Ganizilanani Ndi Kulimbikitsana
Ganizilanani Ndi Kulimbikitsana
“Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino.”—AHEB. 10:24.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
Kodi ‘kuganizilana’ kumatanthauzanji?
Kodi ‘tingalimbikitsane motani pa cikondi ndi nchito zabwino’?
Kodi tiyenela kucita ciani kuti ‘tilimbikitsane’?
1, 2. Kodi n’ciani cinathandiza Mboni za Yehova zokwana 230 kupulumuka ulendo wokaphedwa kumapeto kwa nkhondo yaciŵili ya padziko lonse?
PAMENE ulamulilo wa Nazi unagonja pa nkhondo yaciŵili ya padziko lonse, bomalo linalamula kuti anthu masauzande ambili amene anali atatsala m’ndende zozunzilako anthu aphedwe. Bomalo linalamula kuti akaidi a m’ndende ya Sachsenhausen atengedwe kupita kunyanja ndi kukawakweza m’zombo, ndiyeno pambuyo pake akamize zombo zimenezo m’nyanja. Ciwembu cimeneco cinayamba kudziŵika kuti ulendo wokaphedwa.
2 Akapolo okwana 33,000 amene anali m’ndende ya Sachsenhausen anayenela kuyenda ulendo wa makilomita 250 kupita ku doko la mu mzinda wa Lübeck, ku Germany. Pakati pa anthu amenewo panali Mboni za Yehova zokwana 230 zocokela m’maiko 6, zimene zinalamulidwa kuyenda nao ulendo umenewo. Onse anali ofooka ndi njala ndi matenda. Kodi abale athu anakwanitsa bwanji kuyenda ulendo wokaphedwa umenewo? Mmodzi wa io anati: “Tinapitiliza kulimbikitsana kuti tipitilize kupilila.” Iwo anapulumuka mavuto amenewo cifukwa cakuti anali kukondana ndiponso cifukwa ca “mphamvu yoposa yacibadwa” yocokela kwa Mulungu.—2 Akor. 4:7.
3. N’cifukwa ciani tifunikila kulimbikitsana?
3 Masiku ano sitili pa ulendo wokaphedwa ngati umenewo, koma timakumana ndi mavuto ambili. Pambuyo pa kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu mu 1914, Satana anacotsedwa kumwamba ndipo anam’thamangitsila padziko lapansi. Iye ali ndi “mkwiyo waukulu podziŵa kuti wangotsala ndi kanthawi kocepa.” (Chiv. 12:7-9, 12) Pamene dziko likuyandikila Aramagedo, Satana akuyesa kutifooketsa mwa kuuzimu mwa kugwilitsila nchito ziyeso ndi mavuto. Kuphatikiza pa zimenezi palinso nkhawa zimene timakhala nazo tsiku ndi tsiku. (Yobu 14:1; Mlal. 2:23) Nthawi zina mavuto akaculuka angatifooketse kwambili cakuti ngakhale kuti ndife olimba motani mwa kuuzimu, sitingakwanitse kuwapilila mwa ife tokha. Ganizilani za mbale wina amene kwa zaka zambili anali kuthandiza anthu ambili mwa kuuzimu. Mbaleyo atakalamba, iye ndi mkazi wake anavutika ndi matenda, ndipo anayamba kumva kuti akusoŵa cilimbikitso. Monga mmene zinalili ndi mbale ameneyo, tonse timafunikila “mphamvu yoposa yacibadwa” yocokela kwa Yehova ndi cilimbikitso ca anzathu.
4. Kodi ndi malangizo a mtumwi Paulo ati amene tiyenela kukumbukila ngati tifuna kulimbikitsa ena?
4 Kuti tilimbikitse anzathu, tiyenela kutsatila malangizo amene mtumwi Paulo anapeleka kwa Akristu Aciheberi. Iye anati: “Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena acizoloŵezi cosafika pamisonkhano akucitila. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezele kucita zimenezi, maka-maka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikila.” (Aheb. 10:24, 25) Kodi tingagwilitsile nchito bwanji uphungu wofunika umenewu?
‘GANIZILANANI’
5. Kodi ‘kuganizilana’ kumatanthauzanji? Nanga pamafunika khama lotani kuti zimenezi zitheke?
5 ‘Kuganizilana’ kumatanthauza “kulingalila zosoŵa za ena.” Kodi tingazidziŵe bwanji zosoŵa za ena ngati timangowapatsa moni wacidule pa Nyumba ya Ufumu kapena kungokamba nao nkhani zina zosafunika kweni-kweni? Zingakhale zovuta kudziŵa zosoŵa zao mwa njila imeneyo. N’zoona kuti tiyenela kusamala kuti ‘tisalowelele mu nkhani za ena.’ (1 Ates. 4:11; 1 Tim. 5:13) Koma ngati tifuna kulimbikitsa abale athu, tiyenela kuwadziŵa bwino. Tiyenela kudziŵa mmene zinthu zilili pa umoyo wao, makhalidwe ao, umoyo wao wa kuuzimu, zinthu zimene amacita bwino ndi zifooko zao. Ayenela kutiona monga mabwenzi ao ndipo afunika kudziŵa kuti timawakonda. Kuti zimenezi zitheke, tiyenela kuceza nao nthawi ndi nthawi osati kokha pamene akumana ndi mavuto kapena pamene alefuka.—Aroma 12:13.
6. Kodi n’ciani cingathandize mkulu ‘kuganizila’ nkhosa zimene akusamalila?
6 Akulu mumpingo akulangizidwa kuti ayenela ‘kuweta gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwao,’ mofunitsitsa ndiponso ndi mtima wonse. (1 Pet. 5:1-3) N’zosatheka kuti akulu awete bwino nkhosa ngati io sazidziŵa bwino nkhosa zimene akuyang’anila. (Ŵelengani Miyambo 27:23.) Ngati akulu amamasuka ndi okhulupilila anzao ndiponso amasangalala kuceza nao, sizikhala zovuta kuti nkhosa zipemphe thandizo limene zikufuna. Abale ndi alongo naonso adzakhala omasuka kwambili kufotokozela akulu zakukhosi kwao ndi nkhawa zao, zimene zidzathandiza akulu ‘kuganizila’ nkhosa zimene akusamalila ndi kupeleka thandizo lofunikila.
7. Kodi zinthu “zopanda pake” zimene anthu ovutika maganizo amakamba tiyenela kuziona bwanji?
7 Paulo anauza mpingo wa ku Atesalonika kuti: “Thandizani ofooka.” (1 Atesalonika 5:14.) “Ofooka” amaphatikizapo anthu a mtima wacisoni ndi amene alefulidwa. Lemba la Miyambo 24:10, limati: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zocepa.” Munthu amene wafooka kwambili angalankhule zinthu “zopanda pake.” (Yobu 6:2, 3) Pamene tifuna kuonetsa kuti ‘timaganizila’ anthu a conco, tiyenela kukumbukila kuti nthawi zina amakamba zinthu zimene sanafunikile kukamba. Rachelle anazindikila mfundo imeneyi pamene amai ake anakhala ovutika maganizo kwambili. Iye anati: “Nthawi zambili Amai anali kulankhula zinthu zokhumudwitsa kwambili. Koma nthawi zambili io akalankhula conco, ndinali kuyesa kukumbukila makhalidwe ao abwino, amene ndi cikondi, kukoma mtima ndi kuolowa manja. Ndinazindikila kuti anthu ovutika maganizo amakamba zinthu zambili zimene sanali kufunikila kukamba. Koma munthu angalakwitse kwambili ngati abwezela mau oipa kapena kubwezela zoipa kwa anthu ovutika maganizo.” Lemba la Miyambo 19:11 limati: “Kuzindikila kumacititsa munthu kubweza mkwiyo wake, ndipo kunyalanyaza colakwa kumam’cititsa kukhala wokongola.”
8. Kodi ndani maka-maka amene tiyenela ‘kuwatsimikizila’ kuti timawakonda? Ndipo n’cifukwa ciani tiyenela kutelo?
8 Kodi tingaonetse bwanji kuti ‘timaganizila’ munthu amene akuvutika maganizo kaamba ka manyazi kapena nkhawa cifukwa ca chimo limene anacita kale-kale ngakhale kuti analapa ndi kukonza colakwaco? Ponena za munthu wina wocimwa wa ku Korinto amene analapa, Paulo analemba kuti: “Mukhululukileni ndi mtima wonse ndi kumutonthoza, kuopela kuti mwina woteleyu angamezedwe ndi cisoni cake copitilila malile. Conco ndikukudandaulilani kuti mumutsimikizile kuti mumamukonda.” (2 Akor. 2:7, 8) Malinga ndi buku lina lotanthauzila mau, liu lakuti ‘kutsimikizila’ limatanthauza “kuvomeleza, kupeleka umboni wotsimikiza, kapena kuona cinthu kukhala cofunika mwalamulo.” Sitiyenela kungoganizila cabe kuti munthu wina wake akudziŵa kuti timam’konda ndi kuti timamudela nkhawa. Munthuyo ayenela kudzionela yekha kuti timam’konda mwa mau athu ndi zocita zathu.
“TILIMBIKITSANE PA CIKONDI NDI NCHITO ZABWINO”
9. Kodi ‘kulimbikitsana pa cikondi ndi nchito zabwino’ kumatanthauzanji?
9 Paulo analemba kuti: “Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino.” Tiyenela kulimbikitsa okhulupilila anzathu kuti azionetsa cikondi ndi kucita nchito zabwino. Moto ukatsala pang’ono kuzima, timafunikila kusonkhezela nkhuni ndi kukolezela moto. (2 Tim. 1:6) Mofanana ndi zimenezi, mwacikondi tingalimbikitse abale athu kuonetsa cikondi cao kwa Mulungu ndi anzao. Kuyamikila ena mocokela pansi pa mtima n’kofunika kuti tiwalimbikitse kucita nchito zabwino.
10, 11. (a) Kodi ndani wa ife amene amafunikila kuyamikilidwa? (b) Pelekani citsanzo coonetsa mmene kuyamikila ena kungathandizile munthu amene ‘wayamba kulowela njila yolakwika.’
10 Tonse timafunikila ciyamikilo, kaya ndife ovutika maganizo kapena ai. Mkulu wina anati: “Atate anga sanandiyamikileko ngakhale kamodzi. Cotelo ndinakula ndilibe cidalilo caumwini . . . Ngakhale kuti tsopano ndili ndi zaka 50, ndimayamikila pamene anzanga andiuza kuti ndikusamalila bwino udindo wanga monga mkulu. . . . Zimene ndinakumana nazo pa umoyo wanga, zinandiphunzitsa kuti kulimbikitsa ena n’kofunika kwambili ndipo inenso ndimakonda kuyamikila ena.” Kuyamikila ena kungalimbikitse aliyense, kaya ndi mpainiya, wokalamba kapena amene walefuka.—Aroma 12:10.
11 Pamene akulu athandiza munthu amene wapatuka n’kuyamba kuyenda pa njila yolakwika, kupeleka uphungu wacikondi kwa wolakwayo ndi kumuyamikila pa zimene iye amacita bwino kungathandize kuti ayambenso kucita nchito zabwino. (Agal. 6:1) Zotelo n’zimene zinacitikila mlongo wina dzina lake Miriam. Iye analemba kuti: “Ndinavutika kwambili maganizo pamene anzanga apamtima anasiya coonadi, ndipo panthawi imodzi-modziyo atate anga anadwala matenda a kukha magazi mu ubongo. Pofuna kuthetsa vutolo, ndinayamba cibwenzi ndi mnyamata wina wakunja.” Zimenezi zinapangitsa mlongoyo kuona kuti Yehova samukonda, ndipo anaganiza zosiya coonadi. Iye anakhudzidwa kwambili pamene mkulu wina anam’kumbutsa za utumiki wake wokhulupilika umene anali kucita poyamba. Iye analola kuti akulu amuthandize kuona kuti Yehova amamukonda. Zimenezo zinam’pangitsa kuti ayambenso kukonda Yehova. Mlongoyo anathetsa cibwenzi cake ndi munthu wosakhulupilila uja ndipo anapitiliza kutumikila Yehova.
12. N’cifukwa ciani tifunikila kupewa kucititsa manyazi, kudzudzula mwankhanza ndi kuimba mlandu munthu amene tifuna kuthandiza?
12 Tiyenela kupewa kucititsa manyazi munthu wolefuka mwa kumuyelekezela ndi ena, kum’dzudzula mwankhanza cifukwa cakuti sanatsatile malamulo athu, kapena kum’pangitsa kudziona wolakwa cifukwa cakuti sakucita zambili pa utumiki wake. Kucita zimenezi kungapangitse munthuyo kuongolela mwakanthawi cabe. Koma kuyamikila wokhulupilila mnzathu ndi kum’thandiza kulimbitsa cikondi cake pa Mulungu kungakhale ndi zotsatilapo zabwino ndi zokhalitsa.—Ŵelengani Afilipi 2:1-4.
‘MUZILIMBIKITSANA’
13. Kodi kulimbikitsa ena kumaphatikizapo ciani? (Onani cithunzi-thunzi cimene cili kuciyambi kwa nkhani ino.)
13 Tiyenela ‘kulimbikitsana, ndipo tionjezele kucita zimenezi, maka-maka pamene tikuona kuti tsikulo likuyandikila.’ Kulimbikitsa ena kumaphatikizapo kuwasonkhezela kupitilizabe kutumikila Mulungu. Kulimbikitsana pa cikondi ndi nchito zabwino tingakuyelekezele ndi kusonkhezela moto umene watsala pang’ono kuzima kuti usazime kapena kuti uyake kwambili. Kulimbikitsa ena kumaphatikizapo kutonthoza anthu opsinjika maganizo. Ngati tapatsidwa mwai wolimbikitsa munthu wotelo, tiyenela kulankhula mokoma mtima ndi mofatsa. (Miy. 12:18) Ndiponso tiyenela ‘kukhala wofulumila kumva’, ndi “wodekha polankhula.” (Yak. 1:19) Ngati timvetsela mokoma mtima, tingadziŵe zinthu zimene zimacititsa Mkristu mnzathu kulefuka, ndiyeno tingakambe mau amene angamuthandize kulimbana ndi zimene zimamulefula.
14. Kodi mbale wina amene anali wozilala anathandizidwa bwanji?
14 Ganizilani mmene mkulu wina wacifundo anathandizila mbale wina amene anali wozilala kwa zaka zingapo. Pamene mkuluyo anamvetsela zokamba za m’baleyo, anazindikila kuti m’baleyo anali akali ndi cikondi cacikulu pa Yehova. M’baleyo anali kuŵelenga mwakhama magazini iliyonse ya Nsanja ya Mlonda ndi kuyesetsa kupezeka pa misonkhano nthawi zonse. Koma zocita za ena mumpingo zinamukhumudwitsa. Mkuluyo anamvetsela mwachelu pamene m’baleyo anali kulankhula koma sanamuweluziletu, ndipo mkuluyo anaonetsa kuti amadela nkhawa m’baleyo ndi banja lake. Pambuyo pake, m’baleyo anazindikila kuti anali kulola zinthu zoipa zimene zinam’citikila m’mbuyomu kumulepheletsa kutumikila Mulungu amene iye anali kukonda. Mkuluyo anapempha m’baleyo kuti apitile naye limodzi mu ulaliki. Ndi thandizo la mkuluyo, m’baleyo anayambanso kulalikila ndipo pambuyo pake anayenelela kutumikilanso monga mkulu.
15. Kodi n’ciani cimene tingaphunzile kwa Yehova pa nkhani yolimbikitsa anthu opsinjika maganizo?
15 Nthawi zina zimatenga nthawi kuti munthu wozilala acitepo kanthu pa thandizo limene tam’patsa. Tingafunikile kupitiliza kumulimbikitsa. Paulo anati: “Thandizani ofooka, khalani oleza mtima kwa onse.” (1 Ates. 5:14) Sitiyenela kuleka mwamsanga kuthandiza ofooka ngati taona kuti sakucitapo kanthu, koma tiyenela kupitiliza kuwathandiza. M’mbuyomu, Yehova anacita zinthu moleza mtima ndi atumiki ake amene nthawi zina anali kulefuka. Mwacitsanzo, Mulungu anakomela mtima Eliya ndipo anali kulemekeza maganizo ake. Yehova anapatsa mneneli ameneyo zimene anali kufunikila kuti apitilizebe kum’tumikila. (1 Maf. 19:1-18) Yehova mokoma mtima anakhululukila Davide cifukwa cakuti analapa moona mtima. (Sal. 51:7, 17) Ndiponso Mulungu anathandiza munthu amene analemba Salimo 73, atatsala pang’ono kusiya kum’tumikila. (Sal. 73:13, 16, 17) Yehova ndi wacisomo, ndipo amatikomela mtima maka-maka tikapsinjika maganizo kapena tikalefuka. (Eks. 34:6) Cifundo cake “cimakhala catsopano m’mawa uliwonse” ndipo “sicidzatha.” (Maliro 3:22, 23) Yehova amafuna kuti titsatile citsanzo cake mwa kucita zinthu mokoma mtima ndi anthu opsinjika maganizo.
LIMBIKITSANANI KUYENDABE PA NJILA YA KU MOYO
16, 17. Kodi tiyenela kukhala ndi colinga cotani pamene mapeto a dongosolo lino la zinthu akuyandikila? Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kutelo?
16 Pa akapolo 33,000 amene anatengedwa m’ndende yozunzilako anthu ya Sachsenhausen, akapolo masauzande ambili anafa. Koma Mboni za Yehova zonse zokwana 230 zimene zinali pakati pa akapolo opita kukaphedwa zinapulumuka. Cimene cinawathandiza kwambili kuti apulumuke ulendo wokaphedwa cinali cakuti anali kulimbikitsana ndi kuthandizana.
17 Masiku ano tili pa mseu wopita ku moyo. (Mat. 7:14) Posacedwapa, olambila onse a Yehova mogwilizana adzaloŵa m’dziko latsopano lolungama. (2 Pet. 3:13) Tiyeni tikhale ndi colinga cothandizana pamene tikuyenda pa njila yopita ku moyo wosatha.
[Mafunso Ophunzilila]
[Cithunzi papeji 20]
Muzigwila nchito ya ulaliki wakumunda ndi ena
[Cithunzi papeji 20]
Muzilimbikitsana pa cikondi ndi nchito zabwino
[Cithunzi papeji 21]
Sangalalani ndi maceza olimbikitsa
[Cithunzi papeji 22]
Mvetselani moleza mtima kwa munthu amene afunika cilimbikitso (Onani ndime 14 ndi 15)