Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Phunzitsani Ana Anu Acinyamata Kutumikila Yehova

Phunzitsani Ana Anu Acinyamata Kutumikila Yehova

“Yesu anali kukulabe m’nzelu ndi mu msinkhu. Ndipo Mulungu ndi anthu anapitiliza kukondwela naye.”—LUKA 2:52.

NYIMBO: 41, 89

1, 2. (a) Kodi makolo ena amene ali ndi ana acinyamata amada nkhawa ndi ciani? (b) Kodi ana angacite ciani kuti apindule ndi zaka zao zaunyamata?

MAKOLO amakondwela kwambili ana ao akabatizidwa. Mlongo wina dzina lake Berenice ali ndi ana anai, ndipo onse anabatizidwa asanafike zaka 14. Iye anati: “Panthawiyo tinakondwela kwambili. Tinasangalala kwambili kuti ana athu anasankha kutumikila Yehova. Komabe, tinadziŵanso kuti io adzakumana ndi mavuto ambili popeza anali acinyamata.” Inunso mwina mukuda nkhawa ndi zimenezi ngati mwana wanu wamwamuna kapena wamkazi ndi wacinyamata kapena ali pafupi kukhala wacinyamata.

2 Katswili wina wa zamaganizo a ana, anakamba kuti zaka za unyamata zimakhala zovuta kwa ana ndi makolo. Conco, makolo sayenela kuganiza kuti ana ao acinyamata ndi osaganiza bwino, kapena amacita zinthu mwacibwana. M’malomwake, katswiliyo anakamba kuti acinyamata amakonda kucita zinthu zosiyanasiyana, amakhudzika mtima kwambili, ndipo amafunitsitsa kuceza ndi anzao. Pa cifukwa cimeneci, ana anu acinyamata akhoza kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova monga mmene Yesu anacitila pamene anali wacinyamata. (Ŵelengani Luka 2:52.) Akhozanso kunola luso lao lolalikila ndi kukhala ofunitsitsa kucita zambili mu utumiki wa Mulungu. Ndipo angathe kudzipangila zosankha, monga kutumikila Yehova ndi kumumvela. Monga kholo, n’ciani cimene mungacite kuti muphunzitse ana anu acinyamata kutumikila Yehova? Mungatengele citsanzo ca Yesu ca mmene anali kuphunzitsila ophunzila ake mwacikondi, modzicepetsa, ndiponso mozindikila.

MUZIKONDA ANA ANU ACINYAMATA

3. N’ciani cinacititsa atumwi kuona Yesu monga mnzao?

3 Yesu sanali cabe Mbuye kwa atumwi ake. Iye analinso mnzao wapamtima. (Ŵelengani Yohane 15:15.) M’nthawi za m’Baibulo, kaŵilikaŵili mbuye sanali kukonda kuuza akapolo ake maganizo ake ndi mmene anali kumvelela. Koma Yesu sanali kuona atumwi ake monga akapolo. Iye anali kuwakonda ndi kuceza nao. Anali womasuka kuwauza zimene anali kuganiza ndi mmene anali kumvelela. Ndipo anali kumvetsela bwinobwino pamene io anali kumuuza zimene anali kuganiza ndi mmene anali kumvelela. (Maliko 6:30-32) Kukambilana mwa njila imeneyi kunacititsa Yesu ndi atumwi ake kukhala paubwenzi wolimba. Kunacititsanso atumwi ake kukhala okonzeka kugwila nchito imene anali kudzacita mtsogolo.

4. Makolo, kodi mungakhale bwanji bwenzi la ana anu? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

4 Ngakhale kuti muli ndi ulamulilo pa ana anu, mukhozanso kukhala bwenzi lao. Mabwenzi amakhala ndi nthawi yoceza. Mwina mungacepetseko nthawi yogwila nchito ndi yocita zinthu zina kuti muzikhala ndi nthawi yambili yoceza ndi ana anu. Kuti mucite zimenezi muyenela kuipemphelela nkhaniyi ndi kuiganizila mwakuya. Mabwenzi amakondanso zinthu zofanana. Conco, dziŵani zimene mwana wanu wacinyamata amakonda, monga nyimbo, mafilimu, ndi maseŵela. Ndiyeno yesetsani kukonda zimene amakonda. Ilaria, amene amakhala ku Italy anakamba kuti: “Makolo anga anali kucita cidwi ndi nyimbo zimene ndinali kumvetsela. Atate anafika pokhala mnzanga wapamtima, ndinali womasuka kukamba nao. Ndinali kukambilana nao ngakhale nkhani zimene ena angacite manyazi kuuza atate ao.” Mukakhala bwenzi la ana anu ndi kuwathandiza kukhala bwenzi la Yehova, sizitanthauza kuti mwadzicotsela ulemu monga kholo. (Salimo 25:14) Ana anu adzaona kuti mumawakonda ndi kuwalemekeza, ndipo sadzavutika kukambilana nanu ciliconse.

5. Kodi ophunzila a Yesu akanapindula bwanji pocita nchito ya Yehova?

5 Yesu anali kudziŵa kuti ngati ophunzila ake acita khama potumikila Yehova ndi polalikila uthenga wabwino, adzakhala osangalala kwambili. Conco, anawalimbikitsa kugwila nchito yolalikila mwakhama, ndipo anawalonjeza kuti adzawathandiza.—Mateyu 28:19, 20.

6, 7. Kodi mumaonetsa bwanji kuti mumakonda ana anu mukamawaphunzitsa kucita zinthu zimene timacita nthawi zonse potumikila Yehova?

6 Makolo, mumafuna kuti ana anu azikhalabe paubwenzi ndi Yehova. Ndipo Yehova amafuna kuti muziwaphunzitsa ndi kuwalangiza. Iye wakupatsani udindo wocita zimenezo. (Aefeso 6:4) Motelo, mufunika kuonetsetsa kuti mukuphunzitsa ana anu nthawi zonse. Ganizilani izi: Mumaonetsetsa kuti ana anu apita kusukulu cifukwa mumadziŵa kuti maphunzilo ndi ofunika kwambili, ndipo mumafuna kuti azisangalala kuphunzila zinthu zatsopano. Mofananamo, muzionetsetsa kuti io amapezeka pamisonkhano yampingo, misonkhano ikuluikulu, ndi pa kulambila kwa pabanja. Ndipo maphunzilo ocokela kwa Yehova angapulumutse moyo wao. Conco, athandizeni kuti azikonda kuphunzila za Yehova ndi kudziŵa kuti kucita zimenezo kungawathandize kukhala anzelu. (Miyambo 24:14) Kuonjezela apo, phunzitsani ana anu kuti azipita mu utumiki kaŵilikaŵili. Tengelani citsanzo ca Yesu mwa kuwathandiza kuti azisangalala pophunzitsa ena Mau a Mulungu.

7 Kodi zinthu zimene timacita nthawi zonse potumikila Yehova, monga phunzilo laumwini, misonkhano, ndi ulaliki, zingathandize bwanji acinyamata? Erin, amene amakhala ku South Africa anakamba kuti: “Pamene tinali ana tinali kukonda kudandaula cifukwa cophunzila Baibulo, kusonkhana, ndi kupita mu utumiki. Nthawi zina mwadala tinali kucita zinthu zosokoneza pa phunzilo la banja kuti lisacitike. Koma makolo athu sanaleme nafe.” Iye akuyamikila makolo ake cifukwa com’thandiza kudziŵa kuti zinthu zimenezi n’zofunika kwambili. Masiku ano, iye akalephela kupita ku misonkhano ndi mu ulaliki, mwamsanga amayesetsa kuyambanso kucita zimenezo.

KHALANI ODZICEPETSA

8. (a) Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti ndi wodzicepetsa? (b) Kodi kudzicepetsa kwa Yesu kunathandiza bwanji ophunzila ake?

8 Ngakhale kuti Yesu anali wangwilo, iye anali wodzicepetsa ndipo anauza ophunzila ake kuti amadalila thandizo la Yehova. (Ŵelengani Yohane 5:19.) Kodi zimenezi zinacititsa ophunzila ake kuyamba kumupeputsa? Iyai. Pamene anali kuona kuti iye anali kudalila kwambili Yehova, m’pamenenso io anali kumudalila kwambili. Patapita nthawi, ophunzilawo anatengela citsanzo cake ca kudzicepetsa.—Machitidwe 3:12, 13, 16.

Mukamavomeleza zolakwa zanu, ana anu adzakulemekezani

9. Mungathandize bwanji ana anu acinyamata ngati mumavomeleza zolakwa zanu ndi kupepesa?

9 Mosiyana ndi Yesu, ife ndife opanda ungwilo ndipo timalakwitsa. Conco, khalani odzicepetsa. Dziŵani kuti pali zinthu zambili zimene simungakwanitse kucita, ndipo mukalakwitsa muzivomeleza. (1 Yohane 1:8) Mukacita zimenezi, ana anu acinyamata adzaphunzila kuti ayenela kuvomeleza akalakwitsa, ndipo adzakulemekezani kwambili. Mwacitsanzo, ndani mwa anthu aŵiliwa amene mungalemekeze kwambili? Kodi mungalemekeze bwana wanu amene amavomeleza akalakwitsa kapena amene sapepesa ngakhale pang’ono? Rosemary amene ali ndi ana atatu, anakamba kuti iye ndi mwamuna wake anali kuvomeleza akalakwitsa. Iye anafotokoza kuti: “Zimenezo zinakhudza kwambili ana athu cakuti anali kumasuka kukamba nafe akakhala ndi vuto.” Anakambanso kuti: “Tinaphunzitsa ana athu kumene angapeze thandizo labwino kwambili akakhala ndi mavuto. Iwo akafuna thandizo, tinali kuwathandiza mwa kuwaŵelengela zofalitsa zathu, ndi kupemphela nao pamodzi.”

10. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kudzicepetsa pamene anali kuuza ophunzila ake zocita?

10 Yesu anali ndi mphamvu youza ophunzila ake zocita. Koma cifukwa ca kudzicepetsa, anali kuwafotokozela cifukwa cake afunika kucita zimene awauza. Mwacitsanzo, sanawauze cabe kuti ayenela kufuna Ufumu coyamba ndi cilungamo ca Mulungu. Iye anakambanso kuti: “Ndipo zina zonsezi zidzaonjezedwa kwa inu.” Ndipo pamene Yesu anawauza kuti aleke kuweluza ena, anawauzanso kuti: “Kuti inunso musaweluzidwe, pakuti ciweluzo cimene mukuweluza naco ena inunso mudzaweluzidwa naco.”—Mateyu 6:31–7:2.

11. Kodi ana anu acinyamata angapindule bwanji ngati muwafotolozela cifukwa cimene mwapangila lamulo kapena cosankha cina cake?

11 Mukapanga lamulo kapena cosankha, muzipeza nthawi yoyenelela yofotokozela ana anu acinyamata cifukwa cake mwacita zimenezo. Iwo akamvetsetsa cifukwa cake, adzakhala ofunitsitsa kukumvelani. Barry, amene analelapo ana anai anati: “Kuuza ana cifukwa cimene mwacitila cinthu cina cake kumawacititsa kukukhulupililani.” Ana anu acinyamata adzaona kuti simunapange lamulo kapena cosankha cabe cifukwa cakuti muli ndi mphamvu yocita zimenezo, koma cifukwa cakuti muli ndi zifukwa zomveka. Ndiponso dziŵani kuti ana anu acinyamata salinso ana aang’ono. Iwo tsopano akufuna kuganiza paokha ndi kudzisankhila zocita. (Aroma 12:1) Barry anakamba kuti: “Acinyamata amafunika kuphunzila kupanga zosankha pa zifukwa zomveka osati cifukwa ca mmene akumvelela.” (Salimo 119:34) Conco khalani wodzicepetsa. Ndipo mufotokozeleni mwana wanu wacinyamata cifukwa cimene mwapangila cosankha cina cake. Mukatelo, iye adzaphunzila kudzipangila zosankha. Adzadziŵa kuti mumamulemekeza ndipo mumadziŵa kuti iye akufika pa ucikulile.

KHALANI OZINDIKILA

12. Popeza Yesu anali wozindikila, kodi anathandiza bwanji Petulo?

12 Yesu anali wozindikila ndipo anali kudziŵa mmene angathandizile ophunzila ake. Mwacitsanzo, pamene Yesu anauza ophunzila ake kuti iye adzaphedwa, Petulo anamuuza kuti adzikomele mtima. Yesu anali kudziŵa kuti Petulo amamukonda, koma anadziŵanso kuti apa iye waganiza molakwika. Kodi Yesu anathandiza bwanji Petulo pamodzi ndi ophunzila ena? Coyamba anamuongolela. Ndiyeno, Yesu anafotokoza zimene zidzacitikila anthu amene amalephela kucita cifunilo ca Yehova zinthu zikafika poipa. Yesu anakambanso kuti Yehova adzadalitsa onse amene amapewa kudzikonda. (Mateyu 16:21-27) Apa Petulo anaphunzila mfundo yosaiŵalika.—1 Petulo 2:20, 21.

13, 14. (a) N’ciani cingaonetse kuti mwana wanu wacinyamata afunika kulimbitsa cikhulupililo cake? (b) Mungadziŵe bwanji thandizo limene mwana wanu afunikila?

13 Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala wozindikila kuti mudziŵe mmene mungathandizile ana anu acinyamata. (Salimo 32:8) Mwina mungazindikile kuti mwana wanu saoneka wokondwela. Kapena amakonda kukamba zinthu zoipa ponena za abale ndi alongo. Kapenanso muona kuti pali nkhani ina yake imene sakukuuzani. Musafulumile kuganiza kuti iye akucita cinthu cina coipa kwambili mwakabisila. * (Onani mau a munsi.) Komanso, musanyalanyaze vuto limenelo ndi kuyembekezela kuti lidzatha palokha. Mwina akufunika thandizo lanu kuti alimbitse cikhulupililo cake.

Thandizani mwana wanu wacinyamata kupeza mabwenzi abwino mumpingo (Onani ndime 14)

14 Kuti mudziŵe vuto la mwana wanu wacinyamata, mufunseni mafunso mokoma mtima ndiponso mwaulemu. Kucita zimenezo kuli ngati kutapa madzi m’citsime. Ngati mutapa msangamsanga, simungatape madzi ambili amene mufuna. Mofananamo, ngati simuleza mtima pofunsa mwana wanu wacinyamata kapena mukum’kakamiza kuti akambe, simungadziŵe bwinobwino zimene akuganiza ndi mmene akumvelela. (Ŵelengani Miyambo 20:5.) Ilaria akukumbukila kuti pamene anali wacinyamata, anali kufuna kuceza kwambili ndi anzake a kusukulu, koma anadziŵa kuti kucita zimenezo n’kulakwa. Makolo ake anazindikila kuti pali cina cake cimene cimudetsa nkhawa. Ilaria anakamba kuti: “Tsiku lina madzulo, makolo anga anandiuza kuti ndioneka wosakondwela, ndipo anandifunsa cimene cikundivutitsa maganizo. Nthawi imeneyo ndinalila, ndiyeno ndinawauza vuto langa, ndikuwapempha thandizo. Anandikumbatila ndi kundiuza kuti akumvetsa mmene ndikumvelela, ndipo anandilonjeza kuti adzandithandiza.” Makolo ake mwamsanga anayamba kum’thandiza kupanga mabwenzi abwino mumpingo.

Muziona makhalidwe abwino mwa ana anu acinyamata ndipo muziwayamikila

15. Kodi Yesu anaonetsanso bwanji kuti anali wozindikila?

15 Yesu analinso kuzindikila makhalidwe abwino a ophunzila ake. Mwacitsanzo, pamene Natanayeli anadziŵa kuti Yesu anakulila ku Nazareti, anakamba kuti: “Kodi mu Nazareti mungatuluke kanthu kabwino?” (Yohane 1:46) Mukanakhalapo, kodi mukanaganiza kuti Natanayeli amakonda kukamba zoipa ponena za anthu ena, amaweluza ena, ndipo alibe cikhulupililo? Umu si mmene Yesu anamuonela. M’malomwake, popeza Yesu anali wozindikila, anadziŵa kuti Natanayeli anali woona mtima. Pa cifukwa cimeneci, Yesu anakamba kuti: “Onani Mwisiraeli ndithu, amene mwa iye mulibe cinyengo.” (Yohane 1:47) Yesu anali kudziŵa zimene zinali m’mitima mwa anthu. Ndipo anagwilitsila nchito luso limeneli kuona makhalidwe abwino mwa anthu.

16. Kodi mungalimbikitse bwanji mwana wanu wacinyamata kuti aongolele?

16 Ngakhale kuti n’zosatheka kuti mudziŵe zimene zili mumtima mwa munthu mofanana ndi Yesu, mukhoza kukhala wozindikila. Yehova angakuthandizeni kuona makhalidwe abwino mwa ana anu acinyamata. Ngati mwana wanu wacita cinthu cimene cakukhumudwitsani, musakambe kuti iye ndi munthu woipa, kapena ndi wosamvela. Musayese kumuganizila mwa njila imeneyi. M’malomwake, muuzeni kuti mumaona makhalidwe ake abwino, ndi kuti mukudziŵa kuti amafuna kucita zabwino. Muziyesetsa kuona zimene amacita kuti aongolele ndipo muyamikileni. Muthandizeni kukhalabe ndi makhalidwe abwino mwa kumupatsa nchito zina. N’zimene Yesu anacita kwa ophunzila ake. Patapita caka cimodzi ndi hafu Yesu atakumana ndi Natanayeli (amenenso anali kuchedwa kuti Batolomeyo), anamupatsa udindo wofunika kwambili. Iye anam’sankha kukhala mtumwi, ndipo Natanayeli anakwanilitsa udindo wake mokhulupilika. (Luka 6:13, 14; Machitidwe 1:13, 14) Conco m’malo mocititsa wacinyamata wanu kudzimva kuti palibe cinthu ciliconse cimene amacita bwino, muyamikileni ndi kumulimbikitsa. Mucititseni kudzimva kuti akhoza kukondweletsa inu ndi Yehova ndi kuti angagwilitse nchito maluso ake potumikila Yehova.

KUPHUNZITSA ANA ANU KUDZAKUBWELETSELANI CIMWEMWE COCULUKA

17, 18. Kodi padzakhala zotsatilapo zotani ngati mupitiliza kuphunzitsa ana anu acinyamata kuti azitumikila Yehova?

17 Mwina mungamve monga mmene mtumwi Paulo anamvelela. Iye anali kudela nkhawa kwambili anthu amene anali kuwaona ngati ana ake. Iwo anali anthu amene iye anawathandiza kuphunzila za Yehova, ndipo anali kuwakonda kwambili. Conco anali kupwetekedwa mtima akaganizila kuti ena a io angasiye kutumikila Yehova. (1 Akorinto  4:15; 2 Akorinto 2:4) Victor amene analela ana atatu anati: “Zaka zimene ana anga anali acinyamata zinali zovuta. Komabe, cimwemwe cimene tinali naco cinali cacikulu kuposa mavuto amene tinali kukumana nao. Ndi thandizo la Yehova, tinakhala pa ubwenzi wolimba ndi ana athu.”

18 Makolo, tikuyamikilani kuti mumacita khama kuphunzitsa ana anu cifukwa cakuti  mumawakonda kwambili. Musaleke kucita zimenezo. Mudzakondwela kwambili kuona ana anu akusankha kutumikila Mulungu ndi kupitilizabe kum’tumikila mokhulupilika.—3 Yohane 4.

^ par. 13 Makolo angapeze malangizo othandiza m’buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba, tsamba 317, ndi Buku Laciŵili, tsamba 136 mpaka 141.