Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kwa Ine Kuyandikila Mulungu ndi Cinthu Cabwino

Kwa Ine Kuyandikila Mulungu ndi Cinthu Cabwino

PAMENE ndinali ndi zaka 9, ndinaleka kukula. Tsopano ndili ndi zaka 43, koma ndine wamfupi mita imodzi. Makolo anga atazindikila kuti sindidzatalika kuposa pamenepo, anandilimbikitsa kuti ndizigwila nchito kwambili kuti ndisamaganizile za msinkhu wanga nthawi zonse. Ndinakonza kasitandi kogulisilapo zipatso pa nyumba pathu, ndipo pamalopo ndinali kupasunga paukhondo. Zimenezi zinali kukopa anthu kuti adzagule zipatso.

Kugwila nchito kwambili sikunasinthe ciliconse. Ndinali wamfupi, ndipo ndinali kuvutikabe ndi zinthu zina monga kufikila pa kaunta ya m’sitolo. Zinthu zonse zinali ngati kuti anapangila anthu aatali kuwilikiza kaŵili pa msinkhu wanga. Ndinali kuzimvela cisoni, koma zimenezi zinasintha nditafika zaka 14.

Tsiku lina azimai aŵili a Mboni za Yehova anabwela kudzagula zipatso. Ndiyeno, anandipempha kuphunzila Baibulo. Pasanapite nthawi, ndinazindikila kuti kudziŵa Yehova ndi colinga cake n’kofunika kwambili kuposa msinkhu wanga. Zimenezi zinandithandiza kwambili paumoyo wanga. Ndinayamba kukonda kwambili lemba la Salimo 73: 28. Mbali yoyamba ya lembali limati: “Koma kwa ine kuyandikila kwa Mulungu ndi cinthu cabwino.”

Mosayembekezela, banja lathu linasamuka m’dziko la Côte d’Ivoire kupita ku Burkina Faso, ndipo umoyo wanga unasintha kwambili. Ku Côte d’Ivoire, anthu anali atazoloŵela kundiona ndikugulitsa zipatso. Koma ku Burkina Faso ndinali mlendo, ndipo anthu ambili anali kudabwa akandiona. Iwo anali kukhalila kundiyang’ana. Conco, kwa milungu yambili ndinali kukhala m’nyumba. Kenako, ndinaganizila ubwino woyandikila Yehova. Pa cifukwa cimeneci, ndinalembela kalata ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova. Iwo ananditumizila munthu woyenelela kudzandiphunzitsa Baibulo. Anatumiza mmishonale wina, dzina lake Nani, amene anabwela ndi njinga yake yamoto.

Miseu ya kudela kumene tikhala ili ndi micenga, ndipo ndi yovuta kuyendamo. Nthawi ya mvula imakhala ndi matope. Ndipo nthawi zambili Nani anali kugwa pa njinga yake pobwela kudzandiphunzitsa. Komabe, iye sanataye mtima. Tsiku lina anandipempha kuti ndipite naye ku misonkhano. Ndinadziŵa kuti ndikacoka panyumba, ndidzafunika kupilila ndi anthu amene anali kundiyang’ana. Kuonjezela pamenepa, kundikweza pa njingayo kukanapangitsa kuti kukhale kovuta kwambili kuiyendetsa. Ngakhale zinali conco, ndinavomela cifukwa ndinakumbukila mbali yaciŵili ya lemba la pamtima panga limene limati: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa ndiye pothaŵilapo panga.”

Nthawi zina, Nani ndi ine tinali kugwa m’matope popita ku misonkhano. Koma popeza tinali kukonda misonkhano sitinaleke kusonkhana. Kukamba zoona, ku Nyumba ya Ufumu abale ndi alongo anandionetsa cikondi mwa kumwetulila kusiyana ndi anthu ena amene anali kukhalila kundiyang’ana. Patapita miyezi 9 ndinabatizidwa.

Mbali yomaliza ya lemba limene ndimakonda kwambili limati: “Kuti ndilengeze za nchito zanu zonse.” Ndinadziŵa kuti vuto langa lalikulu lidzakhala kupita mu ulaliki. Ndikumbukila nthawi yoyamba imene ndinapita mu ulaliki wa nyumba ndi nyumba. Ana ndi akulu omwe, anali kungondiyang’ana, kundilondola ndi kundiseka. Zimenezo zinandikhumudwitsa kwambili. Koma ndinazindikila kuti tonse tifunikila Paladaiso, conco ndinapilila.

Kuti ndisamavutike polalikila, ndinagula njinga ya olemala ya mawilo atatu yochova ndi manja. Tikafika pa malo okwela, mnzanga wa mu ulaliki anali kundikankha, koma tikafika pamalo otsika ndinali kum’kwezeka panjingayo. Ngakhale kuti poyamba ndinali kuvutika kwambili kupita mu ulaliki, ndinayamba kusangalala kwambili ndi ulaliki, cakuti mu 1998 ndinakhala mpainiya wa nthawi zonse.

Ndinali kuphunzila Baibulo ndi anthu ambili, ndipo anai anabatizidwa. Kuonjezela apo, mmodzi wa alongo anga anakhala Mboni. Ndikamvela zakuti ena akupita patsogolo ndimalimbikitsidwa, ndipo zimakhala za panthawi yake. Mwacitsanzo, ndinayambitsa phunzilo la Baibulo locititsa coimilila kwa mwana wa sukulu wina wa pa yunivesite ku Burkina Faso, ndipo ndinauza m’bale kuti apitilize kuphunzila naye. Mwana wa sukuluyo anasamukila ku Côte d’Ivoire. Tsiku lina pamene ndinali kudwala malungo, ndinalandila kalata kucokela kwa iye kuti ndi wofalitsa wosabatizika, ndipo ndinakondwela kwambili kumva zimenezo.

Kodi ndimapeza bwanji zosowa zanga za kuthupi? Bungwe lina limene limathandiza olemala linandiphunzitsa kusoka zovala. Mphunzitsi wina ataona mmene ndinali kugwilila nchito anakamba kuti: “Tidzakuphunzitsa kupanga sopo.” Iwo anandiphunzitsadi. Tsopano, ndimapanga sopo yochapila ndi yosambila. Anthu ambili amakonda sopo wanga ndipo amauzako ena. Ndimapita kukagulitsa sopoyu ndi njinga yanga ya mawilo atatu.

Comvetsa cisoni n’cakuti, nditayamba kudwala matenda a msana mu 2004, ndinasiya upainiya. Komabe, ndimalalikila nthawi zonse.

Anthu amakamba kuti ndimadziŵika ndi kumwetulila kwanga. Ndili ndi zifukwa zokwanila zokhalila wosangalala cifukwa kwa ine, kuyandikila kwa Mulungu ndi cinthu cabwino.—Yosimbidwa ndi Sarah Maiga.