Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Yehova Mulungu Amakonda Kukamba ndi Anthu

Yehova Mulungu Amakonda Kukamba ndi Anthu

“Tamvela, ndikufuna ndikulankhule.”—YOBU 42:4.

NYIMBO: 113, 114

1-3. (a) N’ciani cionetsa kuti maganizo ndiponso mau a Mulungu ndi apamwamba kuposa a anthu? (b) Tiphunzila ciani m’nkhani ino?

YEHOVA anapatsa ena moyo n’colinga cakuti iwonso azisangalala. Iye analenga angelo, ndipo m’kupita kwa nthawi analenganso anthu. (Salimo 36:9; 1 Timoteyo 1:11) Coyamba, Yehova analenga mngelo amene mtumwi Yohane anamucha kuti “Mau.” (Yohane 1:1; Chivumbulutso 3:14) Mngelo ameneyo ndi Yesu, ndipo Yehova anali kumuuza maganizo ake ndi mmene anali kumvelela. (Yohane 1:14, 17; Akolose 1:15) Mtumwi Paulo anakamba kuti angelo naonso amakambilana m’cinenelo cosiyana kwambili ndi ca anthu.—1 Akorinto 13:1.

2 Yehova amadziŵa zinthu zonse zokhudza mabiliyoni a angelo ndiponso anthu amene iye analenga. Iye amamvetsela mapemphelo a anthu mamiliyoni ambili panthawi imodzi, mosasamala kanthu kuti akukamba cinenelo cotani. Akamamvetsela mapemphelowo, Yehova amakambanso ndi angelo ndi kuwapatsa malangizo. Yehova amakwanitsa kucita zimenezi cifukwa cakuti maganizo ake ndi mau ake ndi zapamwamba kwambili kuposa za anthu. (Ŵelengani Yesaya 55:8, 9.) Conco, pokamba ndi anthu, Mulungu amasintha ndi kugwilitsila nchito cinenelo cimene anthuwo angamve mosavuta.

3 M’nkhani ino, tiphunzila mmene Yehova amakambila ndi anthu m’njila yosavuta. Tiphunzilanso mmene Mulungu amasinthila mau ake pokambilana ndi anthu mogwilizana ndi zocitika za panthawiyo.

MULUNGU AMAKAMBA NDI ANTHU

4. (a) Kodi Yehova anagwilitsila nchito cinenelo citi pokamba ndi Mose, Samueli, ndi Davide? (b) Ndi nkhani zotani zimene zili m’Baibulo?

4 Pamene anali kukamba ndi munthu woyamba Adamu m’munda wa Edeni, Yehova ayenela kuti anagwilitsila nchito Ciheberi. Pambuyo pake, Yehova anakamba ndi amuna ena monga Mose, Samueli, ndi Davide. Amuna amenewa analemba maganizo a Mulungu osati ao ngakhale kuti anagwilitsila nchito mau awoawo ndi kalembedwe kawokawo ka Ciheberi. Mouzilidwa, io analemba mau ocokela kwa Yehova ndi mbili yokhudza ubwenzi wa pakati pa Mulungu ndi anthu ake. Mwacitsanzo, Baibulo limakamba za kukhulupilika kwao, cikondi cao, zolakwa zao, ndi kusakhulupilika kwao. Mfundo zonsezi zinalembedwa kaamba ka ubwino wathu.—Aroma 15:4.

Olemba Baibulo analemba mau ocokela kwa Yehova ndi mbili yokhudza ubwenzi wa pakati pa Mulungu ndi anthu ake.

5. Kodi Mulungu anali kukamba ndi anthu m’Ciheberi cabe? Fotokozani.

5 Pokamba ndi anthu, sikuti Yehova anali kugwilitsila nchito Ciheberi nthawi zonse. Pamene Aisiraeli anali kumasulidwa ku Babulo, ena a io anali atadziŵa kale kukamba Ciaramu. Mwina ndiye cifukwa cake Danieli, Yeremiya, ndi Ezara analemba mbali zina za Baibulo m’Ciaramu. *

6. N’cifukwa ciani Malemba Aciheberi anamasulidwa m’Cigiriki?

6 M’kupita kwa nthawi, Alexander Wamkulu anagonjetsa maiko ambili padziko lapansi, ndipo anthu ambili m’maikowo anayamba kukamba Cigiriki. Ayuda ambili naonso anayamba kukamba Cigiriki, kenako Malemba Aciheberi anamasulidwa m’Cigiriki. Malemba amenewa amachedwa Septuagint. Limeneli linali Baibulo loyambilila kumasulidwa, ndipo linali limodzi mwa Mabaibulo ofunika kwambili. Akatswili ena amakhulupilila kuti anthu onse amene anagwilako nchito yomasulila Baibulo la Septuagint anali 72. * (Onani mau amunsi.) Ena anamasulila Malemba Aciheberi liu ndi liu, koma ena sanatelo. Ngakhale n’telo, Ayuda okamba Cigiriki komanso Akristu anali kukhulupilila kuti Baibulo la Septuagint linali Mau a Mulungu.

7. Ndi cinenelo citi cimene Yesu anali kukamba pophunzitsa ophunzila ake?

7 Pamene Yesu anali padziko lapansi, ayenela kuti anali kukamba Ciheberi. (Yohane 19:20; 20:16; Machitidwe 26:14) Yesu ayenelanso kuti anali kukamba mau ena a Ciaramu amene anali ofala panthawiyo. Iye anali kudziŵanso Ciheberi cakale cimene Mose ndi aneneli anali kukamba, ndipo zolembedwa zao zinali kuŵelengedwa m’masunagoge mlungu uliwonse. (Luka 4:17-19; 24:44, 45; Machitidwe 15:21) Ngakhale kuti anthu anali kukambanso Cigiriki ndi Cilatini panthawi imene Yesu anali padziko lapansi, Baibulo silichula ngati Yesu anali kukambanso zinenelo zimenezo.

8, 9. N’cifukwa ciani Akristu ambili anali kukamba Cigiriki? Kodi mfundo imeneyi itiphunzitsa ciani za Yehova?

8 Ophunzila a Yesu oyambilila anali kukamba Ciheberi, koma iye atamwalila, ophunzilawo anayamba kukambanso zinenelo zina. (Ŵelengani Machitidwe 6:1.) Pamene uthenga wabwino unayamba kufalikila, Akristu ambili anayamba kukamba Cigiriki m’malo mwa Ciheberi. Popeza kuti anthu ambili anali kukamba Cigiriki, mabuku a Mateyu, Maliko, Luka, ndi Yohane analembedwa m’Cigiriki. * (Onani mau amunsi.) Makalata a mtumwi Paulo komanso mabuku ena a m’Baibulo naonso analembedwa m’Cigiriki.

9 N’zocititsa cidwi kuona kuti olemba Malemba Acikristu Acigiriki akagwila mau m’Malemba Aciheberi, nthawi zambili anali kugwila mauwo kucokela m’Baibulo la Septuagint. Nthawi zina, mauwo anali kusiyana pang’ono ndi mau a Ciheberi coyambilila. Motelo, zimene omasulilawo analemba zinakhala mbali ya Baibulo limene tili nalo masiku ano. Mfundo imeneyi ikutionetsa kuti Yehova saona cinenelo kapena cikhalidwe cina kukhala cabwino kuposa cina.—Ŵelengani Machitidwe 10:34.

Mulungu sayembekezela kuti tizikamba cinenelo cina cake kuti tim’dziŵe ndi kudziŵa zolinga zake

10. N’ciani cimene tikuphunzilapo tikaona mmene Yehova amakambila ndi anthu?

10 Taphunzila kuti Yehova amakamba ndi anthu mogwilizana ndi zocitika za panthawiyo. Mulungu sayembekezela kuti tizikamba cinenelo cina cake n’colinga cakuti tim’dziŵe ndi kudziŵa zolinga zake. (Ŵelengani Zekariya 8:23; Chivumbulutso 7:9, 10.) Taphunzilanso kuti Yehova anauzila olemba Baibulo ndi mzimu woyela, ndipo io analemba maganizo ake osati ao.

MULUNGU ANATETEZA UTHENGA WAKE

11. Ngakhale kuti anthu amakamba zinenelo zosiyanasiyana, n’cifukwa ciani limenelo si vuto kwa Yehova?

11 Anthu amakamba zinenelo zosiyanasiyana, koma limenelo si vuto kwa Yehova. Timadziŵa bwanji zimenezo? M’Baibulo muli mau ocepa a Yesu amene analembedwa m’cinenelo ceniceni cimene iye anali kukamba. (Mateyu 27:46; Maliko 5:41; 7:34; 14:36) Koma Yehova anaonetsetsa kuti uthenga wa Yesu walembedwa ndi kumasulidwa m’Cigiriki, ndipo m’kupita kwa nthawi unamasulidwanso m’zinenelo zina. Ngakhale kuti Ayuda ndi Akristu anakopa Mau a Mulungu mobwelezabweleza, uthenga wa Mulungu unatetezedwa. Makopewo anamasulidwa m’zinenelo zambili. Zaka pafupifupi 400 Kristu atapita kumwamba, John Chrysostom anakamba kuti ziphunzitso za Yesu zinali zitamasulidwa m’zinenelo za Asuri, Aiguputo, Amwenye, Aperisiya, Aitiyopiya ndi m’zinenelo zina zambili.

12. N’ciani cimene anthu acita pofuna kuononga Baibulo?

12 M’mbili yonse ya anthu, adani akhala akuononga Baibulo komanso kupha anthu omasulila ndi kufalitsa Baibulo. Patapita zaka pafupifupi 300 Yesu atabadwa, Mfumu ya Roma yochedwa Diocletian inalamula kuti Mabaibulo onse aonongedwe. Komabe, patapita zaka pafupifupi 1,200, William Tyndale anayamba kumasulila Baibulo m’Cingelezi. Tyndale anakamba kuti ngati Mulungu angamulole kukhala ndi moyo kwa nthawi yaitali, iye adzaonetsetsa kuti ngakhale munthu wosaphunzila adziŵe Baibulo kuposa wansembe. Cifukwa ca cizunzo, Tyndale anacoka ku England ndi kupita ku Ulaya kuti akamasulile ndi kusindikiza Baibulo. Ngakhale kuti atsogoleli a cipembedzo anayesa kutentha Mabaibulo onse amene anapeza, Baibulo limene Tyndale anamasulila linafalitsidwa kwa anthu ambili. Posapita nthawi, Tyndale ananyongedwa ndi kutenthedwa pamtengo. Koma atsogoleli a cipembedzo amenewo sanathe kuononga Baibulo la Tyndale. M’malomwake Baibulo limeneli ndi limene anagwilitsila nchito pomasulila Baibulo lochedwa King James Version.Ŵelengani 2 Timoteyo 2:9.

13. Kodi kupenda mipukutu yakale ya Baibulo kwaonetsa ciani?

13 N’zoona kuti m’Mabaibulo ena akale kwambili, muli zinthu zina zosiyanako pang’ono. Komabe, akatswili a Baibulo anapenda mosamalitsa mipukutu yambilimbili ya Baibulo ndi Mabaibulo ena akale. Pambuyo poyelekezela Mabaibulowo ndi mipukutuyo, akatswili amenewo anapeza mavesi oŵelengeka cabe amene anali osiyanako pang’ono. Koma uthenga wa m’Baibulo sunasinthe. Kufufuza mwa njilayi kwathandiza ophunzila Baibulo oona mtima kukhulupilila kuti Baibulo limene tili nalo masiku ano, ndi Mau ouzilidwa a Yehova.—Yesaya 40:8. * (Onani mau amunsi.)

14. Kodi Baibulo ndi lofala bwanji masiku ano?

14 Baibulo lamasulidwa m’zinenelo zoposa 2,800 ngakhale kuti anthu ena amafuna kuliononga kothelatu. Palibe buku lina limene lamasulidwa m’zinenelo zambili ngati Baibulo. Ngakhale kuti anthu ambili alibe cikhulupililo mwa Mulungu, Mau ake afalitsidwa kwambili kuposa buku lililonse m’mbili yonse ya anthu. N’zoona kuti Mabaibulo ena ndi ovuta kuŵelenga ndipo si olondola kwenikweni, koma pafupifupi onse ali ndi uthenga wopatsa ciyembekezo komanso wotsogolela ku moyo wosatha.

PANAFUNIKA BAIBULO LOSAVUTA KUMVA

15. (a) Kodi mabuku athu ofotokoza Baibulo asintha bwanji kuyambila mu 1919? (b) N’cifukwa ciani zofalitsa zathu coyamba zimalembedwa m’cingelezi?

15 Mu 1919, kagulu kocepa ka Ophunzila Baibulo kanasankhidwa kukhala “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” Panthawiyo, kapolo wokhulupilika anali kukamba kwambili ndi anthu a Mulungu m’Cingelezi. (Mateyu 24:45) Masiku ano, mabuku ofotokoza Baibulo akupezeka m’zinenelo zoposa 700. Mofanana ndi mmene zinalili ndi Cigiriki, anthu ambili amakamba Cingelezi masiku ano makamaka pankhani zokhudza malonda ndi maphunzilo. Pa cifukwa cimeneci, zofalitsa zathu zimalembedwa m’Cingelezi, kenako zimamasulidwa m’zinenelo zina.

16, 17. (a) N’ciani cimene anthu a Mulungu anali kufunikila? (b) Kodi zimenezi zinakwanilitsidwa bwanji? (c) Kodi colinga ca M’bale Knorr cinali ciani?

16 Zofalitsa zathu zonse zimazikidwa pa Baibulo. Poyamba, anthu a Mulungu anali kugwilitsila nchito Baibulo la King James Version, limene anamaliza kulimasulila mu 1611. Komabe, mau ake anali acikale ndi ovuta kumva. M’Baibulo limenelo, dzina la Mulungu linali kupezeka nthawi zoŵelengeka cabe, ngakhale kuti m’mipukutu yakale limapezeka masauzande ambili. M’Baibulo limenelo, munalinso zophophonya zambili, ndipo anaonjezelamo mavesi ena amene sapezeka m’mipukutu yakale. M’Mabaibulo ena a Cingelezi munalinso zophophonya zofananazo.

17 Mwacionekele, anthu a Mulungu anali kufunikila Baibulo lomasulidwa molondola ndi losavuta kumva. Motelo, Komiti Yomasulila Baibulo la Dziko Latsopano inakhazikitsidwa, ndipo abale a m’komiti imeneyi anali kutulutsa zigawozigawo za Baibuloli kuyambila mu 1950 mpaka mu 1960. Cigawo coyambilila pa ma voliyamu 6, cinatulutsidwa pamsonkhano wacigawo pa August 2, 1950. Pamsonkhanowo, M’bale Knorr anakamba kuti anthu a Mulungu afunika Baibulo lomasulidwa mwamakono. Baibulo limenelo linafunika kukhala lolondola, losavuta kumva, limenenso lingathandize anthu kuphunzila coonadi mosavuta. M’bale Knorr anakamba kuti panafunika Baibulo losavuta kuŵelenga ndi kumva monga mmene zolemba za ophunzila a Kristu zinalili. Colinga ca m’bale Knorr cinali cakuti Baibulo la Dziko Latsopano lithandize anthu mamiliyoni ambili kudziŵa Yehova.

18. Ndi makonzedwe otani amene athandiza pa nchito yomasulila Baibulo?

18 Podzafika mu 1963, colinga ca M’bale Knorr cinakwanilitsidwa. Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu linasindikizidwa mu Cidachi, Cifulenci, Cijelemani, Citaliyana, Cipwitikizi, ndi Cisipanishi. Mu 1989, Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova linakhazikitsa dipatimenti yatsopano ku likulu la padziko lonse n’colinga cothandiza omasulila Baibulo. Kenako mu 2005, linapeleka cilolezo cakuti omasulila amene amamasulila Nsanja ya Mlonda m’zinenelo zao, amasulilenso Baibulo m’zinenelo zimenezo. Panopa, Baibulo la Dziko Latsopano, lathunthu kapena mbali yake cabe, likupezeka m’zinenelo zoposa 130.

19. Ndi cocitika capadela citi cimene cinacitika mu 2013? Nanga tidzaphunzila ciani m’nkhani yotsatila?

19 Cingelezi casintha kwambili kucokela pamene Baibulo la Dziko Latsopano linatulutsidwa koyamba. Conco, panafunika kufewetsa mau ena. Pamsonkhano wapacaka wa nambala 129 wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, umene unacitika pa October 5 ndi 6, 2013, panapezeka anthu 1,413,676 ocokela m’maiko 31. Ena anaonelela pulogalamuyi kudzela pa intaneti. Pamsonkhanowo, m’bale wa m’Bungwe Lolamulila analengeza za kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso m’Cingelezi. Osonkhanawo anasangalala kwambili, ndipo ambili anagwetsa misozi yacisangalalo atalandila Baibulo latsopano. Pamene okamba nkhani anayamba kuŵelenga mavesi m’Baibulo lokonzedwanso, zinali zosavuta kwa onse kuzindikila kuti Baibulo lokonzedwanso linali losavuta kuŵelenga ndi kumva. M’nkhani yotsatila, tidzaphunzila zambili zokhudza Baibulo limeneli, ndiponso mmene likumasulidwila m’zinenelo zina.

^ par. 5 Poyamba, mau a pa Ezara 4:8-6:18, 7:12-26; Yeremiya 10:11, ndi pa Danieli 2:4b-7:28 analembedwa m’Ciaramu.

^ par. 6 Liu lakuti Septuagint limatanthauza “70.” Zioneka kuti nchito yomasulila malembawa inayamba zaka pafupifupi 300 Kristu asanabadwe ndipo inatha pambuyo pa zaka 150. Baibulo la Septuagint likali lofunika masiku ano cifukwa limathandiza akatswili kumvetsa mau ndi mavesi ovuta aciheberi.

^ par. 8 Anthu ena amaganiza kuti Mateyu analemba buku lake m’Ciheberi, kenako bukulo linamasulidwanso m’Cigiriki. Mwina Mateyu yemweyo ndi amene analimasulila.

^ par. 13 Onani Buku la Anthu Onse, tsamba 7-9, pa mutu wakuti “Kodi Bukulo Linapulumuka Bwanji?”