Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Muzikondana”

“Muzikondana”

“Muzikondana”

”Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukondelani, inunso muzikondana. Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.”—YOHANE 13:34, 35.

Kodi Mawu Amenewa Amatanthauza Ciani? Khristu anauza otsatila ake kuti azikondana ngati mmene iyeyo anawakondela. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali kukonda anthu? Iye anali kukonda kwambili anthu ngakhale kuti pa nthawiyo khalidwe losankhana mitundu komanso lonyoza akazi linali lofala. (Yohane 4:7-10) Cifukwa ca cikondi, Yesu anali kugwilitsa nchito nthawi komanso mphamvu zake kuti athandize ena. Iye anali kugwilitsanso nchito nthawi yake yopuma kuthandiza anthu. (Maliko 6:30-34) Pamapeto pake Khristu anasonyeza cikondi mwa njila yapadela kwambili. Iye anati: “Ine ndine m’busa wabwino. M’busa wabwino amataya moyo wake cifukwa ca nkhosa.”—Yohane 10:11.

Mmene Akhristu Oyambilila Anali Kucitila Zimenezi: M’nthawi ya atumwi, Akhristu anali kuchulana kuti “m’bale” kapena “mlongo.” (Filimoni 1, 2) Anthu amitundu yonse anali olandilidwa mu mpingo wacikhristu poti onse anali kukhulupilila kuti “palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi Mgiriki, popeza kwa onsewo Ambuye ndi mmodzi.” (Aroma 10:11, 12) Pentekosite wa mu 33 C.E. atatha, ophunzila a Yesu a ku Yerusalemu “anali kugulitsa malo awo ndi zina zimene anali nazo, n’kugawa kwa onse zimene apeza, aliyense malinga ndi kusowa kwake.” Kodi iwo anacita zimenezi cifukwa ciani? Anali kufuna kuti anthu amene angobatizika kumene akhalebe ku Yerusalemuko kuti apitilize “kulabadila zimene atumwiwo anali kuphunzitsa.” (Machitidwe 2:41-45) Kodi n’ciani cinacititsa kuti iwo akhale na mtima wogawana zinthu na ena? Pasanathe zaka 200 kucokela pamene atumwi anafa, munthu wina dzina lake Tertullian analemba zimene anthu ena ananena zokhudza Akhristu kuti: “Iwo amakondana kwambili . . . ndipo ni okonzeka ngakhale kufelana.”

Ndani Akucita Zimenezi Masiku Ano? Buku lina lolembedwa mu 1837, linanena kuti kwa zaka zambili, anthu amene amanena kuti ni Akhristu “akhala akucitilana nkhanza zoopsa kuposa zimene acitilidwa na anthu osapemphela.” (The History of the Decline and Fall of the Roman Empire) Komanso zotsatila za kafukufuku wina amene anacitika posacedwapa ku United Stated zinasonyeza kuti anthu ambili amene amapembedza, maka-maka amene amati ni Akh ristu, amakhala atsankho. Nthawi zambili anthu a chalichi cimodzi amasalana cifukwa cakuti akucokela m’mayiko osiyana ndipo zimenezi zimacititsa kuti asamathandizane pakakhala mavuto.

Mu 2004, mphepo yamkuntho inawomba kanayi motsatizana m’miyezi iŵili yokha mumzinda wa Florida. Izi zitacitika, cheyamani wa komiti ya mumzindawu yoona zogwa mwadzidzidzi (Florida’s Emergency Operations Committee), anali kufuna kuona ngati zinthu zomwe komitiyi inapeleka zinali kagwilitsidwa nchito moyenela. Pambuyo pake, cheyamaniyu ananena kuti panalibe gulu limene linali kucita zinthu mwadongosolo ngati la Mboni za Yehova ndipo ananena kuti anali wokonzeka kupeleka thandizo lililonse limene a Mboniwo angafunikile. Komanso izi zisanacitike, mu 1997, a Mboni za Yehova a m’mayiko ena anapita kudziko la Democratic Republic of Congo kukathandiza a Mboni anzawo komanso anthu ena amene anali kufunikila mankhwala, cakudya komanso zovala. Zinthu zimene anakapelekazo zinali zimene a Mboni za Yehova a ku Ulaya anapeleka ndipo zinali zandalama zokwana madola 1 miliyoni a ku United States.