Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tumikilani Yehova Popanda Cosokoneza

Tumikilani Yehova Popanda Cosokoneza

“Mariya . . . [anali kumvetsela mau a Yesu] . . . Marita anatanganidwa ndi nchito zoculuka.”—LUKA 10:39, 40.

NYIMBO: 94, 134

1, 2. N’cifukwa ciani Yesu anali kum’konda Marita? Nanga n’ciani cimene iye anacita cimene cionetsa kuti anali wopanda ungwilo?

MUKAGANIZILA za Marita mlongo wa Lazaro, kodi muona kuti iye anali munthu wotani? Baibulo limaonetsa kuti Yesu anali kukonda Marita, ndipo anali mabwenzi abwino. Komabe, iye sanali mkazi yekha amene Yesu anali kukonda ndi kulemekeza. Mwacitsanzo, Mariya mlongo wa Marita, analinso bwenzi la pamtima la Yesu. Yesu anali kukondanso Mariya amai ake. (Yohane 11:5; 19:25-27) Nanga n’cifukwa ciani Yesu anali kum’konda Marita?

2 Yesu anali kum’konda Marita cifukwa cakuti anali wokoma mtima, woceleza, ndi wolimbikila nchito. Koma koposa zonse, Yesu anali kum’konda cifukwa cakuti anali ndi cikhulupililo colimba. Iye anali kukhulupilila zonse zimene Yesu anali kuphunzitsa, ndipo sanakaikile kuti anali Mesiya wolonjezedwa. (Yohane 11:21-27) Ngakhale n’conco, Marita anali wopanda ungwilo. Nayenso anali kulakwitsa monga mmene ife timacitila. Mwacitsanzo, nthawi ina pamene Yesu anapita kukawacezela, Marita anakhumudwa ndi mlongo wake Mariya. Iye anauza Yesu kuti am’langize. Marita anati: “Ambuye, kodi sizikukukhudzani kuti m’bale wangayu wandilekelela ndekha nchito? Tamuuzani kuti andithandize.” (Ŵelengani Luka 10:38-42.) N’cifukwa ciani Marita anakamba conco? Nanga tiphunzilapo ciani pa zimene Yesu anamuyankha?

MARITA ANATANGWANIKA

3, 4. N’ciani cimene Mariya anacita cimene Yesu anayamikila? Nanga Marita anaphunzilapo ciani? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

3 Yesu anayamikila kwambili kuti Marita ndi Mariya anamuitana kunyumba kwao. Ndipo iye anafuna kutengelapo mwai wakuti awaphunzitse coonadi ca mtengo wapatali. Mariya mwamsanga anakhala pafupi ndi Yesu, “n’kumamvetsela mau [ake].” Iye anafuna kuphunzila zoonjezeleka kwa Mphunzitsi Wamkulu. Marita nayenso akanasankha kumvetsela kwa Yesu, akanayamikilidwa cifukwa cosiya zimene anali kucita kuti amvetsele kwa iye.

4 Koma Marita anali wotangwanika. Iye anali kukonzela Yesu cakudya capadela, ndi kucita zinthu zambili kuti maceza ao akhale osangalatsa. Ataona kuti Mariya wamulekelela, Marita anakhumudwa cakuti anadandaulila Yesu. Poona kuti Marita anali ndi zocita zambili, Yesu mokoma mtima anamuuza kuti: “Marita, Marita, ukuda nkhawa ndiponso kutanganidwa ndi zinthu zambili.” Anamuuzanso kuti zikanakhala bwino ngati iye akanakonza cakudya cocepa cabe. Motelo, Yesu anayamikila Mariya cifukwa comvetsela bwinobwino kwa iye. Iye anati: “Kumbali yake, Mariya wasankha cinthu cabwino kwambili, ndipo sadzalandidwa cinthu cimeneci.” Mariya ayenela kuti anaiŵala zimene anadya patsikulo. Koma mosakaikila, iye sanaiŵale zimene anaphunzila kwa Yesu, ndiponso ciyamikilo cake. Pambuyo pa zaka zoposa 60, mtumwi Yohane analemba kuti: “Yesu anali kukonda . . . Marita ndi m’bale wake.” (Yohane 11:5) Mau amenewa aonetsa kuti Marita anamvela uphungu umene Yesu anamupatsa mwacikondi, ndipo anatumikila Yehova mokhulupilika kwa moyo wake wonse.

5. N’cifukwa ciani n’kovuta masiku ano kuika maganizo athu pa zinthu zofunika kwambili? Tidzakambilana funso liti?

5 Masiku ano, pali zinthu zambili zimene zingatisokoneze potumikila Yehova kuposa mmene zinalili m’nthawi za m’Baibulo. Nsanja ya Mlonda yacingelezi ya September 15, 1958, inacenjeza abale ndi alongo kuti sayenela kulola zipangizo zamakono kuwasokoneza potumikila Yehova. Ngakhale panthawiyo, zioneka kuti tsiku lililonse panali kutuluka zinthu zatsopano. Zinthu monga magazini okopa, mawailesi, mafilimu, ndi ma TV, zinali zofala kwambili. Nsanja imeneyo inakamba kuti pamene mapeto a dzikoli ali pafupi kwambili, “padzakhala zinthu zambili zosokoneza.” Kuposa kale, masiku ano pali zinthu zambili zimene zingatisokoneze. Kodi tiyenela kucita ciani kuti titengele citsanzo ca Mariya ndi kuika maganizo athu pa kutumikila Yehova?

MUSAGWILITSILE NCHITO DZIKOLI MOKWANILA

6. Kodi anthu a Yehova aseŵenzetsa motani zipangizo zamakono?

6 Anthu a Yehova akhala akuseŵenzetsa zipangizo zamakono kuti alalikile uthenga wabwino. Mwacitsanzo, nkhondo yoyamba ya padziko lonse isanayambe komanso itayamba, io anali kuonetsa “Seŵelo la pa Kanema la Cilengedwe.” Iwo analalikila anthu mamiliyoni m’maiko ambili pogwilitsila nchito zithunzi zokongola za seŵelo limeneli ndi mau ake. Kumapeto kwa seŵelo limeneli, anali kuonetsa mtendele umene udzakhalako Yesu Kristu akadzayamba kulamulila dzikoli. M’kupita kwa nthawi, anthu a Yehova anayamba kufalitsa uthenga wa Ufumu padzilo lonse kupitila pa wailesi. Masiku ano, timagwilitsila nchito makompyuta ndi Intaneti kulalikila anthu kulikonse, ngakhale m’madela ovuta kufikako.

Musalole kuti zinthu zosafunika zikusokonezeni kutumikila Yehova (Onani ndime 7)

7. (a) N’cifukwa ciani ndi ngozi kugwilitsila nchito dzikoli mokwanila? (b) Ndi zinthu ziti zimene tiyenela kusamala nazo? (Onani mau a munsi.)

7 Baibulo limaticenjeza kuti sitiyenela kugwilitsa nchito dzikoli mokwanila. Izi ziphatikizapo kutaila nthawi yathu yambili pa zinthu za m’dzikoli. (Ŵelengani 1 Akorinto 7:29-31.) Zina mwa zinthu zimenezi si zoipa iyai, koma zinthuzo zingatidyele nthawi yathu. Mwacitsanzo, ena a ife mwina timakonda kuŵelenga mabuku, kuonelela TV, kukaona malo osangalatsa, kugula zinthu, ndi kufufuza zipangizo zatsopano kapena zinthu zapamwamba. Ambili amakonda kuceza pa Intaneti, kutuma mauthenga, kumvetsela nyuzi kapena kufufuza za maseŵela. Koma ena angafike pozoloŵela kwambili kucita zinthu zimenezi. * (Onani mau a munsi.) (Mlaliki 3:1, 6) Ngati titaila nthawi yambili pa zinthu zosafunika, tingalephele kuika maganizo athu pa zinthu zofunika kwambili, zimene ndi kulambila Yehova.—Ŵelengani Aefeso 5:15-17.

8. N’cifukwa ciani sitifunika kukonda zinthu za m’dzikoli?

8 Satana amayesetsa kuti atikope ndi zinthu za m’dzikoli, ndiponso kuti atisokoneze potumikila Yehova. Iye anacita zimenezi m’nthawi ya atumwi. Masiku ano amacitanso cimodzimodzi, ndipo wacita kunyanyilatu. (2 Timoteyo 4:10) Conco, tiyenela kupitiliza kudzifufuza mmene timaonela zinthu za m’dzikoli, ndi kusintha ngati pafunika kutelo. Baibulo limatiuza kuti sitiyenela kukonda zinthu za m’dzikoli. M’malo mwake, tiyenela kukulitsa cikondi cathu pa Yehova. Tikacita zimenezi, sizidzativuta kumvela Yehova ndi kukhala naye pa ubwenzi.—1 Yohane 2:15-17.

MUZIIKA MAGANIZO ANU PA ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBILI

9. Kodi Yesu anaphunzitsa ophunzila ake kuika maganizo ao pa ciani? Nanga iye anapeleka citsanzo cotani?

9 Yesu anaphunzitsa ophunzila ake kuti sayenela kulola zinthu zambili kuwasokoneza, monga mmene anauzila Marita mokoma mtima. Iye anawalimbikitsa kuika maganizo ao pa kutumikila Yehova, ndi kuika Ufumu wake pamalo oyamba. (Ŵelengani Mateyu 6:22, 33.) Yesu anapekeka citsanzo cabwino kwambili pankhaniyi. Iye analibe zinthu zambili. Analibe nyumba kapena malo.—Luka 9:58; 19:33-35.

10. Ndi citsanzo cabwino citi cimene Yesu anapeleka kwa ife tonse?

10 Yesu sanalole cinthu ciliconse kum’sokoneza kulalikila. Mwacitsanzo, atayamba kulalikila mumzinda wa Kaperenao, anthu ambili anali kufuna kuti Yesu akhale nthawi yaitali mumzinda wao. Kodi iye anacita ciani? Anaika maganizo ake pa utumiki. Iye anakamba kuti: “Ndiyenela kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, cifukwa ndi zimene anandituma kudzacita.” (Luka 4:42-44) Yesu anali kuyenda mitunda yaitali kukalalikila uthenga wabwino, ndi kuphunzitsa anthu ambili mmene angathele. Iye anali wangwilo. Ngakhale n’conco, anali kutopa ndipo anafunikila kupumula cifukwa cogwila nchito mwakhama.—Luka 8:23; Yohane 4:6.

Yesu anatiphunzitsa kuti ngati tiika maganizo athu pa kukhala ndi zinthu zambili, zingatisokoneze kutumikila Mulungu

11. N’ciani cimene Yesu anacita pamene munthu wina anam’pempha kuti amuthandize pa vuto lake? Ndi mfundo yotani imene Yesu anaphunzitsa ophunzila ake?

11 Pa nthawi ina, pamene Yesu anali kuphunzitsa ophunzila ake mfundo yofunika, munthu wina anam’dula mau mwa kunena kuti: “Mphunzitsi, mundiuzileko m’bale wanga kuti andigaŵileko colowa.” Yesu sanathetse vuto la munthuyo. Iye sanalole kuti zimenezi zim’sokoneze kuphunzitsa ophunzila ake. Ndipo iye anagwilitsila nchito mpata umenewu kuwaphunzitsa kuti ngati aika maganizo ao pa kukhala ndi zinthu zambili, zingawasokoneze kutumikila Mulungu.—Luka 12:13-15.

12, 13. (a) Kodi Yesu anacita ciani cimene cinacititsa cidwi anthu Acigiriki ku Yerusalemu? (b) Yesu anacita ciani Filipo atam’pempha kuti aonane ndi anthuwo?

12 Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, zinthu zinali zovuta kwambili pa umoyo wake. (Mateyu 26:38; Yohane 12:27) Iye anadziŵa kuti adzavutika kwambili mpaka kufa. Anadziŵanso kuti anafunika kucita nchito yaikulu asanaphedwe. Mwacitsanzo, pa Sondo pa Nisani 9, Yesu analoŵa mu Yerusalemu atakwela pa bulu. Gulu la anthu linam’landila monga Mfumu yao. (Luka 19:38) Tsiku lotsatila, Yesu molimba mtima anathamangitsa anthu adyela amene anali kucita malonda mokwela mtengo m’kacisi ndi kubela anthu.—Luka 19:45, 46.

13 Anthu Acigiriki amene anabwela ku Yerusalemu kudzacita cikondwelelo ca Pasika, anaona zimene Yesu anacita cakuti anacita cidwi kwambili. Conco, anapempha mtumwi Filipo kuti ngati n’kotheka, aonane ndi Yesu. Yesu sanali kufuna kupeza anthu amene adzam’cilikiza ndi kumuteteza kwa adani ake. Iye anali kudziŵa zinthu zimene zinali zofunika kwambili. Iye anaika maganizo ake pa kucita cifunilo ca Mulungu, cimene ndi kupeleka moyo wake nsembe. Conco, anakumbutsa ophunzila ake kuti watsala pang’ono kuphedwa. Anawakumbutsanso kuti onse omutsatila afunika kudzipeleka ndi mtima wonse. Iye anati: “Aliyense wokonda moyo wake akuuwononga, koma wodana ndi moyo wake m’dziko lino akuusungila moyo wosatha.” Koma Yesu anawalonjezanso kuti ‘Atate adzalemekeza’ otsatila ake ndi kuwapatsa moyo wosatha. Filipo anauza anthu Acigiriki uthenga wolimbikitsa umenewu.—Yohane 12:20-26.

14. Kodi Yesu anali kuonetsetsa kuti ali ndi nthawi yocita ciani ngakhale kuti anaika nchito yolalikila pamalo oyamba?

14 Pamene Yesu anali padziko lapansi, nchito yake yaikulu inali kulalikila uthenga wabwino. Koma ngakhale kuti anali kuika maganizo ake pa kulalikila, sikuti iye nthawi zonse anali kungoganizila za ulaliki. Mwacitsanzo, iye anapita ku cikwati kumene anasandutsa madzi kukhala vinyo wabwino kwambili. (Yohane 2:2, 6-10) Iye analinso kupita kukaceza kunyumba za mabwenzi ake, ndi kwa ena amene anali kucita cidwi ndi uthenga wabwino. (Luka 5:29; Yohane 12:2) Koposa zonse, Yesu anali kupeza nthawi yopemphela, yosinkhasinkha, ndiponso yopumula.—Mateyu 14:23; Maliko 1:35; 6:31, 32.

‘VULANI COLEMELA CILICONSE’

15. Kodi mtumwi Paulo anakamba kuti Akristu afunika kucita ciani? Nanga iye anapeleka bwanji citsanzo cabwino?

15 Mtumwi Paulo anakamba kuti Akristu ali ngati anthu ocita mpikisano wothamanga. Kuti apambane mpikisano umenewu, io ayenela kucotsa ciliconse cimene cingawabweze m’mbuyo kapena kuwalepheletsa kuthamanga. (Ŵelengani Aheberi 12:1.) Paulo anapeleka citsanzo cabwino pankhaniyi. Akanafuna, iye akanakhala wacuma ndi wochuka popeza anali mtsogoleli wacipembedzo caciyuda. Koma anasiya nchito yake imeneyo kuti aike maganizo ake pa “zinthu zofunika kwambili.” Iye anali kulalikila mwakhama kwambili, ndipo anayenda m’madela ambili monga ku Siriya, Asia Minor, Makedoniya, ndi Yudeya. Paulo anaika maganizo ake pa mphoto yake ya moyo wosatha kumwamba. Iye anati: “Ndikuiŵala zinthu zakumbuyo ndipo ndikuyesetsa kuti ndikapeze zakutsogolo. Ndikuyesetsa kucita zimenezi mpaka nditapeza mphoto.” (Afilipi 1:10; 3:8, 13, 14) Paulo analibe mkazi. Zimenezi zinapangitsa kuti iye ‘atumikile Ambuye nthawi zonse popanda cododometsa.’—1 Akorinto 7:32-35.

Paulo anasiya nchito yake kuti aike maganizo ake pa “zinthu zofunika kwambili”

16, 17. Kaya tili m’cikwati kapena ai, kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Paulo? Kodi Mark ndi Claire anacita bwanji zimenezi?

16 Mofanana ndi Paulo, atumiki ena a Yehova masiku ano asankha kusaloŵa m’banja, n’colinga cakuti acite zambili mu utumiki wa Yehova. (Mateyu 19:11, 12) Anthu amene sali m’cikwati ali ndi maudindo ocepa kuposa anthu a m’cikwati. Komabe, kaya tili m’cikwati kapena ai, tonse ‘tingavule colemela ciliconse’ cimene cingatisokoneze potumikila Yehova. Tingafunike kusiya zizolowezi zathu zimene zingatitaitse nthawi yocita zambili mu utumiki wa Yehova.

17 Mwacitsanzo, Mark ndi Claire, amene anakulila ku Wales, anayamba upainiya atatsiliza sukulu. Ataloŵa m’banja, io anapitiliza kucita upainiya. Koma io anali kufuna kuonjezelanso utumiki wao. Mark anafotokoza kuti: “Tinayamba kukhala ndi umoyo wosalila zambili mwa kusiya nyumba yathu ndi nchito yaganyu n’colinga cakuti tiyambe kuthandiza pa nchito zomanga kumaiko ena.” Kwa zaka 20 zapitazo, io akhala akuyenda m’maiko ambili a mu Africa kuthandiza pa nchito yomanga Nyumba za Ufumu. Ngakhale kuti io amapeza ndalama zocepa, Yehova amawasamalila nthawi zonse. Claire anati: “Tili ndi cimwemwe cacikulu cifukwa cotumikila Yehova tsiku lililonse. Tapeza mabwenzi ambili, ndipo sitisoŵa kanthu kalikonse. Zinthu zocepa zimene tadzimana sitingaziyelekezele ndi cimwemwe cimene cimabwela cifukwa cotumikila Yehova nthawi zonse.” Atumiki anthawi zonse ambili naonso amamva cimodzimodzi. *—Onani mau a munsi.

18. Kodi tiyenela kudzifunsa ciani?

18 Kodi inu muona kuti mungakwanitse kucita zambili potumikila Yehova? Kodi pali zinthu zimene zimakusokonezani kucita zinthu zofunika kwambili? Ngati n’conco, kodi mungacite ciani? Mwina mufunika kuongolela mmene mumaphunzilila Baibulo. Nkhani yotsatila idzafotokoza mmene mungacitile zimenezi.

^ par. 7 Onani nkhani yakuti “Munthu Amene Sadziŵa Zinthu Amakhulupilila Mau Alionse.”

^ par. 17 Mungaonenso mbili ya moyo wa Hadyn ndi Melody Sanderson pa mutu wakuti “Kudziŵa ndi Kuchita Chabwino,” mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 2006. Iwo anali ndi bizinesi imene inali kuyenda bwino m’dziko la Australia. Komabe, anasiya bizinesi imeneyo kuti ayambe utumiki wa nthawi zonse. Ŵelengani kuti mudziŵe zimene zinawacitikila pambuyo pakuti ndalama zao zatha, pamene anali kutumikila monga amishonale ku India.