Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

‘Abale Okhala Ngati Amenewa Muziwalemekeza Kwambili’

‘Abale Okhala Ngati Amenewa Muziwalemekeza Kwambili’

KUYAMBILA m’caka ca 1992, Bungwe Lolamulila lakhala likusankha akulu okhwima kuuzimu, kuti azithandizila makomiti a bungweli kukwanilitsa nchito yao. * (Onani mau amunsi.) Abale amenewa, amene ndi a “nkhosa zina,” amapeleka thandizo lofunikila ku Bungwe Lolamulila. (Yohane 10:16) Iwo amakhala ndi miting’i mlungu uliwonse m’makomiti amene akutumikila. Nchito yao ndi kufotokozela Bungwe Lolamulila mfundo zina zofunika ndi kupelekapo malingalilo ao. Pambuyo pake, bungwelo limapeleka cigamulo pa mfundozo. Ndiyeno, abalewa amaonetsetsa kuti zimene zagamulidwa zacitika. Abale amenewa ndi odzipeleka kucita utumiki ulionse umene apatsidwa. Iwo amayendela limodzi ndi abale a m’Bungwe Lolamulila ku misonkhano yapadela ndi ya maiko. Amapatsidwanso utumiki wocezela maofesi a nthambi monga oimila likulu la Mboni za Yehova.

M’bale wina amene watumikila monga wothandizila kuyambila mu 1992 anati: “Kucita mwakhama utumiki uliwonse umene ndapatsidwa, kumathandiza kuti Bungwe Lolamulila liziika kwambili maganizo ao pa zinthu za kuuzimu.” M’bale wina amene watumikila monga wothandizila kwa zaka 20 nayenso anati: “Umenewu ndi mwai waukulu koposa umene sindinauyembekezele.”

Bungwe Lolamulila lapatsa othandizila ao amenewa nchito yaikulu, ndipo limayamikila abale okhulupilika amenewa cifukwa ca nchito imene amagwila mwakhama. Tiyeni tonse tipitilize kulemekeza kwambili abale okhala ngati amenewa.—Afilipi 2:29.

^ par. 2 Kuti mudziŵe zambili za nchito ya makomiti 6 a Bungwe Lolamula, onani buku lakuti, Ufumu wa Mulungu Ukulamulila, pa tsamba 131.