4 Kodi Tiyenela Kupemphela za Ciani?
ANTHU ena amanena kuti pa mapemphelo onse a Akhristu, pemphelo limene limanenedwa mobweleza-bweleza ni pemphelo lacitsanzo la Yesu, lomwe ena amalichula kuti Pemphelo la Ambuye kapena la Atate Wathu Wakumwamba. Kaya zimenezi ni zoona kapena ayi, mfundo ni yakuti pemphelo limeneli ni limodzi mwa mapemphelo amene anthu ambili sawamvetsa. Anthu ambili analiloweza pamtima ndipo amalinena tsiku lililonse mwinanso kangapo patsiku. Koma colinga ca Yesu pophunzitsa anthu pemphelo limeneli si cinali cimeneci. Kodi tidziwa bwanji zimenezi?
Asananene za pemphelo limeneli, Yesu ananena kuti: “Popemphela, usanene zinthu mobweleza-bweleza.” (Mateyu 6:7) Ndiyeno kodi Yesu akananena mawu amenewa zikanakhala kuti anali kafuna kuti anthu azinena pemphelo limeneli mobweleza-bweleza? Ayi ndithu. Conco, colinga ca Yesu cinali kutiphunzitsa zinthu zimene tiyenela kuchula m’pemphelo. Pemphelo limeneli limatithandizanso kudziwa zinthu zofunika kuzichula coyamba tikamapemphela. Tiyeni tionenso bwino-bwino zimene ananena. Pemphelo limeneli linalembedwa pa Mateyu 6:9-13
“Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeletsedwe.”
Apatu Yesu anakumbutsa otsatila ake kuti mapemphelo onse ayenela kupita kwa Atate, Yehova. Koma kodi mukudziwa kuti n’cifukwa ciani dzina la Yehova lili lofunika ndiponso cifukwa cake liyenela kuyeletsedwa?
Kuyambila kale pamene anthu analengedwa, dzina loyela la Mulungu ladetsedwa na mabodza amene anthu amanena. Satana, yemwe ni mdani wa Mulungu, amanena kuti Yehova ni wabodza, ni Wolamulila wodzikonda ndipo sayenela kumalamulila zolengedwa zake. (Genesis 3:1-6) Anthu ambili agwilizana na Satana. Iwo amaphunzitsa kuti Mulungu ni wopanda cifundo, ni wouma mtima ndiponso amazunza anthu. Iwo amakananso mfundo yakuti Mulungu ni Mlengi wa wazinthu zonse. Ena amalimbana na dzina la Mulungu lenilenilo lakuti Yehova policotsa m’mabaibo awo komanso poletsa anthu kuti asamaligwilitse nchito.
Baibo imasonyeza kuti Mulungu adzathetsa mabodza onsewa. (Ezekieli 39:7) Pocita zimenezo, iye adzathetsanso mavuto anu onse na kukupatsani zofunika zonse. Kodi adzacita bwanji zimenezo? Mawu otsatila amene Yesu ananena m’pempheloli, akupeleka yankho la funso limeneli.
“Ufumu wanu ubwele.”
Masiku ano, atsogoleli a zipembedzo ali na maganizo osiyana-siyana pa nkhani ya Ufumu wa Mulungu. Koma anthu amene anali kumvetsela zimene Yesu anaphunzitsa, anali kudziŵa kuti kale aneneli a Mulungu analosela kuti Mesiya, Mpulumutsi wosankhidwa na Mulungu, adzakhala mfumu ya Ufumu womwe udzasinthe zinthu padziko lapansi. (Yesaya 9:6, 7; Danieli 2:44) Ufumu umenewo udzayeletsa dzina la Mulungu mwa kucititsa kuti mabodza onse a Satana aonekele. Kenako Ufumuwo udzacotsa Satana na nchito zake zonse. Ufumu wa Mulungu udzathetsa nkhondo, matenda, njala ngakhalenso imfa. (Salimo 46:9; 72:12-16; Yesaya 25:8; 33:24) Conco mukamapemphela kuti Ufumu wa Mulungu ubwele, ndiye kuti mukupempha kuti malonjezo onsewa akwanilitsidwe.
“Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzi-modzinso pansi pano.”
Mawu a Yesu amenewa akusonyeza kuti ni zosakayikitsa kuti cifunilo ca Mulungu cidzacitikadi padziko lapansi pano monga mmene cikucitikila kumwamba, kumene Mulungu amakhala. Palibe cimene cinalepheletsa cifunilo ca Mulungu kucitika kumwamba. Kumeneko Mwana wa Mulungu anamenyana na Satana na ziwanda zake ndipo anawaponya padziko lapansi. (Chivumbulutso 12:9-12) Komanso, mofanana na mawu oyambilila m’pemphelo lacitsanzo la Yesu, mawu onena za kucitika kwa cifunilo ca Mulungu amenewa, akutithandiza kuti tiziganizila cinthu cofunika kwambili, cimene ni cifunilo ca Mulungu, osati cathu. Nthawi zonse cifunilo ca Mulungu n’cimene cimabweletsa zinthu zabwino kwambili kwa zolengedwa zonse. Ndiye cifukwa cake Yesu, ngakhale kuti anali wangwilo, anauza Atate wake kuti: “Cifunilo canu cicitike, osati canga.”—Luka 22:42..
“Mutipatse ife lelo cakudya cathu calelo.”
Kenako, Yesu anasonyeza kuti tikhozanso kupemphelela zosowa zathu. Sikulakwa kupempha Mulungu kuti atipatse zimene tikusowa pa moyo wathu. Ndipo kucita zimenezo kumatikumbutsa kuti Yehova ni amene “amapatsa anthu onse moyo, mpweya, na zinthu zonse.” (Machitidwe 17:25) Baibo imasonyeza kuti Yehova ni kholo lacikondi ndipo amasangalala kupatsa ana ake zinthu zimene anawo akufuna. Komabe mofanana na kholo lililonse labwino, iye sapatsa anthu zinthu zimene akudziwa kuti sizingawathandize.
“Mutikhululukile zolakwa zathu.”
Kodi timafunikiladi kuti Mulungu atikhululukile? Anthu ambili masiku ano asiya kukhulupilila kuti anthufe ndife ocimwa ndipo sakuonanso kuti ucimo ni nkhani yaikulu. Koma Baibo imasonyeza kuti ucimo ni umene unayambitsa mavuto onse amene tikukumana nawo ndipo ni umene unacititsa kuti anthufe tizifa. Popeza anthufe tinabadwa ocimwa, nthawi na nthawi timalakwa ndipo kuti tidzakhale na moyo wosatha, zikudalila kuti Mulungu azitikhululukila. (Aroma 3:23; 5:12; 6:23) Ni zolimbikitsa kudziwa kuti Baibo imanena kuti: “Inu Yehova ndinu Mulungu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.”—Salimo 86:5..
“Mutilanditse kwa woipayo.”
Kodi mukudziwa kuti mukufunikila citetezo ca Mulungu mwamsanga? Anthu ena amakana zoti “woipayo,” amene ni Satana, alipodi. Koma Yesu anaphunzitsa kuti Satana alipo ndithu, moti anacita kunena kuti Satanayo ndiye “wolamulila wa dzikoli.” (Yohane 12:31; 16:11) Conco Satana waipitsa maganizo a anthu ambili m’dzikoli, ndipo akufunitsitsa kuipitsanso maganizo anu. Colinga cake n’cakuti musakhale pa ubwenzi wabwino na Atate wanu wakumwamba, Yehova. (1 Petulo 5:8) Ngakhale zili conco, Yehova ni wamphamvu kwambili kuposa Satana ndipo amakhala wofunitsitsa kuteteza anthu amene amamukonda.
Apa sitinachule nkhani zonse zimene tingapemphelele, koma tangofotokoza mwacidule cabe mfundo zikulu-zikulu za m’pemphelo lacitsanzo la Yesu. Kumbukilani kuti lemba la 1 Yohane 5:14 limati: “Ciliconse cimene tingamupemphe [Mulungu] mogwilizana ndi cifunilo cake, amatimvela.” Conco, musaganize kuti mavuto anu ni aang’ono kwambili oti simungamuuze Mulungu.—1 Petulo 5:7.
Nanga bwanji za nthawi yoyenela kupemphela ndiponso malo amene tingapemphelelepo? Kodi zimenezi n’zofunikanso?