Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Baibulo Lomasulidwa Bwino Kwambili

Baibulo Lomasulidwa Bwino Kwambili

“Mau a Mulungu ndi amoyo.”—AHEBERI 4:12.

NYIMBO: 37, 116

1. (a) Ndi udindo wotani umene Mulungu anapatsa Adamu? (b) Kodi anthu a Mulungu akhala akugwilitsila nchito motani cinenelo kuyambila panthawiyo?

YEHOVA MULUNGU anapatsa anthu cinenelo monga mphatso. Mulungu anapatsanso Adamu udindo wopatsa maina nyama zonse m’munda wa Edeni. Adamu anapatsa nyama iliyonse dzina loyenelela. (Genesis 2:19, 20) Kuyambila panthawiyo, anthu a Mulungu akhala akutamanda Yehova ndi kuuza ena za iye mwakugwilitsila nchito cinenelo. M’zaka zaposacedwapa, anthu a Mulungu akhala akugwilitsila nchito cinenelo pomasulila Baibulo n’colinga cakuti anthu aphunzile za Yehova.

2. (a) Ndi mfundo ziti zimene a m’Komiti Yomasulila Baibulo la Dziko Latsopano anatsatila pogwila nchito yao? (b) Tidzaphunzila ciani m’nkhani ino?

2 Pali Mabaibulo ambili amene amasulidwa, ndipo ena ndi olondola kwambili kuposa ena. Kuti amasulile Baibulo molondola, a Komiti Yomasulila Baibulo la Dziko Latsopano anatsatila mfundo zitatu zofunika izi: (1) Kulemekeza dzina la Mulungu ndi kulilemba m’Mau ake mofanana ndi mmene linalembedwela m’mipukutu yoyambilila. (Ŵelengani Mateyu 6:9.) (2) Kumasulila uthenga wake liu ndi liu ngati n’kotheka, koma ngati n’zosatheka, kumasulila tanthauzo lenileni la mauwo. (3) Kugwilitsila nchito cinenelo cosavuta kuŵelenga ndi kumva. * (Onani mau amunsi.) (Ŵelengani Nehemiya 8:8, 12.) Omasulila Baibulo la Dziko Latsopano m’zinenelo zosiyanasiyana zoposa 130, akhala akutsatila mfundo zitatu zimenezi. M’nkhani ino, tiphunzila mmene omasulila Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso la 2013 anagwilitsila nchito mfundozi. Tiphunzilanso mmene omasulila Baibuloli m’zinenelo zina amatsatilila mfundo zimenezi.

BAIBULO LIMENE LIMALEMEKEZA DZINA LA MULUNGU

3, 4. (a) Ndi kuti kumene tingapeze Tetragalamatoni? (b) N’ciani cimene omasulila Baibulo ambili acita ndi dzina la Mulungu?

3 Dzina la Mulungu linalembedwa m’zilembo zinai za Ciheberi zochedwa Tetragalamatoni. Zilembo zimenezi zimapezeka m’mipukutu yakale ya Ciheberi monga Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa. Tingapezenso zilembo za Tetragalamatoni m’Mabaibulo ena a Cigiriki a Septuagint. Mabaibulo amenewa analembedwa kale kwambili, zaka 200 Kristu asanabadwe, ndipo ena analembedwa zaka 100 Kristu atabadwa. Anthu ambili amacita cidwi akaona kuti dzina la Mulungu likuchulidwa nthawi zambilimbili m’mipukutu yakale.

Anthu ambili amacita cidwi akadziŵa kuti dzina la Mulungu limachulidwa nthawi zambilimbili m’mipukutu yakale

4 Mwacionekele, dzina la Mulungu liyenela kupezeka m’Baibulo. Komabe, omasulila ambili salemba dzina la Mulungu m’Mabaibulo ao. Mwacitsanzo, patangopita zaka ziŵili pambuyo potulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu, Baibulo lokonzedwanso lochedwa American Standard Version, linatulutsidwa. M’Baibulo la American Standard Version lotulutsidwa mu 1901 munali dzina la Mulungu, koma limene linatulutsidwa mu 1952 munalibe dzina la Mulungu. N’cifukwa ciani? Omasulila Baibulowo anaona kuti kugwilitsila nchito dzina la Mulungu “sikunali kofunika ngakhale pang’ono.” M’Mabaibulo enanso a Cingelezi ndi a zinenelo zina, anacotsamo dzina la Mulungu.

5. N’cifukwa ciani dzina la Mulungu lifunika kupezeka m’Baibulo?

5 Kodi omasulila afunika kulemba dzina la Mulungu m’Mabaibulo awo? Inde afunika kutelo! Yehova, Mlembi wa Baibulo, afuna kuti anthu adziŵe dzina lake. Womasulila wabwino afunika kudziŵa zimene wolemba nkhani afuna, ndipo zimenezo ziyenela kukhudza mmene angamasulile nkhaniyo. Malemba ambili amaonetsa kuti dzina la Mulungu n’lofunika kwambili ndi kuti tifunika kulilemekeza. (Ekisodo 3:15; Salimo 83:18; 148:13; Yesaya 42:8; 43:10; Yohane 17:6, 26; Machitidwe 15:14) Pogwilitsila nchito mzimu wake, Yehova anauzila olemba Baibulo kuti alembe dzina lake nthawi masauzande ambili m’mipukutu yakale. (Ŵelengani Ezekieli 38:23.) Conco, ngati omasulila acotsa dzina la Mulungu m’Mabaibulo ao, ndiye kuti salemekeza Yehova.

6. N’cifukwa ciani dzina la Mulungu linalembedwanso pa mavesi ena 6 m’Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso?

6  Masiku ano tili ndi umboni wamphamvu woonetsa cifukwa cake tiyenela kugwilitsila nchito dzina la Yehova. Mu Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso la 2013, dzina la Mulungu limapezekamo nthawi zokwana 7,216. Ciŵelengelo cimeneci cikuonetsa kuti dzina la Mulungu lachulidwanso m’mavesi ena 6 kuonjezela pa ciŵelengelo cakale. Mavesi 5 pa mavesi 6 amenewa, anaonjezeledwa cifukwa cakuti dzina la Mulungu linapezedwanso pa Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa imene inafalitsidwa posacedwapa. * (Onani mau amunsi.) Mavesiwa akupezeka pa 1 Samueli 2:25; 6:3; 10:26; 23:14, 16. Vesi lina la nambala 6 pamene pakupezekanso dzina la Mulungu ndi pa Oweluza 19:18, ndipo linaonjezeledwa pambuyo popenda mosamalitsa mipukutu ina yakale ya Baibulo.

7, 8. Kodi dzina lakuti Yehova limatanthauza ciani?

7 Akristu oona amadziŵa kufunika kwa tanthauzo la dzina la Mulungu. Dzina lake limatanthauza kuti “Amacititsa kukhala.” * (Onani mau amunsi.) M’zaka za m’mbuyomu, zofalitsa zathu zakhala zikufotokoza tanthauzo la dzina la Mulungu mwa kugwilitsila nchito lemba la Ekisodo 3:14, limene limati: “Ndidzakhala Amene Ndidzafuna Kukhala.” Baibulo la Dziko Latsopano limene linakonzedwa mu 1984 linafotokoza kuti Yehova angathe kukhala ciliconse cimene angafune kuti akwanilitse zimene analonjeza. * (Onani mau amunsi.) Komabe, Baibulo lokonzedwanso la 2013 limafotokoza kuti: “Dzina lakuti Yehova limatanthauza zambili kuonjezela pa mfundo yakuti iye amasankha kukhala ciliconse cimene akufuna. Dzinali limatanthauzanso kuti Mulungu angapangitse cilengedwe cake kukhala ciliconse cimene iye akufuna kuti akwanilitse colinga cake.”

8 Yehova amacititsa cilengedwe cake kukhala ciliconse cimene iye angafune. Mwacitsanzo, Mulungu anacititsa Nowa kukhala womanga cingalawa, anacititsa Bezaleli kukhala mmisili waluso, anacititsa Gidiyoni kukhala wolimba mtima pa nkhondo, ndipo anacititsa Paulo kukhala m’mishonale. Dzina la Mulungu lili ndi tanthauzo lalikulu kwa anthu a Mulungu, ndiye cifukwa cake a m’Komiti Yomasulila Baibulo la Dziko Latsopano analemba dzina la Mulungu m’Baibuloli.

9. N’cifukwa ciani kumasulila Baibulo m’zinenelo zina n’kofunika kwambili?

9 M’Mabaibulo ambili, mulibe dzina lenileni la Mulungu. M’malomwake, muli dzina la udindo lakuti “Ambuye” kapena dzina la mulungu wa kumaloko. Ici ndiye cifukwa cake Bungwe Lolamulila likuona kuti anthu a zinenelo zonse ayenela kukhala ndi Baibulo limene limalemekeza dzina la Mulungu. (Ŵelengani Malaki 3:16.) Panopa dzina la Yehova likupezeka m’Baibulo la Dziko Latsopano, ndipo Baibulo limeneli likupezeka m’zinenelo zoposa 130. Mwakutelo, dzinalo likulemekezedwa.

BAIBULO LOMVEKA BWINO NDI LOLONDOLA

10, 11. Ndi mavuto otani amene omasulila akumana nao pomasulila Baibulo la Dziko Latsopano m’zinenelo zina?

10 Omasulila akhala akukumana ndi mavuto ena pomasulila Baibulo la Dziko Latsopano la Cingelezi. Mwacitsanzo, Baibulo la Cingelezi linagwilitsila nchito mau Aciheberi akuti “Shelo” pa Mlaliki 9:10 komanso m’mavesi ena. Liu limeneli likupezekanso m’Mabaibulo ena a Cingelezi. Komabe, zinali zovuta kuti lilembedwe m’zinenelo zina cifukwa anthu ambili oŵelenga zinenelozo sanali kulidziŵa liu la Ciheberi limeneli. Mau amenewa mulibe m’madikishonale ao, ndipo ena anali kuganiza kuti ndi dzina la malo ena ake. Pa cifukwa cimeneci, omasulila analoledwa kumasulila mau Aciheberi akuti “Shelo” ndi mau Acigiriki akuti “Hade” kuti “Manda.” Amenewa ndi mau olondola ndiponso omveka bwino.

11 Mau Aciheberi ndi Acigiriki amene anamasulidwa kuti “soul” m’Cingelezi analinso ovuta kuwamasulila m’zinenelo zina. M’zinenelo zimenezo, mau akuti “soul” nthawi zambili amatanthauza mzukwa (cipuku) kapena cinthu cina cake cimene anthu amati cimacoka m’thupi mwa munthu akamwalila. Posafuna kukhala ndi malingalilo olakwika amenewo, omasulila analoledwa kumasulila liu lakuti “soul” mogwilizana ndi nkhani imene akumasulila. Tanthauzo la mau akuti “soul” linafotokozedwa mu New World Translation of the Holy Scriptures—With References, nkhani zakumapeto. Mfundo zina zimene zimafotokoza mau Aciheberi ndi Acigiriki zinalembedwa m’mau amunsi m’Baibulo lokonzedwanso n’colinga cakuti tiziliŵelenga ndi kulimvetsa popanda vuto.

Pokonzanso Baibuloli, a m’Komiti Yomasulila Baibulo anapenda mosamalitsa mafunso masausande ambili ocokela kwa omasulila

12. Ndi masinthidwe ena ati amene anapangidwa mu Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso?

12 Mafunso amene omasulila anali kufunsa anaonetsanso kuti mau ena a m’Baibulo angathe kumveka molakwika. Pa cifukwa cimeneci, mu September 2007, Bungwe Lolamulila linapeleka cilolezo cakuti Baibulo la Dziko Latsopano la Cingelezi likonzedwenso. Pokonzanso Baibulo limeneli, a m’komiti yomasulila Baibulo anapenda mosamalitsa mafunso masausande ambili ocokela kwa omasulila. Mau a Cingelezi amene anali kumveka acikale, anawasintha ndi kulembamo mau ena amakono amene amapangitsa Baibuloli kukhala losavuta kuŵelenga ndi kumva, koma sanasinthe tanthauzo lake. Mabaibulo amene anali atamasulidwa kale m’zinenelo zina, anathandizanso pa nchito yokonzanso Baibulo latsopano la Cingelezi.—Miyambo 27:17.

MAU OYAMIKILA BAIBULO LATSOPANO

13. Kodi anthu ambili akamba zotani pambuyo polandila Baibulo lokonzedwanso la 2013?

13 Kodi anthu ambili akamba ciani pambuyo polandila Baibulo la Dziko Latsopano lacingelezi lokonzedwanso? Abale ndi alongo ambili akhala akutumiza makalata oyamikila kaamba ka Baibuloli ku likulu la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York. Ambili amakamba mofanana ndi mmene mlongo wina analembela kuti: “Baibulo lili monga thumba lokhala ndi zinthu za mtengo wapatali. Kuŵelenga mau a Yehova m’Baibulo lokonzedwanso la 2013, kuli ngati kutenga cinthu camtengo wapatali m’thumbalo ndi kuyang’anitsitsa kukongola kwa cinthuco. Kuŵelenga Malemba olembedwa m’cinenelo cosavuta kwandithandiza kum’dziŵa bwino Yehova. Iye ali monga atate anga amene andifungatila m’manja ao ndi kundiŵelengela mau otsitsimula.”

14, 15. N’ciani cimene anthu ambili akamba ponena za Baibulo la Dziko Latsopano la m’zinenelo zao?

14 Anthu amene amakamba zinenelo zina ayamikilanso kwambili kukhala ndi Baibulo la Dziko Latsopano m’zinenelo zao. Wacikulile wina amene amakhala mumzinda wa Sofia, m’dziko la Bulgaria, anayamikila kukhala ndi Baibulo la Dziko Latsopano m’Cibugariya. Iye anati: “Ndakhala ndikuŵelenga Baibulo kwa zaka zambili, koma sindinaŵelengepo Baibulo losavuta kumva ndi lofika pamtima ngati limeneli.” Mlongo wina wa ku Albania analembanso kuti: “Mau a Mulungu akumveka bwino kwambili m’Ciabaniya! Ndi mwai wamtengo wapatali kuti Yehova akukamba nafe m’cinenelo cathu.”

15 M’maiko ambili, Mabaibulo ndi odula kwambili ndipo ndi ovuta kupeza. Conco, kulandila Baibulo ndi mwai wamtengo wapatali. Ku Rwanda kunacoka lipoti lakuti: “Anthu amene anali kuphunzila Baibulo ndi abale, sanali kupita patsogolo kwa nthawi yaitali cifukwa cakuti analibe Mabaibulo. Anthuwo analibe ndalama zogulila Mabaibulo kuchalichi kwao, ndipo nthawi zambili sanali kumvetsa tanthauzo la mavesi ena m’Mabaibulowo.” Banja lina la ku Rwanda limene lili ndi ana acinyamata anai, linasangalala kwambili pamene Baibulo la Dziko Latsopano linatulutsidwa m’cinenelo cao. Iwo anati: “Tikuyamikila kwambili Yehova ndiponso kapolo wokhulupilika ndi wanzelu potipatsa Baibulo limeneli. Ndife osauka ndipo tinalibe ndalama zogulila Baibulo wina aliyense m’banja lathu. Koma panopa, aliyense wa ife ali ndi Baibulo lake lake. Timaŵelenga Baibulo monga banja masiku onse pofuna kuonetsa ciyamikilo cathu kwa Yehova kaamba ka Baibulo limeneli.”

16, 17. (a) Kodi Yehova afuna kuti anthu ake azicita ciani? (b) Kodi tiyenela kukhala otsimikiza mtima kucita ciani?

16 Baibulo la Dziko Latsopano lidzakhalanso m’zinenelo zambili mtsogolomu. Satana amafuna kulepheletsa nchito yomasulila Baibulo, koma tikudziŵa kuti Yehova afuna kuti anthu ake onse azimvetsela kwa iye pamene akukamba nao m’cinenelo comveka bwino. (Ŵelengani Yesaya 30:21.) Posacedwapa, “dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziŵa Yehova ngati mmene madzi amadzazila nyanja.”—Yesaya 11:9.

17 Tiyeni tikhale otsimikiza mtima kugwilitsila nchito mphatso iliyonse imene Yehova watipatsa, kuphatikizapo Baibulo limene limalemekeza dzina lake. Lolani Yehova kuti azikamba nanu masiku onse kudzela m’Mau ake. Iye amamvetsela mapemphelo athu onse mwachelu. Kukambilana kotelo kudzatithandiza kum’dziŵa bwino Yehova, ndipo cikondi cathu pa iye cidzapitiliza kukula.—Yohane 17:3.

“Ndi mwai wamtengo wapatali kuti Yehova akukamba nafe m’cinenelo cathu”

^ par. 2 Onani nkhani ya mutu wakuti “Kodi Mungadziŵe Bwanji Baibulo Lomasuliridwa Bwino? yopezeka m’Nsanja ya Olonda ya May 1, 2008.

^ par. 6 Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa ndi yakale kwambili, ndipo inalembedwa zaka 1,000 malemba a Ciheberi olembedwa ndi Amasorete asanalembedwe

^ par. 7 Mabuku ena ofufuzila amafotokozanso mfundo imeneyi, koma si akatswili onse amene amavomeleza zimenezi.

^ par. 7 Onani New World Translation of the Holy Scriptures—With References, Zakumapeto 1A “Dzina la Mulungu m’Malemba Aciheberi,” tsamba 1561.