Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Ndili pa Mtendele ndi Mulungu Komanso ndi Amai

Ndili pa Mtendele ndi Mulungu Komanso ndi Amai

AMAI ANGA anandifunsa kuti: “N’cifukwa ciani sulambilako mizimu ya makolo athu? Kodi sudziŵa kuti uli ndi moyo cifukwa ca io? Kodi sungawaonetse ulemu? Kodi ungaleke bwanji kucita miyambo imene yakhalako kwa nthawi yaitali? Kuleka kupeleka ulemu ku mizimu ya makolo n’kupusa.” Atanena mau amenewa, Amai anayamba kulila.

Miyezi ingapo izi zisanacitike, a Mboni za Yehova anapempha amai kuti aziphunzila nao Baibulo. Iwo sanafune kuphunzila, koma pofuna kuonetsa ulemu anawauza kuti aziphunzila ndi ine. Sindinali kuyembekezela kuti amai angakhumudwe nane, cifukwa cakuti ndinali kuwamvela nthawi zonse. Komabe, cifukwa cakuti ndinafuna kukondweletsa Yehova, sindinalole kulambila mizimu ya makolo. Kucita zimenezi kunali kovuta, koma Yehova anandipatsa mphamvu.

KUPHUNZILA ZA YEHOVA

Monga anthu ambili ku Japan, ndinakulila m’banja la cipembedzo ca Cibuda. Koma pambuyo pophunzila Baibulo ndi Mboni za Yehova kwa miyezi iŵili, ndinatsimikizila kuti Baibulo ndi loona. Pamene ndinadziŵa kuti ndili ndi Atate wakumwamba, ndinakhala wofunitsitsa kumudziŵa bwino. Poyamba, ine ndi Amai tinali kukonda kukambitsilana zimene ndaphunzila. Ndinayamba kupezeka pa misonkhano ku Nyumba ya Ufumu pa Sondo. Nditaphunzila zambili, ndinauza Amai kuti ndaleka kucita nao zikondwelelo za Cibuda. Nditangowauza zimenezi, anakhumudwa kwambili. Iwo anati, “Ukana kulambila mizimu ya makolo! Ndiwe mwana wocititsa manyazi kwambili.” Iwo anandikakamiza kuti ndisiye kuphunzila Baibulo ndi kusonkhana. Sindinali kuyembekezela kuti amai anganene zimenezi. Iwo anasinthilatu.

Atate anagwilizana ndi zimene Amai anakamba. M’caputala 6 ca Aefeso, ndinaphunzila kuti Yehova amafuna kuti ndizimvela makolo anga. Ndinali kufuna kuti banja lathu likhalenso pamtendele, ndipo ndinaganiza kuti ndikamvela makolo anga naonso adzandimvetsela. Panthawiyo ndinali kukonzekela mayeso a kusukulu. Conco, kwa miyezi itatu ndinacita zimene makolo anga anali kufuna. Koma ndinalonjeza Yehova kuti ndidzapitiliza kusonkhana pambuyo pa miyezi itatu.

Zimene ndinasankha zinali zolakwika. Ndakamba izi pa zifukwa ziŵili. Coyamba, ndinaganiza kuti pambuyo pa miyezi itatu ndidzakhalabe wofunitsitsa kutumikila Yehova. M’malomwake, ndinayamba kufooka mwakuuzimu. Caciŵili, panthawi imeneyo Atate ndi Amai anacita zilizonse zimene angathe kuti ndisiye kutumikila Yehova.

KUTHANDIZIDWA NDIPONSO KUTSUTSIDWA

Kumisonkhano, ndinapeza abale ndi alongo ambili amene anali kutsutsidwa ndi acibale ao. Iwo ananditsimikizila kuti Yehova adzandithandiza. (Mateyu 10:34-37) Anandifotokozela kuti ndikakhala wokhulupilika kwa Yehova, acibale anga angathe kuphunzila za Iye. Popeza kuti ndinali kudalila Yehova, ndinayamba kupemphela kwa iye mocokela pansi pa mtima.

Acibale anga anali kunditsutsa m’njila zosiyanasiyana. Mwacitsanzo, amai anali kundiletsa kuphunzila, ndipo nthawi zina anali kundinyengelela kuti ndisiye. Nthawi zambili ndinali kungokhala cete. Ndikawayankha tinali kukangana, cifukwa tonse tinali kuona wina kukhala wolakwa. Masiku ano, ndimaona kuti ndikanalemekeza maganizo a amai ndi zikhulupililo zao pokamba nao, zinthu zikanayenda bwino. Makolo anga anali kundipatsa nchito zambili kuti ndisacoke panyumba. Nthawi zina, anali kundikhomela panja kapena kundimana zakudya.

Amai anapempha anthu ena kuti andinyengelele kusintha maganizo anga. Iwo anauza aphunzitsi anga kuti akambe nane, koma sizinaphule kanthu. Ananditengelanso kwa abwana ao amene anandiuza kuti zipembedzo zonse n’zacabecabe. Amai anatumanso foni kwa acibale ao uku akulila, ndipo anali kuwacondelela kuti andithandize kusintha maganizo anga. Izi zinandikhumudwitsa kwambili. Koma kumisonkhano, akulu anandiuza kuti Amai akamauza acibale ao za ine ndiye kuti akulalikila kwa acibalewo.

Makolo anga anali kufuna kuti ndipite ku univesite n’colinga cakuti ndidzapeze nchito yabwino. Tonse tinali okwiya ndipo zinali zovuta kukambilana nkhaniyi mwamtendele. Conco, ndinacita kuwalembela makalata powafotokozela zolinga zanga. Atate anakwiya kwambili ndipo anati: “Ngati uganiza kuti ungapeze nchito, uipeze maŵa, apo ai udzacoka pano pa nyumba.” Ndinapempha Yehova kuti andithandize. Ndiyeno, tsiku lotsatila pamene ndinali mu utumiki, alongo aŵili anandipempha kuti ndiyambe nchito yophunzitsa ana ao. Atate sanasangalale ndi zimenezi cakuti anasiya kukamba nane ndipo anayamba kundipewa. Amai anakamba kuti zikanakhala bwino ndikanakhala cigawenga kuposa kukhala wa Mboni za Yehova.

Yehova anandithandiza kuongolela maganizo anga ndi kudziŵa zoyenela kucita

Nthawi zina ndinali kuganiza kuti sindinali kufunika kukonda Yehova kuposa makolo anga pa mlingo umenewu. Conco, ndinapemphela kwa Yehova ndi kusinkhasinkha zimene Baibulo limakamba ponena za cikondi cake. Izi zinandithandiza kuyamba kuona zinthu moyenela ndi kumvetsa kuti makolowo anali kunditsutsa cifukwa condidela nkhawa. Yehova anandithandiza kuongolela maganizo anga ndi kudziŵa zoyenela kucita. Ndiponso, cifukwa copita mu utumiki kaŵilikaŵili, ndinayamba kuikonda kwambili nchitoyi, cakuti ndinayamba kulakalaka kukhala mpainiya.

KUTUMIKILA MONGA MPAINIYA

Alongo ena atamva kuti ndifuna kuyamba upainiya, anandiuza kuti ndiyembekeze coyamba kuti makolo anga akhazike mtima pansi. Ndinapemphela kwa Mulungu kuti andipatse nzelu, kenako ndinafufuza za nkhaniyi m’zofalitsa zathu. Ndinaganizila cifukwa cake ndifuna kukhala mpainiya, ndipo ndinapemphanso abale ndi alongo okhwima mwa kuuzimu kuti andithandize. Ndiyeno, ndinasankha kusangalatsa mtima wa Yehova. Ndinadziŵanso kuti ngakhale nditayembekeza kwa kanthawi ndisanayambe upainiya, makolo anga adzapitilizabe kunditsutsa.

Ndinayamba kucita upainiya m’caka comaliza ca maphunzilo a kusekondale. Nditacita upainiya kwa kanthawi, ndinafuna kukatumikila ku malo osowa. Koma Amai ndi Atate sanandilole kucoka pa nyumba. Conco, ndinayembekezela mpaka nditakwanitsa zaka 20. Ndiyeno, ndinapempha ofesi ya nthambi kuti ndikatumikile kumwela kwa dziko la Japan pafupi ndi acibale anga kuti Amai asamade nkhawa kwambili.

Pamene ndinali kutumikila kumalo osowa, ndinasangalala kuona ophunzila Baibulo anga akubatizidwa. Ndinayamba kuphunzila Cingelezi kuti ndionjezele utumiki wanga. Nditaona cangu ca Apainiya apadela aŵili amene anali kutumikila pampingo pathu ndi mmene anali kuthandizila ena, ndinayamba kulakalaka kukhala mpainiya wapadela. Panthawiyo, Amai anadwala kaŵili mwakayakaya, ndipo pa maulendo onsewo ndinali kubwelela kunyumba kuti ndikawasamalile. Izi zinawacititsa cidwi moti anayamba kundikomelako mtima.

MADALITSO A YEHOVA

Patapita zaka 7, m’bale Atsushi, mmodzi wa apainiya apadela amene ndinali kutumikila nao pampingo, ananditumila kalata. Iye anali kufuna mlongo woti amange naye banja, ndipo anafuna kudziŵa ngati ndingam’konde. Sindinali kuganizila zokhala pa cibwenzi ndi m’bale Atsushi, ndipo sindinaganizilepo kuti angandifune. Patapita mwezi umodzi, ndinamuyankha kuti ndifuna kumudziŵa bwino coyamba. Pambuyo pake, ndinazindikila kuti tinali ndi zolinga zofanana. Tinali kufuna kupitilizabe utumiki wa nthawi zonse, ndipo tinali okonzeka kucita utumiki uliwonse. Patapita nthawi, tinamanga banja. Ndinasangalala kuona kuti Amai, Atate, ndi acibale anga ena anabwela ku phwando la cikwati cathu.

Nepal

Posapita nthawi, pamene tinali kutumikila monga apainiya a nthawi zonse, Atsushi anaikidwa kukhala woyang’anila dela wogwilizila. Kenako tinaikidwa kukhala apainiya apadela, ndipo pambuyo pake anatitumiza kukatumikila m’dela. Pamene tinamaliza kuyendela mipingo yonse m’dela limene tinapatsidwa, ofesi ya nthambi inatitumila foni. Anatipempha kuti tikapitilize kutumikila m’dela m’dziko la Nepal.

Ndinaphunzila zinthu zambili zokhudza Yehova cifukwa cotumikila m’maiko osiyanasiyana

Ndinali kudela nkhawa kuti makolo anga adzamva bwanji ndikapita kukatumikila kutali. Nditawatumila foni, Atate anandiyankha kuti, “Ndi kumalo kwabwino kumene ufuna kupita.” Panali patapita mlungu umodzi kucokela pamene bwenzi lao linawapatsa buku lonena za dziko la Nepal, ndipo io anali kuona kuti malowo ndi abwino kwambili kukacezako.

Tinali osangalala kutumikila pakati pa anthu aubwenzi ku Nepal. Pambuyo pake, anaonjezela dziko la Bangladesh kuti likhale mbali ya dela lathu. Ngakhale kuti dzikoli lili pafupi kwambili ndi dziko la Nepal, maikowa ndi osiyana kwambili. Tinali ndi zocita zambili mu utumiki wathu m’madela amenewa. Patapita zaka 5, anatipempha kuti tibwelelenso kuno ku Japan, kumene tikupitiliza kutumikila m’dela.

Ndinaphunzila zinthu zambili zokhudza Yehova pamene tinali kutumikila ku Japan, ku Nepal, ndi ku Bangladesh. Anthu m’maikowa ali ndi zikhalidwe ndi miyambo yosiyanasiyana. Ndipo munthu aliyense payekha ndi wapadela. Ndaona mmene Yehova amasamalila munthu aliyense payekha, kumulandila, kumuthandiza ndi kumudalitsa.

Ndili ndi zifukwa zambili zoyamikilila Yehova. Wandilola kuti ndim’dziŵe ndi kum’tumikila. Wandipatsanso mwamuna wabwino amene amakonda Yehova. Mulungu wandithandiza kupanga zosankha zabwino, ndipo pano ndili naye pa ubwenzi wabwino. Ndilinso pa ubwenzi wabwino ndi acibale anga. Cifukwa ca thandizo la Yehova, ndilinso pa ubwenzi ndi Amai. Ndine woyamikila kwambili kuti tsopano ndili pa mtendele ndi Mulungu komanso ndi amai anga.

Timasangalala ndi nchito ya m’dela