Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi ‘Mumakonda Anzanu Mmene Mumadzikondela’?

Kodi ‘Mumakonda Anzanu Mmene Mumadzikondela’?

“Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.”—MATEYU 22:39.

NYIMBO: 73, 36

1, 2. Kodi Malemba amaonetsa bwanji kuti cikondi n’cofunika?

CIKONDI ndi khalidwe lalikulu la Yehova Mulungu. (1 Yohane 4:16) Yesu Kristu, amene Mulungu anayambila kulenga, anakhala kumwamba ndi Atate ake kwa zaka mabiliyoni ambili. Iye anaona kuti Yehova ndi Mulungu wacikondi kwambili. (Akolose 1:15) Yesu amaonetsa cikondi cimeneci nthawi zonse. Iye anaonetsapo cikondi cimeneci akali kumwamba ndiponso atabwela padziko lapansi. Conco, ndife otsimikiza kuti Yehova ndi Yesu adzalamulila mwacikondi nthawi zonse.

2 Pamene munthu wina anafunsa Yesu kuti lamulo lalikulu ndi liti, Yesu anakamba kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambili komanso loyamba. Laciŵili lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.’”—Mateyu 22:37-39.

3. Kodi ‘anzathu’ ndani?

3 Tiyenela kukonda munthu aliyense, ndipo kucita zimenezi n’kofunika kwambili. Yesu anakamba kuti tiyenela kukonda Yehova ndiponso anzathu. Koma kodi ‘anzathu’ ndani? Ngati muli m’cikwati, mnzanu wapamtima ndi mwamuna kapena mkazi wanu. Abale ndi alongo athu mumpingo naonso ndi anzathu. Kuonjezela apo, anthu amene timakumana nao mu ulaliki naonso ndi anzathu. Conco m’nkhani ino, tiphunzila mmene tingaonetsele cikondi kwa anzathu amenewa.

MUZIKONDA MNZANU WA M’CIKWATI

4. N’ciani cingathandize kuti banja liziyenda bwino ngakhale kuti ndife opanda ungwilo?

4 Yehova analenga Adamu ndi Hava ndi kuwaika pamodzi. Cimeneci ndico cinali cikwati coyamba. Mulungu anafuna kuti io akhale ndi cikwati cacimwemwe, ndi kuti adzadze dziko lapansi ndi ana. (Genesis 1:27, 28) Komabe, pambuyo posamvela Yehova, banja lao linaonongeka, ndipo ucimo ndi imfa zinafalikila kwa anthu onse. (Aroma 5:12) Ngakhale ndi conco, banja likhoza kuyenda bwino masiku ano. Yehova amene anayambitsa cikwati, wapeleka malangizo abwino kwambili kwa amuna ndi akazi kudzela m’Baibulo.—Ŵelengani 2 Timoteyo 3:16, 17.

Yehova amafuna kuti amuna azicita umutu wao mwacikondi

5. N’cifukwa ciani cikondi n’cofunika kwambili m’banja?

5 Baibulo limaonetsa kuti cikondi cocokela pansi pamtima n’cofunika kuti anthu azisangalala. Ndipo zimenezi n’zofunika kwambili m’cikwati. Mtumwi Paulo anafotokoza za cikondi ceniceni. Iye anati: “Cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima. Cikondi sicicita nsanje, sicidzitama, sicidzikuza, sicicita zosayenela, sicisamala zofuna zake zokha, sicikwiya. Sicisunga zifukwa. Sicikondwela ndi zosalungama, koma cimakondwela ndi coonadi. Cimakwilila zinthu zonse, cimakhulupilila zinthu zonse, cimayembekezela zinthu zonse, cimapilila zinthu zonse. Cikondi sicitha.” (1 Akorinto 13:4-8) Ngati tisinkhasinkha mau a Paulo amenewa ndi kuwagwilitsila nchito, tidzakhala ndi banja lacimwemwe.

Baibulo limationetsa mmene tingakhalile ndi banja lacimwemwe (Onani ndime 6 ndi 7)

6, 7. (a) Ponena za kukhala mutu wa banja, kodi Baibulo limakamba ciani? (b) Kodi amuna Acikristu ayenela kucita bwanji zinthu ndi akazi ao?

6 Yehova ndiye anasankha amene ayenela kukhala mutu wa banja. Paulo anafotokoza kuti: “Ndikufuna mudziŵe kuti mutu wa mwamuna aliyense ndi Kristu. Mutu wa mkazi ndi mwamuna, ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu.” (1 Akorinto 11:3) Komabe, Yehova amafuna kuti amuna azicita umutu wao mwacikondi, osati mwankhanza. Yehova amacita umutu wake mokoma mtima ndipo amapewa kudzikonda. Izi zimalimbikitsa Yesu kulemekeza ulamulilo wacikondi wa Mulungu. Iye anati: “Ndimakonda Atate.” (Yohane 14:31) Yehova akanakhala kuti anali kucita zinthu mwankhanza, Yesu sakanakamba zimenezi.

7 Ngakhale kuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, Baibulo limakamba kuti iye ayenela kulemekeza mkazi wake. (1 Petulo 3:7) Kodi inu amuna mungacite bwanji zimenezi? Muyenela kulemekeza zinthu zimene akazi anu amakonda ndi kuganizila zimene afuna. Baibulo limakamba kuti: “Amuna inu, pitilizani kukonda akazi anu monga mmene Kristu anakondela mpingo n’kudzipeleka yekha cifukwa ca mpingowo.” (Aefeso 5:25) Yesu anafika popeleka moyo wake cifukwa ca otsatila ake. Ngati mwamuna amacita umutu wake mwacikondi monga Yesu, sicikhala covuta kwa mkazi wake kum’konda, kum’lemekeza, ndiponso kulemekeza zosankha zake.—Ŵelengani Tito 2:3-5.

MUZIKONDA ABALE NDI ALONGO

8. Kodi tiyenela kuwaona bwanji abale ndi alongo athu?

8 Masiku ano, anthu mamiliyoni ambili padziko lonse akulambila Yehova. Amenewa ndi abale ndi alongo athu. Kodi tiyenela kuwaona bwanji? Baibulo limakamba kuti: “Tiyeni ticitile onse zabwino, koma makamaka abale ndi alongo athu m’cikhulupililo.” (Agalatiya 6:10; ŵelengani Aroma 12:10.) Mtumwi Petulo analemba kuti “kukhala omvela coonadi” kuyenela kuticititsa ‘kukonda abale’ mocokela pansi pamtima. Petulo anauzanso Akristu anzake kuti: “Koposa zonse, khalani okondana kwambili.”—1 Petulo 1:22; 4:8.

9, 10. N’cifukwa ciani anthu a Mulungu ndi ogwilizana?

9 Gulu lathu la padziko lonse ndi lapadela kwambili. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa cakuti timakonda abale ndi alongo athu mocokela pansi pamtima. Koposa zonse, cifukwa cokonda Yehova ndi kumvela malamulo ake, iye amatithandiza ndi mzimu wake umene ndi wamphamvu kuposa cina ciliconse m’cilengedwe. Mzimu wa Mulungu umatithandiza kuti tikhale gulu la abale ogwilizana padziko lonse.—Ŵelengani 1 Yohane 4:20, 21.

10 Paulo anaonetsa kuti cikondi n’cofunika kwambili pakati pa Akristu. Iye anati: “Valani cifundo cacikulu, kukoma mtima, kudzicepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima. Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi cifukwa codandaulila za mnzake. Monga Yehova anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso teloni. Koma kuonjezela pa zonsezi, valani cikondi, pakuti cimagwilizanitsa anthu mwamphamvu kwambili kuposa cinthu cina ciliconse.” (Akolose 3:12-14) Ndife oyamikila kuti pakati pathu, tili ndi cikondi cimene “cimagwilizanitsa anthu mwamphamvu kwambili kuposa cinthu cina ciliconse,” mosasamala kanthu za kumene tinacokela.

Mboni za Yehova zimadziŵika kuti ndi otsatila a Kristu oona cifukwa cakuti amakondana ndi kugwilizana, ndipo Mulungu akuwagwilitsila nchito kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse

11. N’ciani cimadziŵikitsa gulu la Mulungu?

11 Cikondi ceniceni ndiponso mgwilizano umene uli pakati pa atumiki a Yehova umawadziŵikitsa kuti ali m’cipembedzo coona. Yesu anakamba kuti: “Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.” (Yohane 13:34, 35) Mtumwi Yohane alembanso kuti: “Ana a Mulungu ndiponso ana a Mdyerekezi amaonekela bwino ndi mfundo iyi: Aliyense amene sacita zolungama sanacokele kwa Mulungu, cimodzimodzinso amene sakonda m’bale wake. Pakuti uwu ndi uthenga umene munamva kuyambila pa ciyambi, kuti tizikondana.” (1 Yohane 3:10, 11) Mboni za Yehova zimadziŵika kuti ndi otsatila a Kristu oona cifukwa cakuti amakondana ndi kugwilizana. Ndipo Mulungu akuwagwilitsila nchito kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse.—Mateyu 24:14.

KUSONKHANITSA A “KHAMU LALIKULU”

12, 13. Kodi a “khamu lalikulu” akucita ciani masiku ano? Nanga ndi madalitso otani amene io adzalandila posacedwapa?

12 Atumiki a Yehova ambili masiku ano ali mbali ya “khamu lalikulu.” Iwo amacokela m’madela osiyanasiyana kuzungulila dziko lonse, ndipo amacilikiza Ufumu wa Mulungu. Amenewa ‘ndi amene adzatuluka m’cisautso cacikulu, ndipo acapa mikanjo yao ndi kuiyeletsa m’magazi a Mwanawankhosa’ cifukwa coonetsa cikhulupililo m’nsembe ya dipo ya Yesu. A “khamu lalikulu” amenewa amakonda Yehova ndi Mwana wake, ndipo amalambila Yehova “usana ndi usiku.”—Chivumbulutso 7:9, 14, 15.

13 Posacedwapa, Mulungu adzaononga dziko loipali pa “cisautso cacikulu.” (Mateyu 24:21; ŵelengani Yeremiya 25:32, 33.) Komabe, Yehova adzateteza atumiki ake ndi kuwatsogolela m’dziko latsopano cifukwa amawakonda. Monga mmene analonjezela zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, “Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” Kodi mukuyembekezela mwacidwi kudzakhala m’Paladaiso mmene simudzakhala kuipa, kuvutika, ndiponso imfa?—Chivumbulutso 21:4.

14. Kodi a khamu lalikulu ndi oculuka motani masiku ano?

14 Pamene masiku otsiliza anayamba mu 1914, panali atumiki a Mulungu ocepa cabe. Cifukwa cokonda anzao ndiponso mothandizidwa ndi mzimu woyela wa Mulungu, abale ndi alongo odzozedwa amenewo analalikila uthenga wabwino wa Ufumu mosasamala kanthu za mavuto amene anali kukumana nao. Kodi pakhala zotulukapo zotani? Masiku ano, khamu lalikulu limene lili ndi ciyembekezo codzakhala padziko lapansi kwamuyaya likusonkhanitsidwa. Pali Mboni za Yehova zoposa 8,000,000 m’mipingo yoposa 115,400 padziko lonse, ndipo ciŵelengelo cikuonjezeka. Mwacitsanzo, m’caka ca utumiki ca 2014, anthu oposa 275,500 anabatizidwa kukhala Mboni. Kutanthauza kuti mlungu uliwonse panali kubatizidwa anthu 5,300.

15. Kodi anthu ambili masiku ano amamvetsela uthenga wabwino m’njila iti?

15 N’zokondweletsa kuona kuti anthu ambili akumvetsela uthenga wabwino wa Ufumu. Masiku ano, zofalitsa zathu zikupezeka m’zinenelo zoposa 700. Magazini imene imafalitsidwa kwambili padziko lonse ndi Nsanja ya Mlonda. Makope a magaziniyi oposa 52,000,000 amasindikizidwa mwezi uliwonse, ndipo magaziniyi imafalitsidwa m’zinenelo 247. Ndipo buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni limene timaphunzitsila Baibulo, lamasulidwa m’zinenelo zoposa 250. Tikunena pano, makope a bukuli oposa 200,000,000 asindikizidwa.

16. N’cifukwa ciani gulu la Yehova likukulilakulila?

16 Gulu lathu likukulilakulila cifukwa cakuti timakhulupilila Mulungu, ndi kuvomeleza kuti Baibulo ndi Mau ake ouzilidwa. (1 Atesalonika 2:13) Timasangalalabe ndi madalitso a Yehova ngakhale kuti Satana amatizonda ndi kutitsutsa.—2 Akorinto 4:4.

MUZIKONDA ENA NTHAWI ZONSE

17, 18. Kodi Yehova amafuna kuti anthu amene samulambila tiziwaona bwanji?

17 Anthu amaona uthenga wathu m’njila zosiyanasiyana. Ena amamvetsela, koma ena amadana nao. Kodi Yehova amafuna kuti anthu amene samulambila tiziwaona bwanji? Mulimonse mmene anthu amaonela uthenga wathu, ife timatsatila malangizo opezeka m’Baibulo. Baibulo limati: “Nthawi zonse mau anu azikhala acisomo, okoma ngati kuti mwawathila mcele, kuti mudziŵe mmene mungayankhile wina aliyense.” (Akolose 4:6) Nthawi zonse tikamafotokoza zimene timakhulupilila, timacita zimenezi “ndi mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambili” cifukwa timakonda anzathu—1 Petulo 3:15.

18 Ngakhale pamene anthu atikwiila ndi kukana uthenga wathu, timaonetsa kuti timakonda anzathu ndipo timatengela citsanzo ca Yesu. Pamene Yesu “anali kunenedwa zacipongwe, sanabwezele zacipongwe. Pamene anali kuvutika, sanaopseze.” M’malo mwake, iye anasiya zonse m’manja mwa Yehova. (1 Petulo 2:23) Ndiye cifukwa cake, nthawi zonse timadzicepetsa ndi kumvela malangizo akuti: “Osabwezela coipa pa coipa kapena cipongwe pa cipongwe, koma m’malomwake muzidalitsa.”—1 Petulo 3:8, 9.

Tiyenela kukonda adani athu mosasamala kanthu za zimene amaticitila

19. Kodi adani athu tiyenela kuwaona bwanji?

19 Kudzicepetsa kumatithandiza kumvela mfundo yofunika kwambili imene Yesu anakamba. Iye anati: “Inu munamva kuti anati, ‘Uzikonda mnzako ndi kudana ndi mdani wako.’ Koma ine ndikukuuzani kuti: Pitilizani kukonda adani anu ndi kupemphelela amene akukuzunzani, kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba. Cifukwa iye amawalitsila dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsila mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” (Mateyu 5:43-45) Popeza ndife atumiki a Mulungu, tiyenela kukonda adani athu mosasamala kanthu za zimene amaticitila.

20. Tidziŵa bwanji kuti anthu mtsogolo padziko lonse lapansi adzakonda Yehova ndi anzao? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

20 Nthawi zonse, tizionetsa kuti timakonda Yehova ndi anzathu. Ngakhale anthu amene amatitsutsa ndi kukana uthenga wathu tiyenela kuwathandiza akafuna thandizo. Paulo analemba kuti: “Anthu inu musamakhale ndi ngongole iliyonse kwa munthu aliyense, kusiyapo kukondana, popeza amene amakonda munthu mnzake wakwanilitsa cilamulo. Cifukwa malamulo onena kuti, ‘Usacite cigololo, usaphe munthu, usabe, usasilile mwansanje,’ ndiponso lamulo lina lililonse limene lilipo, cidule cake cili m’mau awa akuti, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.’ Cikondi sicilimbikitsa munthu kucitila zoipa mnzake, cotelo cilamulo cimakwanilitsidwa m’cikondi.” (Aroma 13:8-10) Atumiki a Mulungu amakonda anzao ndi mtima wonse ngakhale kuti akukhala m’dziko limene likulamulidwa ndi Satana, lodzala ndi magaŵano, ciwawa, ndi zinthu zoipa. (1 Yohane 5:19) Pambuyo pakuti Yehova waononga Satana ndi ziwanda zake, ndiponso dziko loipali, anthu padziko lonse adzakhala okondana. Kukamba zoona, zidzakhala zosangalalatsa kwambili kukhala m’dziko limene onse adzakonda Yehova ndi anzao.

Anzathu: Nthawi zambili timaganiza kuti anzathu ndi anthu amene tikhala nao pafupi, kapena amene amakonda zinthu zimene timakonda. Komabe, anzathu amaphatikizapo mkazi kapena mwamuna wathu, abale ndi alongo mumpingo, ndi anthu amene timakumana nao mu ulaliki. Yesu anatiphunzitsa kuti tifunika kukonda anzathu