Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Muziyamikila Kuolowa Manja kwa Yehova

Muziyamikila Kuolowa Manja kwa Yehova

YEHOVA ndi Mulungu woolowa manja. (Yakobo 1:17) Zinthu zonse zimene analenga zimasonyeza kuti ndi woolowa manja. Iye analenga nyenyezi zambilimbili kumwamba ndi zomela zosiyanasiyana zokongola padziko lapansi.—Salimo 65:12, 13; 147:7, 8; 148:3, 4.

Amene analemba Salimo 104 anayamikila kwambili Yehova cifukwa ca zinthu zonse zimene analenga moti analemba nyimbo yomutamanda. Mukaŵelenga lemba limeneli, kodi nanunso mumayamikila Yehova ngati mmene wamasalimo anacitila? Iye anati: “Ndidzaimbila Yehova moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.” (Salimo 104:33) Kodi inunso mumafuna kutamanda Mulungu?

CITSANZO CABWINO KWAMBILI CA KUOLOWA MANJA

Yehova amafuna kuti tikhale owolowa manja monga mmene iye alili. Ndipo watiuza zifukwa zimene tiyenela kucitila zimenezi. Yehova anauzila mtumwi Paulo kulemba kuti: “Lamula acuma a m’nthawi ino kuti asakhale odzikweza, ndiponso kuti asamadalile cuma cosadalilika, koma adalile Mulungu, amene amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse kuti tisangalale. Uwalamule kuti azicita zabwino, akhale olemela pa nchito zabwino, owolowa manja, okonzeka kugawila ena, ndiponso asunge maziko abwino a tsogolo lao monga cuma, kuti agwile mwamphamvu moyo weniweniwo.”—1 Timoteyo 6:17-19.

M’kalata yake yaciŵili yopita ku Akorinto, Paulo anafotokoza mtima umene tiyenela kukhala nao popatsa zinthu anthu ena. Iye anati: “Aliyense acite mogwilizana ndi mmene watsimikizila mumtima mwake, osati monyinyilika kapena mokakamizika, cifukwa Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.” (2 Akorinto 9:7) Kodi tikakhala owolowa manja ndani amapindula? Paulo ananena kuti anthu ena amapindula tikawapatsa zosowa zao, koma ifenso timapindula cifukwa Yehova amatidalitsa.—2 Akorinto 9:11-14.

Ndiyeno, Paulo anafotokoza umboni waukulu wakuti Mulungu ndi woolowa manja. Iye anati: “Tikuyamika Mulungu cifukwa ca mphatso yake yaulele, imene sitingathe n’komwe kuifotokoza.” (2 Akorinto 9:15) ‘Mphatso yaulele’ yocokela kwa Yehova ndi zinthu zonse zimene iye amatipatsa kudzela mwa Yesu Kristu. Mphatso imeneyi ndi yapamwamba kwambili cakuti sitingathe kuifotokoza.

Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila zinthu zonse zimene Yehova ndi Yesu aticitila ndiponso zimene adzaticitila mtsogolo? Njila imodzi imene tingacitile zimenezi ndi mwa kugwilitsila nchito nthawi yathu, mphamvu zathu, ndi cuma cathu polambila Yehova ndi pothandiza ena kudziŵa za iye. Tingathe kucita zimenezi kaya tili ndi zinthu zambili kapena zocepa.—1 Mbiri 22:14; 29:3-5; Luka 21:1-4.