Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Tionjezeleni Cikhulupililo”

“Tionjezeleni Cikhulupililo”

“Limbitsani cikhulupililo canga!”—MALIKO 9:24.

NYIMBO: 81, 135

1. Kodi cikhulupililo n’cofunika bwanji? (Onani cithunzi pamwamba.)

KODI munadzifunsapo kuti: ‘Kodi Yehova angakonde kundipulumutsa pa cisautso cacikulu?’ Mtumwi Paulo anakamba kuti cikhulupililo ndi khalidwe lofunika kwambili limene tiyenela kukhala nalo kuti tikapulumuke. Iye anati: “Popanda cikhulupililo n’zosatheka kukondweletsa Mulungu.” (Aheberi 11:6) Zimenezi zingaoneke zopepuka. Koma kukamba zoona, “cikhulupililo sicikhala ndi anthu onse.” (2 Atesalonika 3:2) Malemba aŵiliwa atithandiza kuona kuti kulimbitsa cikhulupililo cathu n’kofunika kwambili.

2, 3. (a) Kodi cikhulupililo cathu n’cofunika bwanji? (b) Tikambilana ciani m’nkhani ino?

2 Mtumwi Petulo anakamba za cikhulupililo cimene “cayesedwa.” (Ŵelengani 1 Petulo 1:7.) Cisautso cacikulu cili pafupi kwambili. Conco, tifunika kukhala “mtundu wa anthu okhala ndi cikhulupililo cosunga moyo.” (Aheberi 10:39) Ndipo tifunika kucita zimene tingathe kuti tilimbitse cikhulupililo cathu. Yesu Kristu, Mfumu yathu akadzaonekela, tifunika tidzakhale pakati pa anthu amene adzalandila mphoto. Monga bambo uja amene anapempha Yesu kuti alimbitse cikhulupililo cake, nafenso tingakambe kuti: “Limbitsani cikhulupillilo canga!” (Maliko 9:24) Monga atumwi, tingakambenso kuti: “Tionjezeleni cikhulupililo.”—Luka 17:5.

3 M’nkhani ino, tikambilana mfundo zotsatilazi: mmene tingalimbitsile cikhulupililo cathu, mmene tingaonetsele kuti cikhulupililo cathu n’colimba, ndiponso mmene tingakhalile otsimikiza mtima kuti Mulungu adzayankha tikam’pempha kuti ationjezele cikhulupililo.

MULUNGU AMAKONDWELA NGATI TILIMBITSA CIKHULUPILILO CATHU

4. Ndi zitsanzo ziti zimene zingatithandize kulimbitsa cikhulupililo cathu?

4 Cikhulupililo n’cofunika kwambili. Ndiye cifukwa cake kupitila m’Baibulo, Yehova watipatsa zitsanzo zambili pankhani ya cikhulupililo. Zitsanzo zimenezi “zinalembedwa kuti zitilangize.” (Aroma 15:4) Citsanzo ca Abulahamu, Sara, Isaki, Yakobo, Mose, Rahabi, Gidiyoni, Baraki, ndi ena ambili cingatithandize kulimbitsa cikhulupililo cathu. (Aheberi 11:32-35) Kuonjezela pa zitsanzo zakale, tilinso ndi zitsanzo zabwino za abale ndi alongo athu amene ali ndi cikhulupililo. * (Onani mau a munsi.)

Tili ndi zitsanzo zabwino za abale ndi alongo athu amene ali ndi cikhulupililo

5. Kodi Eliya anaonetsa bwanji kuti anali ndi cikhulupililo colimba mwa Yehova? Nanga tiyenela kudzifunsa ciani?

5 Citsanzo cimodzi ca m’Baibulo ndi ca mneneli Eliya. Pamene musinkhasinkha za citsanzo cake, onani zocitika zisanu pamene anaonetsa cikhulupililo colimba mwa Yehova. (1)  Eliya atauza Mfumu Ahabu kuti Yehova adzabweletsa cilala, iye anakamba motsimikiza kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo, Mulungu wa Isiraeli amene ndimam’tumikila, sikugwa mame kapena mvula.” (1 Mafumu 17:1) (2) Eliya anali ndi cikhulupililo cakuti Yehova adzamusamalila pamodzi ndi atumiki ena panthawi ya cilalaco. (1 Mafumu 17:4, 5, 13, 14) (3)  Eliya analinso wotsimikiza kwambili kuti Yehova adzaukitsa mwana wa mkazi wamasiye. (1 Mafumu 17:21) (4) Sanakaikilenso kuti Yehova adzanyeketsa nsembe imene iye anapeleka pa Phili la Karimeli. (1 Mafumu 18:24, 37) (5) Panthawi imene kunali cilala ndipo mvula inali isanagweko, Eliya anauza Ahabu motsimikiza kuti: “Pitani mukadye ndi kumwa, cifukwa kukumveka mkokomo wa cimvula.” (1 Mafumu 18:41) Pambuyo pophunzila zitsanzo zimenezi, dzifunseni kuti: ‘Kodi cikhulupililo canga n’colimba monga ca Eliya?’

TINGACITE CIANI KUTI TILIMBITSE CIKHULUPILILO CATHU?

6. Tifunika kucita ciani kuti Yehova alimbitse cikhulupililo cathu?

6 Popeza n’zosatheka kulimbitsa cikhulupililo mwa mphamvu zathu, tifunika kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu wake woyela. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti cikhulupililo ndi limodzi mwa makhalidwe amene mzimu woyela umatulutsa. (Agalatiya 5:22) Ngati titsatila malangizo a Yesu akuti tizipempha kuti ationjezele mzimu woyela, ndiye kuti ticita zinthu mwanzelu. Yesu anakamba kuti Yehova “adzapeleka moolowa manja mzimu woyela kwa amene akum’pempha.”—Luka 11:13.

Ngati titsatila malangizo a Yesu akuti tizipempha kuti ationjezele mzimu woyela, ndiye kuti ticita zinthu mwanzelu

7. Fotokozani mmene tingaonjezele cikhulupililo cathu.

7 Tikakhala ndi cikhulupililo colimba mwa Mulungu, tifunika kupitiliza kucionjezela. Cikhulupililo tingaciyelekezele ndi moto. Ngati tayatsa moto, umakhala wamphamvu kwambili. Komabe, ngati sitisonkhela nkhuni, motowo ukhoza kuzima ndi kukhala phulusa. Koma ngati tisonkhela nkhuni kaŵilikaŵili motowo umapitiliza kuyaka. N’cimodzimodzi ndi cikhulupililo cathu. Ngati tipitiliza kuŵelenga ndi kuphunzila Mau a Mulungu tsiku lililonse, cikondi cathu pa Yehova ndi Mau ake cimakula. Zimenezi zidzatithandiza kuonjezela ndi kulimbitsa cikhulupililo cathu.

8. N’ciani cingakuthandizeni kuonjezela ndi kulimbitsa cikhulupililo canu?

8 Simuyenela kukhala okhutila ndi zinthu zokha zimene munaphunzila musanabatizidwe. (Aheberi 6:1, 2) Mwacitsanzo, kuphunzila maulosi a m’Baibulo amene anakwanilitsidwa kale kudzakuthandizani kuonjezela ndi kulimbitsa cikhulupililo canu. Mau a Mulungu angakuthandizeninso kudziŵa ngati cikhulupililo canu n’colimbadi.—Ŵelengani Yakobo 1:25; 2:24, 26.

9, 10. Kodi cikhulupililo cathu cingalimbikitsidwe bwanji ndi (a) mabwenzi abwino? (b) misonkhano ya mpingo? (c) nchito yolalikila?

9 Mtumwi Paulo anakamba kuti Akristu akhoza ‘kulimbikitsana mwa cikhulupililo.’ (Aroma 1:12) Kodi zimenezi zitanthauza ciani? Tikamaceza ndi abale ndi alongo athu, makamaka aja amene cikhulupililo cao cinayesedwapo, timalimbikitsana mwa cikhulupililo. (Yakobo 1:3) Mabwenzi oipa amaononga cikhulupililo, koma mabwenzi abwino amacilimbitsa. (1 Akorinto 15:33) Ndiye cifukwa cake timalimbikitsidwa kuti tidzipezeka pa misonkhano nthawi zonse. Kumeneko ‘timalimbikitsana.’ (Ŵelengani Aheberi 10:24, 25.) Cina, malangizo amene timalandila pamisonkhano amalimbitsa cikhulupililo cathu. Baibulo limakamba kuti “munthu amakhala ndi cikhulupililo cifukwa ca zimene wamva.” (Aroma 10:17) Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimapezeka pamisonkhano nthawi zonse?’

10 Timalimbitsanso cikhulupililo cathu ngati tilalikila ndi kuphunzitsa ena uthenga wabwino wocokela m’Baibulo. Monga Akristu oyambilila, timayamba kukhulupilila Yehova ndi kukamba molimba mtima pa cocitika ciliconse.—Machitidwe 4:17-20; 13:46.

11. N’cifukwa ciani Kalebe ndi Yoswa anali ndi cikhulupililo colimba? Nanga tingatengele bwanji citsanzo cao?

11 Cikhulupililo cathu mwa Yehova cimakula tikaona mmene amatithandizila ndi mmene amayankhila mapemphelo athu. Izi n’zimene zinacitikila Kalebe ndi Yoswa. Iwo anaonetsa cikhulupililo mwa Yehova pamene anapita kukazonda Dziko Lolonjezedwa. M’kupita kwa nthawi, cikhulupililo cao cinali kukulilakulila nthawi zonse akaona mmene Yehova anali kuwathandizila. Conco, Yoswa anauza ana a Isiraeli motsimikiza kuti: “Pamau onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwanilitsidwe.” Kenako, iye anawauzanso kuti: “Tsopano opani Yehova ndi kum’tumikila mosalakwitsa ndiponso mokhulupilika.” Anaonjezelanso kuti: “Koma ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikila Yehova.” (Yoswa 23:14; 24:14, 15) Ngati tikhulupilila Yehova ndi kuona mmene amatithandizila, cikhulupililo cathu cimalimba kwambili.—Salimo 34:8.

MMENE TINGAONETSELE CIKHULUPILILO CATHU

12. Timaonetsa bwanji kuti tili ndi cikhulupililo colimba?

12 Tingaonetse bwanji kuti tili ndi cikhulupililo colimba? Wophunzila Yakobo anakamba kuti: “Ndikuonetsa cikhulupililo canga mwa nchito [zanga].” (Yakobo 2:18) Zocita zathu zimaonetsa ngati tili ndi cikhulupililo colimba. Tiyeni tione mmene tingacitile zimenezi.

Amene amacita zimene angathe muutumiki amaonetsa kuti ali ndi cikhulupililo colimba (Onani ndime 13)

13. Kodi kulalikila kumaonetsa bwanji kuti tili ndi cikhulupililo?

13 Kulalikila ndi njila yabwino koposa imene tingaonetsele kuti tili ndi cikhulupililo. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti tikamalalikila, timaonetsa kuti tikukhulupilila kuti mapeto ali pafupi, ndiponso kuti “sadzacedwa.” (Habakuku 2:3) Kuti tidziŵe ngati cikhulupililo cathu n’colimba, tifunika kudzifunsa kuti: ‘Kodi nchito yolalikila ndi yofunika kwambili kwa ine? Kodi ndimayesetsa kuuzako ena za Mulungu? Kodi ndimafunafuna mipata imene ndingaonjezele utumiki wanga kwa Yehova?’ (2 Akorinto 13:5) Tiyeni tionetse kuti cikhulupililo cathu n’colimba mwa ‘kulengeza poyela za cipulumutso,’ kumatanthauza kulalikila uthenga wabwino.—Ŵelengani Aroma 10:10.

14, 15. (a) Tingaonetse bwanji cikhulupililo pa umoyo wathu? (b) Fotokozani cocika ca banja lina limene linaonetsa cikhulupililo colimba.

14 Tikamapilila mavuto amene tikumana nao m’dziko lino, timaonetsanso kuti tili ndi cikhulupililo mwa Yehova. Tikadwala, tikataya mtima, tikakhala ndi cisoni, tikasauka, kapena tikakumana ndi mavuto ena, tiyenela kukhala ndi cikhulupililo cakuti Yehova ndi Yesu adzatithandiza “pa nthawi imene tikufunika thandizo.” (Aheberi 4:16) Timaonetsanso kuti tili ndi cikhulupililo mwa Yehova pamene tim’pempha thandizo. Yesu anakamba kuti tiyenela kupempha Yehova kutipatsa cakudya cimene tifunikila tsiku lililonse. (Luka 11:3) Nkhani za m’Baibulo zimaonetsa kuti Yehova akhoza kutipatsa ciliconse cimene tifuna. Mwacitsanzo, pamene mu Isiraeli munali cilala cacikulu, Yehova anali kupatsa Eliya cakudya ndi madzi. Baibulo limakamba kuti “akhwangwala ankamubweletsela mkate ndi nyama m’maŵa ndi madzulo, ndipo iye ankamwa madzi mumtsinje umene unali m’cigwaco.” (1 Mafumu 17:3-6) Ifenso tili ndi cikhulupililo cakuti Yehova adzatipatsa zimene tifunikila.

Timaonetsa kuti tili ndi cikhulupililo tikamapilila mavuto amene tikumana nao (Onani ndime 14)

15 Ndife otsimikiza mtima kuti ngati titsatila zimene Baibulo limakamba, tikhoza kusamalila zosoŵa za banja lathu. Mlongo wina wa ku Asia, dzina lake Rebecca, anakamba kuti iye ndi banja lake anatsatila mfundo ya pa Mateyu 6:33 ndi ya pa Miyambo 10:4. Iye anakamba kuti mwamuna wake anaona kuti nchito yake inali kuika ubwenzi wao ndi Yehova pa ngozi. Conco, mwamuna wakeyo anasiya nchito. Iwo anayamba kugulitsa zakudya kuti azisamalila ana ao anai. Anali kugwila nchitoyi mwakhama cakuti anali kupeza ndalama zokwanila kuti asamalile banja lao. Rebecca anati: “Tinaona kuti Yehova sanatisiye. Sitinasoŵepo cakudya.” Kodi muli ndi cocitika cofanana ndi cimeneci cimene cinalimbitsa cikhulupililo canu?

Ndife otsimikiza mtima kuti ngati titsatila zimene Baibulo limakamba, tikhoza kusamalila zosoŵa za banja lathu

16. Kodi kukhulupilila Mulungu kuli ndi phindu lotani?

16 Tisakaikile kuti ngati titsatila malangizo a Yehova, iye adzatithandiza. Paulo anagwila mau a Habakuku akuti: “Wolungama adzakhala ndi moyo mwa cikhulupililo cake.” (Agalatiya 3:11; Habakuku 2:4) Ndiye cifukwa cake tifunika kukhala ndi cikhulupililo colimba mwa Iye amene angatithandizedi. Paulo amatikumbutsa kuti Mulungu ndi “amene angathe kucita zazikulu kwambili kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza, malinga ndi mphamvu yake imene ikugwila nchito mwa ife.” (Aefeso 3:20) Atumiki a Yehova amacita zimene angathe kuti acite cifuno ca Mulungu, koma amadziŵa kuti zinthu zina sangakwanitse. Ndife oyamikila kuti Mulungu ali nafe ndipo amatidalitsa cifukwa ca kuyesayesa kwathu.

MULUNGU AMAYANKHA TIKAPEMPHA CIKHULUPILILO

17. (a) Kodi Yesu anayankha bwanji pempho la atumwi ake? (b) N’cifukwa ciani tiyenela kuyembekezela kuti Yehova adzayankha tikapempha cikhulupililo coonjezeleka?

17 Pa mfundo zimene takambilana, mwina tikumva mmene atumwi anamvelela pamene anapempha Yesu kuti: “Tionjezeleni cikhulupililo.” (Luka 17:5) Yesu anayankha atumwi ake m’njila yapadela kwambili pa Pentekosite mu 33 C.E. Iwo analandila mzimu woyela ndipo anamvetsa mozama cifunilo ca Mulungu. Zimenezi zinalimbitsa cikhulupililo cao. Kodi panakhala zotsatilapo zotani? Iwo anayamba nchito yaikulu yolalikila panthawi imeneyo. (Akolose 1:23) Kodi tiyenela kuyembekezela kuti Mulungu adzatiyankha tikapempha cikhulupililo coonjezeleka? Yehova akutilonjeza kuti adzatiyankha ngati “tingamupemphe mogwilizana ndi cifunilo cake.”—1 Yohane 5:14.

18. Kodi Yehova amadalitsa bwanji anthu amene amalimbitsa cikhulupililo cao?

18 Yehova adzakondwela ngati tim’khulupilila ndi mtima wonse. Iye adzayankha pemphelo lathu lopempha cikhulupililo coonjezeleka, cikhulupililo cathu cidzalimba kwambili, ndipo tidzakhala “oyenelela Ufumu wa Mulungu.”—2 Atesalonika 1:3, 5.

^ par. 4 Onani zitsanzo zina za anthu amenewa monga Lillian Gobitas Klose, mu Galamukani! ya Cingelezi ya July 22, 1993, Feliks Borys, February 22, 1994, ndi Josephine Elias mu Galamukani! ya Chichewa ya September 2009.