Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

N’ciani cimene akatswili ofufuza zinthu zakale apeza cimene cionetsa kuti mzinda wa Yeriko unaonongedwa m’nthawi yocepa?

Lemba la Yoswa 6:10-15, 20 limakamba kuti asilikali a Isiraeli anazungulila mzinda wa Yeriko kamodzi pa tsiku kwa masiku 6. Pa tsiku la 7, asilikaliwo anazungulila mzindawo nthawi zokwana 7. Ndiyeno Mulungu anacititsa kuti mpanda wolimba wa Yeriko ugwe, ndipo Aisiraeli analanda mzindawo. Kodi akatswili ofufuza zinthu zakale apeza umboni uliwonse wosonyeza kuti mzindawo unagonjetsedwa m’nthawi yocepa, monga mmene Baibulo limanenela?

M’nthawi zakale, asilikali anali kuzungulila mpanda wa mzinda kuti aulande. Ngati asilikali azungulila mzindawo kwa nthawi yaitali, anthu mumzindawo anali kukakamizika kudya zakudya zimene anasunga. Ndiyeno asilikali akalanda mzinda, anali kutenga ciliconse cimene afuna, kuphatikizapo cakudya ciliconse cimene catsala. Ndiye cifukwa cake akatswili ofufuza zinthu zakale anapeza cakudya cocepa m’mabwinja a mizinda ya ku Palesitina imene inagongetsedwa mwa njila imeneyi, ndipo m’mizinda ina sanapezemo cakudya ciliconse. Koma zimene anapeza m’mabwinja a Yeriko n’zosiyana ndi zimenezi. Buku lina lofotokoza zinthu zakale limati: “M’mabwinja a Yeriko anapezamo zinthu zambili zoumba. Koma kuonjezela pamenepo, anapezamonso zakudya zambili.” Bukuli limanenanso kuti: “N’zodabwitsa kuti m’mabwinja a Yeriko anapezamo zakudya zambili.”—Biblical Archaeology Review.

Baibulo limakamba kuti Aisiraeli sanatenge cakudya ciliconse mumzinda wa Yeriko cifukwa Yehova anawalamula kuti sayenela kutelo. (Yoswa 6:17, 18) Limakambanso kuti Aisilaeli anaononga mzinda wa Yeriko m’nyengo yokolola, nthawi imene mumzindawo munali zakudya zambili. (Yoswa 3:15-17; 5:10) Monga mmene tanenela, mumzinda wa Yeriko munapezeka zakudya zambili. Izi zionetsa kuti mzindawo unaonongedwadi m’kanthawi kocepa monga mmene Baibulo limanenela.