7 Kodi Mulungu Amamva na Kuyankha Mapemphelo?
ANTHU ambili amafuna kudziŵa yankho la funso limeneli. Baibo imasonyeza kuti Yehova amamvetseladi mapemphelo masiku ano. Komabe kuti iye amve kapena asamve mapemphelo anu zimadalila inuyo.
Yesu anadzudzula atsogoleli acipembedzo amene anali kupemphela mwacinyengo. Iwo anali kungofuna kudzionetsela kuti ni olungama. Iye ananena kuti anthu amenewa ‘anali kulandililatu mphoto yawo yonse.’ Zimenezi zikutanthauza kuti iwo analandila zimene anali kufuna zokhazo, zimene ni ulemu kucokela kwa anthu. Koma Mulungu sanayankhe mapemphelo awo. (Mateyu 6:5) Masiku anonso, anthu ambili amapemphela mogwilizana na zofuna zawo, osati za Mulungu. Mulungu sangamve mapemphelo awo cifukwa amanyalanyaza mfundo za m’Baibo zimene takambilanazi.
Nanga inuyo bwanji? Kodi Mulungu angamve komanso kuyankha mapemphelo anu? Kuti Mulungu amve ndiponso kuyankha mapemphelo anu, si zidalila mtundu wanu, dziko limene mumacokela kapenanso kuti kaya ndinu olemela kapena osauka ayi. Baibo imatitsimikizila kuti: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandila munthu wocokela mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ni kucita cilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Kodi inuyo mumaopa Mulungu ndipo mumacita cilungamo? Ngati mumaopa Mulungu, ndiye kuti mumamulemekeza kwambili ndipo mumaopa kumukhumudwitsa. Ndiponso ngati mumacita cilungamo, ndiye kuti mumayesetsa kucita zimene Mulungu amanena kuti n’zolungama m’malo momangotsatila zofuna zanu kapena za anthu ena. Kodi mukufunadi kuti Mulungu azimvetsela mapemphelo anu? Baibo ingakuthandizeni kuti zimenezi zitheke. *
Komabe, anthu ambili amafuna kuti Mulungu aziyankha mapemphelo awo mozizwitsa. Koma ngakhale pa nthawi imene Baibo inali kulembedwa, Mulungu anali kucita zozizwitsa mwa kamodzi-kamodzi. Pa zozizwitsa zimene zinalembedwa m’Baibo, nthawi zambili pankatha zaka zambili kucokela pamene cozizwitsa cina cinacitika, kudzafika pa cozizwitsa cina. Komanso Baibo imasonyeza kuti nthawi yocita zozizwitsa inatha atumwi onse atatha kufa. (1 Akorinto 13:8-10) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu sayankhanso mapemphelo masiku ano? Ayi ndithu. Taonani ena mwa mapemphelo amene iye amayankha.
Mulungu amapeleka nzelu. Yehova ndiye Cimake ca nzelu zenizeni. Iye amapeleka nzelu zimenezi moolowa manja kwa anthu amene amafuna kudziŵa malangizo ake ndiponso amafunitsitsa kutsatila malangizowo pa moyo wawo.—Yakobo 1:5.
Mulungu amatipatsa mzimu wake woyela pamodzi na madalitso amene amabwela cifukwa ca mzimuwo. Mzimu woyela ni mphamvu ya Mulungu yogwila nchito. Palibe mphamvu yoposa imeneyi. Mzimu woyela umenewu ungatithandize kuti tipilile mayeselo. Ungatithandizenso kupeza mtendele wa mumtima tikamakumana na mavuto. Komanso, ungatithandize kukhala na makhalidwe abwino ndiponso osililika. (Agalatiya 5:22, 23) Yesu anatsimikizila otsatila ake kuti Mulungu amapeleka mphatso imeneyi mowolowa manja.—Luka 11:13..
Mulungu amathandiza anthu amene akufuna kuti amudziŵe. (Machitidwe 17:26, 27) Padziko lonse pali anthu ambilimbili amene akufuna kudziŵa coonadi. Iwo akufuna atadziŵa dzina la Mulungu, colinga cake cokhudza dziko lapansi ndiponso anthu, komanso zimene angacite kuti amuyandikile. (Yakobo 4:8) Nthawi zambili a Mboni za Yehova amakumana na anthu otelewa, ndipo amasangalala kukambilana a anthuwa mayankho a m’Baibo a mafunso amenewa.
Kodi inuyo mwalandila magazini ino kuti mudziŵe zinthu ngati zimenezi? Kodi mukufunitsitsa mutamudziŵa Mulungu? Mwina imeneyi ni njila imene Mulungu akuyankhila mapemphelo anu.
^ ndime 5 Kuti mudziwe zambili zimene mungacite kuti Mulungu aziyankha mapemphelo anu, ŵelengani mutu 17 wa buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni? lofalitsidwa na Mboni za Yehova.