Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Sali Mbali ya Dziko”

“Sali Mbali ya Dziko”

“Sali Mbali ya Dziko”

Dziko likudana nawo, cifukwa sali mbali ya dziko.”—YOHANE 17:14.

Kodi Mawu Amenewa Amatanthauza Ciani? Popeza Yesu sanali mbali ya dziko, sanali kulowelela ndale komanso zocitika zina za m’nthawi yake. Iye ananena kuti: “Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisapelekedwe kwa Ayuda. Koma ufumu wanga si wocokela pansi pano ayi.” (Yohane 18:36) Iye analangizanso otsatila ake kuti azipewa maganizo, malankhulidwe ndiponso makhalidwe amene Mawu a Mulungu amaletsa.—Mateyu 20:25-27.

Mmene Akhristu Oyambilila Anali Kucitila Zimenezi: Munthu wina amene amalemba nkhani zacipembedzo, dzina lake Jonathan Dymond, analemba kuti Akhristu oyambilila “sanali kumenya nawo nkhondo ngakhale zitakhala kuti kucita zimenezi kuwaika m’mavuto monga kunyozedwa, kumangidwa kapena kuphedwa kumene.” Iwo anali kulolela kuvutika kusiyana n’kuti acite nawo zandale. Komanso khalidwe lawo linali kucititsa kuti azisiyana na anthu ena. Akhristu anauzidwa kuti: “Cifukwa cakuti simukupitiliza kuthamanga nawo limodzi m’cithaphwi ca makhalidwe oipa, anthu a m’dzikoli sakumvetsa, conco amakunyozani.” (1 Petulo 4:4) Munthu wina wolemba mbili yakale, dzina lake Will Durant, analemba kuti “anthu akunja, omwe anali kukonda kwambili zinthu zosangalatsa, anali kuona kuti Akhristu anali kuwavutitsa cifukwa Akhristuwo anali kutsatila kwambili cikhulupililo cawo komanso anali osasunthika pa nkhani ya makhalidwe abwino.”

Ndani Akucita Zimenezi Masiku Ano? Ponena za kusalowelela ndale kwa Akhristu, buku lina linanena kuti: “Mfundo yoti Mkhristu asamalowe usilikali cifukwa ca cikumbumtima cake ni yosamveka.” (New Catholic Encyclopedia) Komanso nkhani imene inalembedwa m’nyuzipepala ina inanena kuti lipoti limene bungwe lina loona za ufulu wa anthu a ku Africa linatulutsa linasonyeza kuti machalichi onse anamenya nawo nkhondo ya ku Rwanda m’caka ca 1994, “kupatulapo Mboni za Yehova zokha.”—Reformierte Presse

Ponena za kupha anthu mwankhanza kumene kunacitika mu ulamulilo wa Nazi, mphunzitsi wina anadandaula kuti “panalibe gulu la anthu kapena bungwe lililonse m’dzikolo lomwe linanenapo ciliconse cosonyeza kukhumudwa na mabodza amene anali kunenedwa komanso nkhanza zomwe zinacitika nthawi imeneyi.” Koma mphunzitsiyu atapita kumalo ena osungilako zinthu zakale, kumene anasungako zinthu zokumbukila zimene zinali kacitika m’nthawi ya ulamulilo wa Nazi, iye analemba kuti: “Koma panopa nadziŵa zoona zake.” Mphunzitsiyo anazindikila kuti a Mboni za Yehova anakhalabe olimba pa cikhulupililo cawo ngakhale kuti anali kuzunzidwa.

Nanga bwanji za makhalidwe a Akhristu? Magazini ina ya ku United States inanena kuti: “Acinyamata ambili mu mpingo wa Katolika sagwilizana na zimene cipembedzoci cimaphunzitsa zoti mwamuna na mkazi asamakhalile limodzi asanakwatilane [komanso] asamagonane asanakwatilane.” (U.S. Catholic) M’magaziniyi munalinso mawu a m’busa wa chalichici akuti: “Anyamata na atsikana ambili akamakwatilana amakhala atayamba kale kukhalila limodzi.” Koma buku lina linanena kuti a Mboni za Yehova “amayesetsa kukhala na makhalidwe abwino zivute zitani.”—The New Encyclopædia Britannica