Kuyankha Mafunso a m’Baibo
Kodi Mulungu ndi wotani?
Mulungu ali ndi thupi lauzimu ndipo sitingamuone. Iye analenga kumwamba, dziko lapansi ndi zamoyo zonse. Palibe amene analenga Mulungu ndipo iye alibe ciyambi. (Salimo 90:2) Mulungu amafuna kuti anthu azimufuna-funa ndi kudziŵa zeni-zeni ponena za iye.—Ŵelengani Machitidwe 17:24-27.
Mulungu ali ndi dzina limene amadziwika nalo. Tingadziŵe makhalidwe ake ena mwa kuganizila zinthu zimene anapanga. (Aroma 1:20) Koma kuti tim’dziŵe bwino Mulungu, tifunikila kuphunzila Mau ake, Baibo. Iyo imatithandiza kudziŵa kuti Mulungu ndi wacikondi.—Ŵelengani Salimo 103:7-10.
Kodi Mulungu amamva bwanji akaona kupanda cilungamo?
Mlengi wathu, Yehova, amadana ndi kupanda cilungamo. Ndipo analenga anthu m’cifanizilo cake. (Deuteronomo 25:16) N’cifukwa cake ambili a ife timadana ndi kupanda cilungamo. Si Mulungu amene amacititsa zinthu zopanda cilungamo zimene timaona. Mulungu analenga anthu ndi ufulu wosankha. Koma n’zomvetsa cisoni kuti anthu ambili amagwilitsila nchito molakwa ufulu wao wosankha ndipo amacita zinthu zoipa. Zinthu zimenezi zimapweteka kwambili mtima wa Yehova.—Ŵelengani Genesis 6:5, 6; Deuteronomo 32:4, 5.
Yehova amakonda cilungamo, ndipo sadzalekelela zoipa mpaka kale-kale. (Salimo 37:28, 29) Baibo imalonjeza kuti posacedwapa Mulungu adzathetselatu zinthu zoipa.—Ŵelengani 2 Petulo 3:7-9, 13.
Baibo imalonjeza kuti Mulungu posacedwapa adzathetsa zinthu zonse zopanda cilungamo