NKHANI YA PACIKUTO | BOMA LOPANDA ZIPHUPHU
Vuto la Ziphuphu za m’Boma
Ziphuphu za m’boma zimatanthauza kugwilitsila nchito udindo umene munthu ali nao m’boma kuti adzipindulitse. Vuto limeneli linayamba kalekale. Mwacitsanzo, m’Baibulo muli lamulo loletsa oweluza kulandila ziphuphu poweluza milandu, ndipo lamulo limeneli likuonetsa kuti anthu anali kucita ziphuphu zaka zoposa 3,500 zapitazo. (Ekisodo 23:8) Kucita ziphuphu sikutanthauza kulandila cabe ndalama kuti munthu umucitile cinacake. Nthawi zina akuluakulu a boma amaba katundu wa boma, ndalama, kapena kuuza anthu ena kuti awacitile zinazake zimene sayenela kuwacitila. Kuonjezela apo, ena amagwilitsila nchito udindo wao kuti acite zinthu zokondela anzao kapena abale ao.
Ngakhale kuti m’mabungwe osiyanasiyana mumacitika ziphuphu, zikuoneka kuti vuto la ziphuphu za m’boma lafika poipa kwambili. Mwacitsanzo, lipoti la mu 2013 lofalitsidwa ndi bungwe lina loona za ziphuphu linanena kuti anthu padziko lonse amaona kuti pali magulu asanu a anthu amene amacita ziphuphu kwambili. Anthu amenewa ndi andale, apolisi, akuluakulu a boma, opanga malamulo, ndi oweluza. (Transparency International) Onani malipoti ali munsimu amene akusonyeza kukula kwa vuto limeneli.
AFRICA: Mu 2013, akuluakulu a m’boma pafupifupi 22,000 ku South Africa anawapeza ndi mlandu wocita ziphuphu.
AMERICA: Mu 2012, anthu 25 ku Brazil anawapeza ndi mlandu wogwilitsila nchito ndalama za boma pokopa anthu kuti akawavotele pa masankho. Mmodzi mwa anthu amenewa anali mkulu wa asilikali, amene anali ndi udindo wapamwamba kwambili m’dzikolo kuposa onse kupatulako pulezidenti yekha.
ASIA: Mu 1995, anthu 502 anafa m’sitolo ina yaikulu mumzinda wa Seoul, ku South Korea. Ocita kafukufuku anapeza kuti akuluakulu a mumzindawo analandila ciphuphu kuti alole anthu ogwila nchito yomanga kugwilitsila nchito zipangizo zosalimba pomanga sitoloyo ndiponso kuti asatsatile malamulo a kamangidwe kovomelezeka.
EUROPE: Mmodzi wa akuluakulu a bungwe la European Commission, amai Cecilia Malmström, anakamba kuti: “Vuto limeneli [la ziphuphu] ku Europe lafika poipa kwambili.” Iwo ananenanso kuti “maboma sacita khama kuti athetse ziphuphu.”
Vuto la ziphuphu za m’boma n’lovuta kwambili kuthetsa. Pulofesa Susan Rose-Ackerman, amene ndi katswili pankhani yothetsa ziphuphu, analemba kuti “maboma angafunike kusintha kwambili mmene amacitila zinthu” kuti akwanitse kuthetsa vuto limeneli. Anthu amaona kuti ziphuphu sizingathe, koma Baibulo limaonetsa kuti zinthu zidzasintha ndipo ziphuphu zidzatha.