipo amayesetsa kumvetsetsa Baibulo mmene angathele. Nthawi zonse iye amafufuza Malemba kuti apeze coonadi cozama cifukwa amadziŵa kuti “cakudya cotafuna ndi ca anthu okhwima mwauzimu.” (Aheberi 5:14) Mkristu wofikapo amafuna ‘kudziŵa molondola’ coonadi ca m’Baibulo. (Aefeso 4:13) Conco, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimaŵelenga Baibulo tsiku lililonse? Kodi ndili ndi ndandanda ya phunzilo laumwini? Kodi timacita kulambila kwa pabanja mlungu uliwonse?’ Mukamaphunzila Baibulo, muzifufuza mfundo zimene zingakuthandizeni kudziŵa maganizo a Yehova ndi mmene amamvelela. Ndipo muzigwilitsila nchito mfundozo popanga zosankha. Kucita zimenezo kudzakuthandizani kuyandikila kwambili Yehova.

10. Kodi Mkristu wofikapo amawaona bwanji malangizo ndi mfundo za Mulungu?

10 Mkristu wofikapo sadziŵa cabe zimene Baibulo limakamba. Iye afunika kukonda malangizo ndi mfundo za Mulungu. Ndipo amaonetsa cikondi cimeneci mwa kucita cifunilo ca Yehova osati cake. Iye amafika posintha umoyo wake, kaganizidwe kake, ndi zocita zake. Mwacitsanzo, iye amatengela Yesu ndi kukhala ndi umunthu watsopano umene “unalengedwa mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu ndipo umatsatila zofunika pa cilungamo ceniceni ndi pa kukhulupilika.” (Ŵelengani Aefeso 4:22-24.) Tisaiŵale kuti Mulungu anagwilitsila nchito mzimu wake woyela kutsogolela anthu amene analemba Baibulo. Conco, Mkristu akamaphunzila Baibulo, mzimu woyela wa Mulungu umam’thandiza kukhala ndi cidziŵitso cakuya, cikondi cacikulu, ndiponso kulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova.

MUZILIMBIKITSA MGWILIZANO

11. Kodi Yesu anali kukhala ndi anthu otani padziko lapansi?

11 Yesu anali munthu wangwilo. Komabe, pamene anali padziko lapansi anali kukhala ndi anthu opanda ungwilo. Makolo ake, abale ndi alongo ake onse anali opanda ungwilo. Ngakhale otsatila ake amene anali anzake panthawi ina anaonetsa mzimu wodzikuza ndi wodzikonda. Mwacitsanzo, usiku wakuti maŵa aphedwa, ophunzila ake anali kukangana pakati pao “za amene anali kuoneka wamkulu kwambili.” (Luka 22:24) Ngakhale kuti io anali ndi maganizo olakwika cifukwa ca kupanda ungwilo, Yesu anadziŵa kuti otsatila akewo adzakhala Akristu ofikapo ndipo adzapanga mpingo wogwilizana. Usiku umenewo Yesu anawapemphelela kuti akhale ogwilizana. Iye anapempha Atate wake wakumwamba kuti athandize otsatila ake kukhala ogwilizana monga mmene iye alili wogwilizana ndi atate wake.—Yohane 17:21, 22.

12, 13. (a) Kodi ife Akristu tili ndi colinga cotani? (b) Kodi m’bale wina anaphunzila bwanji kulimbikitsa mgwilizano mumpingo?

12 Mkristu wofikapo amalimbikitsa mgwilizano mumpingo. (Ŵelengani Aefeso 4:1-6, 15, 16.) Monga Akristu colinga cathu ndi kukhala ‘olumikizika bwino ndi ogwilizana,’ kutanthauza kugwilila nchito pamodzi mogwilizana. Kuti Mkristu akhale wogwilizana ndi ena afunika kukhala wodzicepetsa. Ngakhale ngati Akhristu anzake amukhumudwitsa, Mkristu wofikapo amayesetsa kulimbikitsa mgwilizano mumpingo. Conco, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimacita bwanji ngati m’bale kapena mlongo walakwitsa zinazake? Ndimamvela bwanji ngati munthu wina wandikhumudwitsa? Kodi ndimaleka kukambitsana naye? Kapena ndimayesetsa kukonzanso ubwenzi wathu?’ Mkristu wofikapo amayesetsa kuthetsa mikangano m’malo mokhala cokhumudwitsa kwa ena.

13 Ganizilani citsanzo ca Uwe. Kale, iye anali kukhumudwa ndi zocita za abale ndi alongo. Ndiyeno, anaganiza zakuti aphunzile za umoyo wa Davide. Kuti acite zimenezi, anayamba kuŵelenga Baibulo ndi buku la Insight on the Scriptures. N’cifukwa ciani anasankha kuphunzila za Davide? Cifukwa cakuti Davide nayenso anakumanapo ndi mavuto ocokela kwa atumiki ena a Mulungu. Mwacitsanzo, Mfumu Sauli anafuna kupha Davide, anthu ena anafuna kumuponya miyala, ndipo ngakhale mkazi wake anamuseka. (1 Samueli 19:9-11; 30:1-6; 2 Samueli 6:14-22) Koma mosasamala kanthu za zinthu zimene anthu anamucita, Davide anali kukondabe Yehova ndi kum’khulupilila. Davide analinso wacifundo. Uwe anakamba kuti nayenso anafunika kutsatila citsanzo ca Davide. Cifukwa cophunzila Baibulo, iye anazindikila kuti afunika kusintha mmene amamvelela cifukwa ca zimene abale amalakwitsa. Iye anafunikila kuiŵala zolakwa zao ndi kulimbikitsa mgwilizano mumpingo. Kodi inunso mufuna kucita zimenezi?

SANKHANI MABWENZI PAKATI PA ATUMIKI A MULUNGU

14. Kodi Yesu anali kusankha bwanji mabwenzi ake?

14 Yesu Kristu anali waubwenzi ndi anthu. Amuna ndi akazi, okalamba ndi acicepele, ngakhalenso ana, anali kumasuka naye. Koma anali kusamala posankha mwabwenzi. Iye anauza atumwi ake kuti: “Mupitiliza kukhala mabwenzi anga mukamacita zimene ndikukulamulani.” (Yohane 15:14) Yesu anasankha mabwenzi ake apamtima pakati pa anthu amene anali kumutsatila mokhulupilika ndiponso amene anali kukonda Yehova ndi kum’tumikila. Kodi mumasankha mabwenzi amene amakonda Yehova ndi mtima wonse? N’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kofunika?

Kodi mumasankha mabwenzi amene amakonda Yehova ndi mtima wonse?

15. Kodi acinyamata angapindule bwanji cifukwa cokhala paubwenzi ndi Akristu ofikapo?

15 Zipatso zambili zimapsa bwino pamene dzuŵa likuwala bwino. Mofananamo, cikondi ca abale ndi alongo athu cingakuthandizeni kukhala Mkristu wofikapo. Kodi ndinu mnyamata kapena mtsikana ndipo mufuna kusankha zimene mudzacita ndi umoyo wanu? Ngati n’conco, mufunika kusankha mabwenzi amene atumikila Yehova kwa nthawi yaitali ndipo amalimbikitsa mgwilizano mumpingo. Mwina io anakumanapo ndi mavuto pa umoyo wao ndipo anapilila zambili potumikila Yehova. Conco, angakuthandizeni kusankha moyo wabwino koposa. Mukamaceza nao, adzakuthandizani kupanga zosankha mwanzelu ndi kukhala Mkristu wofikapo.—Ŵelengani Aheberi 5:14.

16. Kodi Akristu ena mumpingo anathandiza bwanji mlongo wina pamene anali mtsikana?

16 Mlongo wina dzina lake Helga, akukumbukila kuti kutatsala pang’ono kuti atsilize sukulu, anzake ambili a m’kalasi anali kukamba za zolinga zao za mtsogolo. Ambili anali kufuna kupita ku yunivesite n’colinga cakuti akapeze nchito yabwino. Koma Helga anakambilana nkhaniyi ndi anzake ofikapo kuuzimu mumpingo. Iye anati: “Ambili anali aakulu msinkhu kuposa ine, ndipo anandithandiza kwambili. Anandilimbikitsa kuyamba utumiki wa nthawi zonse. Ndiyeno, ndinatumikila monga mpainiya kwa zaka 5. Tsopano, ngakhale kuti papita zaka zambili, ndikusangalala kuti pamene ndinali mtsikana ndinatumikila Yehova. Ndikuona kuti ndinasankha mwanzelu.”

17, 18. Tingacite ciani kuti titumikile bwino Yehova?

17 Tikamatengela Yesu, timakula ndi kukhala Akristu ofikapo kuuzimu, timayandikila Yehova kwambili, ndipo timakhala ofunitsitsa kum’tumikila. Mkristu wofikapo kuuzimu amatumikila bwino Yehova. Yesu analimbikitsa otsatila ake kuti: “Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone nchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wakumwamba.”—Mateyu 5:16.

18 M’nkhani ino, taphunzila mmene Mkristu wofikapo kuuzimu angathandizile mpingo. Mmene Mkristu amagwilitsila nchito cikumbumtima cake, zimaonetsa kuti ndi wofikapo kuuzimu kapena ai. Kodi cikumbumtima cathu cingatithandize bwanji kupanga zosankha zanzelu? Nanga tingalemekeze bwanji cikumbumtima ca ena? Mafunso amenewa adzayankhidwa m’nkhani yotsatila.

^ par. 6 Mwacitsanzo, abale okalamba amene atumikila kwa nthawi yaitali angapemphedwe kutula pansi udindo wao kuti acilikize abale acinyamata amene apatsidwa udindowo.