Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Uthenga Wabwino Uwu wa Ufumu Udzalalikidwa”

“Uthenga Wabwino Uwu wa Ufumu Udzalalikidwa”

“Uthenga Wabwino Uwu wa Ufumu Udzalalikidwa”

“Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”MATEYU 24:14.

Kodi Mawu Amenewa Amatanthauza Ciani? Luka, yemwe analemba nawo Uthenga Wabwino, ananena kuti Yesu “anayamba ulendo woyenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi. Ulendowu unali wokalalikila na kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.” (Luka 8:1) Komanso Yesuyo ananena kuti: “Ndiyenela kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu . . . cifukwa ndi zimene anandituma kudzacita.” (Luka 4:43) Iye anatumiza ophunzila ake kuti akalalikile uthenga wabwino m’matauni na m’midzi ndipo kenako anawauza kuti: “Mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.”—Machitidwe 1:8; Luka 10:1.

Mmene Akhristu Oyambilila Anali kicitila Zimenezi: Ophunzila a Yesu sanacedwe kuyamba kugwila nchito imene Yesu anawauzayi. “Tsiku ndi tsiku m’kachisi ndiponso kunyumba ndi nyumba, anapitiliza mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu.” (Machitidwe 5:42) Anthu onse anali kugwila nawo nchito yolalikilayi, osati kungosiyila anthu apadela okha. Wolemba mbili yakale wina, dzina lake Neander, analemba kuti “Celsus, yemwe anali munthu woyamba kulemba nkhani zotsutsa Cikhristu, anali kunyoza Akhristu cifukwa anthu osaphunzila monga owomba nsalu, osoka nsapato komanso ofufuta zikopa anali kulalikila nawo uthenga wabwino.” Munthu wina, dzina lake Jean Bernardi, analemba m’buku lake kuti: “[Akhristu] anali kufunika kupita kulikonse na kukalalikila kwa munthu aliyense. Anali kulalikila m’misewu, m’mizinda, m’misika ndiponso m’nyumba za anthu. Anali kucita zimenezi kaya alandilidwe kapena ayi. . . . Ndipo anali kufunika kukafika kumalekezelo a dziko lapansi.”—The Early Centuries of the Church.

Ndani Akucita Zimenezi Masiku Ano? Wansembe wina wa chalichi ca Anglican, dzina lake David Watson, analemba kuti: “Cifukwa cina cimene cikucititsa kuti masiku ano anthu ambili a m’chalichi cathu asamakhale na cidwi cotumikila Mulungu n’cakuti, chalichici siciona nkhani yolalikila komanso kuphunzitsa kukhala yofunika.” Munthu wina, dzina lake José Luis Pérez Guadalupe, analemba m’buku lina zokhudza anthu a m’chalichi ca Evanjeliko, ca Adventist komanso machalichi ena. Iye analemba kuti “anthu amenewa samapita kunyumba na nyumba.” Koma ponena za a Mboni za Yehova, wansembeyu analemba kuti: “Iwo amalalikila kunyumba na nyumba ndipo amayesetsa kufika nyumba iliyonse.”—Why Are the Catholics Leaving?

Mfundo yocititsa cidwi komanso yoona ni imene munthu wina dzina lake Jonathan Turley analemba m’buku lina. Iye anati: “Ukangochula kuti Mboni za Yehova, anthu ambili nthawi yomweyo amaganiza za anthu amene amabwela kunyumba zathu mwadzidzidzi n’kumadzatilalikila. Kwa a Mboni za Yehova, kukopa anthu kunyumba na nyumba si nkhani yongofuna kuti anthu ambili ayambe kutsatila cikhulupililo cawo ayi, koma iwo amaona kuti kucita zimenezi kumawathandizanso kukhala na cikhulupililo colimba.”—Cato Supreme Court Review, 2001-2002.

[Bokosi]

Kodi Ndani Amasonyeza Kuti Ni Akhristu Oona?

Mukaganizila mfundo za m’Malemba zimene takambilana mu nkhanizi, kodi inuyo mukuona kuti ni ndani amene akucita zinthu zosonyeza kuti ni Akhristu oona? Ngakhale kuti pali anthu ambili amene amati ni Akhristu, kumbukilani mawu amene Yesu anauza otsatila ake. Iye anati: “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akucita cifunilo ca Atate wanga wakumwamba.” (Mateyu 7:21) Kudziŵa anthu amene akucita cifunilo ca Atate kapena kuti amene amacita zinthu zosonyeza kuti ni Akhristu oona, n’kuyamba kupita kumisonkhano yawo, kungakuthandizeni kuti mudzapeze madalitso ambili mu Ufumu wa Mulungu. Kuti mudziŵe zambili zokhudza madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweletse, funsani a Mboni za Yehova amene anakupatsani magaziniyi.—Luka 4:43.