Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Zaka 100 za Ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu

Zaka 100 za Ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu

“Mulungu wamtendele . . . ” akukonzekeletseni ndi ciliconse cabwino kuti mucite cifunilo cake.”—AHEBERI 13:20, 21.

NYIMBO: 136, 14

1. Kodi nchito yolalikila inali yofunika motani kwa Yesu? Fotokozani.

YESU anali kukonda kukamba za Ufumu wa Mulungu. Pamene anali padziko lapansi, nkhani imene anali kukamba nthawi zambili inali yonena za Ufumu wa Mulungu. Pa utumiki wake, Yesu anakamba za Ufumu nthawi zoposa 100. Ufumu wa Mulungu unalidi wofunika kwambili kwa Yesu.Ŵelengani Mateyu 12:34.

2. Ndi anthu angati amene anamva Yesu akupeleka lamulo limene lili pa Mateyu 28:19, 20? Nanga n’cifukwa ciani takamba conco?

2 Patapita nthawi yocepa Yesu ataukitsidwa, anakumana ndi gulu la ophunzila ake oposa 500. (1 Akorinto 15:6) Mwina panthawiyo m’pamene Yesu analamula ophunzila ake kuti azilalikila “anthu a mitundu yonse.” Nchito imeneyo siinali yopepuka. * (Onani mau amunsi.) Iye anawauza kuti nchitoyi idzacitika kwa nthawi yaitali, mpaka “m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” Pamene mulalikila uthenga wabwino, mumathandiza kukwanilitsa ulosi umenewo.Mateyu 28:19, 20.

3. Ndi zinthu zitatu ziti zimene zatithandiza kulalikila uthenga wabwino?

3 Yesu atalamula ophunzila ake kuti azilalikila, anakamba kuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu.” (Mateyu 28:20) Conco Yesu analonjeza otsatila ake kuti iye adzawatsogolela pa nchito yolalikila, ndipo adzawathandiza kulalikila padziko lonse lapansi. Nayenso Yehova ali ndi ife. Iye watipatsa “ciliconse cabwino” kuti atithandize kulalikila. (Aheberi 13:20, 21) M’nkhani ino, tikambilana zinthu zitatu mwa zinthu zabwino zimenezi: (1) zida zimene tapatsidwa, (2) njila zimene tagwilitsila nchito, ndiponso (3) maphunzilo amene talandila. Coyamba, tiyeni tikambilane zina mwa zida zimene tagwilitsila nchito pa zaka 100 zapitazi.

ZIDA ZIMENE ZATHANDIZA ATUMIKI A MULUNGU KULALIKILA

4. Kodi zida zosiyanasiyana zatithandiza bwanji pa nchito yathu yolalikila?

4 Yesu anayelekezela uthenga wabwino wa Ufumu ndi mbeu imene yabyalidwa pa nthaka zosiyanasiyana. (Mateyu 13:18, 19) Pokonza nthaka, mlimi amagwilitsila nchito zida zosiyanasiyana. Mofananamo, Mfumu yathu yatipatsa zida zimene tingagwilitsile nchito kuti tithandize anthu kulandila uthenga wathu. Zida zina tinazigwilitsila nchito kwa nthawi yocepa, koma zina tikali kuzigwilitsila nchito. Komabe, zida zonsezi zatithandiza kunola luso lathu pa nchito yolalikila.

Khadi la ulaliki linathandiza ambili kuyamba kulalikila

5. Kodi khadi la ulaliki linali ciani? Ndipo linali kugwilitsidwa nchito bwanji?

5 Mu 1933, ofalitsa anayamba kugwilitsila nchito makadi aulaliki. Cida cimeneci cinathandiza ambili kuyamba kulalikila. Khadi la ulaliki linali kapepala kakang’ono kokhala ndi uthenga wacidule ndi wosavuta wa m’Baibulo. Pakapita nthawi anali kufalitsa khadi lina lokhala ndi uthenga watsopano. M’bale Erlenmeyer anali ndi zaka pafupifupi 10 zakubadwa pamene anagwilitsila nchito khadi la ulaliki kwa nthawi yoyamba. Iye anakamba kuti: “Nthawi zambili tinali kuyamba ndi mau akuti, ‘Kodi mungakonde kuŵelenga kapepala aka?’ Pambuyo pakuti mwininyumba waŵelenga kapepalako, tinali kumugaŵila kapepalako ndi kupitiliza ulendo.”

6. Kodi makadi a ulaliki anali othandiza bwanji?

6 Makhadi a ulaliki anathandiza ofalitsa m’njila zosiyanasiyana. Mwacitsanzo ofalitsa ena anali amanyazi. Ngakhale kuti anali ofunitsitsa kulalikila, sanali kudziŵa zimene angakambe. Koma ofalitsa ena anali olimba mtima kwambili. Iwo anali kukwanitsa kuuza mwininyumba zinthu zambili pa nthawi yocepa. Koma nthawi zina zimene anali kulalikila sizinali zogwila mtima. Makadi a ulaliki anathandiza ofalitsa onse kulalikila uthenga momveka bwino.

7. Pogwilitsila nchito makhadi a ulaliki, kodi panali mavuto otani?

7 Ngakhale n’conco, panalinso zovuta zina. Mlongo Grace Estep anakamba kuti: “Nthawi zina, anthu anali kutifunsa kuti, ‘Kodi khadi limeneli limakamba za ciani? Kodi simungandiuze cabe zimene limakamba?’ ” Komanso, ena sanali kukwanitsa kuŵelenga khadi lathu. Ndipo ena anali kungotenga osaliŵelenga ndi kutseka citseko. Anthu ena anali kudana ndi uthenga wathu, moti akatenga khadilo anali kungoling’amba. Ngakhale kuti panali mavuto amenewa, makadi a ulaliki anathandiza ofalitsa kulalikila anzao ndiponso anawadziŵikitsa kuti ndi alengezi a Ufumu.

8. Kodi galamafoni inali kugwilitsidwa nchito bwanji? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

8 Cida cina cimene cinali kugwilitsidwa nchito pambuyo pa caka ca 1930 ndi galamafoni yonyamulila m’manja. Mboni zina zinali kuicha kuti Aroni cifukwa galamafoni inali kulankhula m’malo mwa io. (Ŵelengani Ekisodo 4:14-16.) Ngati mwininyumba wavomela kumvetsela, wofalitsa anali kutsegula nkhani yaifupi yojambulidwa, ndipo pamapeto pake anali kumugaŵila zofalitsa. Nthawi zina, banja lonse linali kusonkhana pamodzi kuti limvetsele nkhaniyo. Mu 1934, gulu la Yehova linayamba kupanga magalamafoni onyamulila m’manja opita nao mu ulaliki. Conco, abale anajambula nkhani 92 zosiyanasiyana.

9. Kodi galamafoni inali yothandiza bwanji?

9 Pamene Hillary Goslin anamvetselako nkhani imodzi, anabweleka galamafoni kwa mlungu umodzi kuti akauzeko anzake uthenga wa m’Baibulo. Pambuyo pake, anthu ena anacita cidwi ndi coonadi ndipo anabatizidwa. Patapita nthawi, ana aŵili aakazi a M’bale Goslin analowa Sukulu ya Gileadi ndi kukhala amishonale. Magalamafoni naonso anathandiza ofalitsa ambili kuyamba kulalikila monga mmene makadi a ulaliki anacitila. M’kupita kwa nthawi, Mfumu yathu inaphunzitsa anthu ake kuti akhale aphunzitsi aluso pogwilitsila nchito Sukulu ya Ulaliki.

KUGWILITSILA NCHITO NJILA ZOSIYANASIYANA POLALIKILA

10, 11. Kodi manyuzipepala ndi wailesi zinali kugwilitsidwa nchito motani polalikila uthenga wabwino? Ndipo n’cifukwa ciani njila zimenezo zinali zothandiza?

10 Motsogoledwa ndi Mfumu yathu, anthu a Mulungu agwilitsila nchito njila zosiyanasiyana kuti afikile anthu ambili polalikila. Njila zimenezo zinali zothandiza kwambili makamaka panthawi imene kunali anchito ocepa. (Ŵelengani Mateyu 9:37.) Mwacitsanzo, zaka zambili zapitazo, atumiki a Mulungu anali kugwilitsila nchito manyuzipepala polalikila uthenga wabwino. Mlungu uliwonse, M’bale Russell anali kutumiza nkhani za m’Baibulo ku bungwe lofalitsa nkhani. Kenako, io anali kuzitumiza kwa olemba manyuzipepala a ku Canada, Europe, ndi ku United States. Pofika mu 1913, nkhani za M’bale Russell zinali kufalitsidwa m’manyuzipepala 2,000. Ndipo zinali kuŵelengedwa ndi anthu pafupifupi 15,000,000.

Manyuzipepala ndi wailesi zinathandiza atumiki a Mulungu kufikila anthu ambili m’malo amene munali ofalitsa ocepa

11 Wailesi inali kugwilitsidwanso nchito polalikila uthenga wabwino. Pa April 16, 1922, M’bale Rutherford anakamba nkhani yake yoyamba ya pa wailesi, ndipo anthu pafupifupi 50,000 anamvetsela. Pasanapite nthawi yaitali, tinayamba kugwilitsila nchito wailesi yathu yochedwa WBBR. Ndipo pulogalamu yoyamba inaulutsidwa pa February 24, 1924. Magazini ya Watch Tower ya December 1, 1924 inakamba kuti: “Tikukhulupilila kuti wailesi ndiyo njila yochipa komanso yogwila mtima kwambili polengeza uthenga wa coonadi.” Mofanana ndi manyuzipepala, wailesi inatithandiza kufikila anthu ambili m’malo amene munali ofalitsa ocepa.

Ofalitsa a Ufumu ambili amakonda ulaliki wapoyela ndi kuuza anthu za webusaiti yathu (Onani ndime 12 ndi 13)

12. (a)Ndi mtundu uti wa ulaliki wapoyela umene mumakonda kwambili? (b) N’ciani cingatithandize kuti tisamacite mantha pocita ulaliki wapoyela?

12 Ulaliki Wapoyela ndi njila yothandiza imene timagwilitsila nchito kuti tifikile anthu ambili masiku ano. Timayesetsanso kulalikila anthu m’malo okwelela mabasi, m’masitesheni a sitima, m’malo oimikapo magalimoto, kuphatikizapo, m’miseu, ndi m’misika. Kodi mumacita mantha kucita ulaliki wa poyela? Ngati n’conco, pemphelani kwa Yehova kuti akuthandizeni, ndipo ganizilani zimene M’bale Manera, woyang’anila woyendela anakamba. Iye anati: “Tinali kuona njila yatsopano ya ulaliki ngati njila ina yotumikila Yehova. Tinali kuiona kuti ndi mwai wathu woonetsa kuti timam’khulupilila, ndipo tinali okonzeka kum’tumikila m’njila iliyonse.” Ngati tiyesetsa kulalikila molimba mtima ndi kugwilitsila nchito njila zatsopano polalikila, tidzayamba kudalila kwambili Yehova ndipo tidzakhala alaliki aluso.Ŵelengani 2 Akorinto 12:9, 10.

13. N’cifukwa ciani webusaiti yathu ndi njila yothandiza kwambili polalikila? Fotokozani zocitika za mu ulaliki zimene mwakhala nazo pogwilitsila nchito webusaiti yathu.

13 Ofalitsa ambili amakonda kuuza anthu ena za webusaiti yathu ya jw.org. Pa webusaiti imeneyi anthu angaŵelenge ndi kutenga zofalitsa zofotokoza Baibulo m’zinenelo zoposa 700. Tsiku lililonse, anthu oposa 1.6 miliyoni amapita pa webusaiti yathu. Kale, atumiki a Mulungu anali kulalikila uthenga wabwino kwa anthu okhala m’madela akutali pogwilitsila nchito wailesi. Masiku ano, webusaiti yathu imatithandizanso kulalikila anthu okhala m’madela akutali.

KUPHUNZITSA ALENGEZI A UTHENGA WABWINO

14. Kodi ofalitsa anafunika kuphunzitsidwa ciani? Nanga ndi sukulu iti imene yawathandiza kukhala alaliki ogwila mtima?

14 Zida ndiponso njila zosiyanasiyana zimene takambilana zakhala zothandiza kwambili. Komabe, ofalitsa ambili nthawi imeneyo anafunika kuphunzitsidwa mmene angalalikilile. Mwacitsanzo, nthawi zina mwininyumba sanali kugwilizana ndi uthenga umene wamvetsela pa galamafoni. Koma nthawi zina, anali kumvetsela ndipo anali kufuna kuphunzila zoonjezeleka. Ofalitsa anafunika kudziŵa mmene angayankhile anthu otsutsa ndiponso mmene angaphunzitsile ena mogwila mtima. Mothandizidwa ndi mzimu woyela wa Mulungu, M’bale Knorr, anaona kuti ofalitsa afunika kuphunzitsidwa mmene angalalikilile. Conco kuyambila mu 1943, mipingo inayamba kucita Sukulu ya Ulaliki. Sukuluyi inathandiza ofalitsa onse kukhala alaliki ogwila mtima.

15. (a)Kodi ena anali kumvela bwanji pokamba nkhani za m’Sukulu ya Ulaliki? (b) Kodi lonjezo la Yehova limene lili pa Salimo 32:8 linakwanilitsidwa bwanji kwa inu?

15 Abale ambili sanali kudziŵa kulankhula pa gulu la anthu. M’bale Ramu anakamba nkhani yake yoyamba m’sukulu ya ulaliki mu 1944. Nkhaniyo inali kukamba za Doegi amene amachulidwa m’Baibulo. Pofotokoza mmene anamvela pokamba nkhaniyo, iye anati: “Cifukwa ca mantha, nkhongono zanga zinali kugundana, manja anga anali kunjenjemela, ndipo mano anga anali kulumana. Imeneyo ndiyo inali nthawi yanga yoyamba kukamba nkhani pa pulatifomu, koma sindinasiye kukamba nkhani m’sukulu.” Ngakhale kuti kukamba nkhani sikunali kopepuka, ana naonso anali kukamba nkhani m’sukulu. M’bale Manera ananenanso zimene zinacitika pamene mnyamata wina wamng’ono anali kukamba nkhani yake yoyamba. Iye anati: “Mnyamatayo anali ndi mantha kwambili cakuti pamene anayamba kukamba nkhani, anayambanso kulila. Koma cifukwa cakuti anali wofunitsitsa kukamba nkhaniyo, anakamba nkhani yonse uku akulila.” Mwina inu simuyankhapo pamisonkhano ndi kukamba nkhani m’sukulu cifukwa ca manyazi kapena cifukwa coona ngati simungakwanitse. Ngati n’conco, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuthetsa mantha. Iye adzakuthandizani monga mmene anathandizila Akristu akale amene anali kukamba nkhani za m’Sukulu ya Ulaliki.Ŵelengani Salimo 32:8.

Amishonale oposa 8,500 amene analoŵa Sukulu ya Gileadi atumizidwa m’maiko 170 kuyambila mu 1943

16. (a) Kodi colinga ca Sukulu ya Gileadi cinali cotani kale? (b) Kodi colinga ca Sukuluyi cakhala cotani kuyambila 2011?

16 Gulu la Mulungu limapelekanso maphunzilo kudzela m’Sukulu ya Gileadi. Colinga cimodzi ca sukulu imeneyi ndi kuthandiza ana a sukulu kukonda nchito yolalikila uthenga wabwino. Sukulu ya Gileadi inayamba mu 1943, ndipo kuyambila nthawi imeneyo, ana a sukulu okwanila 8,500 aphunzitsidwa ndi kutumizidwa m’maiko 170. Kuyambila mu 2011, amene amaitanidwa ku sukuluyi ndi apainiya apadela, oyang’anila oyendela, atumiki a pa Beteli, ndi amishonale amene sanaloŵepo sukuluyi.

17. Kodi Sukulu ya Gileadi yathandiza bwanji?

17 Kodi Sukulu ya Gileadi yakhala yothandiza? Inde. Mwacitsanzo, mvelani zimene zinacitika ku Japan. Mu August 1949, m’dzikolo munali ofalitsa osakwana 10. Koma pofika kumapeto kwa caka cimeneco, amishonale 13 anatumizidwa kumeneko. Masiku ano, ku Japan kuli ofalitsa 216,000 ndipo pafupifupi hafu ya io ndi apainiya.

18. Ndi masukulu ena ati amene tili nao?

18 Tili ndi masukulu ena ambili monga, Sukulu ya Utumiki wa Ufumu, Sukulu ya Apainiya, Sukulu ya Alengezi a Ufumu, Sukulu ya Oyang’anila Oyendela ndi Akazi ao, ndi Sukulu ya a m’Komiti ya Nthambi ndi Akazi ao. Masukulu amenewa aphunzitsa abale ndi alongo ndi kulimbitsa cikhulupililo cao. N’zoonekelatu kuti Yesu akupitilizabe kuphunzitsa anthu ambili.

19. Kodi M’bale Russell anakamba ciani ponena za nchito yolalikila? Nanga zimenezo zakwanilitsidwa bwanji?

19 Ufumu wa Mulungu wakhala ukulamulila kwa zaka zoposa 100. Pa zaka zonsezi, Mfumu yathu Yesu Kristu, yakhala ikutsogolela nchito yolalikila. Mu 1916, M’bale Russell anali ndi cidalilo cakuti uthenga wabwino udzalalikidwa padziko lonse lapansi. Iye anati: “Nchitoyi ikukula kwambili ndipo idzapitiliza kukula cifukwa cakuti ‘uthenga wa Ufumu’ uyenela kulalikidwa padziko lonse.” (Buku lakuti Faith on the March, lolembedwa ndi A. H. Macmillan, tsamba 69) Nchito imeneyi ikucitikadi masiku ano. Tiyamikila Yehova, Mulungu wa mtendele cifukwa cakuti amatipatsa zilizonse zofunikila kuti ticite cifunilo cake.

^ par. 2 Zikuoneka kuti anthu ambili m’gulu limenelo anakhala Akristu. Takamba conco cifukwa cakuti mtumwi Paulo anawachula kuti “abale 500.” Iye anakambanso kuti: “Ambili a io akali ndi moyo mpaka lelo, koma ena anagona mu imfa.” Motelo, zioneka kuti Paulo ndi Akristu ena anali kuwadziŵa anthu ambili amene anamva mwacindunji pamene Yesu anali kulamula ophunzila ake kuti azilalikila.