6 Kodi Kupemphela N’kothandiza?
KODI kupemphela kungatithandize? Inde, cifukwa Baibo imanena kuti mapemphelo a atumiki okhulupilika a Mulungu amawathandizadi. (Luka 22:40; Yakobo 5:13) Ndipotu, kupemphela kungatithandize kwambili pa zinthu zauzimu. Kungatithandizenso kuti maganizo athu akhale m’malo ndiponso kuti tikhale na thanzi labwino. Kodi zimenezi zingacitike bwanji?
Tiyelekeze kuti muli na mwana wamng’ono amene wapatsidwa mphatso. Kodi mungamuphunzitse kuti azingoyamikila mphatsoyo camumtima? Kapena mungamuphunzitse kuti azinena mawu osonyeza kuti akuyamikila? Tikauza munthu wina mmene tikumvela mumtima mwathu pa nkhani inayake yofunika, timayamba kuganizila kwambili za nkhaniyo ndipo imakhazikika mumtima mwathu. Kodi zimenezi zimacitikanso tikamalankhula na Mulungu? Inde. Taganizilani zitsanzo izi.
Mapemphelo oyamikila. Kuyamikila Atate wathu pa zabwino zimene zaticitikila, kumacititsa kuti tiziganizila zinthu zabwino zimene iye amaticitila. Zimenezi zingacititse kuti tikhale na mtima woyamikila, tizisangalala komanso tisamangokhalila kudandaula nthawi zonse.—Afilipi 4:6.
Citsanzo: Yesu anayamikila Atate wake cifukwa ca mmene anali kuyankhila mapemphelo ake.—Yohane 11:41.
Mapemphelo opempha cikhululuko ca Mulungu. Tikapempha Mulungu kuti atikhululukile, timakhala na cikumbumtima cabwino, timalapadi mocokela pansi pamtima ndipo timazindikila kuopsa kwa zimene tinacitazo. Timapezanso mtendele wa mumtima m’malo mokhala munthu wacisoni.
Citsanzo: Davide anapemphela posonyeza kulapa ndiponso cisoni cimene anali naco.—Salimo 51.
Kupemphela kuti Mulungu atitsogolele ndiponso atipatse nzelu. Kupempha Yehova kuti atitsogolele kapena kuti atipatse nzelu zotithandiza kupanga zisankho zabwino, kungatithandize kukhala odzicepetsa zenizeni. Kungatikumbutse kuti pali zina zimene sitingathe kucita ndipo kungatithandizenso kuti tizikhulupilila kwambili Atate wathu wakumwamba.—Miyambo 3:5, 6..
Citsanzo: Solomo anapemphela modzicepetsa kuti Mulungu amutsogolele komanso kuti amupatse nzelu zomuthandiza kulamulila Aisiraeli.—1 Mafumu 3:5-12
Kupemphela tikakhala pa mavuto. Tikamutulila Mulungu nkhawa zathu zonse timapeza mtendele wa mumtima, ndipo tidzayamba kudalila kwambili Yehova, m’malo modzidalila tekha.—Salimo 62:8.
Citsanzo: Mfumu Asa anapemphela ataopsezedwa na mdani wamphamvu kwambili.—2 Mbiri 14:11.
Kupemphelela ena. Kupemphelela ena kumatithandiza kupewa kudzikonda ndipo kumatithandiza kukulitsa mtima wacifundo na woganizila ena.
Citsanzo: Yesu anapemphelela otsatila ake.—Yohane 17:9-17.
Mapemphelo otamanda Mulungu. Tikamatamanda Yehova cifukwa ca zinthu zosangalatsa zimene analenga ndiponso makhalidwe ake ocititsa cidwi timayamba kumupatsa ulemu komanso kumuyamikila kwambili. Mapemphelo amenewo angatithandizenso kuti tiyandikile Mulungu, Atate wathu.
Citsanzo: Davide anatamanda Mulungu na mtima wonse cifukwa ca zimene analenga.—Salimo 8..
Ubwino wina wa pemphelo ni wakuti, timapeza “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Afilipi 4:7) M’dziko lamavutoli, n’zosowa kupeza mtendele wotelewu. Mtendele wa mumtima umacititsanso kuti tikhale na thanzi labwino. (Miyambo 14:30) Komabe kodi mtendele umenewu tingaupeze mwa kulimbikila kwathu kokha? Kapena palinso cinthu cina cofunika kwambili?
Pemphelo limatithandiza kuti tikhale na thanzi labwino, kuti maganizo athu akhale m’malo komanso kuti tikhale pa ubwenzi wabwino na Mulungu