Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Tiyenela Kupemphela kwa Yesu?

Kodi Tiyenela Kupemphela kwa Yesu?

POSACEDWAPA, wofufuza wina anafunsa acinyamata oposa 800 ocokela m’zipembedzo 12 zosiyanasiyana, kuti akambe ngati amakhulupilila kuti Yesu amayankha mapemphelo. Acinyamata oposa 60 pelesenti anayankha kuti amakhulupililadi kuti Yesu amayankha. Ngakhale ndi conco, wacinyamata mmodzi anakamba kuti si Yesu amene amayankha mapemphelo, koma ndi “Mulungu.”

Kodi inuyo muganiza bwanji? Kodi tiyenela kupemphela kwa Mulungu kapena kwa Yesu? * Kuti tipeze yankho, coyamba tiyeni tione mmene Yesu anaphunzitsila ophunzila ake kupemphela.

KODI YESU ANATIPHUNZITSA KUTI TIYENELA KUPEMPHELA KWA NDANI?

Yesu anatiphunzitsa ndi kutionetsa kwa amene tiyenela kupemphela.

Popemphela kwa Atate wake wakumwamba Yesu anapeleka citsanzo coti tizitsatila

ZIMENE ANAPHUNZITSA: Mmodzi wa ophunzila a Yesu anamupempha kuti, “Ambuye tiphunzitseni kupemphela.” Ndiyeno Yesu anayankha kuti: “Mukamapemphela muzinena kuti ‘Atate.’” (Luka 11:1, 2) Kuonjezela apo, pa ulaliki wake wochuka wa pa phili, Yesu analimbikitsa omvela kuti azipemphela. Iye anati: “Pemphela kwa Atate wako.” Anawatsimikizilanso mwa kuwauza kuti: “Atate wanu amadziŵa zimene mukufuna musanapemphe n’komwe.” (Mateyu 6:6, 8) Pa usiku womaliza monga munthu padziko lapansi, Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Ngati mupempha ciliconse kwa Atate m’dzina langa adzakupatsani.” (Yohane 16:23) Motelo, Yesu anatiphunzitsa kupemphela kwa Atate wake, amenenso ndi Atate wathu, Yehova Mulungu.—Yohane 20:17.

CITSANZO CAKE: Yesu anapemphela mogwilizana ndi mmene anaphunzitsila ena kupemphela. Iye anapemphela kuti: “Atate ndikukutamandani pamaso pa onse, inu Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi.” (Luka 10:21) Pa cocitika cina, “Yesu anakweza maso ake kumwamba ndi kunena kuti: ‘Atate, ndikukuyamikilani kuti mwandimva.’”(Yohane 11:41) Ndipo pamene anali kufa, anapemphela kuti: “Atate ndikuikiza mzimu wanga m’manja mwanu.” (Luka 23:46) Yesu popemphela kwa Atate wake wakumwamba, amene ndi “Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi,” anapeleka citsanzo cabwino kwa onse cofunika kucitsatila. (Mateyu 11:25; 26:41, 42; 1 Yohane 2:6) Kodi ophunzila a Yesu oyambilila anamvetsela malangizo amenewa?

KODI AKRISTU OYAMBILILA ANALI KUPEMPHELA KWA NDANI?

Patangopita milungu yocepa Yesu atabwelela kumwamba, ophunzila ake anazunzidwa ndi kuopsezedwa ndi otsutsa. (Machitidwe 4:18) Iwo anapemphela kuti athandizidwe, koma kodi anapemphela kwa ndani? “Onse pamodzi anafuula kwa Mulungu mokweza mau,” ndi kupemphela kuti apitilize kuwathandiza “m’dzina la Yesu, mtumiki [wake] woyela.” (Machitidwe 4:24, 30) Conco, ophunzila a Yesu anatsatila malangizo ake pankhani ya pemphelo. Iwo anapemphela kwa Mulungu osati kwa Yesu.

Patapita zaka, mtumwi Paulo anafotokoza njila imene iye ndi anzake anapemphelela. Polembela Akristu anzake, iye anati: “Nthawi zonse tikamakupemphelelani timayamika Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu.” (Akolose 1:3) Paulo analembelanso okhulupilila anzake kuti, ‘m’dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, nthawi zonse muziyamika Mulungu, Atate wathu, pa zinthu zonse.’ (Aefeso 5:20) Mwa mau amenewa zikuonekelatu kuti Paulo analimbikitsa ena kupemphela kwa ‘Mulungu  Atate wake,’ koma m’dzina la Yesu.—Akolose 3:17.

Monga Akristu oyambilila, nafenso tingaonetse kuti timakonda Yesu potsatila malangizo ake pa nkhani ya pemphelo. (Yohane 14:15) Tikamapemphela kwa Atate wathu wakumwamba, mau apa Salimo 116:1, 2 adzaticititsa kukhala ndi cidalilo cakuti Yehova amamva mapemphelo athu, ndipo tidzamva monga mmene wamasalimo anamvela. Iye anati: “Mtima wanga ndi wodzaza ndi cikondi, cifukwa Yehova amamva mau anga, . . . Ndipo ndidzaitanila pa iye masiku onse a moyo wanga.” *

^ par. 3 Malemba amaonetsa kuti Yesu ndiponso Mulungu si olingana. Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani 4 m’buku lakuti, Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ par. 11 Kuti mapemphelo athu akhale ovomelezeka kwa Mulungu, tiyenela kuyesetsa kucita zinthu mogwilizana ndi zofuna zake. Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani 17 m’buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni