Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Phunzitsani Ana Anu Kutumikila Yehova

Phunzitsani Ana Anu Kutumikila Yehova

“Lolani kuti munthu wa Mulungu woona . . . adzatilangize zoyenela kucita ndi mwana amene adzabadweyo.”—OWERUZA 13:8.

NYIMBO: 88, 120

1. Kodi Manowa anacita ciani atamva kuti adzakhala kholo?

MANOWA ndi mkazi wake anali kuganiza kuti sangakhale ndi ana. Ndiyeno tsiku lina, mngelo wa Yehova anauza mkazi wa Manowa kuti adzakhala ndi mwana wamwamuna. Zimenezi zinali zosangalatsa kwambili. Pamene Manowa anauzidwa uthengawo ndi mkazi wake, iye anakondwela kwambili. Komabe, anaganizilanso zimene Yehova anali kuyembekezela kuti iye acite monga kholo. Kodi iye ndi mkazi wake akanaphunzitsa bwanji mwana wao kukonda Yehova ndi kum’tumikila popeza anthu ambili mu Isiraeli anali kucita zinthu zoipa pa nthawiyo? Manowa anapempha Yehova kuti atumizenso mngelo uja. Iye anati: “Lolani kuti munthu wa Mulungu woona amene munam’tuma, abwelenso kuti adzatilangize zoyenela kucita ndi mwana amene adzabadweyo.”—Oweruza 13:1-8.

2. N’ciani cimene muyenela kuphunzitsa ana anu? Nanga mungacite bwanji zimenezo? (Onani bokosi lakuti “Maphunzilo Anu a Baibulo Ofunika Kwambili.”)

2 Ngati ndinu kholo, mwacionekele mukumvetsa mmene Manowa anamvelela. Inunso muli ndi udindo wothandiza ana anu kudziŵa Yehova ndi kum’konda. (Miyambo 1:8) Pa kulambila kwanu kwa pabanja, mungathandize ana anu kupitiliza kuphunzila za Yehova ndi Baibulo. Kukamba zoona, mufunika kucita zambili kuposa kungophunzila Baibulo ndi ana anu mlungu uliwonse. (Ŵelengani Deuteronomo 6:6-9.) N’ciani cina cingakuthandizeni kuwaphunzitsa kukonda Yehova ndi kum’tumikila? M’nkhani ino, tikambilana citsanzo ca Yesu. Ngakhale kuti sanali kholo, mungaphunzile kwa iye poona mmene anali kuphunzitsila otsatila ake. Yesu anali kuwakonda ophunzila ake ndipo analinso wodzicepetsa. Komanso anali wozindikila, kutanthauza kuti anali kudziŵa mmene ophunzila ake anali kumvelela ndi mmene angawathandizile. Tiyeni tione mmene tingatengele citsanzo ca Yesu.

MUZIWAKONDA ANA ANU

3. Kodi ophunzila a Yesu anadziŵa bwanji kuti iye anali kuwakonda?

3 Yesu anali kuuza ophunzila ake mobwelezabweleza kuti anali kuwakonda. (Ŵelengani Yohane 15:9.) Analinso kupeza nthawi yambili yoceza nao. (Maliko 6:31, 32; Yohane 2:2; 21:12, 13) Yesu sanali cabe mphunzitsi wao, koma analinso mnzao wapamtima. Conco, ophunzila ake sanakaikile kuti iye anali kuwakonda. Kodi mungaphunzile ciani kwa Yesu?

4. Mungaonetse bwanji ana anu kuti mumawakonda? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

4 Muziwauza ana anu kuti mumawakonda, ndipo zocita zanu zizionetsa kuti mumawaona kukhala ofunika kwambili. (Miyambo 4:3; Tito 2:4) Samuel, amene amakhala ku Australia, anakamba kuti: “Pamene ndinali wamng’ono, Atate anali kundiŵelengela Buku Langa la Nkhani za M’baibo usiku uliwonse. Anali kuyankha mafunso amene ndinali kuwafunsa. Analinso kundikumbatila ndi kundipsompsona ndisanagone. Ndinadabwa kwambili kudziŵa kuti Atate analeledwa m’banja limene kukumbatilana ndi kupsompsonana sizinali zofala. Koma anayesetsa kundionetsa cikondi mwa njila imeneyo. Pa cifukwa cimeneci, ndinayamba kuwakonda kwambili, ndipo ndinali kudzimva kukhala wokhutila ndiponso wotetezeka.” Thandizani mwana wanu kudzimva kuti mumam’konda mwa kumuuza nthawi zonse kuti, “Ndimakukonda kwambili.” Muzipeza nthawi yoceza ndi ana anu, kudya nao, kuseŵela nao, kapena kuwakumbatila.

5, 6. (a) N’ciani cimene Yesu anacita cifukwa cokonda ophunzila ake? (b) Kodi muyenela kuwalanga bwanji ana anu?

5 Yesu anakamba kuti: “Onse amene ndimawakonda, ndimawadzudzula ndi kuwalanga.” * (Onani mau a munsi.) (Chivumbulutso 3:19) Mwacitsanzo, nthawi zambili ophunzila ake anali kukangana za amene anali wamkulu pakati pao. Yesu sananyalanyaze vutolo. M’malomwake, iye moleza mtima anawalangiza mobwelezabweleza. Anali kucita zimenezi mokoma mtima, ndipo anali kuyembekeza nthawi yabwino ndi kupeza malo oyenelela kuti awaongolele.—Maliko 9:33-37.

Pezani nthawi yabwino ndi malo oyenelela kuti mulangize ana anu, ndipo citani zimenezo mokoma mtima

6 Makolo amene amakonda ana ao ayenela kuwalanga akalakwitsa. Nthawi zina kungowafotokozela cifukwa cake zinthu zina n’zabwino zina n’zoipa n’kokwanila. Koma bwanji ngati sakukumvelani? (Miyambo 22:15) Tengelani citsanzo ca Yesu. Pitilizani kuwalanga moleza mtima mwa kuwatsogolela, kuwaphunzitsa, ndi kuwaongolela. Pezani nthawi yabwino ndi malo oyenelela kuti muwalangize, ndipo citani zimenezo mokoma mtima. Mlongo wina wa ku South Africa dzina lake Elaine amakumbukila mmene makolo ake anali kumulangizila. Nthawi zonse anali kumuuza zimene ayenela kucita. Makolo ake akamuuza kuti amupatsa cilango cifukwa colakwitsa zina zake, anali kuonetsetsa kuti amupatsadi cilangoco. Mlongoyu anati: “Makolo anga sanandilangepo ali okwiya kapena popanda kundiuza cifukwa cake akundilanga.” Cifukwa ca ici, mlongoyu anadziŵa kuti makolo ake anali kumukonda kwambili.

KHALANI ODZICEPETSA

7, 8. (a) Kodi ophunzila a Yesu anaphunzilapo ciani pa pemphelo lake? (b) Nanga mapemphelo anu angaphunzitse bwanji ana anu kudalila Mulungu?

7 Yesu atatsala pang’ono kugwidwa ndi kuphedwa, anapempha Atate wake kuti: “Abba, Atate, zinthu zonse n’zotheka kwa inu. Ndicotseleni kapu iyi. Komatu osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.” * (Onani mau a munsi.) (Maliko 14:36) Ganizilani mmene ophunzila a Yesu anamvelela pamene anamva, kapena kudziŵa za pemphelo lake. Iwo anadziŵa kuti Yesu anali kupemphabe Atate wake kuti amuthandize ngakhale kuti anali wangwilo. Conco, ophunzilawo anaphunzilapo kuti naonso anayenela kukhala odzicepetsa ndi kudalila Yehova.

Ana anu akamakumvelani mukupempha Yehova kuti akuthandizeni, amaphunzila kuti naonso afunika kudalila Yehova

8 Ana anu angaphunzile zambili m’mapemphelo amene mumapeleka. N’zoona kuti simupemphela n’colinga cakuti muphunzitse ana anu. Koma ngati mumapemphela nao pamodzi, ana anu angaphunzile kudalila Yehova. Mukamapemphela, muzipempha kuti Yehova athandize ana anu ndiponso kuti akuthandizeni inuyo panokha. Mlongo wina dzina lake Ana, amene amakhala ku Brazil, anati: “Panthawi ya mavuto, monga pamene agogo anali kudwala, makolo anga anali kupempha Yehova kuti awapatse mphamvu kuti apilile mavutowo. Ndiponso anali kupempha nzelu kuti apange zosankha zabwino. Ngakhale pa mavuto aakulu, anali kungozisiya m’manja mwa Yehova. Cifukwa ca zimenezo, ndinaphunzila kudalila Yehova.” Ana anu akamakumvelani mukupempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala olimba mtima kuti mulalikile anansi anu, kapena kupempha abwana anu kuti akuloleni kupita ku msonkhano wacigawo, adzadziŵa kuti mumadalila Yehova, ndipo naonso adzacita cimodzimodzi.

9. (a) Kodi Yesu anaphunzitsa bwanji ophunzila ake kukhala odzicepetsa ndi kupewa kudzikonda? (b) N’ciani cimene ana anu angaphunzile ngati ndinu wodzicepetsa ndipo mumapewa kudzikonda?

9 Yesu anauza ophunzila ake kuti afunika kukhala odzicepetsa ndi kupewa kudzikonda, ndipo anawapatsa citsanzo pa nkhaniyo. (Ŵelengani Luka 22:27.) Ophunzila ake anaona kuti iye anadzipeleka kuti atumikile Yehova ndi anthu, ndipo naonso anaphunzila kucita cimodzimodzi. Nanunso mungaphunzitse ana anu mwa citsanzo canu cabwino. Mlongo Debbie, amene ali ndi ana aŵili, anati: “Popeza mwamuna wanga anali mkulu, sindinali kucita nsanje ngati akuceza ndi ena mumpingo. Ndinali kudziŵa kuti akhoza kutisamalila nthawi ina iliyonse.” (1 Timoteyo 3:4, 5) Kodi citsanzo ca mlongo Debbie ndi amuna ake cinathandiza bwanji banja lao? Amuna ake, a Pranas, anakamba kuti ana ao anali kudzipeleka nthawi zonse kuthandiza ena pa misonkhano ikuluikulu. Anali kukhala okondwela nthawi zonse, anapanga mabwenzi abwino, ndiponso anali kukonda kukhala ndi abale ndi alongo. Zotsatilapo zake n’zakuti, tsopano onse m’banjalo akutumikila Yehova muutumiki wa nthawi zonse. Ngati ndinu wodzicepetsa ndipo mumapewa kudzikonda, mumaphunzitsa ana anu kukhala ofunitsitsa kuthandiza ena.

KHALANI OZINDIKILA

10. Kodi Yesu anagwilitsila nchito bwanji luso lozindikila pamene anthu a ku Galileya anapita kukamufunafuna?

10 Yesu anali wozindikila kwambili. Sanali kungoona zimene anthu anali kucita, koma anali kudziŵanso cifukwa cake anthuwo anali kucita zimenezo. Iye anali kudziŵa zimene zinali m’mitima yao. Mwacitsanzo, pa nthawi ina anthu a ku Galileya anapita kukamufunafuna. (Yohane 6:22-24) Iye anadziŵa kuti cifukwa cacikulu cimene io anali kumufunila cinali cakuti awapatse cakudya, osati kuti amve zimene anali kuphunzitsa. (Yohane 2:25) Yesu anali kudziŵa zimene zinali m’mitima yao. Ndiyeno, moleza mtima anawaongolela ndi kuwauza zimene anafunika kucita kuti asinthe maganizo ao.—Ŵelengani Yohane 6:25-27.

Thandizani ana anu kukonda utumiki (Onani ndime 11)

11. (a) Mungadziŵe bwanji mmene ana anu amaonela utumiki? (b) Nanga mungawathandize bwanji kuyamba kukonda utumiki?

11 Ngakhale kuti simungadziŵe zimene zili m’mitima ya anthu, nanunso mungakhale ndi luso lozindikila. Mwacitsanzo, mungayese kudziŵa mmene ana anu amaonela utumiki. Mungadzifunse kuti, ‘Kodi ana anga amakonda utumiki cifukwa cakuti amangofuna kuti tiime pamalo ena ake ndi kuwagulila cakudya kapena zakumwa zozizilitsa kukhosi?’ Ngati mwaona kuti ana anu sakonda kwambili utumiki, athandizeni kuyamba kusangalala ndi utumiki. Mukapita nao muutumiki, apatseni zocita kuti azidzimva kukhala ofunika.

12. (a) N’ciani cimene Yesu anacenjeza ophunzila ake? (b) N’cifukwa ciani ophunzila a Yesu anafunikadi cenjezo limenelo?

12 Kodi Yesu anaonetsanso bwanji kuti ndi wozindikila? Iye anali kudziŵa kuti colakwa cimodzi cikhoza kutsogolela ku cina, mpaka munthu angafike pocita chimo lalikulu. N’cifukwa cake Yesu anacenjeza ophunzila ake za zimenezi. Mwacitsanzo, ophunzila ake anali kudziŵa kuti ciwelewele n’coipa. Koma Yesu anawacenjeza za zimene zingapangitse munthu kucita ciwelewele. Iye anakamba kuti: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wacita naye kale cigololo mumtima mwake. Tsopano ngati diso lako lakumanja limakucimwitsa, ulikolowole ndi kulitaya.” (Mateyu  5:27-29) Ophunzila a Yesu anali kukhala pakati pa Aroma amene anali kukonda kucita zaciwelewele, ndi kuonelela maseŵela a zamalisece amenenso munali mau oipa. Conco, Yesu anacenjeza ophunzila ake mwacikondi kuti afunika kupewa ciliconse cimene cikanawalepheletsa kucita zabwino.

13, 14. Kodi mungaphunzitse bwanji ana anu kupewa zosangulutsa zoipa?

13 Monga kholo, kukhala wozindikila n’kofunika kuti muteteze ana anu kuti asacite ciliconse cimene cingakhumudwitse Yehova. N’zomvetsa cisoni kuti masiku ano, ngakhale ana aang’ono ali pangozi yoonelela zamalisece ndi zinthu zina zoipa. Muyenela kuuza ana anu kuti kuonelela zamalisece n’koipa. Komabe, pali zambili zimene mungacite kuti muwateteze. Dzifunseni kuti: ‘Kodi ana anga amadziŵa cifukwa cake kuonelela zamalisece n’koipa? N’ciani cingawacititse kufuna kuonelela zithunzi zamalisece zimenezo? Kodi ndine womasuka nao cakuti amatha kundiuza ciliconse, ndipo angathe kundipempha thandizo ngati ayesedwa kuonelela zamalisece?’ Ngakhale pamene ana akali aang’ono, mungawauze kuti: “Ukaona ciliconse pa Intaneti cimene cakucititsa kufunitsitsa kuonelela zamalisece, uzindiuza. Usamaope kapena kucita manyazi kupempha thandizo langa. Ndine wofunitsitsa kukuthandiza.”

14 Pamene musankha zosangulutsa, mufunika kusamala kuti mupeleke citsanzo cabwino kwa ana anu. M’bale Pranas, amene tamuchula poyamba, anati: “Ungakambe zinthu zambili kwa ana ako, koma io amangoona zimene umakonda kucita ndipo amatengela zimenezo.” Ngati mumasankha nyimbo, mabuku, ndi mafilimu oyenelela, mumaphunzitsa ana anu kucita cimodzimodzi.—Aroma 2:21-24.

YEHOVA ADZAKUTHANDIZANI

15, 16. (a) N’cifukwa ciani ndinu otsimikiza kuti Yehova adzakuthandizani kuphunzitsa ana anu? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

15 N’ciani cinacitika Manowa atapempha Yehova kuti amuthandize kukhala kholo labwino? “Mulungu woona anamvetsela mau a Manowa.” (Oweruza 13:9) Makolo, nanunso Yehova adzamvetsela mapemphelo anu. Adzakuthandizani kuphunzitsa ana anu. Ndipo adzakuthandizaninso kuonetsa cikondi kwa ana anu, kukhala odzicepetsa, ndiponso ozindikila.

16 Monga mmene Yehova angakuthandizileni kuphunzitsa ana anu akali aang’ono, adzakuthandizaninso kuwaphunzitsa ngakhale atakhala acinyamata. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mmene makhalidwe a Yesu monga cikondi, kudzicepetsa, ndi kuzindikila angakuthandizileni kuphunzitsa ana anu acinyamata kutumikila Yehova.

^ par. 5 Baibulo limaphunzitsa kuti kulanga kumatanthauza kuphunzitsa, kutsogolela, kuongolela, ndiponso nthawi zina kupeleka cilango. Makolo ayenela kulanga ana ao mwacikondi. Ndipo ayenela kupewa kuwalanga pamene ali okwiya.

^ par. 7 M’nthawi ya Yesu, ana anali kuitana atate ao kuti Abba. Mauwa anali kusonyeza cikondi ndi ulemu.—The International Standard Bible Encyclopedia.