Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pangani Zosankha Mwanzelu Mukali Acinyamata

Pangani Zosankha Mwanzelu Mukali Acinyamata

‘Inu anyamata ndi inunso anamwali. . . . tamandani dzina la Yehova.’—SAL. 148:12, 13.

1. Kodi ndi zocitika ziti zimene Akristu acinyamata ambili akusangalala nazo?

 TIKUKHALA m’nthawi yapadela kwambili. Mosiyana ndi kale lonse, anthu mamiliyoni ambili amitundu yonse akutsatila kulambila koona. (Chiv. 7:9, 10) Acinyamata ambili akusangalala ndi zocitika zosangalatsa, pamene akuthandiza ena kumvetsetsa coonadi ca m’Baibo copulumutsa moyo. (Chiv. 22:17) Acinyamata ena amatsogoza maphunzilo a Baibo kuti athandize anthu kusangalala ndi umoyo wabwino. Ena ali yakali-yakali kufalitsa uthenga wabwino m’magawo a cinenelo cina. (Sal. 110:3; Yes. 52:7) Kodi mungacite ciani kuti mugwile nao nchito yosangalatsa imeneyi?

2. Kodi citsanzo ca Timoteyo cimasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wofunitsitsa kupatsa acinyamata maudindo? (Onani cithunzi-thunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

2 Monga wacinyamata, mungapange zosankha zimene zingakuthandizeni kuti mudzakhale ndi mipata ina yotumikila Mulungu mtsogolo. Mwacitsanzo, Timoteyo wa ku Lusitara anapanga zosankha mwanzelu. Zosankha zake zinamuthandiza kukhala mmishonale pamene anali ndi zaka pafupi-fupi 20 kapena kuposelapo. (Mac. 16:1-3) Patapita miyezi yocepa kucokela pamene Timoteyo anakhala mmishonale, Paulo anam’pempha kuti apite ku mpingo watsopano ku Tesalonika kumene abale anali kuzunzidwa mwankhanza. Paulo anakakamizika kucoka kumeneko, koma anali ndi cikhulupililo cakuti Timoteyo adzapita kukalimbikitsa abale kumeneko. (Mac. 17:5-15; 1 Ates. 3:1, 2, 6) Kodi muganiza kuti Timoteyo anamva bwanji atapatsidwa udindo umenewo?

COSANKHA COFUNIKA KWAMBILI CIMENE MUNGAPANGE

3. Kodi cosankha cofunika kwambili cimene mungapange paumoyo wanu n’citi? Nanga mungacipange liti?

3 Pamene muli wacinyamata ndi nthawi yabwino yopanga zosankha zofunika. Kodi ndi cosankha cofunika kwambili citi cimene muyenela kupanga? Ndi cosankha cotumikila Yehova. Nanga nthawi yabwino yopanga cosankha cimeneci ndi iti? Yehova akuuza acinyamata kuti ‘akumbukile Mlengi wao Wamkulu masiku a unyamata wao.’ (Mlal. 12:1) Njila yokha yabwino ‘yokumbukila’ Yehova ndiyo kum’tumikila mokwanila. (Deut. 10:12) Cosankha canu cotumikila Mulungu ndi mtima wanu wonse n’cofunika kwambili kuposa cosankha cina ciliconse cimene mungapange. Cosankhaco cidzakonza tsogolo lanu lonse.—Sal. 71:5.

4. Kuonjezela pa kutumikila Yehova, kodi n’zosankha zofunika zina ziti zimene zingakhudze utumiki wanu kwa Mulungu?

4 Cosankha canu cotumikila Yehova si cosankha cokha cimene cimakhudza tsogolo lanu. Mwacitsanzo, mwina mumaganizapo kuti kaya mudzakwatila kapena kukwatiwa, ndi kuti mudzakwatilana ndi munthu wotani, ndiponso kuti mudzagwila nchito yotani. N’zoona kuti zosankha zimenezi n’zofunika kwambili. Koma, mungacite bwino coyamba kusankha kutumikila Yehova ndi mtima wonse. (Deut. 30:19, 20) Cifukwa ninji? Cifukwa cakuti zosankha zimene tingapange, zingakhudzenso zosankha zina. Cosankha cimene mungapange, kaya ndi cokhudza cikwati kapena nchito cingakhudzenso utumiki wanu kwa Mulungu. (Yelekezelani ndi Luka 14:16-20.) Colinga canu cotumikila Mulungu cingakhudzenso zosankha zanu ponena za cikwati ndi nchito. N’cifukwa cake n’kwanzelu kuti coyamba mupange zosankha pankhani zofunika kwambili.—Afil. 1:10.

KODI MUDZACITA CIANI PAUNYAMATA WANU?

5, 6. Fotokozani mmene kupanga zosankha zabwino kumakhalila ndi zotsatilapo zabwino mtsogolo.

5 Sankhani kutumikila Yehova, ndipo dziŵani zimene iye afuna kuti mucite. Ndiyeno sankhani mmene mudzagwilitsila nchito umoyo wanu. M’bale wina wa ku Japan analemba kuti: “Pamene ndinali ndi zaka 14, ndinapita muulaliki ndi mkulu wina ndipo iye anaona kuti sindinali kusangalala ndi utumiki. Conco, mokoma mtima iye anandiuza kuti: ‘Yuichiro pita kunyumba ndipo ukasinkhe-sinkhe mofatsa zimene Yehova wakucitila.’ Nditafika kunyumba ndinacitadi zimenezo ndipo kwa masiku angapo ndinali kusinkha-sinkha ndi kupemphela. Posapita nthawi, ndinasintha mmene ndinali kuonela zinthu ndipo ndinayamba kutumikila Yehova mosangalala. Ndinayamba kukonda kuŵelenga nkhani zokhudza amishonale kenako ndinayamba kuganizila zoonjezela utumiki wanga kwa Mulungu.”

6 Yuichiro anapitiliza kunena kuti: “Ndinaganizanso zoyamba kupanga zosankha zimene zidzandithandiza kutumikila Yehova kumaiko ena mtsogolo. Mwacitsanzo, ndinasankha kosi yophunzila Cingelezi. Nditamaliza sukulu, ndinayamba nchito yaganyu yophunzitsa Cingelezi n’colinga cakuti ndicite upainiya. Pamene ndinali ndi zaka 20, ndinayamba kuphunzila Cimongoliya ndipo ndinakhala ndi mwai wocezela kagulu ka ofalitsa olankhula Cimongoliya. Pambuyo pa zaka ziŵili, m’caka ca 2007, ndinapita ku Mongolia. Pamene ndinapita muulaliki ndi apainiya ena ndinaona kuti anthu ambili anali kufunitsitsa kuphunzila coonadi. Conco ndinaganiza zosamukila kumeneko kuti ndikathandize anthuwo. Ndinabwelela ku Japan kuti ndikakonzekele. Ndakhala ndikutumikila monga mpainiya ku Mongolia kuyambila mu April 2008. Ngakhale kuti zinthu n’zovuta kuno, anthu akulandila uthenga wabwino, ndipo ndikuwathandiza kuyandikila kwa Yehova. Ndimaona kuti ndinapanga cosankha cabwino kwambili paumoyo.”

7. Kodi tiyenela kupanga zosankha zotani? Nanga Mose anatisiila citsanzo cotani?

7 Munthu aliyense ayenela kupanga cosankha ca mmene adzagwilitsila nchito umoyo wake monga mmodzi wa Mboni za Yehova. (Yos. 24:15) Sitingakuuzeni kuti mukwatile kapena ai, sitingakusankhileni munthu amene mungakwatilane naye, kapena nchito imene muyenela kugwila. Kodi mudzasankha nchito yosafuna maphunzilo apamwamba? Akristu ena acinyamata mumakhala kumadela osauka, pamene ena mumakhala ku mizinda yotukuka. Kuzungulila dziko lonse, inu acinyamata mumasiyana umunthu, maluso, cidziŵitso, zokonda ndi zimene mumakhulupilila. Mwina mumasiyana ndi acinyamata ena monga mmene Mose analili wosiyana ndi acinyamata aciheberi ku Iguputo. Ali wacinyamata, Mose anali ndi mwai wokhala m’nyumba yacifumu pamene Aheberi ena anali akapolo. (Eks. 1:13, 14; Mac. 7:21, 22) Mofanana ndi inu, ionso anali kukhala m’nthawi yapadela. (Eks. 19:4-6) Aliyense anayenela kupanga cosankha ca mmene adzagwilitsilila nchito umoyo wake. Mose anapanga cosankha cabwino.—Ŵelengani Aheberi 11:24-27.

8. Kodi ndi kuti kumene acinyamata angapeze thandizo popanga zosankha pa umoyo?

8 Yehova angakuthandizeni kupanga zosankha mwanzelu mukali acinyamata. Iye amakuphunzitsani mfundo za m’Baibo zimene mungagwilitsile nchito mosasamala kanthu ndi mmene zinthu zilili paumoyo wanu. (Sal. 32:8) Komanso makolo anu acikristu ndi akulu mumpingo angakuthandizeni kudziŵa mmene mungagwilitsile nchito mfundo zimenezo. (Miy. 1:8, 9) Tiyeni tikambitsilane mfundo zitatu za m’Baibo zimene zingakuthandizeni kupanga zosankha zabwino zimene zingakupindulitseni mtsogolo.

MFUNDO ZITATU ZA M’BAIBO ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI

9. (a) Kodi Yehova watilemekeza bwanji potipatsa ufulu wosankha? (b) Kodi mudzapindula motani ngati ‘mufuna-funa Ufumu coyamba’?

9 Funa-funani Ufumu coyamba ndi cilungamo cake. (Ŵelengani Mateyo 6:19-21, 24-26, 31-34.) Yehova anakulemekezani mwa kukupatsani ufulu wosankha nokha mmene mudzagwilitsila nchito nthawi yanu. Iye samakuuzani kuti muyenela kuthela nthawi yanu yonse kulalikila za Ufumu. Koma, Yesu anatiphunzitsa kuti tifunika kufuna-funa Ufumu coyamba. Mukamafuna-funa Ufumu coyamba, mudzakhala ndi mipata yambili ya utumiki. Mwacitsanzo, mudzakhala ndi mipata yambili yoonetsa kuti mumakonda Yehova ndi anthu. Mudzakhalanso ndi mipata yoonetsa kuti mumayamikila kwambili ciyembekezo ca moyo wosatha. Pamene musinkha-sinkha zomanga banja ndi kuyamba nchito, ganizilani ngati zosankha zanu zidzakupangitsani kuganizila kwambili zinthu zakuthupi kuposa kufuna-funa Ufumu wa Mulungu coyamba ndi cilungamo cake.

10. N’ciani cinacititsa Yesu kukhala wacimwemwe? Nanga ndi zosankha ziti zimene zidzakucititsani kukhala wacimwemwe?

10 Pezani cimwemwe potumikila ena. (Ŵelengani Machitidwe. 20:20, 21, 24, 35.) Yesu anatiphunzitsa mfundo yofunika kwambili imeneyi paumoyo. Iye anali munthu wosangalala kwambili cifukwa cakuti anali kucita cifunilo ca Atate wake osati cake. Yesu anali kusangalala kuona anthu ofatsa akulandila uthenga wabwino. (Luka 10:21; Yoh. 4:34) Mwina inunso muli ndi cimwemwe cifukwa cothandiza ena. Conco, ngati mupanga zosankha zogwilizana ndi mfundo zimene Yesu anaphunzitsa, mudzapeza cimwemwe ndipo mudzakondweletsa Yehova.—Miy. 27:11.

11. N’cifukwa ciani Baruki anasoŵa cimwemwe? Nanga Yehova anamupatsa uphungu wotani?

11 Timakhala ndi cimwemwe coculuka cifukwa cotumikila Yehova. (Miy. 16:20) Baruki, mlembi wa Yeremiya, anaiŵala mfundo imeneyi. Panthawi ina, kutumikila Yehova sikunali kum’sangalatsa. Conco Yehova anamuuza kuti: “Iwe ukufuna-funabe zinthu zazikulu. Leka kuzifuna-funa. Anthu onse ndikuwagwetsela tsoka ndipo iwe ndidzakupatsa moyo wako monga cofunkha cako kulikonse kumene ungapite.” (Yer. 45:3, 5) Kodi muganiza n’ciani cikanacititsa Baruki kukhala wacimwemwe? Kodi ndi kufuna-funa zinthu zazikulu kapena kupulumuka cionongeko ca Yerusalemu monga mtumiki wokhulupilika wa Mulungu?—Yak. 1:12.

12. Kodi Ramiro anasankha kucita ciani kuti akhale ndi cimwemwe pa umoyo wake?

12 M’bale wina amene anapeza cimwemwe potumikila ena ndi Ramiro. Iye anati: “Ndinakulila m’banja losauka m’mudzi wa ku maphili a Andes. Conco, pamene mkulu wanga ananena kuti adzandilipilila maphunzilo a ku yunivesite, ndinaona kuti unali mwai waukulu. Panthawi imeneyo, ndinali nditangobatizidwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Panthawi imodzi-modziyo, mpainiya wina anandipempha kuti ndipite kukalalikila naye ku tauni ina yaing’ono. Ndinapita kumeneko ndipo ndinaphunzila kumeta tsitsi, ndiyeno ndinatsegula malo anga ometela tsitsi kuti ndizipezako zofunika. Pamene tinali kuphunzitsa anthu Malemba, ambili analabadila. Pambuyo pake ndinagwilizana ndi mpingo umene unangokhazikitsidwa kumene ndipo unali kugwilitsila nchito cinenelo camakolo anga. Tsopano ndakhala muutumiki wa nthawi zonse kwa zaka 10. Palibe nchito iliyonse imene ingandipatse cimwemwe cofanana ndi cimene ndimakhala naco pothandiza anthu kuphunzila za uthenga wabwino m’cinenelo cao.”

13. N’cifukwa ciani inu acinyamata muyenela kutumikila Yehova mokwanila tsopano?

13 Tumikilani Yehova mosangalala mukali acinyamata. (Ŵelengani Mlaliki 12:1.) Simuyenela kuganiza kuti muyenela kupeza nchito coyamba kuti mudzatumikile Yehova mtsogolo. Mukhoza kutumikila Yehova mokwanila mukali acinyamata. Acinyamata ambili ali ndi maudindo ocepa m’banja, ndipo ali ndi thanzi ndi mphamvu cakuti angakwanitse kugwila nchito zovuta. Kodi mungakonde kum’citila ciani Yehova mukali wacinyamata? Mwina mufuna kukhala mpainiya, kapena kutumikila ku magawo a cinenelo cina. Kapenanso mukuona kuti mukhoza kucitako mautumiki ena pampingo wanu. Kaya zosankha zanu n’zotani, muyenela kugwila nchito inayake kuti muzipeza zofunika pa umoyo wa tsiku ndi tsiku. Ndiyeno mungadzifunse kuti: Kodi ndidzasankha nchito yotani ndipo nchito imeneyi imafuna maphunzilo otani?

GWILITSILANI NCHITO MFUNDO ZA M’BAIBO KUTI MUPANGE ZOSANKHA ZANZELU

14. Kodi muyenela kusamala za ciani pamene mufuna-funa nchito?

14 Mfundo zitatu za m’Baibo zimene takambilana zingakuthandizeni pamene mufuna kusankha nchito. Mosakaikila alangizi anu akusukulu amadziŵa bwino nchito zimene zili m’dela lanu. Mwina bungwe lina lake la boma lingakuuzeni nchito zimene n’zofunika kwanuko kapena ku dela limene mufuna kukatumikila. Kufunsila nzelu kwa anthu amenewa kungakhale kothandiza, koma muyenela kukhala wosamala. Anthu amene sakonda Yehova angayese kukusonkhezelani kuti mukhale ndi mzimu wokonda dziko. (1 Yoh. 2:15-17) Pamene muona zinthu za m’dzikoli, musaiwale kuti mtima wanu ungakunyengeni.—Ŵelengani Miyambo 14:15; Yer. 17:9.

15, 16. Ndani angakupatseni malangizo abwino kwambili okhudza nchito?

15 Mukadziŵa nchito zimene zimapezeka kwanuko, muyenela kupeza malangizo amene angakuthandizeni. (Miy. 1:5) Ndani angakuthandizeni kudziŵa nchito imene mungasankhe pogwilitsila nchito mfundo za m’Baibo? Mvelani anthu amene amakonda Yehova, amene amakukondani ndiponso amene amadziŵa bwino mikhalidwe yanu. Iwo adzakuthandizani kuganizila maluso amene muli nao ndiponso zolinga zanu. Mwina zimene angakuuzeni zingakuthandizeni kuganizilanso zolinga zanu. Ngati muli ndi makolo amene amakonda Yehova naonso angakuthandizeni. Ndiponso akulu mumpingo angakuthandizeni cifukwa cakuti ndi okhwima mwa kuuzimu. Mungafunsenso apainiya kapena oyang’anila oyendela cifukwa cake io anasankha kuyamba utumiki wa nthawi zonse. Kodi zinali bwanji kuti ayambe upainiya? Nanga anali kugwila nchito yanji kuti azipeza zosoŵa za paumoyo wao? Kodi apeza madalitso otani cifukwa ca utumiki wao?—Miy. 15:22.

16 Anthu amene amakudziŵani bwino angakulangizeni mwanzelu. Mwacitsanzo, bwanji ngati mufuna kuleka sukulu yasekondale cifukwa cakuti mwatopa nayo ndipo mufuna kuyamba upainiya? Munthu amene amakukondani akadziŵa kuti mukufuna kuleka sukulu angakuthandizeni kuzindikila kuti sukulu idzakuthandizani kukhala munthu wakhama pocita zinthu. Khalidwe limeneli n’lofunika kwambili ngati mufuna kutumikila Yehova kwamuyaya.—Sal. 141:5; Miy. 6: 6- 10.

17. Kodi tiyenela kupewa zosankha zotani?

17 Mtumiki aliyense wa Yehova angakumane ndi zinthu zimene zingafooketse cikhulupililo cake ndi kumupatutsa kwa Yehova. (1 Akor. 15:33; Col. 2:8) Koma nchito zina zimaika umoyo wathu wakuuzimu pangozi kuposa nchito zina. Kodi anthu ena m’dela lanu “cikhulupililo cao casweka ngati ngalawa” cifukwa cosasankha bwino nchito? (1Tim. 1:19) Mungacite bwino kupewa nchito imene ingaononge ubwenzi wanu ndi Mulungu.—Miy. 22:3.

SANGALALANI POKHALA MKRISTU WACINYAMATA

18, 19. Ngati mulibe colinga cocita upainiya pakali pano, kodi muyenela kucita ciani?

18 Ngati mufunitsitsa kutumikila Yehova, gwilitsilani nchito mwai umene iye wakupatsani pamene mukali wacinyamata. Pangani zosankha zimene zidzakuthandizani kutumikila Yehova mosangalala m’nthawi yapadela ino.—Sal. 148:12, 13.

19 Bwanji ngati pakali pano mulibe maganizo ocita upainiya? Musaleke kulimbitsa cikhulupililo canu mwa Yehova. Paulo anafotokoza zimene anacita kuti alandile dalitso la Yehova. Iye anati: “Ngati muli ndi maganizo osiyana ndi amenewa m’mbali ina iliyonse, Mulungu adzakuululilani maganizo oyenelawo. Komabe, mulimonse mmene tapitila patsogolo, tiyeni tipitilize kupita patsogolo mwa kuyenda moyenela m’njila yomweyo.” (Afil. 3:15, 16) Pitilizani kuganizila za cikondi ca Mulungu ndi malangizo ake anzelu. Kuposa wina aliyense, Yehova angakuthandizeni kupanga zosankha mwanzelu mukali acinyamata.